Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Malemba amatchula za “buku la Yasari” komanso “buku la Nkhondo za Yehova.” (Yos. 10:13; Num. 21:14) Koma mabuku awiri amenewa sapezeka pa mndandanda wa mabuku ovomerezeka a m’Baibulo. Kodi amenewa ndi mabuku ouziridwa amene anasowa?

Palibe chifukwa choganizira kuti mabuku awiri amenewa anali ouziridwa koma kenako anasowa. Anthu amene analemba Baibulo mouziridwa anatchula mabuku ena angapo. Ena mwa mabukuwo angakhale mabuku amene ali m’Baibulo koma ankawatchula ndi mayina ena osiyana ndi amene ife masiku ano timawadziwa. Mwachitsanzo, lemba la 1 Mbiri 29:29 limanena za buku la “mawu a Samueli mlauli,” la “mawu a Natani mneneri” ndi la “mawu a Gadi mlauli.” Mabuku atatu onsewa angathe kukhala omwe masiku ano timawadziwa kuti 1 Samueli ndi 2 Samueli kapenanso buku la Oweruza.

Komabe, nthawi zina Malemba amatchula mabuku ena amene ali ndi mayina ofanana ndi mabuku a m’Baibulo, ngakhale kuti mabukuwo si a m’Baibulo. Chitsanzo ndi mabuku anayi akale awa: “Buku la machitidwe a mafumu a Yuda,” “buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli,” “buku la mafumu a Israyeli” ndi “buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda.” Ngakhale kuti mayina a mabukuwa angafanane ndi mayina a mabuku a m’Baibulo amene timawadziwa monga 1 Mafumu ndi 2 Mafumu, mabuku anayiwo sanali ouziridwa ndipo sali pa mndandanda wa mabuku ovomerezeka a m’Baibulo. (1 Maf. 14:29; 2 Mbiri 16:11; 20:34; 27:7) Iwo ayenera kuti anali mabuku a mbiri yakale amene analipo m’nthawi imene mneneri Yeremiya ndi Ezara ankalemba nkhani zimene zili m’Baibulo.

Ndi zoona kuti olemba Baibulo ena anatchula kapena kufufuza m’mabuku a mbiri yakale kapenanso zikalata zomwe zinalipo panthawiyo ngakhale kuti sizinali zouziridwa. Mwachitsanzo, lemba la Estere 10:2 limatchula “buku la mbiri ya mafumu a Mediya ndi Perisiya.” Nayenso Luka, mmene ankafuna kulemba nkhani yake ya Uthenga Wabwino, ‘anafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pachiyambi.’ Apa iye ayenera kuti ankatanthauza kuti, polemba mndandanda wa makolo a Yesu womwe uli mu Uthenga Wabwino umene analemba, iye anafufuza m’mabuku amene analipo panthawiyo. (Luka 1:3; 3:23-38) Ngakhale kuti mabuku amene Luka anagwiritsa ntchito pofufuza sanali ouziridwa, Uthenga Wabwino umene iye analemba ndi wouziridwa ndipo ndi wofunika kwambiri kwa ife.

Nanga bwanji za mabuku awiri amene tawatchula mu funso lija, “buku la Yasari” komanso “buku la Nkhondo za Yehova”? Zikuoneka kuti mabuku amenewa analipodi koma sanali ouziridwa. Pachifukwa chimenechi, Yehova sanakonze zoti mabukuwa asungidwe. Popeza kuti Baibulo limatchula mabuku awiri amenewa, akatswiri a Baibulo akuganiza kuti mabuku awiriwo anali a ndakatulo kapena nyimbo zofotokoza za nkhondo za Aisiraeli ndi adani awo. (2 Sam. 1:17-27) Ndipo insaikulopediya ina ya Baibulo imanena kuti m’mabuku awiri amenewa muyenera kuti munali “nyimbo zonse zodziwika za akatswiri oimba a ku Isiraeli amene anathandiza kuti ndakatulo ndi nyimbo za chikhalidwe cha Aisiraeli zisungidwe.” Ndiponso amuna ena amene Mulungu nthawi zina anawagwiritsa ntchito monga aneneri kapena amasomphenya, analemba mabuku amene Yehova sanawauzire komanso amene sanawasankhe kuwaika m’Malemba omwe ngakhale masiku ano ndi “opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu.”​—2 Tim. 3:16; 2 Mbiri 9:29; 12:15; 13:22.

Ndi zoona kuti mabuku ena anatchulidwa m’Baibulo komanso kuti mfundo zake zina anazigwiritsa ntchito, koma zimenezi zisatipangitse kuganiza kuti mabuku onsewo anali ouziridwa. Komabe, Yehova Mulungu wasunga zolemba zonse zomwe zili ndi “mawu a Mulungu wathu,” ndipo zolemba zimenezi ‘zidzakhala nthawi zachikhalire.’ (Yes. 40:8) Zoonadi, zimene Yehova anasankha kuti zikhale m’mabuku 66 a m’Baibulo limene tili nalo, ndi zokhazo zimene timafunikira kuti tikhale “okonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.”​—2 Tim. 3:16, 17.