Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungakatumikire Kumene Kukufunika Ofalitsa Ufumu Ambiri?

Kodi Mungakatumikire Kumene Kukufunika Ofalitsa Ufumu Ambiri?

 Kodi Mungakatumikire Kumene Kukufunika Ofalitsa Ufumu Ambiri?

“Tinali ndi moyo wabwino kwambiri ku United States, koma tinkada nkhawa kuti mzimu wokonda zinthu zakuthupi ukanatisokoneza ifeyo ndi ana athu awiri. Ine ndi mkazi wanga tinachitapo umishonale, ndipo tinkafuna kuti tiyambirenso kukhala ndi moyo wosafuna zambiri koma wosangalatsa umenewu.”

CHIFUKWA cha chikhumbo chimenechi, m’chaka cha 1991 Ralph ndi mkazi wake Pam anaganiza zolembera makalata maofesi a nthambi angapo. Iwo anafotokoza kuti akufuna kutumikira kudera limene kukufunika ofalitsa Ufumu ambiri. Ofesi ya nthambi ya ku Mexico inawayankha kuti pakufunikira mwamsanga ofalitsa Ufumu ambiri oti azikalalikira anthu olankhula Chingelezi m’dzikolo. Ndipo ofesi ya nthambiyo inanena kuti gawolo ‘n’loyera kale ndipo n’lofunika kukolola.’ (Yoh. 4:35) Pasanapite nthawi, Ralph ndi Pam limodzi ndi ana awo aamuna awiri, wazaka 8 ndi wazaka 12, anayamba kukonzekera zosamukira ku Mexico.

Gawo Lalikulu Kwambiri

Ralph ananena kuti: “Tisanachoke ku United States, abale ndi alongo ena potiganizira, ankatiuza kuti: ‘Kusamukira kudziko lina ndi chinthu choopsa kwambiri.’ ‘Nanga bwanji mukakadwala kumeneko?’ ‘Mukudzivutitsiranji kukalalikira kugawo la Chingelezi? Anthu olankhula Chingelezi sangakachite chidwi ndi choonadi.’ Komabe ife tinali titatsimikiza kale zosamukira kumeneko. Ndiponso pamene tinkasankha zoti tisamuke, tinali titaganizira bwinobwino nkhaniyi. Tinali titakonzekera kwa zaka zambiri. Tinali titapewa kutenga ngongole zimene zikanatitengera nthawi yaitali kuti tibweze, tinasungira ndalama ndiponso tinakambirana kwambiri pabanja pathu zokhudza mavuto amene tikanatha kukumana nawo.”

Ralph ndi banja lake atafika ku Mexico, choyamba anakayendera ofesi ya nthambi. Kumeneko abale anawasonyeza mapu a dziko lonse la Mexico ndipo anawauza kuti, “Gawo lanu ndi limeneli.” Banjali linakakhala kutawuni ya San Miguel de Allende imene ili ndi anthu ambiri ochokera kumayiko ena. Tawuniyi ili kumpoto chakumadzulo kwa mzinda wa Mexico City pamtunda wa makilomita 240. Patatha zaka zitatu ali kumeneku, mpingo wa Chingelezi unakhazikitsidwa m’tawuniyo ndipo unali ndi ofalitsa 19. Umenewu unali mpingo wa Chingelezi woyamba kukhazikitsidwa ku Mexico. Koma panali ntchito yambiri yoti achite.

Ku Mexico kuli anthu pafupifupi 1 miliyoni ochokera ku United States. Kuwonjezera pamenepa, kulinso anthu ambiri antchito zapamwamba komanso ana a sukulu amene amadziwa Chingelezi. Ralph anafotokoza kuti: “Tinkapemphera kuti kubwere antchito ena ambiri. Ndipo nyumba  yathu inali ndi chipinda choti abale ndi alongo akabwera, azikhalamo ‘kuti adzazonde dzikoli,’ titero kunena kwake.”​—Num. 13:2.

Anasintha Moyo Wawo Kuti Achite Zambiri mu Utumiki

Posakhalitsa abale ndi alongo amene ankafuna kuchita zambiri mu utumiki wawo anafika. Pagulu la ofalitsa amenewa panali Bill ndi Kathy amene anachokera ku United States. Iwo anali atatumikirapo kale kwa zaka 25 kumadera omwe kunkafunika ofalitsa ambiri. Poyamba ankaganiza zoti aphunzire Chisipanishi, koma anasintha maganizo pamene anasamukira kutawuni ya Ajijic imene ili m’mphepete mwa nyanja ya Chapala, ndipo kumeneku kuli anthu ambiri amene anapuma pa ntchito ochokera ku United States. Bill ananena kuti: “Titafika ku Ajijic, tinatanganidwa ndi kufunafuna anthu olankhula Chingelezi amene ankafuna kuphunzira choonadi.” Patangotha zaka ziwiri zokha ali kumeneku, mpingo unakhazikitsidwa. Bill ndi Kathy anasangalala kwambiri kuona mpingo wa Chingelezi wachiwiri ukukhazikitsidwa ku Mexico.

Nayenso Ken ndi Joanne a ku Canada anasintha zinthu zina pa moyo wawo kuti akhale ndi nthawi yambiri yochita ntchito ya Ufumu. Iwonso anasamukira ku Mexico. Ken ananena kuti: “Zinanditengera nthawi kuti ndizolowere kukhala kudera lomwe timatha kukhala popanda madzi otentha, magetsi kapenanso foni kwa masiku angapo.” Komabe iwo ankasangalala kwambiri ndi ntchito yolalikira. Pasanapite nthawi yaitali, Ken anakhala mtumiki wothandiza ndipo patapita zaka ziwiri anakhala mkulu. Poyamba zinalinso zovuta kwa mwana wawo wamkazi, dzina lake Britanny, kuti azolowere kukhala mumpingo waung’ono wa Chingeleziwu chifukwa munali achinyamata ochepa. Komabe iye atayamba kuthandiza ntchito yomanga Nyumba za Ufumu, anapeza anzake abwino ambiri m’madera osiyanasiyana a m’dzikolo.

Patrick ndi Roxanne a ku Texas m’dziko la United States, anasangalala atamva kuti pafupi ndi kwawo, pali gawo la anthu olankhula Chingelezi lomwe limafunikira ofalitsa ambiri. Patrick ananena kuti: “Titayendera tawuni ya Monterrey yomwe ili kumpoto chakum’mawa kwa dziko la Mexico, tinaona kuti Yehova ndi amene akufuna kuti tibwere kuno kudzathandiza.” Pa masiku asanu okha, Patrick ndi Roxanne anagulitsa nyumba yawo ku Texas ndipo ‘anaolokera ku Makedoniya.’ (Mac. 16:9) Ku Mexico, zakhala zovuta kupeza zofunika pamoyo. Koma atangokhalako kwa zaka ziwiri, anasangalala kwambiri ataona kagulu ka Mboni 17 katakula n’kukhala mpingo wa ofalitsa 40.

Nayenso Jeff ndi mkazi wake Deb, anayamba kukhala moyo wosalira zambiri pofuna kuti awonjezere utumiki wawo. Iwo anagulitsa nyumba yawo yaikulu imene inali ku United States ndipo anasamukira m’kanyumba kakang’ono mumzinda wa Cancún, womwe uli m’mphepete mwa nyanja kum’mawa kwa Mexico. Ali kwawo ankachitira misonkhano m’nyumba imene munali zipangizo zoziziritsira mpweya ndipo nyumbayo inali kufupi ndi kwawoko. Koma ku Mexico, malo ochitira misonkhano ya Chingelezi ndi opanda denga ndipo iwo ankayenda ulendo wa maola 8 kuti akafike kumeneko. Koma iwo anali osangalala ataona kuti ku Cancún kwakhazikitsidwa mpingo wa ofalitsa 50.

Abale ndi alongo ena a ku Mexico nawonso anayamba kuthandiza pa ntchito yolalikira  kwa anthu olankhula Chingelezi. Mwachitsanzo, Rubén ndi banja lake anabwera kudzathandiza atamva kuti ku San Miguel de Allende kwakhazikitsidwa mpingo woyamba wa Chingelezi, womwe gawo lake linali dziko lonse la Mexico. Chifukwa cha zimenezi, iwo anaphunzira Chingelezi komanso chikhalidwe cha anthu olankhula Chingeleziwo. Ndipo mlungu uliwonse, iwo ankayenda ulendo wautali wamakilomita 800 popita kumisonkhano. Rubén ananena kuti: “Tinali osangalala kwambiri kuwalalikira anthu ochokera m’mayiko ena amene anabwera ku Mexico kuno kale kwambiri, amene pa nthawiyi kunali koyamba kumva uthenga wabwino m’chilankhulo cha kwawo. Ena ankachita kugwetsa misozi posonyeza kuyamikira.” Rubén ndi banja lake atathandiza mpingo wa ku San Miguel de Allende, anakachita upainiya m’tawuni ya Guanajuato, m’chigawo chapakati cha Mexico. Kumeneko anathandiza kuti mpingo wa Chingelezi wa ofalitsa oposa 30 ukhazikitsidwe. Tsopano akutumikira m’kagulu ka Chingelezi kamene kali m’tawuni ya Irapuato pafupi ndi Guanajuato.

Kulalikira Anthu Ovuta Kuwapeza

Ku Mexico kulinso anthu ambiri odziwa kulankhula Chingelezi kuwonjezera pa anthu ochokera kumayiko ena. Koma nthawi zambiri zimavuta kuwalalikira uthenga wa Ufumu chifukwa amakhala m’madera a anthu olemera kwambiri, ndipo nthawi zambiri timangolankhula ndi antchito awo. Nthawi zina tikakumana ndi eni nyumbazo, safuna kumvetsera uthenga wathu chifukwa amaganiza kuti Mboni za Yehova ndi kachipembedzo kampatuko ka m’dziko lomwelo. Koma ngati eni nyumbazo afikiridwa ndi Mboni zakumayiko akunja, ena amamvetsera.

Taganizirani za Gloria amene amakhala m’mzinda  wa Querétaro m’chigawo chapakati cha Mexico. Iye akufotokoza kuti: “M’mbuyomu Mboni zolankhula Chisipanishi zinkabwera kudzandilalikira koma sindinkamvetsera. Komabe pamene banja langa komanso anzanga tinakumana ndi mavuto, ndinali ndi nkhawa ndipo ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kupeza njira yothetsera mavutowo. Pasanapite nthawi, mayi wina amene ankalankhula Chingelezi anafika pakhomo pathu, ndipo anandifunsa ngati pa banja pathupo panali munthu amene amatha kulankhula Chingelezi. Ndinachita naye chidwi chifukwa anali wochokera dziko lina ndipo ndinamuuza kuti ndimalankhula Chingelezi. Pamene ankandifotokozera uthenga wakewo, mumtima mwanga ndinkaganiza kuti, ‘Kodi mayi waku America ameneyu akudzatani kwathu kuno?’ Koma popeza ndinali nditam’pempha Mulungu kuti andithandize, ndinaganiza kuti mwina Mulungu ndi amene wamutumiza poyankha pemphero langa lija.” Gloria anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anapita patsogolo mwamsanga kenako anabatizidwa ngakhale kuti ankatsutsidwa ndi achibale ake. Panopo Gloria ndi mpainiya wokhazikika ndipo mwamuna wake komanso mwana wake wamwamuna akutumikira Yehova.

Anthu Amene Amawonjezera Utumiki Wawo Amapeza Madalitso

Kutumikira kumalo amene kumafunika ofalitsa Ufumu ambiri kuli ndi mavuto ake, koma madalitso ake amakhala ambiri. Ralph, amene tamutchula poyamba uja ananena kuti: “Tinkachita maphunziro a Baibulo ndi anthu ochokera ku Britain, China, Jamaica, Sweden, ngakhalenso anthu olemera ochokera ku Ghana. Ena mwa anthu ophunzira Baibulo amenewa, anayamba utumiki wa nthawi zonse. Pa zaka zapitazi, banja langa laona mipingo 7 ya Chingelezi ikukhazikitsidwa. Ana athu onse anayamba upainiya limodzi ndi ife ndipo tsopano akutumikira pa Beteli m’dziko la United States.”

Panopo ku Mexico kuli mipingo ya Chingelezi yokwana 88 komanso magulu ambiri amene sanakhalebe mipingo. Kodi n’chiyani chathandiza kuti zinthu ziyende bwino choncho? Anthu ambiri amene amalankhula Chingelezi ku Mexico, anali asanakumanepo ndi Mboni. Ena anamvetsera choonadi chifukwa chakuti analibe anzawo amene akanawabwezera m’mbuyo ngati mmene zikanakhalira akanakhala kuti ali kwawo. Komanso ena anavomera kuphunzira Baibulo chifukwa chakuti anapuma pa ntchito, choncho anali ndi nthawi yophunzira Baibulo. Kuwonjezera pamenepa, anthu oposa theka la ofalitsa m’mipingo ya Chingelezi amachita upainiya. Ndipo zimenezi zikuthandiza kuti ofalitsa akhale achangu komanso kuti mipingoyi ikhale ndi anthu ochuluka.

Inunso Mungapeze Madalitso

Mosakayikira anthu ambiri padziko lonse angamvetsere choonadi atalalikiridwa uthenga wa Ufumu m’chilankhulo chawo. Choncho n’zolimbikitsa kuona abale ndi alongo ambiri amene akufuna kuwonjezera utumiki wawo akusamukira kumadera amene kukufunika ofalitsa Ufumu ambiri. Ena mwa ofalitsawa ndi ana, achikulire, osakwatira komanso okwatira. N’zoona kuti amakumana ndi mavuto, koma akapeza anthu achidwi amene amalandira choonadi cha m’Baibulo, iwo amasangalala kwambiri n’kuiwala mavutowo. Kodi inuyo mungathe kusintha zinthu zina pa moyo wanu kuti musamukire kudera lina m’dziko lanu lomwelo kapena dziko lina kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri? * (Luka 14:28-30; 1 Akor. 16:9) Ngati mungathe kuchita zimenezi, dziwani kuti mudzapeza madalitso ambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza kutumikira kudera limene kukufunika thandizo, onani buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, masamba 111-112.

[Bokosi patsamba 21]

Anachita Chidwi ndi Anthu Osangalala Opuma pa Ntchito

Beryl atachoka ku Britain kupita ku Canada, anakakhala bwana wa makampani akuluakulu padziko lapansi. Iye analinso katswiri wokwera mahatchi, moti m’chaka cha 1980 anakaimira dziko la Canada pa masewera a Olimpiki. Atapuma pa ntchito anakakhala ku Chapala, m’dziko la Mexico. Beryl ndi mwamuna wake ankakonda kupita kumalo odyerako alendo. Iye akapita kumeneko ankaona anthu ena osangalala kwambiri opuma pa ntchito. Iye ankawauza dzina lake ndi kuwafunsa zimene ankachita ku Mexico. Nthawi zambiri anthu osangalala amenewa ankakhala a Mboni za Yehova. Beryl ndi mwamuna wake anaganiza kuti ngati munthu chifukwa chodziwa Mulungu amakhala wosangalala ndiponso amakhala ndi cholinga m’moyo, ndiye kuti nawonso afunikira kumudziwa Mulunguyo. Atapita kumisonkhano kwa miyezi ingapo, Beryl anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa. Kenako anachita upainiya wokhazikika kwa zaka zambiri.

[Bokosi patsamba 22]

“Ndi Dalitso Kukhala ndi Anthu Amenewa”

Abale a m’mayiko amene akufunikira ofalitsa Ufumu ambiri, amayamikira kwambiri ofalitsa a m’mayiko ena amene amabwera kudzawathandiza. Mwachitsanzo ofesi ya nthambi ina ya ku Caribbean, inalemba kuti: “Abale ambirimbiri ochokera kumayiko ena amene akutumikira kuno atati abwerere kwawo, mipingo yambiri siingakhale yokhazikika monga mmene ilili pano. Ndi dalitso kukhala ndi anthu amenewa.”

Mawu a Mulungu amanena kuti “akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.” (Sal. 68:11) Choncho n’zosadabwitsa kuti pali alongo ambiri osakwatiwa amene amakatumikira kumayiko ena. Alongo odzipereka amenewa, amathandiza kwambiri. Ofesi ya nthambi ya dziko lina la kum’mawa kwa Ulaya inanena kuti: “M’mipingo yathu yambiri muli alongo ochuluka, moti m’mipingo ina amaposa theka la ofalitsa. Ambiri mwa alongowa ndi achatsopano, ndipo apainiya osakwatiwa amene anachokera m’mayiko ena amathandiza kwambiri chifukwa amaphunzitsa achatsopanowo. Alongo ochokera m’mayiko ena amenewa timawayamikira kwambiri.”

Kodi alongo amene amakatumikira m’mayiko ena amenewa amaona bwanji utumiki umenewu? Angelica yemwe ndi wazaka zoposa 30, anachitapo upainiya m’mayiko osiyanasiyana kwa zaka zambiri ali wosakwatiwa. Iye ananena kuti: “Pali mavuto ambiri. Mwachitsanzo, ndili m’dziko lina tsiku lililonse ndinkayenda movutikira m’misewu yamatope. Komanso nthawi zonse ndinkaona anthu ovutika ndipo zimenezi zinkandikhumudwitsa. Komabe ndinkasangalala kwambiri ndikamathandiza anthu muutumiki. Alongo akumeneku ankandithokoza chifukwa chobwera kudzawathandiza ndipo izi zinkandilimbikitsa kwambiri. Mlongo wina anandiuza kuti zimene ndinachita kuchoka dziko lakwathu kubwera m’dziko lawo kudzachita upainiya, zinamulimbikitsa kuti nayenso ayambe utumiki wa nthawi zonse.”

Sue, yemwe ndi mpainiya ndipo ali ndi zaka zoposa 50, ananena kuti: “Ndimakumanadi ndi mavuto koma sangafanane ndi madalitso amene ndimalandira. Utumiki umasangalatsa kwambiri. Popeza ndimakhala muutumiki nthawi yambiri ndi alongo achitsikana, ndimawafotokozera zinthu zimene ndimaphunzira m’Baibulo komanso m’mabuku athu, zimene zimandithandiza kuthana ndi mavuto. Iwo amandiuza kuti akuona kuti angathe kuthana ndi mavuto amene angakumane nawo pa moyo wawo, chifukwa amaona kuti ineyo ndimapirira mavuto amene ndakhala ndikukumana nawo pa zaka zonse zimene ndakhala ndikuchita upainiya ndili wosakwatiwa. Ndimasangalala kwambiri podziwa kuti ndikuthandiza alongo amenewa.”

[Mapu patsamba 20]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MEXICO

Monterrey

Guanajuato

Irapuato

Ajijic

Chapala

Lake Chapala

San Miguel de Allende

Querétaro

MEXICO CITY

Cancún

[Chithunzi patsamba 23]

Ena amasangalala kulalikira anthu akumayiko ena amene ndi koyamba kumva uthenga wabwino