Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Sangalalani ndi Ntchito Yopanga Ophunzira

Sangalalani ndi Ntchito Yopanga Ophunzira

 Sangalalani ndi Ntchito Yopanga Ophunzira

“Choncho pitani mukapange ophunzira.”​—MAT. 28:19.

1-3. (a) Kodi anthu ambiri amamva bwanji akamachititsa maphunziro a Baibulo? (b) Kodi tikambirana mafunso otani?

M LONGO wina amene amasonkhana ndi kagulu kolankhula Chihindi ku United States analemba kuti: “Milungu 11 yapitayi, ndakhala ndikuphunzira ndi banja lina la ku Pakistan, moti pano ndife mabwenzi. Koma ndikaganiza zakuti posachedwapa banjali libwerera kwawo ku Pakistan, ndimafuna kulira. Ndimakhala ndi chisoni ndikaganizira kuti ndidzasiyana nawo komanso ndikaganizira za chisangalalo chimene ndakhala nacho powaphunzitsa za Yehova.”

2 Kodi inuyo, mofanana ndi mlongo ameneyu, munasangalalapo chifukwa chophunzira Baibulo ndi munthu wina? Yesu ndi ophunzira ake ankasangalala kwambiri ndi ntchito yopanga ophunzira. Ophunzira 70 amene Yesu anawaphunzitsa atabwera ndi lipoti losangalatsa, Yesu mwiniwakeyo “anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera.” (Luka 10:17-21) Masiku anonso, anthu ambiri amasangalala kwambiri ndi ntchito yopanga ophunzira. Mwachitsanzo, mu 2007, ofalitsa akhama ndiponso osangalala ankachititsa maphunziro a Baibulo 6.5 miliyoni mwezi uliwonse.

3 Koma ofalitsa ena analibe chisangalalo chimene chimabwera chifukwa chophunzitsa munthu Baibulo. Mwina enanso papita zaka asanachititse phunziro. Kodi tingakumane ndi mavuto otani pamene tikuyesetsa kuti tichititse phunziro la Baibulo? Kodi tingagonjetse bwanji mavutowo?  Ndipo kodi timapeza madalitso otani tikamachita zonse zomwe tingathe kuti timvere lamulo la Yesu lakuti: “Pitani mukapange ophunzira”?​—Mat. 28:19.

Mavuto Amene Angatilepheretse Kusangalala

4, 5. (a) Kodi m’madera ena padzikoli anthu ambiri amalabadira bwanji uthenga wathu? (b) Kodi ndi mavuto otani omwe ofalitsa m’madera ena amakumana nawo?

4 M’madera ena padzikoli, anthu amakonda kwambiri mabuku athu ndipo amafunitsitsa kuti tiziphunzira nawo Baibulo. Banja lina la ku Australia, limene linatumikira kwakanthawi ku Zambia, linalemba kuti: “Zimene anthu amanena ndi zoona. Zambia ndi dziko labwino kwambiri kulalikira. Ulaliki wa mumsewu umakhala wosangalatsa kwambiri. Anthu amachita kubwera okha, ndipo ena amachita kutchula magazini amene akufuna.” Chaka china posachedwapa, abale ndi alongo ku Zambia anachititsa maphunziro a Baibulo oposa 200,000. Zimenezi zikutanthauza kuti wofalitsa mmodzi anachititsa maphunziro a Baibulo oposa pa limodzi.

5 Koma m’madera ena, ofalitsa amavutika kugawira mabuku ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo mokhazikika. N’chifukwa chiyani? Nthawi zambiri anthu sapezeka pakhomo, ndipo anthu amene amapezeka sachita chidwi ndi zachipembedzo. Mwina sachita chidwi chifukwa anakulira m’mabanja osapembedza kapena amanyansidwa ndi chinyengo chimene amaona m’zipembedzo zonyenga. Anthu ambiri ndi ovulala mwauzimu, okalikakalika ndipo atayidwa ndi abusa onyenga. (Mat. 9:36) M’pomveka kuti anthu ngati amenewa salola chisawawa kukambirana za Baibulo.

6. Kodi ena amalimbana ndi mavuto otani?

6 Ofalitsa ena okhulupirika amakumana ndi vuto lina lomwe lingawalepheretse kusangalala. Ngakhale kuti panthawi ina anali olimbikira pantchito yopanga ophunzira, panopa akulephera kuchita zambiri chifukwa cha matenda kapena ukalamba. Palinso maganizo amene tingakhale nawo amene angatilepheretse kupanga ophunzira. Mwachitsanzo, kodi mumaona kuti simungathe kuchititsa phunziro la Baibulo? Mwina mungaganize choncho, ngati mmene Mose anaganizira pamene Yehova anamuuza kuti apite kukalankhula ndi Farao. Mose anati: “Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale.” (Eks. 4:10) Kuwonjezera pa maganizo akuti simungakwanitse, palinso maganizo oopa kulephera. Tingade nkhawa kuti mwina munthuyo sadzakhala wophunzira chifukwa chakuti sindife mphunzitsi waluso. Poopa zimenezi, tingaganize zopewa kuchititsa phunziro. Kodi tingatani kuti tilimbane ndi mavuto tatchulawa?

Konzekeretsani Mtima Wanu

7. Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Yesu kuchita utumiki?

7 Choyamba, tiyenera kukonzekeretsa mtima wathu. Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mu mtima.” (Luka 6:45) Chimene chinalimbikitsa Yesu kuchita utumiki ndi mtima wofuna kuthandiza ena. Mwachitsanzo, ataona kuti Ayuda anzake anali ovutika kwambiri mwauzimu, “anawamvera chisoni.” Iye anauza ophunzira ake kuti: “Zokolola n’zochuluka . . . Pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.”​—Mateyo 9:36-38.

8. (a) Kodi ndi bwino kuganizira chiyani? (b) Kodi zimene wophunzira Baibulo wina ananena zikutiphunzitsa chiyani?

8 Tikamagwira ntchito yopanga ophunzira, ndi bwino kuganizira kwambiri za mmene ifeyo tapindulira chifukwa chakuti wina anapatula nthawi kuti atiphunzitse Baibulo. Tiziganiziranso za anthu amene tikumane nawo muutumiki ndi mmene angapindulire akamva uthenga wathu. Mayi wina analembera kalata ofesi ya nthambi ya dziko limene akukhala. Iye anati: “Ndati ndikuuzeni kuti ndimayamikira kwambiri a Mboni amene amabwera kunyumba kwathu kudzandiphunzitsa. Ndikudziwa kuti nthawi zina mwina amatopa nane chifukwa cha mafunso anga ambirimbiri ndiponso chifukwa chakuti ndimawachedwetsa kubwerera kwawo. Koma iwo amaleza mtima ndipo amafunitsitsa kundiuza zimene aphunzira. Ndikuthokoza Yehova ndi Yesu chifukwa chodziwana ndi anthu amenewa.”

9. Kodi Yesu anaika maganizo ake onse pa chiyani, ndipo tingamutsanzire bwanji?

9 Komatu si onse amene analabadira zimene  Yesu anali kuphunzitsa. (Mat. 23:37) Ena anamutsatira kwakanthawi koma kenako sanagwirizane ndi ziphunzitso zake ndipo “sanayendenso naye.” (Yoh. 6:66) Komabe, Yesu sanalole kusalabadira kwa anthu ena kumuchititsa kuganiza kuti uthenga wake ndi wopanda phindu. Ngakhale kuti zambiri mwa mbewu zimene anafesa sizinabale zipatso, Yesu anaika maganizo ake onse pa zabwino zimene iye anali kuchita. Iye anaona kuti m’minda mwayera ndipo m’mofunika kukolola ndiponso anasangalala kwambiri kuthandiza pantchito yokololayo. (Werengani Yohane 4:35, 36.) M’malo mongoyang’ana mbali yosabala zipatso ya munda, kodi si bwino kuika maganizo athu onse pa mbali yomwe ingabale zipatso m’gawo lathu? Tiyeni tikambirane mmene tingakhalire ndi maganizo abwino ngati a Yesu.

Pofesa, Muzikhala ndi Cholinga Chodzakolola

10, 11. Kodi mungatani kuti musasiye kusangalala?

10 Mlimi akamafesa mbewu, amakhala ndi cholinga choti adzakolole. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo, tifunika kulalikira ndi cholinga choti tiyambitse maphunziro a Baibulo. Nanga bwanji ngati nthawi zonse mukapita muutumiki wakumunda, mumapeza anthu ochepa panyumba zawo kapena zimaoneka kuti mumalephera kupezanso anthu pamaulendo anu obwereza? Zimenezi zingakhale zokhumudwitsa kwambiri. Koma kodi zikatero, ndiye kuti muyenera kusiya utumiki wa khomo ndi khomo? Ayi, simuyenera kutero. Anthu ambiri akupezekabe m’njira imeneyi yomwe yakhala ikugwiritsidwa ntchito kwa nthawi yaitali.

11 Kuti musasiye kusangalala, bwanji osapeza njira zinanso zolalikirira kuti muzipeza anthu? Mwachitsanzo, kodi mwayesapo kulalikira anthu m’misewu kapena kuntchito kwawo? Kodi n’zotheka kuimbira anthu foni kapena kupempha manambala a foni kwa anthu amene munawauzapo uthenga wa Ufumu kuti mupitirize  kumakambirana nawo? Mwa kuchita khama ndi kukhala wotha kusintha muutumiki, mudzasangalala kupeza anthu amene adzalabadira uthenga wa Ufumu.

Zimene Tingachite Ngati Anthu Sachita Chidwi

12. Kodi tingatani ngati anthu ambiri a m’gawo lathu amaoneka kuti sachita chidwi?

12 Bwanji ngati anthu ambiri m’gawo lanu sachita chidwi ndi zachipembedzo? Kodi mungasinthe ulaliki wanu kuti ugwirizane ndi nkhani zimene amakonda? Mtumwi Paulo analembera okhulupirira anzake ku Korinto kuti: “Kwa Ayuda ndinakhala ngati Myuda . . . Kwa anthu opanda chilamulo ndinakhala ngati wopanda chilamulo . . . Ngakhale zili choncho, sikuti ndine wopanda chilamulo kwa Mulungu.” Kodi cholinga cha Paulo chinali chiyani? Iye anati: “Ndakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana, kuti mulimonse mmene zingakhalire ndipulumutsepo ena.” (1 Akor. 9:20-22) Kodi nafenso sitingapeze nkhani zimene anthu a m’gawo lathu angachite nazo chidwi? Anthu ambiri omwe sapembedza amafuna kuti mabanja awo aziyenda bwino. Mwinanso angakhale akufunafuna kudziwa cholinga cha moyo. Bwanji osalalikira uthenga wathu wa Ufumu m’njira yakuti anthu amenewa achite nawo chidwi?

13, 14. Kodi tingatani kuti tizisangalala kwambiri ndi tchito yopanga ophunzira?

13 Ofalitsa ambiri akusangalala kwambiri ndi ntchito yopanga ophunzira, ngakhale m’madera omwe anthu ambiri amaoneka kuti alibe chidwi. Kodi zimenezi zatheka bwanji? Zatheka chifukwa chakuti iwo aphunzira chinenero china. Mwamuna wina ndi mkazi wake a zaka za m’ma 60 anaona kuti ana a sukulu ambiri a ku China ndi achibale awo anali kukhala m’gawo la mpingo wawo. Mwamunayo anati: “Titaona zimenezi, tinalimbikitsidwa kuphunzira chinenero cha Chitchaina. Ngakhale kuti tsiku lililonse tinkathera nthawi yochuluka kuphunzira chilankhulochi, pamapeto pake tinasangalala kwambiri chifukwa tinayambitsa maphunziro a Baibulo ambiri ndi anthu olankhula Chitchaina a m’dera lathu.”

14 N’kutheka kuti simungakwanitse kuphunzira chinenero china. Ngati ndi choncho, mungagwiritse ntchito kabuku kakuti, Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse mukakumana ndi anthu olankhula chinenero china. Popita muutumiki, mungamatengenso mabuku a chinenero chimene anthuwo amalankhula. N’zoona kuti pamafunika nthawi ndiponso khama kuti mulankhule ndi anthu achinenero ndi chikhalidwe china. Koma musaiwale mfundo ya m’Mawu a Mulungu yakuti: “Wobzala mowumira adzakololanso zochepa; ndipo wobzala mowolowa manja adzakololanso zochuluka.”​—2 Akor. 9:6.

Ntchitoyi Ndi ya Mpingo Wonse

15, 16. (a) N’chifukwa chiyani ntchito yopanga ophunzira ndi ya mpingo wonse? (b) Kodi okalamba amathandiza bwanji?

15 Kunena zoona, kupanga ophunzira sikudalira khama la munthu mmodzi. M’malo mwake kumadalira mpingo wonse. Chifukwa chiyani? Chifukwa cha zimene Yesu ananena, kuti: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yoh. 13:35) Ndipo ndi zoonadi chifukwa pamene ophunzira Baibulo afika pamisonkhano, amachita chidwi ndi chikondi chimene timasonyeza. Wophunzira Baibulo wina analemba kuti: “Ndimasangalala kwambiri kufika pamisonkhano. Anthu ake amakulandira bwino kwambiri.” N’zoona kuti Yesu anati anthu amene amakhala otsatira ake angatsutsidwe ndi achibale awo. (Werengani Mateyo 10:35-37.) Komabe iye analonjeza kuti mumpingo anthuwa adzapeza “abale ndi alongo ndi amayi ndi ana” auzimu ambiri.​—Maliko 10:30.

16 Abale ndi alongo okalamba amagwira ntchito yaikulu yothandiza ophunzira Baibulo kupita patsogolo. M’njira yotani? Ngakhale kuti ena mwa okalambawa sangathe kuchititsa phunziro la Baibulo, ndemanga zawo zolimbikitsa pamisonkhano yampingo zimalimbitsa chikhulupiriro cha ena onse. Chifukwa choyenda “m’njira ya chilungamo,” iwo amawonjezera kukongola kwa mpingo ndipo amachititsa kuti anthu amitima yabwino alowe m’gulu la Mulungu.​—Miy. 16:31.

Kuthetsa Mantha

17. Kodi tingachite chiyani kuti tithetse maganizo akuti sitingakwanitse kuchititsa phunziro?

17 Nanga bwanji ngati mumaganiza kuti simungakwanitse  kuchititsa phunziro la Baibulo? Kumbukirani kuti Yehova anathandiza Mose mwa kumupatsa mphamvu ya mzimu woyera komanso kumupatsa m’bale wake Aroni kuti azimuthandiza. (Eks. 4:10-17) Yesu analonjeza kuti mzimu wa Mulungu udzatithandiza pantchito yathu. (Mac. 1:8) Ndiponso Yesu anatumiza anthu awiriawiri kukagwira ntchito yolalikira. (Luka 10:1) Choncho ngati zimakuvutani kuchititsa phunziro la Baibulo, pemphani Mulungu kuti akupatseni mzimu wake woyera kuti mukhale anzeru. Ndipo kenaka pezani munthu woyenda naye muutumiki amene angakuthandizeni kukhala wolimba mtima komanso amene luso lake lingakuthandizeni. N’zolimbitsa chikhulupiriro kudziwa kuti Yehova anasankha kugwiritsa ntchito “zofooka za dziko,” kapena kuti anthu wamba, pantchito yofunika kwambiri imeneyi.​—1 Akor. 1:26-29.

18. Kodi tingatani kuti tithetse maganizo oopa kulephera?

18 Kodi tingathetse bwanji maganizo oopa kulephera? Tiyenera kukumbukira kuti kupanga ophunzira sikuli ngati kuphika chakudya. Kuti chakudya chipse kapena ayi zimadalira wophikayo, koma kupanga ophunzira kumadalira mbali zitatu. Yehova ndi amene amagwira ntchito yaikulu chifukwa ndi amene amakoka munthuyo kuti abwere kwa iye. (Yoh. 6:44) Ife ndi anthu ena mumpingo timayesetsa kuphunzitsa mwaluso kuti tithandize wophunzirayo kupita patsogolo. (Werengani 2 Timoteyo 2:15.) Ndipo wophunzirayo amafunikira kuchitapo kanthu pa zimene waphunzira. (Mat. 7:24-27) Ngati munthu wasiya kuphunzira Baibulo zimakhumudwitsa chifukwa timafuna kuti ophunzira Baibulo asankhe mwanzeru. Komabe, tisaiwale kuti munthu aliyense “adzadziyankhira yekha kwa Mulungu.”​—Aroma 14:12.

Madalitso a Ntchito Yopanga Ophunzira

19-21. (a) Kodi ndi madalitso otani amene timalandira tikamachititsa maphunziro a Baibulo? (b) Kodi Yehova amaona bwanji anthu onse amene amachita ntchito yolalikira?

19 Kuchititsa maphunziro a Baibulo kumatithandiza kuti tiike maganizo athu onse pa Ufumu choyamba. Komanso kumatithandiza kuti choonadi cha Mawu a Mulungu chizike mizu m’mitima ndi m’maganizo mwathu. N’chifukwa chiyani tikutero? Mpainiya wina dzina lake Barak anati: “Kuchititsa maphunziro a Baibulo kumakupangitsa kuti uziwerenga kwambiri Mawu a Mulungu. Ndimaona kuti ndiyenera kumvetsa bwino mfundo zomwe ndikukaphunzitsa ena kuti ndikawaphunzitse mogwira mtima.”

20 Ngati mulibe phunziro la Baibulo, kodi zikutanthauza kuti utumiki wanu ndi wopanda phindu kwa Mulungu? Ayi ndithu. Yehova amayamikira kwambiri khama lathu pomutamanda. Anthu onse amene amagwira nawo ntchito yolalikira ndi “antchito anzake a Mulungu.” Komabe, kuchititsa phunziro la Baibulo kumathandiza kuti tikhale osangalala kwambiri tikamaona Mulungu akukulitsa mbewu imene tinabzala. (1 Akor. 3:6, 9) Mpainiya wina dzina lake Amy anati: “Ukamaona wophunzira Baibulo akupita patsogolo, umathokoza kwambiri Yehova chifukwa chokugwiritsa ntchito kupatsa munthuyo mphatso yamtengo wapatali, yomwe ndi mwayi wodziwa Yehova ndiponso wodzalandira moyo wosatha.”

21 Kuyesetsa kwambiri kuyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo kumatithandiza kuika maganizo athu onse pa kutumikira Mulungu panopa ndiponso kumalimbitsa chiyembekezo chathu chopulumuka kulowa m’dziko latsopano. Ndi dalitso la Yehova, tingathandizenso kupulumutsa anthu amene amamvetsera uthenga wathu. (Werengani 1 Timoteyo 4:16.) Zimenezitu zingakhale zosangalatsa kwambiri.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ndi mavuto otani omwe angalepheretse anthu ena kuchititsa maphunziro a Baibulo?

• Kodi tingachite chiyani ngati anthu ambiri m’gawo lathu amaoneka kuti alibe chidwi?

• Kodi ndi madalitso otani amene timalandira tikamachititsa phunziro la Baibulo?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 9]

Kodi mumayesa njira zinanso zolalikirira kuti mupeze anthu amaganizo oyenerera?