Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Simudziwa Zimene Zidzalola

Simudziwa Zimene Zidzalola

 Simudziwa Zimene Zidzalola

“Mamawa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino.”​—MLAL. 11:6.

1. N’chifukwa chiyani kuona mmene mbewu zimakulira n’kochititsa chidwi ndipo kumatithandiza kudzichepetsa?

MLIMI amafunika kukhala woleza mtima. (Yak. 5:7) Akafesa mbewu, amafunika kudikirira kuti ziphuke ndi kukula. Ngati zinthu zili bwino, mmera umang’amba nthaka pang’onopang’ono n’kuyamba kuonekera. Mmerawo umakula ndi kutulutsa ngala. Pamapeto pake mbewuzo zimacha kuti mlimiyo akolole. N’zochititsa chidwi kwambiri kuona mmene mbewu zimakulira modabwitsa. Komanso kudziwa Gwero la kukula kumeneku kumatithandiza kudzichepetsa. Ife tingasamalire mbewu. Tingathandize kuthirira. Koma ndi Mulungu yekha amene amakulitsa.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 3:6.

2. Kodi Yesu anaphunzitsa mfundo zotani zokhudza kukula kwauzimu m’mafanizo amene tinakambirana m’nkhani yapitayo?

2 Malinga ndi nkhani yapitayo, Yesu anayerekezera ntchito yolalikira Ufumu ndi mmene mlimi amafesera mbewu. M’fanizo la dothi losiyanasiyana, Yesu anatsindika mfundo yakuti mlimi amafesa mbewu yabwino, koma mtima wa munthu ndi umene umalola kuti mbewuyo ikule mpaka kukhwima kapena ayi. (Maliko 4:3-9) M’fanizo la wofesa mbewu amene amagona, Yesu anatsindika mfundo yakuti mlimiyo samvetsa bwinobwino mmene mbewu zimakulira. Zili choncho kaamba kakuti mbewu zimakula chifukwa cha mphamvu ya Mulungu, osati khama la anthu. (Maliko 4:26-29) Tsopano tiyeni tikambirane mafanizo enanso atatu a Yesu, fanizo la kambewu ka mpiru, la chofufumitsa ndi la khoka. *

Fanizo la Kambewu ka Mpiru

3, 4. Kodi fanizo la kambewu ka mpiru likusonyeza mbali ziti za uthenga wa Ufumu?

3 Fanizo la kambewu ka mpiru, lomwe lilinso m’chaputala 4 cha Maliko, likusonyeza zinthu ziwiri. Chinthu choyamba ndi kukula kochititsa chidwi kwa uthenga wa Ufumu. Chachiwiri ndi chitetezo chimene anthu amene amalabadira uthenga amakhala nacho. Yesu anati: “Kodi ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani, kapena tiufotokoze ndi fanizo lotani? Uli ngati kambewu ka mpiru, kamene panthawi yofesa kamakhala kakang’ono kwambiri mwa njere zonse za padziko lapansi​—koma akakafesa, kamamera ndi kukula kuposa mbewu zonse za kudimba ndipo kamapanga nthambi zikuluzikulu, mwakuti mbalame za mlengalenga zimatha kupeza malo okhala mu mthunzi wake.”​—Maliko 4:30-32.

4 Pamenepa akusonyeza kukula kwa “ufumu wa Mulungu.” Kukulaku kunaonekera mwa kufalikira kwa uthenga wa Ufumu komanso kukula kwa mpingo wachikhristu, kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E. kumka m’tsogolo. Kambewu ka mpiru ndi kanjere kakang’ono kwambiri kamene kangaimire kanthu kakang’ono kwambiri.  (Yerekezerani ndi Luka 17:6.) Koma m’kupita kwa nthawi, kambewu ka mpiru kangakule mpaka kufika mamita atatu kapena asanu n’kukhala ndi nthambi zolimba, motero tingati kamakhala mtengo.​—Mat. 13:31, 32.

5. Kodi mpingo wachikhristu wa m’nthawi ya atumwi unakula motani?

5 Mpingo wachikhristu unayamba kukula kuchokera pa gulu laling’ono mu 33 C.E. pamene ophunzira pafupifupi 120 anadzozedwa ndi mzimu woyera. Patangopita nthawi yochepa chabe, mpingo waung’ono wa ophunzira umenewu unakhala ndi okhulupirira zikwizikwi. (Werengani Machitidwe 2:41; 4:4; 5:28; 6:7; 12:24; 19:20.) M’zaka 30 zokha, chiwerengero cha ogwira ntchito yokolola chinali chitakula kwambiri, motero kuti mtumwi Paulo anatha kuuza mpingo wa ku Kolose kuti uthenga wabwino unali ‘utalalikidwa m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.’ (Akol. 1:23) Koma ndiye kumeneku kunali kukula kodabwitsa!

6, 7. (a) Kodi ndi kukula kotani kumene kwakhalapo kuyambira mu 1914? (b) Kodi padzakhalanso kukula kwina kotani?

6 Kuchokera pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, nthambi za “mtengo” wa mpiru zakula kwambiri mosayembekezereka. Anthu a Mulungu aona kukwaniritsidwa kwa ulosi umene Yesaya analemba wakuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.” (Yes. 60:22) Zinali zosatheka kuti kagulu kochepa ka odzozedwa amene anali kugwira ntchito ya Ufumu kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, kadziwe kuti pomafika chaka cha 2008, Mboni pafupifupi 7 miliyoni zidzakhala zikugwira ntchitoyi m’mayiko oposa 230. Kumenekutu ndi kukula kodabwitsa, kofanana ndi kukula kwa kambewu ka mpiru m’fanizo la Yesu.

7 Koma kodi kukulaku kwathera pamenepa? Ayi. M’kupita kwa nthawi, nzika za Ufumu wa Mulungu zidzadzaza dziko lonse lapansi. Adani onse adzakhala atachotsedwa. Zimenezi zidzachitika osati chifukwa cha khama la anthu, koma chifukwa chakuti Ambuye Mfumu Yehova adzalowerera zochitika za padziko lapansi. (Werengani Danieli 2:34, 35.) Kenako tidzaona kukwaniritsidwa komaliza kwa ulosi winanso wolembedwa ndi Yesaya wakuti: “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”​—Yes. 11:9.

8. (a) Kodi mbalame za m’fanizo la Yesu zikuimira ndani? (b) Kodi tikutetezedwa ku chiyani ngakhale panopa?

8 Yesu anati mbalame za m’mlengalenga zimatha kupeza malo okhala mu mthunzi wa Ufumuwu. Mbalame zimenezi sizikuimira adani a Ufumu amene amadya mbewu zabwinozo, ngati mmene zinalili ndi mbalame za m’fanizo la munthu amene anamwaza mbewu padothi losiyanasiyana. (Maliko 4:4) M’malomwake, m’fanizo limeneli mbalame zikuimira anthu amitima yabwino amene amafunafuna chitetezo mumpingo wachikhristu. Ngakhale panopa, anthu amenewa akutetezedwa ku zizolowezi zodetsa mwauzimu ndi ku makhalidwe onyansa a dziko loipali. (Yerekezerani ndi Yesaya 32:1, 2.)  Komanso, Yehova anayerekezera Ufumu wa Mesiya ndi mtengo, ndipo analosera kuti: ‘Paphiri lothuvuka la Israyeli ndidzauwoka, ndipo udzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nudzakhala mkungudza wokoma, ndi m’munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko alionse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira.’​—Ezek. 17:23.

Fanizo la Chofufumitsa

9, 10. (a) Kodi Yesu anatsindika mfundo yotani m’fanizo la chofufumitsa? (b) Kodi chofufumitsa nthawi zambiri chimaimira chiyani m’Baibulo, ndipo tikambirana funso lotani lokhudza mmene Yesu anagwiritsira ntchito chofufumitsa?

9 Si nthawi zonse pamene kukula kumaoneka ndi maso. Yesu anatsindika mfundo imeneyi m’fanizo lake lina. Iye anati: “Ufumu wa kumwamba uli ngati zofufumitsa, zimene mkazi anazitenga ndi kuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zazikulu zopimira, ndipo wonsewo unafufuma.” (Mat. 13:33) Kodi chofufumitsa chimenechi chikuimira chiyani, ndipo chikugwirizana bwanji ndi kukula kwa Ufumu?

10 M’Baibulo, chofufumitsa nthawi zambiri chimaimira uchimo. Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chofufumitsa mwa njira imeneyi pamene ananena za munthu wochimwa amene anali kuipitsa mpingo wa ku Korinto. (1 Akor. 5:6-8) Ndiyeno kodi apa Yesu anagwiritsa ntchito chofufumitsa kuimira kukula kwa chinthu choipa?

11. Kodi kale Aisiraeli ankagwiritsa ntchito chofufumitsa motani?

11 Tisanayankhe funso limeneli, tifunikira kukumbukira mfundo zofunika zitatu. Yoyamba, ngakhale kuti Yehova sanalole chofufumitsa paphwando la Pasika, nthawi zina anali kulandira nsembe zokhala ndi chofufumitsa. Chofufumitsa chinkagwiritsidwa ntchito pansembe zoyamika za chiyanjano. Munthu ankapereka nsembe zimenezi mwaufulu poyamikira Yehova chifukwa cha madalitso ake ambiri. Akadya chakudyachi anali kusangalala kwambiri.​—Lev. 7:11-15.

12. Kodi tikuphunzira chiyani ndi mmene Baibulo limagwiritsira ntchito mafanizo?

12 Mfundo yachiwiri ndi yakuti, ngakhale kuti nthawi ina chinthu china m’Malemba chingaimire chinthu choipa, panthawi ina chinthu chomwecho chingagwiritsidwe ntchito kuimira chinthu chabwino. Mwachitsanzo pa 1 Petulo 5:8, Satana akuyerekezeredwa ndi mkango, posonyeza kuopsa ndi kulusa kwake. Koma pa Chivumbulutso 5:5, Yesunso akuyerekezeredwa ndi mkango, pomutchula kuti “Mkango wa fuko la Yuda.” Pamenepa, agwiritsa ntchito mkango kuimira kulimba mtima pochita chilungamo.

13. Kodi fanizo la Yesu la chofufumitsa likusonyeza chiyani za kukula kwauzimu?

13 Mfundo yachitatu ndi yakuti, m’fanizo lake, Yesu sananene kuti chofufumitsa chinaipitsa ufawo, n’kukhala wosatheka kuugwiritsa ntchito. M’malomwake, iye anangonena zimene zimachitika popanga mkate. Mkaziyo anachita kuikamo chofufumitsa, ndipo zotsatira zake zinali zabwino. Chofufumitsa chinasakanizidwa, kapena kuti chinabisidwa mu ufa. Chotero, njira imene chofufumitsacho chinali kugwirira ntchito inali yobisika kwa mkaziyo. Zimenezi zikutikumbutsa za munthu uja amene amafesa mbewu ndi kugona usiku. Yesu ananena kuti: “Mbewuzo zimamera ndi kukula. Koma kwenikweni mmene zimenezi zimachitikira, [munthuyo] sadziwa ayi.” (Maliko 4:27) Imeneyitu ndi njira yosavuta yofanizira mmene kukula kwauzimu kumachitikira mosaoneka. Poyamba sitingaone kukulako, koma m’kupita kwa nthawi zotsatira zake zimayamba kuonekera.

14. Kodi ndi mbali iti ya ntchito yolalikira imene ikusonyezedwa ndi mfundo yakuti chofufumitsa chikufufumitsa ufa wonse?

 14 Kuwonjezera pa mfundo yakuti kukula sikuoneka ndi maso, kukulako kumafalikira paliponse. Fanizo la chofufumitsa likutsindikanso mbali imeneyi. Chofufumitsacho chikufufumitsa ufa wonsewo, “wokwana mbale zopimira zazikulu zitatu.” (Luka 13:21) Mofanana ndi chofufumitsa, ntchito yolalikira Ufumu imene yachititsa kukula kwauzimu kumeneku yafalikira paliponse, motero kuti Ufumuwo ukulalikidwa “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8; Mat. 24:14) Ndi mwayi wapadera kwambiri kuthandiza nawo kuti ntchito ya Ufumu ifalikire mochititsa chidwi chonchi.

Khoka

15, 16. (a) Fotokozani mwachidule fanizo la khoka. (b) Kodi khokali likuimira chiyani, ndipo kodi fanizo limeneli likusonyeza mbali iti ya kukula kwa Ufumu?

15 Chofunika kwambiri kuposa chiwerengero cha anthu omwe amati ndi ophunzira a Yesu Khristu ndicho mtundu wa ophunzirawo. Yesu anasonyeza mbali imeneyi ya kukula kwa Ufumu pamene ananenanso fanizo la khoka. Iye anati: “Ndiponso ufumu wa kumwamba uli ngati khoka loponyedwa m’nyanja limene limasonkhanitsa nsomba zamitundumitundu.”​—Mat. 13:47.

16 Khokali, lomwe likuimira ntchito yolalikira Ufumu, limasonkhanitsa nsomba zamitundumitundu. Yesu anapitiriza kuti: “[Khokalo] likadzala amalikokera kumtunda ndipo amakhala pansi, kenako amasankha zabwino ndi kuziika m’zotengera, koma zosafunika amazitaya. Ndi mmenenso zidzakhalira pamapeto a dongosolo lino la zinthu: angelo adzapita ndi kukachotsa oipa pakati pa olungama ndipo adzawaponya mu ng’anjo yamoto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”​—Mat. 13:48-50.

17. Kodi kusankha, kapena kuti kulekanitsa, kotchulidwa m’fanizo la khoka kukuchitika nthawi iti?

17 Kodi kusankha kumeneku, kapena kuti kulekanitsa, kukunena za chiweruzo chomaliza cha nkhosa ndi mbuzi chimene Yesu anati chidzachitika iye akadzafika mu ulemerero wake? (Mat. 25:31-33) Ayi. Chiweruzo chomaliza chimenecho chidzachitika Yesu akadzabwera pa chisautso chachikulu. Koma kulekanitsa kumene kukunenedwa m’fanizo la khoka kukuchitika “pamapeto,” kapena kuti nthawi ya mathedwe “a dongosolo lino la zinthu.” * Nthawi imeneyi ndi imene tikukhalamoyi, imene ikutifikitsa ku chisautso chachikulu. Ndiyeno kodi ntchito yolekanitsa imeneyi ikuchitika motani masiku ano?

18, 19. (a) Kodi ntchito yolekanitsa ikuchitika motani masiku ano? (b) Kodi anthu amitima yabwino akufunika kuchita chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi patsamba 21.)

18 Nsomba zophiphiritsa mamiliyoni ambiri zochokera m’nyanja ya anthu zimabwera mu mpingo wa Yehova masiku ano. Zina zimapezeka pa Chikumbutso, zina zimabwera ku misonkhano yathu, ndipo zinanso zimasangalala  kuphunzira Baibulo. Koma kodi nsomba zonsezi zimakhala Akhristu enieni? Nsombazo ‘zingakokeredwe kumtunda’ inde, koma Yesu akunena kuti “zabwino” zokha ndi zimene akuzisonkhanitsa m’zotengera, ndipo zotengerazi zikuimira mipingo yachikhristu. Zosafunika zikutayidwa, ndipo pamapeto pake zidzaponyedwa m’ng’anjo ya moto yophiphiritsa, imene ikuimira chiwonongeko cha m’tsogolo.

19 Mofanana ndi nsomba zosafunika, anthu ambiri amene ankaphunzira Baibulo ndi anthu a Yehova asiya kuphunzira. Ena omwe anabadwira m’mabanja achikhristu sanafunepo kukhala otsatira mapazi a Yesu. Mpaka pano iwo akhala asakufuna kutumikira Yehova, kapena atamutumikira kwa nthawi ndithu, asiya kumutumikira. * (Ezek. 33:32, 33) Komabe, m’pofunika kwambiri kuti anthu onse amitima yabwino alole kusonkhanitsidwa m’mipingo yonga zotengera ndi kukhalabe m’malo achitetezo amenewa lisanafike tsiku lomaliza la chiweruzo.

20, 21. (a) Kodi taphunzira chiyani pambuyo pokambirana mafanizo a Yesu okhudza kukula? (b) Kodi inu mukufunitsitsa kuchita chiyani?

20 Ndiyeno, kodi taphunzira chiyani pambuyo pokambirana mwachidule mafanizo a Yesu okhudza kukula? Choyamba, mofanana ndi kukula kwa kambewu ka mpiru, zinthu za Ufumu zakula modabwitsa kwambiri padziko lapansi. Palibe chimene chingaletse ntchito ya Yehova kufalikira. (Yes. 54:17) Ndiponso, chitetezo chauzimu chaperekedwa kwa anthu amene ‘apeza malo okhala mu mthunzi [wa mtengowo].’ Chachiwiri, Mulungu ndi amene amakulitsa. Mofanana ndi mmene chofufumitsa chobisika chimafufumitsira ufa wonse, kukula kumeneku kwakhala kovuta kukuzindikira kapena kukumvetsa, koma kukulako kukuchitika ndithu. Chachitatu, sikuti anthu onse amene analabadira asonyeza kuti ndi nsomba zofunika. Ena akhala ngati nsomba zosafunika za m’fanizo la Yesu.

21 Ngakhale zili choncho, n’zolimbikitsa kwambiri kuona kuti anthu ambiri ofunika akukokedwa ndi Yehova. (Yoh. 6:44) Zimenezi zathandiza kuti anthu awonjezereke kwambiri m’mayiko osiyanasiyana. Ulemerero wonse ukupita kwa Yehova Mulungu chifukwa cha kukula kumeneku. Poona zimenezi, aliyense wa ife ayenera kukhala wofunitsitsa kumvera malangizo amene analembedwa zaka mazana ambiri zapitazo akuti: “Mamawa fesa mbewu zako, . . . pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.”​—Mlal. 11:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Zimene tifotokoze m’nkhani ino zikusintha zimene zinafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1992, masamba 17-22, ndi ya Chingelezi ya October 1, 1975, masamba 589-608.

^ ndime 17 Ngakhale kuti lemba la Mateyo 13:39-43 likunena mbali ina ya ntchito yolalikira Ufumu, nthawi ya kukwaniritsidwa kwake ndi nthawi yomwenso fanizo la khoka likukwaniritsidwa, yomwe ndi “pamapeto,” kapena kuti nthawi ino ya mathedwe “a dongosolo lino la zinthu.” Ntchito yolekanitsa nsomba zophiphiritsa ndi yochitika mopitiriza, monga mmene ntchito yofesa ndi kukolola ikupitirizira panthawi yonseyi.​—Nsanja ya Olonda, October 15, 2000, masamba 25-26; Lambirani Mulungu Woona Yekha, masamba 178-181, ndime 8-11.

^ ndime 19 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti munthu akasiya kuphunzira kapena kusonkhana ndi anthu a Yehova, ndiye kuti ndi wosafunika ndipo watayidwa ndi angelo? Ayi, si choncho. Ngati munthu akufunadi kubwerera kwa Yehova, khomo ndi lotseguka.​—Mal. 3:7.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi fanizo la Yesu la kambewu ka mpiru likutiphunzitsa chiyani za kukula kwa Ufumu ndi chitetezo chauzimu?

• Kodi chofufumitsa m’fanizo la Yesu chikuimira chiyani, ndipo ndi mfundo iti yokhudza kukula kwa Ufumu imene Yesu akutsindika?

• Kodi ndi mbali iti ya kukula kwa Ufumu imene ikusonyezedwa m’fanizo la khoka?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhalebe m’gulu la anthu omwe ‘aikidwa m’zotengera’?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 18]

Kodi fanizo la kambewu ka mpiru likutiphunzitsa chiyani za kukula kwa Ufumu?

[Chithunzi patsamba 19]

Kodi tikuphunzira chiyani m’fanizo la chofufumitsa?

[Chithunzi patsamba 21]

Kodi kulekanitsa nsomba zabwino ndi zosafunika kukuimira chiyani?