Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Yehova Akuyankhira Pemphero Lochokera Pansi Pamtima

Mmene Yehova Akuyankhira Pemphero Lochokera Pansi Pamtima

 Mmene Yehova Akuyankhira Pemphero Lochokera Pansi Pamtima

“Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”​—SAL. 83:18.

1, 2. Kodi anthu ambiri amamva bwanji akadziwa dzina la Mulungu, nanga tingafunse mafunso otani?

ZAKA zingapo zapitazo, mayi wina anakhudzidwa kwambiri ndi ngozi imene inachitika m’dera limene amakhala. Popeza anabadwira m’banja la Chikatolika, iye anapita kwa wansembe kuti akamulimbikitse, koma wansembeyo sanafune n’kulankhula naye komwe. Ndiye mayiyo anapemphera kwa Mulungu kuti: “Sindikukudziwani . . . , koma ndikudziwa kuti muliko. Ndithandizeni kuti ndikudziweni.” Patapita nthawi pang’ono, kunyumba kwake kunabwera Mboni za Yehova zimene zinamulimbikitsa ndi kumuthandiza kudziwa zimene amafuna kudziwazo. Anaphunziranso kuti Mulungu ali ndi dzina lake, lomwe ndi Yehova. Kuphunzira zimenezi kunamusangalatsa kwambiri. Iye anati: “Ameneyu ndiye Mulungu amene ndakhala ndikufuna kumudziwa kuyambira ndili wamng’ono.”

2 Umu ndi mmene anthu ambiri amamvera akaphunzira dzina la Mulungu. Nthawi zambiri amaona koyamba dzina lakuti Yehova akawerenga lemba la Salmo 83:18. M’Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, lembali limati: “Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” Kodi mumadziwa chifukwa chake Salmo 83 linalembedwa? Kodi n’chiyani chingachititse kuti aliyense adziwe kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona? Kodi salmo limeneli lingatiphunzitse chiyani masiku ano? Tikambirana zimenezi m’nkhani ino. *

Anachitira Chiwembu Anthu a Yehova

3, 4. Kodi Salmo 83 linalembedwa ndi ndani, ndipo anafotokoza kuti Aisiraeli anakumana ndi vuto lotani?

3 Malinga ndi timawu tapamwamba, Salmo 83 ndi ‘nyimbo ya Asafu.’ Wolemba salmoli ayenera kuti anali mbadwa ya Asafu Mlevi, yemwe anali katswiri poimba nyimbo m’nthawi ya Mfumu Davide. Wamasalmo ameneyu anapempha Yehova kuti achite zinthu zotsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira ndiponso kuti anthu adziwe dzina lake. Salmoli liyenera kuti linalembedwa Solomo atamwalira. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa nthawi imene Davide ndi Solomo ankalamulira, mfumu ya ku Turo inali paubwenzi ndi Aisiraeli. Koma panthawi imene Salmo 83 limalembedwa, anthu a ku Turo anali atadana ndi Aisiraeli ndipo iwo ankagwirizana ndi adani awo.

 4 Wamasalmo ameneyu anatchula mitundu khumi imene inkafuna kuchitira anthu a Mulungu chiwembu. Mitundu ya adani imeneyi inali m’madera ozungulira Isiraeli ndipo iye anaitchula motere: “Mahema a Edomu ndi a Aismayeli; Moabu ndi Ahagara; Gebala ndi Amoni ndi Amaleki; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala m’Turo. Asuri anaphatikana nawo.” (Sal. 83:6-8) Kodi salmo limeneli limanena za chiyani? Ena amati limanena za nthawi imene Aisiraeli anaukiridwa ndi mitundu ya a Amoni, Amoabu, ndi anthu a m’phiri la Seiri m’nthawi ya Yehosafati. (2 Mbiri 20:1-26) Enanso amati Salmoli limanena za nthawi yonse imene Aisiraeli ankavutitsidwa ndi adani awo.

5. Kodi Salmo 83 limathandiza bwanji Akhristu masiku ano?

5 Mulimonse mmene zinthu zinalili, Yehova Mulungu ndiye anauzira kuti salmoli lilembedwe panthawi imene mtundu wake unaukiridwa ndi adani. Salmoli limalimbikitsanso atumiki a Mulungu masiku ano, amene nthawi ndi nthawi akhala akukumana ndi mavuto oyambitsidwa ndi adani awo omwe amafuna kuwawononga. Salmoli lidzatilimbikitsanso kutsogoloku panthawi imene Gogi wa ku Magogi adzasonkhanitsa magulu ake ankhondo n’cholinga chakuti awononge onse amene amalambira Mulungu mu mzimu ndi m’choonadi.​—Werengani Ezekieli 38:2, 8, 9, 16.

Chimene Chinkamudetsa Nkhawa Kwambiri Wamasalmo

6, 7. (a) M’mawu oyamba a Salmo 83, kodi wamasalmo ankapempha chiyani? (b) Kodi n’chiyani chimene wamasalmo ankada nacho nkhawa kwambiri?

6 Taonani mmene wamasalmo anafotokozera maganizo ake m’pemphero. Iye anati: “Mulungu musakhale chete; musakhale du, osanena kanthu, Mulungu. Pakuti taonani, adani anu aphokosera: Ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu. Apangana mochenjera pa anthu anu, . . . pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi; anachita chipangano cha pa Inu.”​—Sal. 83:1-3, 5.

7 Kodi n’chiyani chinkamudetsa nkhawa kwambiri wamasalmoyu? Ayenera kuti ankadera nkhawa kwambiri za moyo wake ndi wabanja lake. Komabe, mfundo yaikulu ya m’pemphero lake inali yokhudza mmene anthu ankanyozera dzina la Yehova ndiponso mmene ankawopsezera mtundu wodziwika ndi dzina lake. Ndi bwino kuti tonse tikhale ndi maganizo amenewa pamene tikupirira mavuto a m’masiku otsiriza a dziko lakale lino.​—Werengani Mateyo 6:9, 10.

8. Kodi mitundu ina inkachitira chiwembu Aisiraeli chifukwa chiyani?

8 Wamasalmoyu anagwira mawu amene adani a Aisiraeli ankanena akuti: “Tiyeni tiwawononge asanakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Isiraeli lisakumbukikenso.” (Sal. 83:4) Anthu amenewa ankadana kwambiri ndi anthu osankhidwa a Mulungu. Koma anali ndi chifukwa chinanso chimene ankadera Aisiraeli. Iwo ankasirira dziko la Isiraeli n’kumati: “Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu.” (Sal. 83:12) Kodi zoterezi zikuchitikanso masiku ano? Inde zikuchitika.

“Pokhala Panu Poyera”

9, 10. (a) Kodi kale malo oyera okhalamo Mulungu anali chiyani? (b) Kodi otsalira odzozedwa ndi a “nkhosa zina” ali ndi madalitso otani?

9 Kale, Dziko Lolonjezedwa linkatchedwa malo oyera okhalamo Mulungu. Kumbukirani nyimbo imene Aisiraeli anaimba atapulumutsidwa kuchoka ku Iguputo yakuti: “Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawawombola; mwa mphamvu yanu mudawalondolera njira yakumka pokhala panu poyera.” (Eks. 15:13) Kenako pamalo ‘okhala’ amenewa panali kachisi ndi ansembe ake. Likulu lake linali Yerusalemu ndipo mafumu ake omwe ankakhala pa mpando wachifumu wa Yehova ankasankhidwa kuchokera mu mzera wa Davide. (1 Mbiri 29:23) N’chifukwa chake Yesu anatchula Yerusalemu kuti ndi “mzinda wa Mfumu yaikulu.”​—Mat. 5:35.

10 Nanga bwanji masiku ano? Mu 33 C.E., mtundu watsopano womwe ndi “Isiraeli wa Mulungu,” unabadwa. (Agal. 6:16) Mtundu umenewu, womwe ndi wopangidwa ndi abale odzozedwa a Yesu Khristu, unachita ntchito imene Isiraeli wakuthupi analephera kuchita. Ntchito  imeneyi inali yochitira umboni dzina la Mulungu. (Yes. 43:10; 1 Pet. 2:9) Yehova anapanga nawo pangano lofanana ndi limene anapangana ndi Isiraeli wakale lakuti: “Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.” (2 Akor. 6:16; Lev. 26:12) Mu 1919, Yehova anayanja otsalira a “Isiraeli wa Mulungu” amenewa, ndipo panthawi imeneyi iwo anakhala mu “dziko,” lomwe ndi paradaiso wauzimu. (Yes. 66:8) Kuyambira m’ma 1930, anthu mamiliyoni ambiri a “nkhosa zina” agwirizana nawo. (Yoh. 10:16) Chisangalalo ndi chuma chauzimu chimene Akhristu ali nacho masiku ano ndi umboni wamphamvu wakuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. (Werengani Salmo 91:1, 2.) Komatu zimenezi zimam’kwiyitsa kwambiri Satana.

11. Kodi cholinga chachikulu cha adani a Mulungu n’chotani?

11 M’nthawi yonse ya mapeto ino, Satana wakhala akulimbikitsa anthu ake kuti azitsutsa otsalira odzozedwa ndi anzawo a nkhosa zina. Zimenezi zinachitika kumadzulo kwa Ulaya mu ulamuliro wa chipani cha Nazi ndiponso kum’mawa kwa Ulaya mu ulamuliro wa chikomyunizimu wa dziko la Soviet Union. Zinachitikanso m’mayiko ena ambiri, ndipo zidzachitikanso, makamaka panthawi imene Gogi wa Magogi adzaukire anthu a Mulungu komaliza. Panthawi imeneyi anthu otsutsa adzalanda katundu ndi chuma cha anthu a Yehova monga mmene akhala akuchitira m’mbuyomu. Komabe, nthawi zonse cholinga chachikulu cha Satana n’chakuti atifafanize kuti dzina limene Mulungu watipatsa lisadzamvekenso. Kodi Yehova amatani ndi anthu onyoza ulamuliro wake? Taganiziraninso mawu a wamasalmo aja.

Zimene Zikusonyeza Kuti Yehova Adzapambana

12-14. Kodi wamasalmo analemba kuti Aisiraeli anapambana nkhondo ziwiri ziti pafupi ndi mzinda wa Megido?

12 Taonani kuti wamasalmo ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova adzalepheretsa zolinga za adani ake. Iye analemba za nkhondo ziwiri zikuluzikulu zimene Aisiraeli anagonjetsa adani awo pafupi ndi mzinda wakale wa Megido, womwe unali m’chigwa chomwe chinkatchedwanso kuti Megido. M’nthawi ya chilimwe, mtsinje wonse wa Kisoni unkaoneka bwinobwino mmene wayendera m’chigwachi. Koma m’nthawi ya mvula, mtsinjewu unkasefukira m’chigwa chonse cha Megido. Mwina n’chifukwa chake mtsinjewu umatchedwanso kuti “madzi a Megido.”​—Ower. 4:13; 5:19.

13 Phiri la More linali pa mtunda wa makilomita 15 kuchokera mu mzinda wa Megido. M’nthawi ya woweruza Gidiyoni, magulu a Amidyani, Aamaleki, ndi anthu akum’mawa anasonkhana pamalo amenewa kuti amenyane ndi Aisiraeli. (Ower. 7:1, 12) Gulu la nkhondo la Gidiyoni linali ndi asilikali 300 okha, koma Yehova anawathandiza kugonjetsa adani awo ambiriwo. Kodi anawagonjetsa bwanji? Mulungu anawauza kuti azungulire msasa wa adani awo usiku atanyamula mbiya zomwe anaikamo miuni. Iwo anatsatira malangizo amenewa ndipo Gidiyoni atawapatsa chizindikiro, asilikaliwo anaphwanya mbiyazo ndipo nthawi yomweyo miuni ija inaonekera. Ndiyeno anayamba kuimba malipenga awo n’kufuula kuti: “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.” Adani awowo anasokonezeka ndipo anayamba kuphana okhaokha. Anthu amene anapulumuka anathawa ndi kuwoloka mtsinje wa Yorodano. Aisiraeli ena ambiri anathamangitsa nawo adaniwo. Adani onse omwe anaphedwa pankhondoyi analipo 120,000.​—Ower. 7:19-25; 8:10.

14 Phiri la Tabori linali pa mtunda wa makilomita  6 kuchokera ku phiri la More kudutsa m’chigwa cha Megido. Nthawi ina Woweruza Balaki anasonkhanitsa ankhondo okwana 10,000 pamalo amenewa kuti amenyane ndi asilikali a Yabini, mfumu ya Akanani ya ku Hazori, omwe ankatsogozedwa ndi Sisera, mkulu wankhondo. Gulu la nkhondo la Akanani limeneli linali ndi magaleta ankhondo okwana 900, okhala ndi zikwakwa zachitsulo ku mawilo awo. Magulu ankhondo a Aisiraeli omwe analibe zida zambiri atasonkhana pa phiri la Tabori, asilikali a Sisera anathamangira ku chigwa chimenechi. Kenako, “Ambuye anawononga Sisera, ndi magareta onse ndi gulu lankhondo lonse.” Zikuoneka kuti mvula imene inagwa mwadzidzidzi inachititsa kuti magaletawa atitimire pamene mtsinje wa Kisoni unasefukira. Gulu lonse la nkhondo linaphedwa ndi Aisiraeli.​—Ower. 4:13-16; 5:19-21.

15. (a) Kodi wamasalmo anapempha kuti Yehova achite chiyani? (b) Kodi dzina la nkhondo yomaliza ya Mulungu limatikumbutsa chiyani?

15 Wamasalmo anapempha Yehova kuti achite zimene anachitira mitundu imene inawopseza Aisiraeli. Iye anapemphera kuti: “Muwachitire monga munachitira Midyani; ndi Sisera, ndi Jabini ku mtsinje wa Kisoni. Amene anawonongeka ku Endoro; anakhala ngati ndowe ya kumunda.” (Sal. 83:9, 10) N’chifukwa chake nkhondo yomaliza pakati pa Mulungu ndi dziko la Satana imatchedwa kuti Aramagedo kapena Haramagedo (kutanthauza “Phiri la Megido”). Dzina limeneli limatikumbutsa za nkhondo zikuluzikulu zimene zinachitika pafupi ndi phiri limeneli. Kupambana kwa Yehova pankhondo zakale zimenezi kumatitsimikizira kuti iye adzapambananso pa Aramagedo.​—Chiv. 16:13-16.

Pempherani Kuti Yehova Asonyeze Kuti Iye Ndiye Woyenera Kulamulira

16. Kodi nkhope za adani ‘zachititsidwa manyazi’ motani masiku ano?

16 M’nthawi yonse ya “masiku otsiriza” ano, Yehova walepheretsa njira zonse za adani zofuna kuwononga anthu ake. (2 Tim. 3:1) Chifukwa cha zimenezi, anthu otsutsa achita manyazi. Lemba la Salmo 83:16 linaneneratu zimenezi kuti: “Achititseni manyazi pankhope pawo; kuti afune dzina lanu, Yehova.” M’mayiko ambiri adani alephera mochititsa manyazi kuletsa ntchito ya Mboni za Yehova. M’mayiko amenewa, kukhulupirika ndi kupirira kwa anthu amene amalambira Mulungu woona, kwakhala umboni kwa anthu a mitima yabwino ndipo ambiri ayamba ‘kufuna dzina la Yehova.’ M’mayiko ochuluka omwe Mboni za Yehova zinazunzidwa kwambiri, kuli Mboni zambirimbiri zomwe zikutamanda Yehova mosangalala. Umenewu ndi umboni wakuti Yehova wapambana ndiponso wakuti adani ake alephera mochititsa manyazi.​—Werengani Yeremiya 1:19.

17. Kodi n’chiyani chidzachitike kutsogoloku, ndipo tidzakumbukira chiyani posachedwapa?

17 Tikudziwa kuti nkhondo siinathe. Choncho tipitirizabe kulalikira uthenga wabwino, ngakhale kwa anthu omwe ndi adani athu. (Mat. 24:14, 21) Komabe, mwayi umene adani amenewa ali nawo wakuti alape ndi kupulumutsidwa, utha posachedwapa. Kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kupulumutsidwa kwa anthu. (Werengani Ezekieli 38:23.) Mitundu ya padziko lapansi ikadzagwirizana kuwononga anthu a Mulungu, monga mmene Malemba analoserera, tidzakumbukira pemphero la wamasalmo lakuti: “Achite manyazi, naopsedwe kosatha; ndipo asokonezeke, nawonongeke.”​—Sal. 83:17.

18, 19. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu otsutsa ulamuliro wa Yehova? (b) Kodi nkhani yakuti Yehova posachedwapa atsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira imakukhudzani bwanji?

 18 Anthu amene amatsutsa ulamuliro wa Yehova adzawonongedwa mochititsa manyazi. Mawu a Mulungu amanena kuti pa Aramagedo anthu onse “osamvera uthenga wabwino” adzawaweruza kuti alandire “chiwonongeko chamuyaya.” (2 Ates. 1:7-9) Chiwonongeko chimenechi ndiponso kupulumutsidwa kwa anthu amene amalambira Yehova m’choonadi, kudzakhala umboni wotsimikizira kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona. Kupambana kwa Yehova kumeneku sikudzaiwalika m’dziko latsopano. Anthu “olungama ndi osalungama” amene adzaukitsidwe adzaphunzira ntchito zazikulu za Yehova. (Mac. 24:15) M’dziko latsopano limeneli, iwo adzaona umboni wosonyeza kuti ndi nzeru kutsatira ulamuliro wa Yehova. Ndipo anthu ofatsa omwe adzakhalepo sadzavutika kudziwa kuti Yehova ndi Mulungu yekha woona.

19 Limeneli ndi tsogolo labwino kwambiri lomwe Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi wakonzera olambira ake okhulupirika. Zimenezi zikulimbikitseni kupemphera kuti Yehova posachedwapa ayankhe komaliza pemphero la wamasalmo lakuti: “[Adani anu] asokonezeke, nawonongeke: Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”​—Sal. 83:17, 18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Musanawerenge nkhani ino, mungachite bwino kuwerenga Salmo 83 kuti muidziwe bwino nkhani yake.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi zinthu zinali bwanji kwa Aisiraeli pamene Salmo 83 limalembedwa?

• Kodi wolemba Salmo 83 ankadera nkhawa kwambiri chiyani?

• Kodi ndani amadedwa kwambiri ndi Satana masiku ano?

• Kodi Yehova adzayankha bwanji komaliza pemphero la pa Salmo 83:18?

[Mafunso]

[Mapu patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kodi nkhondo zimene zinachitika kale pafupi ndi Megido zikukhudza motani tsogolo lathu?

Mtsinje wa Kisoni

Haroseti

Phiri la Karimeli

Chigwa cha Yezreeli

Megido

Taanaki

Phiri la Giliboa

Chitsime cha Harodi

More

Endoro

Phiri la Tabori

Nyanja ya Galileya

Mtsinje wa Yorodano

[Chithunzi patsamba 12]

Kodi n’chiyani chinachititsa wamasalmo wina kulemba pemphero lochokera pansi pamtima?