Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Kukhulupirika kwa Itai

Tsanzirani Kukhulupirika kwa Itai

 Tsanzirani Kukhulupirika kwa Itai

“NTCHITO zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Njira zanu ndi zolungama ndi zoona, Mfumu ya muyaya inu. Uyo amene sadzakuopani ndani, inu Yehova, ndani sadzalemekeza dzina lanu? Pakuti inu nokha ndinu wokhulupirika.” Nyimbo imeneyi inaimbidwa kumwamba ndi “amene anapambana ndi kubwerako ku chilombo chija, ku chifaniziro chake,” ndipo imanena za kukhulupirika kwa Mulungu. (Chiv. 15:2-4) Yehova amafuna kuti anthu omulambira azimutsanzira posonyeza kukhulupirika.​—Aef. 4:24.

Komano, Satana Mdyerekezi amachita chilichonse chimene angathe kuti alepheretse anthu kukonda Mulungu. Ngakhale zili choncho, atumiki ambiri a Mulungu akhalabe okhulupirika ngakhale pokumana ndi mavuto adzaoneni. Tiyenera kuyamikira Yehova chifukwa choti iye amasangalala kwambiri akaona anthu okhulupirika. Inde, Baibulo limatitsimikizira kuti: “Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa  ake.” (Sal. 37:28) Pofuna kutithandiza kukhala okhulupirika, iye anachititsa kuti nkhani za anthu ena okhulupirika zilembedwe m’Mawu ake. Imodzi mwa nkhani zoterezi ndi ya Itai Mgiti.

Anali ‘Mlendo ndi Wopitikitsidwa’

Zikuoneka kuti Itai anali wochokera mumzinda wotchuka wa Afilisti wotchedwa Gati. Kumeneku kunalinso kwawo kwa chimphona chotchedwa Goliati ndiponso adani ena oopsa a Aisiraeli. Popanda kunena za mbiri yake, Baibulo limangoyamba kunena zimene Itai anachita pofotokoza za nthawi imene Abisalomu anaukira Mfumu Davide. Itai ndi anthu 600 amene ankamutsatira anathawa kwawo n’kukakhala kudera la pafupi ndi Yerusalemu.

Zimene zinamuchitikira Itai, ziyenera kuti zinakumbutsa Davide nthawi imene anathawira kudera la Afilisiti limodzi ndi Aisiraeli 600 ankhondo. Iye anakakhala kudera limene Akisi mfumu ya Gati inkalamulira. (1 Sam. 27:2, 3) Kodi Itai ndi anthu ake anatani Davide ataukiridwa ndi mwana wake Abisalomu? Kodi iwo anakhala kumbali ya Abisalomu, ya Davide kapena sanalowerere mbali ina iliyonse?

Tangoganizirani mmene zinalili panthawiyo. Davide atathawa ku Yerusalemu, anaima pamalo otchedwa “Nyumba ya Payokha.” N’kutheka kuti nyumbayi inali yomalizira pochoka ku Yerusalemu kupita ku Phiri la Maolivi, tisanadutse chigwa cha Kidroni. (2 Sam. 15:17) Akudutsa pamenepa, Davide anawerenganso asilikali ake. Iye anadabwa atapeza kuti m’gululi munali Aisiraeli okhulupirika komanso Akereti ndi Apeleti. Panalinso Itai ndi asilikali ake okwana 600 omwe anali Agiti.​—2 Sam. 15:18.

Pamenepa, Davide anafunsa Itai kuti: “Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu [ayenera kuti amatanthauza Abisalomu]; pakuti uli mlendo ndi wopitikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha. Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe.”​—2 Sam. 15:19, 20.

Kukhulupirika kwenikweni kwa Itai kunaonekera ndi mawu amene anayankha. Iye anati: “Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena m’paimfa kapena m’pamoyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.” (2 Sam. 15:21) Pamenepa mwina Davide anakumbukira mawu a Rute, yemwe anali agogo a bambo ake. (Rute 1:16, 17) Mawu a Itai anam’khudza mtima kwambiri Davide moti anamuuza kuti: “Tiye nuoloke” chigwa cha Kidroni. Pamenepo “Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ake onse, ndi ana aang’ono onse amene anali naye.”​—2 Sam. 15:22.

“Zitilangize Ife”

Lemba la Aroma 15:4 limati: “Pakuti zonse zimene zinalembedweratu zinalembedwa kuti zitilangize ife.” Motero ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Itai?’ Taganizirani zimene mwina zinam’chititsa kukhala wokhulupirika kwa Davide. Ngakhale kuti Itai anali mlendo yemwe anapitikitsidwa kwawo kudziko la Afilisiti, iye ankadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu wamoyo ndiponso kuti Davide anali wodzozedwa Wake. Itai sanasunge mumtima chidani chimene chinalipo pakati pa Aisiraeli ndi Afilisiti. Ngakhale kuti Davide anapha Goliati, chimphona cha fuko lake la Afilisiti ndiponso Afilisiti ena ambirimbiri, Itai sankaganizira zimenezi. (1 Sam. 18:6, 7) Itai anaona kuti Davide anali munthu wokonda Yehova ndipo n’zosakayikitsa kuti anaonanso makhalidwe abwino kwambiri amene Davide anali nawo. Izi zinachititsanso kuti Davide ayambe kukonda kwambiri Itai. Ndipo Davide anapereka gawo limodzi mwa magawo atatu a asilikali ake kuti “aliyang’anire Itai” pa nkhondo yaikulu yomenyana ndi Abisalomu.​—2 Sam. 18:2.

Ifenso tiziyesetsa kusaganizira kwambiri za chikhalidwe, fuko, mtundu kapena zinthu zina zilizonse zimene zingachititse kuti tizisala kapena kudana ndi anthu ena. M’malomwake, tiziganizira kwambiri za makhalidwe abwino amene anthuwo ali nawo. Mgwirizano umene unali pakati pa Davide ndi Itai umasonyeza kuti kudziwa Yehova ndi kuyamba kum’konda kungatithandizenso kuona ena m’njira yoyenerera.

 Poganizira chitsanzo cha Itai, tingadzifunse kuti: ‘Kodi inenso ndimasonyeza kukhulupirika ngati kumeneku kwa Khristu Yesu, yemwe ndi Davide Wamkulu? Kodi ndimasonyeza kukhulupirika kwanga pochita nawo mwakhama ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira?’ (Mat. 24:14; 28:19, 20) Tingadzifunsenso kuti ‘Kodi ndingalolere kupirira zinthu zotani kuti ndisonyeze kukhulupirika kwanga?’

Mitu ya mabanja ingapindulenso kwambiri posinkhasinkha za chitsanzo cha Itai cha kukhulupirika. Zimene anachita posafuna kulekana ndi Davide ndiponso posankha kukhala m’gulu la mfumu yodzozedwa ndi Mulungu imeneyi zinakhudzanso anthu amene anali naye. Ndi mmenenso zilili ndi zinthu zimene mitu ya banja imasankha kuchita pofuna kuchirikiza kulambira koona. Nazonso zimakhudza anthu a m’banja mwawo ndipo nthawi zina zingathe kuwabweretsera mavuto ena. Komabe, Baibulo limatitsimikizira kuti: ‘Pa munthu wangwiro [kapena kuti wokhulupirika] Yehova amakhalanso wangwiro.’​—Sal. 18:25.

Pambuyo pofotokoza za nkhondo imene Davide anamenyana ndi Abisalomu, Malemba satchulapo chilichonse chokhudza Itai. Komabe, nkhani yachidule yonena za Itai, yomwe ili m’Mawu a Mulungu imatithandiza kwambiri kumudziwa bwino. Timatero poona zimene anachita pa nthawi yovuta kwambiri pa moyo wa Davide. Popeza kuti nkhani ya Itai imapezeka m’Baibulo, zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amaona ndipo amadalitsa anthu okhulupirika.​—Aheb. 6:10.