Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Maso Onyezimira” a Yehova Amasanthula Anthu Onse

“Maso Onyezimira” a Yehova Amasanthula Anthu Onse

 “Maso Onyezimira” a Yehova Amasanthula Anthu Onse

“Maso onyezimira [a Yehova] amasanthula ana a anthu.”​—SAL. 11:4, NW.

1. Kodi timakonda anthu otani?

KODI mumawaona bwanji anthu amene amakukondani kwambiri? Mukawapempha kuti akuuzeni maganizo awo pankhani inayake, amakufotokozerani moona mtima. Ndipo mukavutika, amakuthandizani. Mukalakwitsa chinachake, iwo amakulangizani mwachikondi. (Sal. 141:5; Agal. 6:1) Mwachionekere nanunso mumawakonda. Umu ndi mmene Yehova ndi Mwana wake amachitira. Ndipotu amakukondani kuposa mmene munthu wina aliyense angakukondereni. Chikondi chawo n’chopanda dyera chifukwa amafuna kukuthandizani kuti ‘mukagwire zolimba moyo weniweniwo.’​—1 Tim. 6:19; Chiv. 3:19.

2. Kodi Yehova amakonda bwanji atumiki ake?

2 Wamasalmo Davide anasonyeza mmene Yehova amatikondera pamene anati: “Maso onyezimira [a Yehova] amasanthula ana a anthu.” (Sal. 11:4) Mulungu sikuti amangotiyang’ana koma amatisanthula. Davide analembanso kuti: “Mwasanthula mtima wanga, mwandifufuza usiku. . . . Mudzaona kuti sindinaganizire kuchita choipa chilichonse.” (Sal. 17:3, NW.) N’zoonekeratu kuti Davide ankadziwa kuti Yehova ankamukonda kwambiri. Iye ankadziwa kuti angakwiyitse kapena kudana ndi Yehova ngati atakhala ndi maganizo oipa kapena mtima woipa. Kodi Yehova mumamudziwa bwino monga mmene Davide ankachitira?

Yehova Amaona mu Mtima

3. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti saganizira kwambiri zolakwa zathu?

3 Yehova amachita chidwi kwambiri ndi mtima wathu kapena kuti umunthu wathu wa mkati. (Sal. 19:14; 26:2) Chifukwa chakuti amatikonda, iye saika mtima pa zolakwa zathu zazing’ono. Mwachitsanzo, Sara mkazi wa Abulahamu, atalephera kunena zoona kwa mngelo, mngeloyo anadziwa kuti wanena zimenezi chifukwa cha mantha kapena manyazi. Motero, Sara anangodzudzulidwa pang’ono. (Gen. 18:12-15) Ndipo Yobu atanena kuti anali “wolungama, wosati Mulungu,” Yehova anadziwa kuti wanena zimenezi chifukwa chakuti anavutitsidwa kwambiri ndi Satana ndipo sanamumane madalitso. (Yobu 32:2; 42:12) Yehova sanakwiye ndi mawu osapita m’mbali amene mkazi wamasiye wa ku Zarefati anauza mneneri Eliya. Iye anadziwa kuti mkaziyo wanena mawu amenewa chifukwa cha imfa ya mwana wake.​—1 Maf. 17:8-24.

4, 5. Kodi Yehova anam’komera mtima motani Abimeleki?

4 Chifukwa chakuti Yehova amasanthula mitima, iye amaganizira ngakhale anthu osakhulupirira. Taganizirani nkhani ya Abimeleki, mfumu ya Afilisiti ya mzinda wa Gerari. Abimeleki anatenga Sara kuti akhale mkazi wake. Iye sanadziwe kuti anali mkazi wa Abulahamu. Koma Abimeleki asanachite naye chilichonse, Yehova anamuuza m’maloto kuti: “Inde ndidziwa ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine; chifukwa chake sindinakuloleza iwe kuti um’khudze mkaziyo. Tsopano, um’bwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo.”​—Gen. 20:1-7.

5 Kunena zoona, Yehova akanatha kulanga Abimeleki yemwe anali wolambira milungu yonyenga. Koma Mulungu anaona kuti munthuyu sanalakwe pankhaniyi. Podziwa zimenezi, Yehova mokoma mtima anauza mfumuyo zimene ingachite kuti ikhululukidwe ndi  ‘kukhalabe ndi moyo.’ Kodi simungakonde kulambira Mulungu wotere?

6. Kodi Yesu anatsanzira Atate wake m’njira zotani?

6 Yesu anatsanzira kwambiri Atate wake ndipo ankayang’ana kwambiri zabwino zimene ophunzira ake ankachita komanso sankachedwa kuwakhululukira akalakwitsa. (Maliko 10:35-45; 14:66-72; Luka 22:31, 32; Yoh. 15:15) Zochita za Yesu zimagwirizana ndi mawu ake a pa Yohane 3:17 akuti: “Mulungu anatumiza Mwana wake m’dziko, osati kuti mwanayo adzaweruze dziko, koma kuti mwa iye, dziko lipulumutsidwe.” Ndithudi, Yehova ndi Yesu amatikonda kwambiri nthawi zonse. Timadziwa zimenezi chifukwa chakuti amafuna kuti tidzapeze moyo. (Yobu 14:15) Yehova amatisanthula chifukwa amatikonda, ndipo mmene amationera komanso mmene amachitira ndi zimene waonazo ndi umboni wa zimenezi.​—Werengani 1 Yohane 4:8, 19.

Amatisanthula Mwachikondi

7. Kodi Yehova amatisanthula ndi cholinga chotani?

7 Choncho, n’kulakwa kumuona Yehova ngati wapolisi amene amatifufuza n’cholinga choti atipeze tikuchita zolakwa. Koma Satana ndi amene amatilondalonda. (Chiv. 12:10) Iye amaganizira anthu zoipa ngakhale asanalakwe. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Ponena za Mulungu, wamasalmo analemba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?” (Sal. 130:3) Yankho lake ndi lakuti palibe ndi mmodzi yemwe. (Mlal. 7:20) M’malo mwake, Yehova amatiyang’ana mwachifundo ndi mokoma mtima ngati kholo limene likufuna kuteteza ana ake okondedwa. Nthawi zambiri amatichenjeza za zolakwa ndi zofooka zathu n’cholinga choti tisadzivulaze.​—Sal. 103:10-14; Mat. 26:41.

8. Kodi Yehova amalangiza atumiki ake motani?

8 Mulungu amasonyeza chikondi chake akamatilangiza kudzera m’Malemba komanso m’chakudya chauzimu choperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45; Aheb. 12:5, 6) Yehova amatithandizanso kudzera mumpingo wachikhristu ndiponso mwa “mphatso za amuna.” (Aef. 4:8) Kuwonjezera pa zimenezi, Yehova amatiyang’ana kuti aone mmene tikutsatirira malangizo ake ndipo amafuna kutithandiza. Lemba la Salmo 32:8 limati: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” Motero, n’kofunika kwambiri kumvera Yehova nthawi zonse. Tifunika kukhala odzichepetsa pamaso pake pozindikira kuti iye ndi Mphunzitsi ndi Tate wathu wachikondi.​—Werengani Mateyo 18:4.

9. Kodi tiyenera kupewa makhalidwe otani, ndipo chifukwa chiyani?

9 Choncho, mtima wathu usaumitsidwe ndi kudzikuza, kupanda chikhulupiriro, kapena “chinyengo champhamvu cha uchimo.” (Aheb. 3:13; Yak. 4:6) Nthawi zambiri, makhalidwe amenewa amayamba ngati munthu ali ndi maganizo kapena zikhumbo zoipa. Ndipo munthu wotero angafike pokana malangizo oyenera a m’Malemba. Choopsa kwambiri n’chakuti, angalowerere kwambiri m’makhalidwe kapena m’njira zoipa moti angakhale mdani wa Mulungu. (Miy. 1:22-31) Taganizirani nkhani ya Kaini, mwana woyamba wa Adamu ndi Hava.

 Yehova Amaona Zonse Ndipo Amachita Mogwirizana ndi Zochita Zathu

10. N’chifukwa chiyani Yehova sanalandire mphatso ya Kaini, nanga Kaini anatani?

10 Kaini ndi Abele atapereka nsembe kwa Yehova, Iye sanaganizire kwambiri za mphatso zawo zokha koma anaonanso zolinga zawo. Choncho, Mulungu analandira mphatso ya Abele yomwe anaipereka ndi chikhulupiriro koma anakana ya Kaini yemwe analibe chikhulupiriro. (Gen. 4:4, 5; Aheb. 11:4) M’malo mophunzira kanthu pa zimenezi ndi kusintha maganizo ake, Kaini anakwiyira kwambiri m’bale wake.​—Gen. 4:6.

11. Kodi Kaini anasonyeza bwanji kuti mtima ndi wonyenga, ndipo tikuphunzirapo chiyani pankhaniyi?

11 Yehova anaona kuti Kaini anali ndi maganizo oipa ndipo analankhula naye mokoma mtima ndi kumuuza kuti akachita zabwino, adzalandiridwa. N’zomvetsa chisoni kuti, Kaini ananyalanyaza malangizo a Mlengi wake ndipo anapha m’bale wake. Kuipa mtima kwa Kaini kunaonekera pa mwano umene anayankha Mulungu atamufunsa kuti: “Ali kuti Abele mphwako? Kaini anati: “Sindidziwayi: kodi ndine woyang’anira mphwanga?” (Gen. 4:7-9) Mtima ndi wonyengadi kwambiri moti ungachititse munthu kukana malangizo achindunji ochokera kwa Mulungu. (Yer. 17:9) Motero, titengerepo phunziro pa nkhani ngati zimenezi ndipo tizipewa maganizo ndi zikhumbo zoipa. (Werengani Yakobe 1:14, 15.) Tikalandira malangizo a m’Malemba, tiziyamikira ndi kuwaona kuti ndi umboni woti Yehova amatikonda.

Palibe Tchimo Lobisika kwa Yehova

12. Kodi Yehova amatani ndi anthu ochimwa?

12 Anthu ena amaganiza kuti ngati palibe yemwe wawaona akuchita tchimo, ndiye kuti tchimolo silingadziwike. (Sal. 19:12) Koma palibe tchimo lobisika chifukwa Baibulo limati: “Zinthu zonse zili pambalambanda ndi zoonekera poyera pamaso pake. Inde, pamaso pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.” (Aheb. 4:13) Yehova ndi woweruza amene amasanthula zolinga zathu, ndipo anthu akachimwa amawaweruza mwachilungamo. Iye ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” Koma, iye ‘samasula wopalamula’ omwe ndi anthu osalapa amene ‘amachita tchimo mwadala’ kapena amene amasonyeza mtima wonyenga ndi woipa. (Eks. 34:6, 7; Aheb. 10:26) Umboni wa zimenezi timaupeza pa zimene Yehova anachita ndi Akani ndiponso Hananiya ndi Safira.

13. Kodi maganizo olakwika anam’chimwitsa bwanji Akani?

13 Mzinda wa Yeriko utawonongedwa, Akani anaphwanya lamulo la Mulungu potenga zinthu mu mzindawo n’kuzibisa mu hema wake. Mwachionekere anachita zimenezi mogwirizana ndi banja lake. Izi zitadziwika, Akani anazindikira kuti wachita tchimo lalikulu, popeza anati: “Ndachimwira Yehova.” (Yos. 7:20) Monga Kaini, Akani analinso ndi mtima woipa. Pankhani ya Akani vuto lalikulu linali dyera ndipo linapangitsa kuti achite chinyengo. Popeza zinthu za ku Yeriko zinali za Yehova, ndiye kuti Akani anabera Mulungu, ndipo zimenezi zinaphetsa iye ndi banja lake.​—Yos. 7:25.

14, 15. Kodi Mulungu analanga Hananiya ndi Safira chifukwa chiyani, nanga zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?

14 Hananiya ndi mkazi wake Safira, anali Akhristu a mumpingo wachikhristu woyambirira ku Yerusalemu. Pentekoste wa mu  33 C.E. atachitika, panakhazikitsidwa thumba la ndalama zothandizira okhulupirira atsopano ochokera m’madera akutali amene anatsala ku Yerusalemu. Anthu ankapereka ndalama ku thumbali mwa kufuna kwawo. Hananiya anagulitsa munda n’kupereka ndalama zina ku thumbali. Ndipo mkazi wake anadziwa kuti mwamuna wake sanapereke ndalama zonse. Komabe, mwamunayo anasonyeza ngati wapereka ndalama zonse. Mwachionekere, cholinga cha banjali chinali chakuti apatsidwe ulemu wapadera mu mpingomo. Komabe iwo anachita chinyengo. Yehova anaulula mozizwitsa chinyengo chimenechi kwa mtumwi Petulo, amene anafunsa Hananiya za nkhaniyi. Izi zitangochitika, Hananiya anagwa pansi ndi kumwalira. Patapita nthawi pang’ono Safira nayenso anamwalira.​—Mac. 5:1-11.

15 Hananiya ndi Safira sanachite zimenezi chifukwa chakuti anangofooka panthawiyi. Iwo anachita kugwirizana kuti achite chinyengocho pofuna kunamiza atumwi. Choipa kwambiri n’chakuti ‘ananamiza mzimu woyera ndi Mulungu.’ Zimene Yehova anachita zinasonyezeratu kuti ndi wokonzeka kuteteza mpingo wake kwa anthu achinyengo. Ndithudi, “ndi chinthu choopsa kugwa m’manja mwa Mulungu wamoyo.”​—Aheb. 10:31.

Khalani Okhulupirika Nthawi Zonse

16. (a) Kodi Satana akuyesetsa bwanji kusokoneza anthu a Mulungu? (b)  Kodi Mdyerekezi akugwiritsa ntchito njira ziti pofuna kusokoneza athu m’dera lathu?

16 Satana akuchita zonse zimene angathe kuti atisokoneze n’cholinga chakuti Yehova asiye kutikonda. (Chiv. 12:12, 17) Zolinga zoipa za Mdyerekezi n’zofala m’dzikoli, limene n’lokonda zachiwerewere ndi zachiwawa. Masiku ano, zinthu zolaula zingaonedwe pakompyuta kapena pa zipangizo zina. Tisagonje pa zinthu za Satana zimenezi koma tikhale ndi maganizo ngati a wamasalmo Davide amene analemba kuti: “Ndidzachita mwanzeru m’njira yangwiro; . . . ndidzayenda m’nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.”​—Sal. 101:2.

17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova amavumbula machimo obisika? (b) Kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chotani?

17 Masiku ano, Yehova saulula mozizwitsa machimo aakulu ndi makhalidwe achinyengo ngati mmene ankachitira kale. Komabe, iye amaona zonse ndipo adzavumbula zinthu zonse zobisika panthawi yake komanso m’njira imene iye akufuna. Paulo anati: “Machimo a anthu ena amaonekera poyera, kuwatsogolera mwachindunji ku chiweruzo. Koma anthu ena, machimo awo amadzaonekera pambuyo pake.” (1 Tim. 5:24) Yehova amavumbula machimo chifukwa cha chikondi. Iye amakonda mpingo ndipo amafuna kuuteteza kuti ukhale woyera. Iye amachitiranso chifundo anthu ochimwa amene alapa moona mtima. (Miy. 28:13) Choncho, tiyeni tipitirize kukhala ndi mtima wangwiro  pamaso pa Mulungu ndi kupewa makhalidwe oipa.

Khalanibe ndi Mtima Wangwiro

18. Kodi Mfumu Davide anafuna kuti mwana wake adziwe chiyani ponena za Mulungu?

18 Mfumu Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Um’dziwe Mulungu wa atate wako, um’tumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo.” (1 Mbiri 28:9) Davide sanafune kuti mwana wake angokhulupirira Mulungu koma anafuna kuti Solomo adziwe kuti Yehova amakonda kwambiri atumiki Ake. Kodi nanunso mumayamikira Yehova chifukwa chakuti amakonda kwambiri atumiki ake?

19, 20. Malinga ndi Salmo 19:7-11, kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuyandikira kwa Mulungu, ndipo tingam’tsanzire bwanji Davide?

19 Yehova amadziwa kuti anthu amene amafuna kukhala naye paubwenzi amamukonda ndipo amayandikira kwa iye akadziwa makhalidwe ake. Choncho, Yehova amafuna kuti tim’dziwe komanso kuti tidziwe bwino kwambiri makhalidwe ake. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingatero mwa kuphunzira Mawu ake ndi kuona mmene watidalitsira.​—Miy. 10:22; Yoh. 14:9.

20 Kodi mumawerenga Baibulo tsiku lililonse podziwa kuti linachokera kwa Mulungu? Kodi mumapempha Mulungu kuti akuthandizeni kugwiritsa ntchito zimene mukuwerengazo? Kodi mumaona phindu lotsatira mfundo za m’Baibulo? (Werengani Salmo 19:7-11.) Ngati ndi choncho, chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu mwa Yehova chidzapitiriza kukula. Ndipo iyenso adzayandikira kwa inu ndipo zidzakhala ngati mukuyenda naye atakugwirani dzanja. (Yes. 42:6; Yak. 4:8) Yehova adzasonyeza kuti amakukondani mwa kukudalitsani ndi kukutetezani mwauzimu pamene mukuyenda pa njira yopapatiza ya kumoyo.​—Sal. 91:1, 2; Mat. 7:13, 14.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Yehova amatisanthula chifukwa chiyani?

• Kodi n’chiyani chinachititsa kuti anthu ena akhale adani a Mulungu?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti Yehova timamudziwa bwino?

• Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtima wangwiro kwa Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 4]

Kodi Yehova monga Atate wachikondi amatiyang’ana chifukwa chiyani?

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi tikuphunzira chiyani pankhani ya Hananiya?

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi n’chiyani chingatithandize kutumikirabe Yehova ndi mtima wangwiro?