Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Utumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba Uli Wofunika Kwambiri Masiku Ano?

N’chifukwa Chiyani Utumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba Uli Wofunika Kwambiri Masiku Ano?

 N’chifukwa Chiyani Utumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba Uli Wofunika Kwambiri Masiku Ano?

“Tsiku ndi tsiku m’kachisi ndiponso ku nyumba ndi nyumba, anapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, Yesu.”​—MAC. 5:42.

1, 2. (a) Kodi Mboni za Yehova zimadziwika ndi njira yolalikirira iti? (b) Kodi mu nkhani ino tikambirana chiyani?

ANTHU awiri ovala bwino akufika pa nyumba ya munthu kuti akambirane naye uthenga wachidule wa m’Baibulo wonena za Ufumu wa Mulungu. Mwininyumbayo akuchita chidwi ndi uthengawo, ndipo iwo akum’patsa mabuku ofotokoza za Baibulo, n’kukonza zoti aziphunzira naye Baibulo kwaulere. Kenako iwo akupita nyumba ina. Zimenezi zimachitika pafupifupi dziko lililonse. Ngati inu mumagwira nawo ntchito imeneyi, mosakayikira mwaona kuti anthu amakuzindikirani kuti ndinu wa Mboni za Yehova, musanayambe ndi kulankhula komwe. Ndithudi, utumiki wa ku nyumba ndi nyumba wakhala chizindikiro chathu.

2 Pogwira ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira imene Yesu anatipatsa, timagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. (Mat. 28:19, 20) Timalalikira m’misika, m’misewu ndi m’malo ena amene anthu amapezeka. (Mac. 17:17) Timalankhula ndi anthu ambiri patelefoni ndi m’makalata. Timauza anthu amene timakumana nawo pantchito zathu za tsiku ndi tsiku choonadi cha m’Baibulo. Tilinso ndi adiresi yathu pa Intaneti imene anthu angapezepo mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’zinenero zoposa 300. * Njira zonsezi n’zothandiza. Komabe m’madera ambiri, njira yaikulu imene timafalitsira uthenga wabwino ndiyo kulalikira nyumba ndi nyumba. Kodi njira imeneyi tinaitenga kuti? Kodi anthu a Mulungu amakono anayamba bwanji kugwiritsa ntchito kwambiri njira imeneyi? Ndipo n’chifukwa chiyani ili yofunika kwambiri masiku ano?

Atumwi Ankalalikira Nyumba ndi Nyumba

3. Kodi Yesu anapatsa atumwi malangizo otani okhudza kulalikira, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti iwo sanayenera kudikira chiyani kuti alalikire?

3 Ntchito yolalikira uthenga wabwino ku nyumba ndi nyumba ndi yozikidwa m’Malemba. Yesu potumiza atumwi kukalalikira, anawalangiza kuti: “Mukalowa mu mzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenerera.” Kodi akanafufuza bwanji anthu oyenerera? Yesu anawauza kuti apite m’nyumba za anthu. Iye anati: “Pamene mukulowa m’nyumba, perekani moni kwa a m’banja limenelo; ndipo ngati nyumbayo ili yoyenerera, mtendere umene mukuifunira ukhale panyumbayo.” Kodi akanangopita m’nyumba za anthu popanda kuitanidwa? Onaninso zina zimene Yesu ananena. Iye anati: “Kulikonse kumene munthu sakakulandirani kapena kumvetsera mawu anu, potuluka m’nyumba imeneyo kapena mu mzinda umenewo sansani fumbi kumapazi anu.” (Mat. 10:11-14) Malangizo amenewa akusonyeza bwino kuti atumwiwo ‘atanyamuka ndi kulowa m’deralo m’mudzi ndi mudzi, kulengeza uthenga wabwino,’ anayenera kufikira anthu m’nyumba zawo popanda kudikira kuti aitanidwe.​—Luka 9:6.

4. Kodi ndi pati m’Baibulo pamene amatchula ulaliki wa ku nyumba ndi nyumba?

4 Baibulo limachita kutchula kuti atumwi ankalalikira nyumba ndi nyumba. Mwachitsanzo, pa Machitidwe 5:42 pamanena za atumwi kuti: “Tsiku ndi tsiku m’kachisi ndiponso ku nyumba ndi nyumba, anapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, Yesu.” Patapita zaka pafupifupi 20,  mtumwi Paulo anakumbutsa akulu a kumpingo wa ku Efeso kuti: “Sindinakubisireni chilichonse chopindulitsa, kapena kuleka kukuphunzitsani poyera komanso ku nyumba ndi nyumba.” Kodi Paulo anayendera akuluwo iwo asanakhale okhulupirira? Zikuonekadi choncho, chifukwa mwa zina anawaphunzitsa “za kulapa pamaso pa Mulungu ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu.” (Mac. 20:20, 21) Pothirira ndemanga Machitidwe 20:20, buku lina lolembedwa ndi Robertson limati: “N’zochititsa chidwi kuti mlaliki wachangu ndi wapadera ameneyu ankalalikira nyumba ndi nyumba.”​—Word Pictures in the New Testament.

Dzombe Lamakono Longa Gulu Lankhondo

5. Kodi ulosi wa Yoweli umafotokoza chiyani za ntchito yolalikira?

5 Ntchito yolalikira m’nthawi ya atumwi inachitira chithunzi ntchito yaikulu imene ikuchitika masiku athu ano. Mneneri Yoweli anayerekezera ntchito yolalikira imene Akhristu odzozedwa amachita ndi mliri woopsa wa tizilombo, kuphatikizapo dzombe. (Yow. 1:4) Poyenda ngati gulu lankhondo, dzombelo likukwera zotchinga, kulowa m’nyumba ndi kudya chilichonse chimene lapeza. (Werengani Yoweli 2:2, 7-9.) Zimenezi zikusonyeza bwino kuti anthu a Mulungu amachita khama ndipo amapita pena paliponse pogwira ntchito yolalikira masiku ano. Njira yaikulu imene Akhristu odzozedwa limodzi ndi anzawo a “nkhosa zina” amagwiritsa ntchito pokwaniritsa ulosi umenewu ndi utumiki wa ku nyumba ndi nyumba. (Yoh. 10:16) Kodi ife Mboni za Yehova tinayamba bwanji kugwiritsa ntchito njira yolalikirira imene atumwi ankaigwiritsa ntchito?

6. Kodi mu 1922 Akhristu analimbikitsidwa motani kulalikira nyumba ndi nyumba, koma ena anatani?

6 Kuyambira mu 1919, udindo wolalikira umene Mkhristu aliyense ali nawo wakhala ukugogomezeredwa kwambiri. Mwachitsanzo, nkhani yakuti “Utumiki Ndi Wofunika” imene inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1922, inakumbutsa Akhristu odzozedwa kuti afunika “kupereka uthenga kwa anthu mokangalika ndi kulankhula nawo m’nyumba zawo, kuchitira umboni kuti ufumu wa kumwamba wayandikira.” Maulaliki atsatanetsatane ankalembedwa mu Bulletin (imene masiku ano ndi Utumiki Wathu wa Ufumu). Komabe, poyamba anthu amene ankalalikira  nyumba ndi nyumba anali ochepa. Ena sanafune. Ankapereka zifukwa zosiyanasiyana, koma vuto lenileni linali lakuti iwo ankaona kuti kulalikira nyumba ndi nyumba kungawachotsere ulemu wawo. Gulu la Yehova litayamba kulimbikitsa kwambiri ntchito yolalikira, ambiri mwa anthu oterowo m’kupita kwa nthawi ananyanyala ndi kusiya gulu.

7. Kodi m’ma 1950 panaoneka vuto lotani ndipo panafunika chiyani?

7 Patapita zaka zambiri, anthu ambiri anayamba kulalikira. Koma zinali zoonekeratu kuti anthu afunika kuphunzitsidwa kulalikira nyumba ndi nyumba. Mwachitsanzo, kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1950, Mboni 28 pa 100 zilizonse ku United States zinali kungolalikira mwa kugawira timapepala basi kapena kuima m’misewu ndi magazini. Mboni zoposa 40 pa 100 zilizonse zinali zosakhazikika m’ntchito yolalikira, ndipo zinkatha miyezi yambiri popanda kulalikira. Kodi gulu likanatani pofuna kuthandiza Akhristu onse odzipereka kuti azilalikira nyumba ndi nyumba?

8, 9. Kodi mu 1953 panakhazikitsidwa ntchito yowaphunzitsa chiyani abale, ndipo zotsatira zake n’zotani?

8 Pamsonkhano wa mayiko umene unachitikira ku New York City mu 1953, nkhani ya utumiki wa ku nyumba ndi nyumba inakambidwa mwapadera. M’bale Nathan H. Knorr ananena kuti ntchito yaikulu ya oyang’anira achikhristu ikhale kuthandiza Mboni iliyonse kukhala mtumiki wokhazikika wotha kulalikira nyumba ndi nyumba. Iye anati: “Aliyense afunika kuti azitha kulalikira uthenga wabwino ku nyumba ndi nyumba.” Kuti zimenezi zitheke, panakhazikitsidwa ntchito yophunzitsa abale padziko lonse. Anthu amene anali asanayambe kulalikira nyumba ndi nyumba anaphunzitsidwa mmene angafikire anthu panyumba pawo, kupereka mfundo zogwira mtima za m’Baibulo, ndi kuyankha mafunso awo.

9 Ntchito yophunzitsa abale imeneyi inali ndi zotsatira zabwino kwambiri. M’zaka 10 zokha, chiwerengero cha ofalitsa padziko lonse chinawonjezereka ndi 100 peresenti, cha maulendo obwereza ndi 126 peresenti, ndipo cha maphunziro a Baibulo ndi 150 peresenti. Panopa, ofalitsa Ufumu pafupifupi 7 miliyoni akulalikira uthenga wabwino padziko lonse. Zimenezi ndi umboni wakuti Yehova akudalitsa khama la anthu ake muutumiki wa ku nyumba ndi nyumba.​—Yes. 60:22.

Kulemba Anthu Chizindikiro Kuti Adzapulumuke

10, 11. (a) Kodi Ezekieli anaona masomphenya otani, olembedwa pa Ezekieli chaputala 9? (b) Kodi masomphenyawo akukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

10 Masomphenya a mneneri Ezekieli angatithandize kuona kufunika kwa utumiki wa ku nyumba ndi nyumba. Ezekieli anaona amuna 7. Amuna 6 ananyamula zida, ndipo wa 7 anavala bafuta komanso anali ndi cholembera m’chuuno mwake. Mwamunayu anauzidwa ‘kupita pakati pa mudzi’ ndi ‘kulemba chizindikiro pa mphumi za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zochitidwa pakati pake.’ Atamaliza ntchito yolemba anthu chizindikiro, amuna 6 onyamula zida analamulidwa kupha anthu onse amene analibe chizindikiro.​—Werengani Ezekieli 9:1-6.

11 Ife timazindikira kuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa m’njira yakuti mwamuna “wovala bafuta” akuimira otsalira a Akhristu odzozedwa ndi mzimu. Kudzera m’ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira, odzozedwa mophiphiritsa amalemba chizindikiro anthu amene amakhala “nkhosa zina” za Khristu. (Yoh. 10:16) Kodi chizindikiro chimenecho n’chiyani? Ndi umboni wakuti nkhosazo zinadzipereka ndi kubatizidwa kukhala ophunzira a Yesu Khristu, ndipo zavala umunthu watsopano wofanana ndi wa Khristu. Umboniwu umaonekera bwino, ngati kuti walembedwa pamphumi pawo popanda kuphimbika. (Aef. 4:20-24) Anthu onga nkhosa amenewa amakhala gulu  limodzi ndi Akhristu odzozedwa ndipo amathandiza odzozedwawo pantchito yawo yofunika kwambiri yolemba chizindikiro anthu enanso.​—Chiv. 22:17.

12. Kodi masomphenya a Ezekieli olemba chizindikiro anthu pamphumi pawo, akusonyeza bwanji kufunika kwa ntchito imene tikuchita yofufuza anthu onga nkhosa?

12 Masomphenya a Ezekieli akusonyeza chifukwa china chimene tiyenera kugwirira mwachangu ntchito imene tikuchitayi, yofufuza anthu amene “akuusa moyo ndi kulira.” Chifukwa chake n’chakuti miyoyo ili pa chiswe. Posachedwapa, magulu a Yehova akumwamba amene ali ndi mphamvu yakupha, oimiridwa ndi amuna 6 onyamula zida, adzawononga anthu onse amene alibe chizindikiro. Ponena za chiweruzo chimene chikubwera, mtumwi Paulo analemba kuti Ambuye Yesu ndi “angelo ake amphamvu . . . adzabwezera chilango kwa osadziwa Mulungu ndi kwa osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.” (2 Ates. 1:7, 8) Onani kuti anthu adzaweruzidwa malinga ndi mmene akulabadirira uthenga wabwino. N’chifukwa chake ntchito yolengeza uthenga wa Mulungu siyenera kuima koma iyenera kupitirizabe mpaka mapeto. (Chiv. 14:6, 7) Zimenezi zikutanthauza kuti atumiki onse odzipereka a Yehova ali ndi udindo waukulu.​—Werengani Ezekieli 3:17-19.

13. (a) Kodi mtumwi Paulo ankaona kuti ali ndi udindo wotani, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi inuyo mumaona kuti muli ndi udindo wotani kwa anthu a m’gawo lanu?

13 Mtumwi Paulo ankaona kuti ndi udindo wake kuuza anthu ena uthenga wabwino. Iye analemba kuti: “Ineyo ndili ndi ngongole kwa Agiriki ndiponso kwa anthu amene si Agiriki, kwa anzeru ndiponso kwa opusa. Chotero ndikufunitsitsa kudzalengeza uthenga wabwino kwa inunso kumeneko ku Roma.” (Aroma 1:14, 15) Poyamikira chifundo chimene anachitiridwa, Paulo anakakamizika kuthandiza ena kuti apindule ndi kukoma mtima kwa m’chisomo kwa Mulungu monga mmene iyeyo anapindulira. (1 Tim. 1:12-16) Zinali ngati kuti iye anali ndi ngongole kwa munthu wina aliyense amene anakumana naye. Ndipo ngongoleyo akanaibweza kokha mwa kumuuza munthuyo uthenga wabwino. Kodi inuyo mumaona kuti muli ndi ngongole ngati imeneyi kwa anthu a m’gawo lanu?​—Werengani Machitidwe 20:26, 27.

14. Kodi chifukwa chachikulu chomwe timalalikirira kwa anthu onse komanso ku nyumba ndi nyumba n’chiyani?

14 Ngakhale kuti ntchito yopulumutsa miyoyo ya anthu ndi yofunika, pali chifukwa china chachikulu chomwe timalalikirira nyumba ndi nyumba. Mu ulosi wa pa Malaki 1:11, Yehova anati: “Kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo . . . adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu.” Pokwaniritsa ulosi umenewu, atumiki odzipereka a Yehova akutamanda dzina lake pakati pa anthu padziko lonse lapansi pamene modzichepetsa akuchita utumiki wawo. (Sal. 109:30; Mat. 24:14) Choncho, chifukwa chachikulu chimene timalalikirira kwa anthu onse komanso ku nyumba ndi nyumba n’chakuti ‘tipereke nsembe ya chitamando’ kwa Yehova.​—Aheb. 13:15.

Tikuyembekezera Zochitika Zazikulu

15. (a) Kodi Aisiraeli anawonjezera bwanji zochita zawo poguba mozungulira Yeriko patsiku la  7? (b) Kodi zimenezi zikusonyeza chiyani za ntchito yolalikira?

15 Kodi tikuyembekezera zotani pantchito yolalikira? Yankho lake likupezeka m’nkhani ya kuwonongedwa kwa Yeriko, yolembedwa m’buku la Yoswa. Kumbukirani kuti Mulungu atatsala pang’ono kuwononga Yeriko, anauza Aisiraeli kuti  agube mozungulira mzindawo kamodzi patsiku kwa masiku 6. Koma patsiku la 7, anafunika kuwonjezera zochita zawo. Yehova anauza Yoswa kuti: ‘Muzungulire mudziwo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe alize mphalasa. Ndipo kudzakhala kuti akaliza chilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, . . . anthu onse afuule mfuu yaikulu; ndipo linga la mudziwo lidzagwa pomwepo.’ (Yos. 6:2-5) N’kutheka kuti mofanana ndi zimenezi, ntchito yathu yolalikira idzawonjezereka. Mosakayikira, dongosolo lomwe lilipoli likamadzawonongedwa, dzina la Mulungu ndi Ufumu wake zidzakhala zitalalikidwa kwambiri kuposa kale lonse.

16, 17. (a) Kodi n’chiyani chimene chidzakhala chitachitika “chisautso chachikulu” chisanathe? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

16 Nthawi ingadzafike pamene uthenga umene timalalikira udzakhala ngati “mfuu yaikulu” ya nkhondo. M’buku la Chivumbulutso, mauthenga amphamvu a chiweruzo akuwasonyeza monga “matalala aakulu, lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20.” Ndipo lemba la Chivumbulutso 16:21 limati: “Mliriwo unali waukulu modabwitsa.” Pakali pano, sitikudziwa kuti utumiki wa ku nyumba ndi nyumba udzakhala wofunika motani pa ntchito yolengeza mauthenga omaliza achiweruzo. Koma chimene tikudziwa n’chakuti “chisautso chachikulu” chisanathe, dzina la Yehova lidzakhala litadziwika kwambiri kuposa kale lonse.​—Chiv. 7:14; Ezek. 38:23.

17 Ndiyetu tiyeni tipitirize kulalikira mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu pamene tikuyembekezera zochitika zazikuluzo. Pogwira ntchito imeneyi, kodi ndi mavuto otani amene timakumana nawo muutumiki wa ku nyumba ndi nyumba, ndipo kodi tingatani nawo? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso amenewa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Adiresi ya pa Intaneti ndi www.jw.org.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi maziko a m’Malemba a ntchito yolalikira nyumba ndi nyumba ndi ati?

• Kodi utumiki wa ku nyumba ndi nyumba wakhala ukulimbikitsidwa motani m’nthawi zamakono?

• N’chifukwa chiyani atumiki odzipereka a Yehova ali ndi udindo wolalikira?

• Kodi ndi zochitika zazikulu ziti zimene tikuyembekezera?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 4]

Mofanana ndi mtumwi Paulo, kodi inuyo mumaona kuti muli ndi udindo wolalikira kwa ena?

[Chithunzi patsamba 5]

M’bale Knorr, mu 1953