Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mapeto Ayenera Kudzakupezani Muli Kuti?

Kodi Mapeto Ayenera Kudzakupezani Muli Kuti?

 Kodi Mapeto Ayenera Kudzakupezani Muli Kuti?

KODI Yehova akamadzawononga dongosolo loipali zinthu zidzawathera bwanji anthu olungama? Lemba la Miyambo 2:21, 22 limayankha kuti: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”

Kodi zidzatheka bwanji kuti anthu angwiro adzatsale m’dziko? Kodi padzakhala malo amene adzabisaleko? Kodi anthu oongoka mtima ayenera kukhala ali kuti mapeto akamadzafika? M’Malemba muli nkhani zinayi za chipulumutso zotithandiza kuyankha mafunso amenewa.

Anapulumuka Chifukwa Chokhala Pamalo Oyenerera

Lemba la 2 Petulo 2:5-7 limafotokoza zimene zinachititsa kuti Nowa ndi Loti apulumuke. Lembali limati: “[Mulungu] anaperekanso chilango pa dziko lakale lija osalilekerera, koma anasunga Nowa, mlaliki wa chilungamo, pom’pulumutsa pamodzi ndi ena asanu ndi awiri, pamene anabweretsa chigumula padziko la anthu osaopa Mulungu. Anaweruzanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora mwa kuinyeketsa ndi moto, kuti chikhale chitsanzo cha zinthu zodzachitikira anthu osaopa Mulungu m’tsogolo. Koma anapulumutsa Loti wolungamayo, amene anavutika mtima kwambiri ndi anthu ophwanya malamulo, mwa kulowerera kwawo khalidwe lotayirira.”

Kodi Nowa anapulumuka bwanji chigumula? Mulungu anauza Nowa kuti: “Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzawononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi. Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale.” (Gen. 6:13, 14) Nowa anamanga chingalawa motsatira ndendende malangizo amene Yehova anamuuza. Kutatsala masiku 7 kuti chigumula chiyambe, Yehova anauza Nowa kuti asonkhanitse nyama kuti adzalowe nazo m’chingalawa pamodzi ndi banja lake. Masiku 7 atatha, chitseko cha chingalawacho chinatsekedwa ndipo “mvula inali pa dziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku.” (Gen. 7:1-4, 11, 12, 16) Koma Nowa ndi banja lake ‘anapulumuka pamadziwo.’ (1 Pet. 3:20) Kuti apulumuke, iwo anayenera kukhala m’chingalawacho. Panalibenso malo ena padziko lapansi amene akanapulumukirako.​—Gen. 7:19, 20.

Malangizo amene Mulungu anapatsa Nowa anali osiyana ndi amene anapatsa Loti. Angelo awiri anamuuza Loti kuti asakhale malo enaake. Angelowo anamuuza kuti iye ndiponso am’banja mwake ‘onse amene anali nawo m’mudzi wa Sodomu, atuluke.’ Anapitiriza kuti: “Popeza ife tidzawononga malo ano.” Iye ndi am’banja mwake anayenera ‘kuthawira kuphiri.’​—Gen. 19:12, 13, 17.

Nkhani ya Nowa ndi Loti imasonyeza kuti, “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye m’mayesero. Koma anthu osalungama amawasungira tsiku loweruza kuti akawawononge.” (2 Pet. 2:9) Pa nthawi zonsezi anthuwo anayenera kupezeka pamalo oyenera kuti apulumuke. Nowa anafunika kulowa m’chingalawa pomwe Loti anafunika kutuluka mu Sodomu. Koma kodi nthawi zonse malo amakhala ofunika kuti munthu apulumuke? Kodi Yehova angathe kupulumutsa anthu olungama pamalo amene ali popanda kuwauza kuti apite kumalo ena? Kuti tipeze yankho, tiyeni tione zitsanzo zinanso ziwiri za mmene Yehova anapulumutsira anthu.

Kodi Malo Amakhala Ofunika Nthawi Zonse Kuti Munthu Apulumuke?

M’nthawi ya Mose, Yehova asanalange Aiguputo ndi mliri womaliza, analamula Aisiraeli  kuti awaze magazi a nyama ya Pasika pamphuthu za nyumba zawo. N’chifukwa chiyani anatero? Anatero kuti ‘Yehova akadzapita pakatipo kukantha Aigupto; n’kuona mwaziwo pamphuthu pamwamba ndi pambali, adzapitirire pakhomopo, osalola wowononga alowe m’nyumba zawo kuwakantha.’ Usiku womwewo, “Yehova anakantha ana oyamba onse a m’dziko la Aigupto, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam’nsinga ali mkaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.” Ana onse oyamba kubadwa a Aisiraeli anapulumuka popanda kupita kumalo enaake.​—Eks. 12:22, 23, 29.

Taganiziraninso nkhani ya Rahabi, mkazi wadama amene ankakhala mumzinda wa Yeriko. Aisiraeli anali atatsala pang’ono kulanda Dziko Lolonjezedwa. Rahabi atazindikira kuti Aisiraeli akubwera kudzawononga mzinda wa Yeriko, anauza azondi awo awiri kuti mzinda wonse unali njenjenje kuopa Aisiraeliwo. Iye anabisa azondi awiriwo n’kuwauza kuti alumbire kuti adzamupulumutsa limodzi ndi abale ake akamadzawononga mzindawo. Azondiwo anauza Rahabi kuti asonkhanitse abale ake m’nyumba yake, yomwe inali palinga la mzindawo. Akanangoyerekeza kutuluka m’nyumbamo akanawonongedwa limodzi ndi anthu onse a mumzindawo. (Yos. 2:8-13, 15, 18, 19) Koma kenako Yehova anauza Yoswa kuti “linga la mudziwo lidzagwa pomwepo.” (Yos. 6:5) Malo amene azondiwo anauza Rahabi kuti abisale, tsopano anaoneka ngati osatetezeka. Ndiyeno kodi Rahabi ndi abale ake akanapulumutsidwa bwanji?

Nthawi yolanda Yeriko itafika, Aisiraeli anafuula ndiponso kuimba mphalasa. Lemba la Yoswa 6:20 limati: “Ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo.” Palibe munthu aliyense amene akanaletsa lingalo kuti lisagwe. Komabe mozizwitsa linga lonselo linagwa, kupatula mbali imene panali nyumba ya Rahabi. Yoswa anauza azondi awiri aja kuti: “Lowani m’nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kutulutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munam’lumbirira iye.” (Yos. 6:22) Anthu onse amene anali m’nyumba ya Rahabi anapulumutsidwa.

Chimene Chinali Chofunika Kwambiri

Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani za kupulumutsidwa kwa Nowa, Loti, Rahabi ndiponso Aisiraeli a m’nthawi ya Mose? Kodi nkhani zimenezi zimatithandiza bwanji kuganizira kumene tiyenera kukhala dongosolo loipali likamadzawonongedwa?

Nowa anapulumuka chifukwa choti anali m’chingalawa. Koma kodi n’chiyani chinamuchititsa kuti alowe m’chingalawamo? Iye anachita zimenezi chifukwa choti anali ndi  chikhulupiriro ndiponso anali womvera. Baibulo limati: “Nowa, monga mwa zonse anam’lamulira iye Mulungu, momwemo anachita.” (Gen. 6:22; Aheb. 11:7) Nanga bwanji ifeyo? Kodi tikuchita zonse zimene Mulungu watilamula? Nowa analinso “mlaliki wa chilungamo.” (2 Pet. 2:5) Kodi ifenso timagwira nawo ntchito yolalikira mwakhama ngakhale ngati anthu ambiri m’gawo lathu safuna kumvetsera?

Pamene mzinda wa Sodomu unkawonongedwa, Loti anathawa ndipo anapulumuka. Iye anapulumutsidwa chifukwa chakuti anali wolungama komanso ankawawidwa mumtima chifukwa cha makhalidwe oipa amene ankachitika mu Sodomu ndi Gomora. Kodi ifenso zimatiwawa mumtima tikaganizira makhalidwe oipa amene akuchitika m’dzikoli? Kapena kodi tangofika pozolowera moti sizitikhudzanso ena akamachita zoipa? Kodi tikuyesetsa kuti tidzapezedwe ‘opanda thotho, opanda chilema ndiponso tili mu mtendere’?​—2 Pet. 3:14.

Aisiraeli ku Iguputo ndiponso Rahabi ku Yeriko, anapulumutsidwa chifukwa chokhalabe m’nyumba zawo. Kuti asatuluke m’nyumbazo, iwo anafunika kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso omvera. (Aheb. 11:28, 30, 31) Taganizirani mmene zinthu zinalili panthawi ya Aisiraeli. Ayenera kuti pamene anamva “kulira kwakukulu” m’mabanja a Aiguputo ankangoyang’anitsitsa ana awo achisamba. (Eks. 12:30) N’kutheka kuti nayenso Rahabi anakumbatirana ndi banja lake lonse mwamantha ataona kuti linga la Yeriko layamba kugwa. Panthawiyi mwina iye ankaganiza kuti mbali imene kunali nyumba yake igwanso. Kuti akhalebe m’nyumbayo anafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso kukhala womvera.

Posachedwapa, dziko la Satanali lidzawonongedwa. Sitikudziwa kuti Yehova adzapulumutsa bwanji anthu ake pa “tsiku la mkwiyo” wake lomwe ndi loopsa kwambiri. (Zef. 2:3) Kaya pa nthawiyo tidzakhala tili kuti, ngati tili ndi chikhulupiriro komanso ngati timamumvera, sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatipulumutsa. Mu ulosi wake wina, Yesaya anatchula za zipinda. Ndi bwino kuti masiku ano tiziganizira mofatsa za “zipinda” zimenezi.

“Lowani M’zipinda Mwanu”

Lemba la Yesaya 26:20 limati: “Lowani m’zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.” Ulosi umenewu unakwaniritsidwa koyamba mu 539 B.C.E. pamene Amedi ndi Aperisi anagonjetsa Babulo. Polowa mu Babulo, Koresi analamula kuti anthu onse akhale m’nyumba zawo chifukwa anauza asilikali ake kuti aphe aliyense wopezeka kunja.

Masiku ano, mawu akuti “zipinda” n’kutheka kuti akuimira mipingo pafupifupi 100,000 ya Mboni za Yehova padziko lonse. Mipingo imeneyi ndi yofunika kwambiri kwa ife panopa mpaka pa “chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:14) Anthu a Mulungu akulamulidwa kuti alowe ‘m’zipinda zawo, n’kubisala kanthawi kufikira mkwiyo utapita.’ Choncho tiyenera kuona kuti mpingo wathu ndi wofunika kwambiri ndipo tizichita zonse zotheka kuti tikhalebe mumpingowo. Tiyenera kutsatira malangizo a Paulo akuti, ‘tiganizirane wina ndi mnzake, kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga chilili chizolowezi kwa ena, koma tilimbikitsane wina ndi mnzake. Tiwonjezeredi kuchita zimenezi, makamaka pamene tikuona kuti tsikulo likuyandikira.’​—Aheb. 10:24, 25.

[Zithunzi patsamba 7]

Kodi zimene Mulungu anachita m’mbuyomu populumutsa anthu zikutiphunzitsa chiyani?

[Chithunzi patsamba 8]

Kodi masiku ano “zipinda” zingaimire chiyani?