Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Yesu Anaphunzitsa Zimatithandiza Kukhala Osangalala

Zimene Yesu Anaphunzitsa Zimatithandiza Kukhala Osangalala

 Zimene Yesu Anaphunzitsa Zimatithandiza Kukhala Osangalala

“[Yesu] anakwera paphiri; ndipo . . . ophunzira ake anabwera kwa iye. Kenako anayamba kuwaphunzitsa.”​—MAT. 5:1, 2.

1, 2. (a) Kodi zinthu zinali bwanji panthawi imene Yesu anali kulalikira pa phiri? (b) Kodi Yesu anayamba motani ulalikiwu?

M’CHAKA cha 31 C.E., Yesu anadukiza kaye ulendo wake wolalikira ku Galileya, kuti apite ku Yerusalemu kukachita mwambo wa Pasika. (Yoh. 5:1) Atabwerera ku Galileya, iye anapemphera kwa Mulungu usiku wonse kuti amutsogolere posankha atumwi ake 12. Tsiku lotsatira, khamu la anthu linasonkhana pamene Yesu anali kuchiritsa odwala. Kenako, iye anakhala pansi m’mbali mwa phiri n’kuyamba kuphunzitsa khamulo ndiponso ophunzira ake.​—Mat. 4:23–5:2; Luka 6:12-19.

2 Nkhani imene Yesu anakamba panthawiyi imatchedwa kuti ulaliki wa pa phiri. Iye anayamba kuphunzitsa anthuwo mwa kusonyeza kuti munthu amakhala wosangalala akakhala paubwenzi ndi Mulungu. (Werengani Mateyo 5:1-12.) Mawu akuti chisangalalo amatanthauza ‘kukhala ndi chimwemwe mumtima.’ Ndipo zinthu 9 zochititsa anthu kukhala osangalala zimene Yesu anatchula, zikusonyeza chifukwa chimene Akhristu amakhalira osangalala. Ngakhale kuti Yesu anaphunzitsa zinthu zimenezi zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, panopa zidakali zopindulitsa kwambiri mofanana ndi mmene zinalili panthawiyo. Tsopano tiyeni tione zinthu zimenezi, chilichonse pachokhapachokha.

“Amene Amazindikira Zosowa Zawo Zauzimu”

3. Kodi kuzindikira zosowa zathu zauzimu kumatanthauza chiyani?

3 “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.” (Mat. 5:3) “Amene amazindikira zosowa zawo zauzimu” amadziwa kuti Mulungu amafunikira kuwatsogolera ndiponso kuwachitira chifundo.

4, 5. (a) N’chifukwa chiyani anthu ozindikira zosowa zawo zauzimu amakhala osangalala? (b) Kodi tingatani kuti tisakhale osowa mwauzimu?

4 Anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu amakhala osangalala “popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.” Ophunzira oyambirira a Yesu atavomereza kuti iye ndi Mesiya, anapatsidwa mwayi wodzalamulira naye limodzi mu Ufumu wa Mulungu kumwamba. (Luka 22:28-30) Tonsefe, kaya tikuyembekezera kukalamulira ndi Khristu kumwamba kapena kudzalandira moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansili mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, tingakhale osangalala ngati timazindikira zosowa zathu zauzimu ndiponso ngati timadziwa kuti timafunikira kutsogoleredwa ndi Mulungu.

5 Si anthu onse amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, chifukwa chakuti ambiri alibe chikhulupiriro ndiponso sayamikira zinthu zopatulika. (2 Ates. 3:1, 2; Aheb. 12:16) Zina mwa zinthu zimene tingachite kuti tisakhale osowa mwauzimu ndizo kuphunzira Baibulo mwakhama, kukhala achangu pantchito yopanga ophunzira ndiponso kupezeka pamisonkhano yachikhristu nthawi zonse.​—Mat. 28:19, 20; Aheb. 10:23-25.

Omva Chisoni Koma “Osangalala”

6. Kodi anthu “amene akumva chisoni” ndani ndipo n’chifukwa chiyani amakhala “osangalala”?

6 “Osangalala ali iwo amene akumva chisoni, popeza adzasangalatsidwa.” (Mat. 5:4) Anthu “amene akumva chisoni” ndi ofanana ndi “amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” Sikuti iwo amamva chisoni kapena kuti amadandaula chifukwa cha mmene zinthu zilili pamoyo wawo, koma  chifukwa chakuti ndi opanda ungwiro ndiponso chifukwa cha mmene zinthu zaipira m’dzikoli. N’chifukwa chiyani anthu amenewa amakhala “osangalala”? Chifukwa chakuti amakhulupirira Mulungu ndi Khristu ndiponso amalimbikitsidwa pokhala paubwenzi wabwino ndi Yehova.​—Yoh. 3:36.

7. Kodi zinthu za m’dziko la Satanali tiziziona motani?

7 Kodi ifeyo patokha timamva chisoni chifukwa cha kupanda chilungamo komwe kwachuluka kwambiri m’dziko la Satanali? Kodi zinthu za m’dzikoli timaziona motani? Mtumwi Yohane analemba kuti: “Chilichonse cha m’dziko, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pamoyo wake, sizichokera kwa Atate.” (1 Yoh. 2:16) Koma kodi tingatani ngati taona kuti moyo wathu wauzimu wayamba kusokonezedwa ndi “mzimu wa dziko,” womwe ndi maganizo amphamvu amene anthu otalikirana ndi Mulungu amayendera? Zikatero, tiyenera kupemphera mwakhama, kuphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kupempha akulu kuti atithandize. Tikamachita zinthu zimenezi, zomwe zingatithandize kuyandikira kwa Yehova, iye ‘adzatitonthoza’ pa mavuto alionse amene tingakumane nawo.​—1 Akor. 2:12; Sal. 119:52; Yak. 5:14, 15.

Anthu “Ofatsa” Amakhala Osangalala Kwambiri

8, 9. Kodi kukhala munthu wofatsa kumatanthauza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani anthu ofatsa amakhala osangalala?

8 “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mat. 5:5) ‘Kufatsa’ kumene Yesu ananena palembali sikutanthauza kupusa kapena kudzichepetsa kwachinyengo. (1 Tim. 6:11) Tingasonyeze kuti ndife ofatsa ngati timachita chifuniro cha Yehova ndiponso kutsatira malangizo ake. Tingasonyezenso kuti ndife ofatsa malinga ndi zimene timachita ndi Akhristu anzathu ndiponso anthu ena. Kufatsa kotero kumagwirizana ndi malangizo a mtumwi Paulo.​—Werengani Aroma 12:17-19.

9 N’chifukwa chiyani anthu ofatsa amakhala osangalala? Chifukwa cha zimene Yesu ananena, kuti iwo “adzalandira dziko lapansi.” Iye ndi wofatsa ndipo ndi munthu woyamba kulandira dziko lapansi. (Sal. 2:8; Mat. 11:29; Aheb. 2:8, 9) Anthu “olowa ufumu anzake a Khristu,” omwenso ndi ofatsa, adzalandira naye pamodzi dziko lapansi. (Aroma 8:16, 17) Mu ulamuliro wa Ufumu wa Yesu, anthu enanso ambiri ofatsa adzalandira moyo wosatha padziko lapansi.​—Sal. 37:10, 11.

10. Kodi munthu yemwe si wofatsa angakhale ndi udindo mumpingo, nanga ubwenzi wake ndi anthu ena umakhala wotani?

10 Mofanana ndi Yesu, ifenso tiyenera kukhala ofatsa. Koma bwanji ngati ndife munthu waukali kapena wosachedwa kukwiya? Khalidwe limeneli lingachititse kuti anthu ena azitipewa. Ngati ndife m’bale ndipo tikukalamira udindo mumpingo, khalidwe limeneli lingachititse kuti tisayenerere udindowo. (1 Tim. 3:1, 3) Paulo anauza Tito kuti azikumbutsa Akhristu a ku Kerete kuti “asakhale aukali, [koma] akhale ololera, osonyeza kufatsa kwa anthu onse.” (Tito 3:1, 2) N’zoonekeratu kuti anthu ena amasangalala kwambiri ndi munthu wofatsa.

Akumva Njala ya “Chilungamo”

11-13. (a) Kodi kumva njala ndi ludzu la chilungamo kumatanthauza chiyani? (b) Kodi anthu amene ali anjala ndi ludzu la chilungamo ‘amakhuta’ motani?

11 “Osangalala ali iwo amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, popeza adzakhuta.” (Mat. 5:6) “Chilungamo” chomwe Yesu ananena palembali, chikutanthauza khalidwe lochita zinthu zoyenera  mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndiponso malamulo Ake. Wamasalmo ananena kuti mtima wake ‘unasweka ndi kukhumba’ mfundo zolungama za Mulungu. (Sal. 119:20) Kodi ifeyo timafunitsitsa chilungamo moti tinganene kuti tili ndi njala ndiponso ludzu la chilungamo?

12 Yesu ananena kuti anthu amene ali ndi njala ndiponso ludzu la chilungamo adzasangalala chifukwa “adzakhuta.” Zimenezi zinayamba kutheka pambuyo pa Pentekosite wa mu 33 C.E., chifukwa chakuti panthawiyo mzimu woyera wa Yehova unayamba ‘kupereka umboni wotsimikizika ku dzikoli wonena za . . . chilungamo.’ (Yoh. 16:8) Pogwiritsa ntchito mzimu woyerawu, Mulungu anauzira anthu kuti alembe Malemba Achigiriki Achikhristu, omwe ndi opindulitsa pa “kulangiza m’chilungamo.” (2 Tim. 3:16) Mzimu wa Mulungu umatithandizanso “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo choona.” (Aef. 4:24) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti anthu amene alapa, n’kupempha Mulungu kuti awakhululukire machimo awo kudzera mu nsembe yadipo ya Yesu, angathe kukhala olungama pamaso pa Mulungu.​—Werengani Aroma 3:23, 24.

13 Ngati tikuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, njala ndi ludzu lathu la chilungamo zidzatheratu tikadzalandira moyo wosatha m’dziko lachilungamo. Koma panopa, tiyeni tikhale otsimikiza mtima kutsatira mfundo za Yehova pamoyo wathu. Yesu anati: “Pitirizani kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo [cha Mulungu].” (Mat. 6:33) Kuchita zimenezi kudzatithandiza kukhala ndi zochita zambiri potumikira Mulungu ndiponso kukhala osangalala kwambiri.​—1 Akor. 15:58.

Anthu “Achifundo” Amakhala Osangalala

14, 15. Kodi tingasonyeze motani chifundo, ndipo n’chifukwa chiyani anthu “achifundo” amakhala osangalala?

14 “Osangalala ali iwo amene ali achifundo, popeza adzachitiridwa chifundo.” (Mat. 5:7) Anthu “achifundo” amamvera chisoni anthu ena. Yesu anathandiza anthu ambiri mozizwitsa chifukwa cha chifundo. (Mat. 14:14) Mofanana ndi Yehova, amene mwachifundo amakhululukira anthu olapa, anthu amasonyezananso chifundo akakhululukira anzawo amene awalakwira. (Eks. 34:6, 7; Sal. 103:10) Nafenso tingasonyeze chifundo mwa kuchita zimenezi komanso mwa kulankhula ndi kuchita zinthu mokoma mtima kwa anthu amene akuvutika. Njira yabwino kwambiri yosonyezera ena chifundo ndiyo kuwafotokozera mfundo za choonadi cha m’Baibulo. Yesu atamvera chifundo khamu la anthu, “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”​—Maliko 6:34.

15 Tili ndi zifukwa zomveka zotipangitsa kugwirizana ndi mfundo ya Yesu yakuti: “Osangalala ali iwo amene ali achifundo, popeza adzachitiridwa chifundo.” Tikamachitira ena chifundo, nawonso adzatichitira chifundo. Ndiponso, poweruzidwa ndi Mulungu, mwina iye angasankhe kutichitira chifundo ngati timachitira anthu ena chifundo. (Yak. 2:13) Ndi anthu achifundo okha amene angakhululukidwe  machimo awo ndiponso kulandira moyo wosatha.​—Mat. 6:15.

Anthu “Oyera Mtima” Amakhala Osangalala

16. Kodi kukhala “oyera mtima” kumatanthauza chiyani, ndipo anthu oyera mtima ‘amaona Mulungu’ motani?

16 “Osangalala ali iwo amene ali oyera mtima, popeza adzaona Mulungu.” (Mat. 5:8) Anthu “oyera mtima” amadziwika ndi zokonda, zolakalaka ndiponso zolinga zawo. Anthu otere amasonyeza “chikondi chochokera mu mtima woyera.” (1 Tim. 1:5) Tikakhala oyera mtima, ‘tidzaona Mulungu.’ Zimenezi sizikutanthauza kumuonadi Yehova, chifukwa “palibe munthu [angaone Mulungu] ndi kukhala ndi moyo.” (Eks. 33:20) Komabe, Yesu anasonyeza ndendende makhalidwe a Mulungu ndipo n’chifukwa chake iye anati: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:7-9) Pamene tikulambira Yehova padziko lapansi pano, tingathe ‘kuona Mulungu’ mwa kuona zimene akutichitira. (Yobu 42:5) Kwa Akhristu odzozedwa, kuona Mulungu kumafika pachimake akaukitsidwa n’kupatsidwa moyo wauzimu chifukwa amaonadi Atate wawo wakumwamba.​—1 Yoh. 3:2.

17. Kodi kukhala oyera mtima kumakhudza motani moyo wathu?

17 Anthu oyera mtima amakhala oyera mwamakhalidwe ndi mwauzimu ndipo amapewa kuganizira zinthu zimene Yehova amaona kuti n’zodetsedwa. (1 Mbiri 28:9; Yes. 52:11) Ngati tili oyera mtima, zonena ndi zochita zathu zidzakhala zoyera ndiponso sitingachite chinyengo chilichonse potumikira Yehova.

Anthu “Amene Adzetsa Mtendere” Amakhala Ana a Mulungu

18, 19. Kodi anthu ‘odzetsa mtendere’ amachita zinthu zotani?

18 “Osangalala ali iwo amene adzetsa mtendere, popeza adzatchedwa ‘ana a Mulungu.’” (Mat. 5:9) Anthu ‘odzetsa mtendere’ amadziwika ndi zimene amachita. Ngati tili ndi khalidwe la anthu amene Yesu ankawanena palembali, ndiye kuti ndife odzetsa mtendere ndipo ‘sitibwezera choipa pa choipa kwa wina aliyense.’ M’malomwake, ‘nthawi zonse timayesetsa kuchita chabwino kwa ena onse.’​—1 Ates. 5:15.

19 Kuti tikhale m’gulu la anthu odzetsa mtendere tiziyesetsa kuchita zinthu zodzetsadi mtenderewo. Anthu odzetsa mtendere sachita chilichonse chimene chingawononge ubwenzi wa anthu ogwirizana. (Miy. 16:28) Popeza ndife odzetsa mtendere, timayesetsa “kusunga mtendere ndi anthu onse.”​—Aheb. 12:14.

20. Kodi ndani amene ali “ana a Mulungu” panopa, ndipo ndi anthu enanso ati amene adzakhale ana a Mulungu?

20 Anthu ‘odzetsa mtendere’ amakhala osangalala chifukwa “adzatchedwa ‘ana a Mulungu.’” Akhristu okhulupirika odzozedwa anatengedwa kukhala ana a Yehova ndipo amatchedwa “ana a Mulungu.” Panopa, iwo akusangalala ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova monga ana ake chifukwa choti iwo amakhulupirira Khristu, ndiponso ndi mtima wawo wonse, amalambira “Mulungu wachikondi ndi wamtendere.” (2 Akor. 13:11; Yoh. 1:12) Nanga bwanji za “nkhosa zina” za Yesu zomwenso zimayesetsa kudzetsa mtendere? Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu adzakhala “Atate Wosatha” kwa “nkhosa zina.” Koma kumapeto kwa ulamuliro umenewu, Yesu adzadziika pansi pa Yehova ndipo anthuwa adzakhaladi ana a Mulungu.​—Yoh. 10:16; Yes. 9:6; Aroma 8:21; 1 Akor. 15:27, 28.

21. Kodi munthu ‘wokhala mwa mzimu’ amachita zinthu motani?

21 “Ngati tikukhala mwa mzimu,” anthu adzaona mosavuta kuti ndife odzetsa mtendere. Ndipo sitidzakhala anthu “oyambitsa mpikisano pakati pathu.” (Agal. 5:22-26) M’malomwake, tidzayesetsa ‘kukhala mwamtendere ndi anthu onse.’​—Aroma 12:18.

 Osangalala Ngakhale Kuti Akuzunzidwa

22-24. (a) N’chifukwa chiyani anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo amakhala osangalala? (b) Kodi tiphunzira zotani m’nkhani ziwiri zotsatirazi?

22 “Osangalala ali iwo amene azunzidwa chifukwa cha chilungamo, popeza uli wawo ufumu wa kumwamba.” (Mat. 5:10) Powonjezera pamfundo imeneyi, Yesu anati: “Osangalala muli inu pamene anthu akunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Kondwerani, lumphani ndi chisangalalo, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba; pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.”​Mat. 5:11, 12.

23 Mofanana ndi aneneri akale, Akhristu amayembekezera kunyozedwa, kuzunzidwa ndiponso kunamiziridwa zinthu zoipa “chifukwa cha chilungamo.” Koma tikakhala okhulupirikabe n’kupirira zimenezi, timakhala osangalala podziwa kuti tikusangalatsa ndiponso kulemekeza Yehova. (1 Pet. 2:19-21) Mavuto amene timakumana nawo sangatilepheretse kutumikira Yehova mosangalala, panopa ngakhalenso m’tsogolo. Tonsefe tili ndi chimwemwe chachikulu, popeza kuti ena mwa ife tikuyembekezera kukalamulira ndi Khristu mu Ufumu wakumwamba ndipo enafe tikuyembekezera kudzalandira moyo wosatha padziko lapansi pano mu ulamuliro wa Ufumuwu. Ndipo mavuto amene timakumana nawo sangathetse chimwemwe chimenechi. Madalitso amenewa amasonyeza kuti Mulungu amatikonda ndiponso kuti ndi wowolowa manja.

24 Pali zinthu zambiri zimene tingaphunzire kuchokera pa ulaliki wa pa phiri. Nkhani ziwiri zotsatirazi zili ndi mfundo zinanso zosiyanasiyana zimene Yesu Khristu anaphunzitsa. Tiyeni tione mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zimenezi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani anthu “amene amazindikira zosowa zawo zauzimu” amakhala osangalala?

• N’chifukwa chiyani anthu “ofatsa” amakhala osangalala?

• N’chifukwa chiyani Akhristu amakhala osangalala ngakhale kuti akuzunzidwa?

• Pa zinthu zimene Yesu anatchula zochititsa munthu kukhala wosangalala, ndi chiti chimene chakuchititsani chidwi kwambiri inuyo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 7]

Zinthu 9 zochititsa anthu kukhala osangalala zimene Yesu anatchula, zidakali zopindulitsa kwambiri mofanana ndi mmene zinalili panthawiyo

[Chithunzi patsamba 8]

Njira yabwino kwambiri yosonyezera chifundo kwa ena ndiyo kuwafotokozera mfundo za choonadi cha m’Baibulo