Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’

‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’

 ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’

“Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo tsiku ndi tsiku, ndi kunditsatira.”​—LUKA 9:23.

1, 2. (a) Kodi Yesu anapereka pempho lotani? (b) Kodi inuyo munavomera pempho la Yesu?

KUMAPETO kwa utumiki wake, Yesu anali kulalikira ku Pereya, tsidya lina la Yorodano kumpoto cha kum’mawa kwa Yudeya. Ali kumeneko, mnyamata wina anamufunsa zimene angachite kuti akapeze moyo wosatha. Yesu ataona kuti mnyamatayo anali kutsatira Chilamulo cha Mose mokhulupirika, anamupempha mwapadera, kuti: “Pita, kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndi kupatsa ndalamazo osauka, pamenepo chuma udzakhala nacho kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.” (Maliko 10:21) Tangoganizirani kupemphedwa kuti mutsatire Yesu, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu Wam’mwambamwamba.

2 Mnyamatayu anakana pempho la Yesu, koma ena anavomera. M’mbuyomo Yesu anali atauza Filipo kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” (Yoh. 1:43) Filipo anavomera ndipo anakhala mtumwi. Yesu anapemphanso Mateyo, ndipo naye anavomera. (Mat. 9:9; 10:2-4) Yesu anaperekanso pempho lomweli kwa anthu onse okonda chilungamo pamene anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo tsiku ndi tsiku, ndi kunditsatira mosalekeza.” (Luka 9:23) Choncho aliyense angakhale wotsatira wa Yesu ngati akufunadi. Kodi ndi zimene inu mukufuna? Ambiri a ife tavomera kale pempho la Yesu, ndipo muutumiki wa kumunda, timapemphanso anthu kutsatira Yesu.

3. Kodi tingapewe bwanji kutengeka pang’onopang’ono mpaka kusiya kutsatira Yesu?

3 Koma ndi zomvetsa chisoni kuti anthu ena amene amasonyeza chidwi pa choonadi cha m’Baibulo sapitiriza. Iwo amayamba kufooka ndipo m’kupita kwa nthawi, ‘amatengeka pang’onopang’ono’ mpaka kusiya kutsatira Yesu. (Aheb. 2:1) Kodi tingapewe bwanji msampha umenewu? Tingachite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Kodi n’chifukwa chiyani ndinasankha kutsatira Yesu? Kodi kutsatira Yesu kumatanthauza chiyani?’ Kukumbukira mayankho a mafunso awiri amenewa kungatithandize kuti tisasiye njira yabwino imene tinasankha. Kungatithandizenso kulimbikitsa ena kutsatira Yesu.

N’chifukwa Chiyani Timatsatira Yesu?

4, 5. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ali woyenera kutitsogolera?

4 Mneneri Yeremiya ananena kuti: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yer. 10:23) Mbiri ya anthu yasonyeza kuti mawu a Yeremiya amenewa ndi oona. Ndipo panopa zikuonekera kwambiri kuti anthu opanda ungwiro sangathe kudzilamulira okha. Tinavomera pempho la Yesu lakuti timutsatire chifukwa tinaphunzira kuti iye ndi woyenerera kukhala Mtsogoleri wathu kuposa munthu wina aliyense. Tsopano tiyeni tikambirane zina mwa ziyeneretso za Yesu.

5 Choyamba, Yesu anasankhidwa ndi Yehova mwiniwakeyo kukhala Mesiya Mtsogoleri. Kodi alipo amene angadziwe kusankha woyenerera kukhala Mtsogoleri wathu kuposa Mlengi wathu? Chachiwiri, Yesu ali ndi makhalidwe osiririka amene tingatengere. (Werengani Yesaya 11:2, 3.) Iye ndi chitsanzo changwiro. (1 Pet. 2:21) Chachitatu, Yesu amakonda kwambiri anthu amene amamutsatira, ndipo anasonyeza zimenezi pamene anapereka moyo wake chifukwa cha iwo. (Werengani Yohane 10:14, 15.) Iye amasonyeza kuti ndi m’busa wachikondi chifukwa amatitsogolera kuti tikhale ndi moyo wosangalatsa panopa ndipo akutitsogolera kuti tidzakhale ndi moyo wosatha waulemerero. (Yoh. 10:10, 11; Chiv. 7:16, 17) Pazifukwa zimenezi ndi zinanso, sitinalakwitse pamene tinasankha kumutsatira. Koma kodi kutsatira Yesu kumatanthauza chiyani?

6. Kodi kutsatira Yesu kumatanthauza chiyani?

 6 Kukhala otsatira a Khristu kumatanthauza zambiri osati kungonena kuti ndife Akhristu. Masiku ano anthu pafupifupi 2 biliyoni amadzitcha kuti ndi Akhristu, koma zochita zawo zimasonyeza kuti iwo ndi “anthu osamvera malamulo.” (Werengani Mateyo 7:21-23.) Anthu akachita chidwi ndi pempho lakuti atsatire Yesu, timawafotokozera kuti Akhristu oona amatsatira ziphunzitso za Yesu ndi chitsanzo chake pamoyo wawo watsiku ndi tsiku. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tikambirane zina mwa zinthu zimene tikudziwa ponena za Yesu.

Tengerani Nzeru za Yesu

7, 8. (a) Kodi nzeru ndi chiyani, nanga n’chifukwa chiyani Yesu anali ndi nzeru zochuluka? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali ndi nzeru, ndipo tingamutsanzire bwanji?

7 Yesu anali ndi makhalidwe ambiri apadera koma tikambirana anayi okha: nzeru zake, kudzichepetsa kwake, changu chake ndi chikondi chake. Choyamba tiyeni tikambirane za nzeru zake. Nzeru ndi luso logwiritsa ntchito zimene munthu ukudziwa ndiponso luntha lako pochita zinthu zopindulitsa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwa [Yesu], chuma chonse cha nzeru ndi kudziwa zinthu chinabisidwa mosamala.” (Akol. 2:3) Kodi nzeru zimenezi Yesu anazitenga kuti? Iye anati: “Ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.” (Yoh. 8:28) Nzeru zake zinachokera kwa Yehova, choncho sitidabwa ndi kaganizidwe kozama ka Yesu.

8 Mwachitsanzo, Yesu anaganiza mozama posankha zochita pamoyo wake. Iye anasankha kukhala ndi zinthu zochepa n’cholinga chakuti maganizo ake akhale pa chinthu chimodzi: Kuchita chifuniro cha Mulungu. Iye anagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zake mwanzeru kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu. Timatsatira chitsanzo cha Yesu mwa kuyesetsa kukhala ndi ‘diso lolunjika chimodzi,’ ndipo mwa kuchita zimenezi timapewa kudzilemetsa ndi zinthu zosafunika kwenikweni zimene zingawononge mphamvu zathu kapena zimene zingatisokoneze maganizo. (Mat. 6:22) Akhristu ambiri apeza njira zochepetsera zina ndi zina pamoyo wawo n’cholinga chakuti azithera nthawi yochuluka muutumiki. Ena ayamba upainiya. Ngati inunso mwachita zimenezo, mwachita bwino kwambiri. “Kufuna ufumu choyamba” kumabweretsa chimwemwe chachikulu.​—Mat. 6:33.

Khalani Odzichepetsa Ngati Yesu

9, 10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kudzichepetsa?

9 Mbali yachiwiri ya umunthu wa Yesu imene tikambirane ndiyo kudzichepetsa. Nthawi zambiri anthu opanda ungwiro akapatsidwa udindo, amayamba kudzikuza. Zimenezitu ndi zosiyana kwambiri ndi mmene Yesu analili. Ngakhale kuti ali ndi udindo waukulu pokwaniritsa cholinga cha Yehova, iye sanadzikuze ngakhale pang’ono. Ndipo ifeyo tikulimbikitsidwa kutengera kudzichepetsa kwake. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo. Ngakhale kuti iye anali ndi maonekedwe a Mulungu, kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande. Sanatero ayi, koma anakhuthula zonse za mwa iye n’kukhala ngati kapolo, nakhala wofanana ndi anthu.” (Afil. 2:5-7) Kodi zimenezi zinatheka bwanji?

10 Yesu anali ndi mwayi wapadera wokhala kumwamba limodzi ndi Atate wake, koma ‘anadzikhuthula.’ Moyo wake unasamutsidwira m’mimba mwa namwali wachiyuda, ndipo anapitiriza kukula kwa miyezi 9. Kenako anabadwira m’banja la Yosefe, kalipentala wosauka, monga kamwana kodalira ena kukateteza. M’nyumbayi, Yesu pang’ono  ndi pang’ono anakula n’kuyamba kuyenda, kuthamanga mpaka kufika pa unyamata. Iye analibe uchimo. Ngakhale zinali choncho, iye nthawi zonse ankamvera makolo ake opanda ungwiro ndi ochimwa. (Luka 2:51, 52) Ukutu kunali kudzichepetsa kwambiri.

11. Kodi tingatengere kudzichepetsa kwa Yesu pazinthu ziti?

11 Timatengera kudzichepetsa kwa Yesu pamene timalola kugwira ntchito zimene zimaoneka ngati zonyozeka. Mwachitsanzo, taganizirani za ntchito yolalikira uthenga wabwino. Ntchito imeneyi ingaoneke ngati yonyozeka, makamaka ngati anthu sakulabadira, akutinyoza kapena kutikwiyira. Komabe tikapitiriza kulalikira, timathandiza anthu ena kulabadira pempho la Yesu lakuti amutsatire. Tikatero, timathandiza kupulumutsa miyoyo ya anthu. (Werengani 2 Timoteyo 4:1-5.) Chitsanzo china ndi ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu. Ntchito imeneyi ingaphatikizepo zinthu monga kutaya zinyalala, kukolopa ndi kuyeretsa zimbudzi, zomwe ndi ntchito zooneka ngati zonyozeka zofuna kudzichepetsa. Ngakhale zili choncho, timadziwa kuti tikamakonza Nyumba ya Ufumu, omwe ndi malo athu olambirira, timakhala tikuchita utumiki wopatulika. Ngati timadzipereka kugwira nawo ntchito zooneka ngati zonyozeka zimenezi, timasonyeza kudzichepetsa ndipo timatsatira mapazi a Khristu.

Khalani Achangu Ngati Yesu

12, 13. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji changu chake, ndipo n’chiyani chimene chinamulimbikitsa kuchita zimenezo? (b) Kodi n’chiyani chimene chingatilimbikitse kuti tikhale achangu muutumiki?

12 Tsopano tiyeni tikambirane changu chimene Yesu anali nacho muutumiki. Iye ali padziko lapansi, anachita zinthu zambiri. Chakumayambiriro kwa moyo wake, ayenera kuti ankagwira ntchito ya ukalipentala ndi bambo ake omulera a Yosefe. Pautumiki wake, Yesu anachita zozizwitsa monga kuchiritsa odwala ndi kuukitsa akufa. Koma ntchito yake yaikulu inali yolalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa anthu ofuna kumvetsera. (Mat. 4:23) Monga otsatira ake, tilinso ndi ntchito yomweyo. Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo chake? Tingatero ngati tili ndi zifukwa zofanana ndi zimene Yesu anali nazo pochita ntchito imeneyi.

13 Chinthu chachikulu chimene chinalimbikitsa Yesu kulalikira ndi kuphunzitsa anthu, chinali chikondi chake pa Mulungu. Komanso iye anakonda mfundo za choonadi zimene anali kuphunzitsa. Iye ankaona choonadi kukhala chuma chamtengo wapatali, ndipo ankakonda kugawira ena. Ifenso monga ‘aphunzitsi a anthu,’ tili ndi mtima womwewo. Tangoganizirani mfundo zina za choonadi zamtengo wapatali zimene taphunzira kuchokera m’Mawu a Mulungu. Timadziwa bwino za nkhani ya woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndi mmene idzathere.  Timadziwanso zimene Malemba amaphunzitsa pa zimene zimachitika munthu akamwalira ndi madalitso amene adzakhalapo m’dziko latsopano la Mulungu. Kaya mfundo zimenezi taziphunzira panopa kapena tinaziphunzira kalekale, siziguga. Kunena zoona, mfundo za choonadi zakale kapena zatsopano ndi chuma chamtengo wapatali. (Werengani Mateyo 13:52.) Tikamalalikira ndi mtima wonse, timasonyeza anthu kuti timakonda zimene Yehova watiphunzitsa.

14. Kodi tingatsanzire bwanji kaphunzitsidwe ka Yesu?

14 Taganiziraninso mmene Yesu ankaphunzitsira. Nthawi zonse akamalankhula ndi omvera ake, ankagwiritsa ntchito Malemba. Pofuna kutchula mfundo yofunika, iye kawirikawiri ankayamba ndi mawu akuti: “Malemba amati.” (Mat. 4:4; 21:13) Malinga ndi mawu ake amene analembedwa, iye anagwira malemba kapena kungotchula mfundo ya malemba, ndipo anatchula malemba oposa theka la malemba onse a m’mabuku a Malemba Achiheberi. Mofanana ndi Yesu, timadalira kwambiri Baibulo muutumiki wathu ndipo timayesetsa kuwerenga Malemba ngati n’kotheka. Mwa kuchita zimenezi, timathandiza anthu amaganizo oyenera kuona okha kuti timaphunzitsa maganizo a Mulungu osati athu. Timasangalala kwambiri munthu wina akavomera kuwerenga Baibulo ndi kukambirana naye za ubwino wa Mawu a Mulungu ndi zimene amatanthauza. Ndipo anthu otere akavomera pempho lakuti akhale otsatira a Yesu, timakhala ndi chimwemwe chosaneneka.

Kutsatira Yesu Kumatanthauzanso Kukonda Ena

15. Kodi khalidwe lapadera limene Yesu ali nalo ndi lotani, ndipo tikamaliganizira limatikhudza bwanji?

15 Mbali yomaliza ya umunthu wa Yesu imene tikambirane ndi yosangalatsa kwambiri. Mbali imeneyi ndi chikondi chake pa anthu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikondi chimene Khristu ali nacho chitikakamiza.” (2 Akor. 5:14) Tikamaganizira za chikondi chimene Yesu ali nacho pa anthu onse komanso pa wina aliyense wa ife, timakhudzidwa mtima ndipo timakakamizika kutsatira chitsanzo chake.

16, 17. Kodi Yesu anasonyeza chikondi chake kwa ena m’njira zotani?

16 Kodi Yesu anasonyeza bwanji chikondi chake kwa ena? Njira yoposa imene Yesu anasonyezera chikondi chake inali kupereka moyo wake chifukwa cha anthu onse. (Yoh. 15:13) Komabe pochita utumiki wake, Yesu anasonyezanso chikondi m’njira zina. Mwachitsanzo, anamvera chisoni anthu amene anali kuvutika. Ataona Mariya ndi anthu ena akulira chifukwa cha imfa ya Lazaro, iye anakhudzidwa kwambiri ndi chisoni cha anthuwo. Ngakhale kuti anali atatsala pang’ono kuukitsa Lazaro, Yesu anakhudzidwa kwambiri mpaka “anagwetsa misozi.”​—Yoh. 11:32-35.

17 Chakumayambiriro kwa utumiki wa Yesu, munthu wina wakhate anamufikira ndi kunena kuti: “Mukangofuna, mukhoza kundiyeretsa.”  Kodi Yesu anatani? Baibulo limati: “Anagwidwa chifundo.” Kenako anachita chinthu chodabwitsa. “Anatambasula dzanja lake nam’khudza, ndi kumuuza kuti: ‘Ndikufuna. Khala woyera.’ Nthawi yomweyo khatelo linachoka, ndipo anakhala woyera.” Malinga ndi Chilamulo cha Mose, anthu akhate anali odetsedwa, ndipo Yesu akanatha kuchiritsa munthuyo popanda kumukhudza. Koma pochiritsa wakhateyo mwa kumukhudza, Yesu anapatsa mwayi munthu wakhateyo womva mmene zimakhalira munthu wina akakukhudza. Ndipo mwina aka kanali koyamba kwa munthu ameneyu kukhudzidwa ndi wina. Chimenechitu chinali chifundo chachikulu.​—Maliko 1:40-42.

18. Kodi tingatani kuti tikhale “omverana chisoni”?

18 Monga otsatira a Khristu, timauzidwa kusonyeza chikondi mwa kukhala “omverana chisoni.” (1 Pet. 3:8) Zingakhale zovuta kumvetsa mmene wokhulupirira mnzathu yemwe akudwala matenda aakulu kapena kuvutika maganizo kwambiri akumvera, makamaka ngati zimenezo sizinatichitikirepo. Komabe, Yesu ankamvera chisoni anthu odwala ngakhale kuti iye sanadwalepo. Mofanana ndi Yesu, kodi ifeyo tingatani kuti tizimvera chisoni anthu ena? Tizimvetsera moleza mtima anthu amene akuvutika akamatiuza zakukhosi kwawo. Tingadzifunsenso kuti, ‘Ndikanakhala ine, kodi ndikanamva bwanji?’ Tikamayesetsa kudziwa mmene ena akumvera, tidzatha ‘kulankhula molimbikitsa kwa a mtima wachisoni.’ (1 Ates. 5:14) Tikatero, tidzakhala tikutsatira Yesu.

19. Kodi chitsanzo cha Yesu chimatikhudza bwanji?

19 Kunena zoona, timaphunzira zinthu zambiri zosangalatsa pa zimene Yesu Khristu ananena ndi kuchita. Tikamaphunzira zambiri zokhudza Yesu, m’pamenenso timafunitsitsa kukhala ngati iyeyo ndipo m’pamenenso timafunitsitsa kuthandiza ena kuti akhale ngati Yesu. Choncho, tiyeni tonse tizisangalala potsatira Mfumu Mesiya mpaka muyaya.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi tingasonyeze bwanji nzeru ngati mmene Yesu anachitira?

• Kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa?

• Kodi tingatani kuti tikhale achangu muutumiki?

• Kodi tingatsanzire bwanji Yesu posonyeza chikondi kwa ena?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 5]

BUKU LATSOPANO LIMENE LINGATITHANDIZE KUTSANZIRA KHRISTU

Pamsonkhano wachigawo wa 2007, panatuluka buku lamasamba 192 lachingelezi lakuti “Come Be My Follower.” Buku latsopanoli linalembedwa kuti lithandize Akhristu kuphunzira za Yesu, makamaka makhalidwe ake ndi zochita zake. Pambuyo pa mitu iwiri yoyambirira, chigawo choyamba chimafotokoza makhalidwe apadera a Yesu monga kudzichepetsa, kulimba mtima, nzeru, kumvera ndi kupirira.

Zigawo zotsatira zimafotokoza zimene Yesu anachita monga mphunzitsi ndiponso monga mlaliki wa uthenga wabwino komanso njira zina zimene anasonyezera kukula kwa chikondi chake. M’buku lonseli, muli mfundo zothandiza Mkhristu kutsanzira Yesu.

Tikukhulupirira kuti buku latsopanoli litithandiza tonse kudzifufuza bwinobwino ndi kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikutsatiradi Yesu? Kodi ndingamutsatire bwanji mosamalitsa?’ Lithandizanso “onse amene [ali] ndi maganizo oyenerera moyo wosatha” kukhala otsatira a Khristu.​—Mac. 13:48.

[Chithunzi patsamba 4]

Yesu analola kubwera padziko lapansi ndi kudzabadwa ngati khanda. Kodi panafunika khalidwe lotani kuti achite zimenezi?

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi n’chiyani chingatilimbikitse kuti tikhale achangu muutumiki?