Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mulungu Ndi Amene Amakulitsa’!

‘Mulungu Ndi Amene Amakulitsa’!

 ‘Mulungu Ndi Amene Amakulitsa’!

“Wobzala kapena wothirira sali kanthu, koma Mulungu amene amakulitsa.”​—1 AKOR. 3:7.

1. Kodi ndife “antchito anzake a Mulungu” motani?

“ANTCHITO anzake a Mulungu.” Mtumwi Paulo ananena mawu amenewa pofotokoza mwayi umene tonsefe tingakhale nawo. (Werengani 1 Akorinto 3:5-9.) Apa Paulo anali kunena za ntchito yopanga ophunzira. Iye anayerekezera ntchitoyi ndi kubzala ndi kuthirira mbewu. Kuti tikwanitse ntchito yofunikayi, tifunikira thandizo la Yehova. Paulo akutikumbutsa kuti ‘Mulungu ndi amene amakulitsa.’

2. N’chifukwa chiyani mfundo yakuti ‘Mulungu ndi amene amakulitsa’ imatithandiza kuona moyenera utumiki wathu?

2 Kudziwa mfundo imeneyi kumatithandiza kukhala odzichepetsa ndiponso kuona moyenera utumiki wathu. Ife tingakhale akhama polalikira ndi kuphunzitsa, koma pamapeto pake mbewuyo ikakula, ulemerero wonse umapita kwa Yehova. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kaya tikhale akhama chotani, sitimvetsa kakulidwe ka mbewu, ndipo sitingathe ngakhale pang’ono kulamulira kakulidwe kakeko. Mfumu Solomo inafotokoza bwino zimenezi polemba kuti: “Sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.”​—Mlal. 11:5.

3. Kodi pali kufanana kotani pakati pa ntchito yofesa mbewu zenizeni ndi yopanga ophunzira?

3 Popeza kuti sitimvetsa kakulidwe ka mbewu, kodi ndiye kuti ntchito yathu ndi yosasangalatsa? Ayi si choncho. M’malomwake, m’pamene imasangalatsa kwambiri. Mfumu Solomo inati: “Mamawa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.” (Mlal. 11:6) Ndithudi, tikamafesa mbewu zenizeni, sitidziwa zimene zingamere kapenanso ngati zingamere n’komwe. Pamakhala zochitika zambiri zimene ife sitingathe kuzilamulira. Umu ndi mmenenso zilili ndi ntchito yopanga ophunzira. Yesu anasonyeza mfundo imeneyi m’mafanizo awiri, ofunika kuti tiwaone, olembedwa m’chaputala 4 cha Uthenga Wabwino wa Maliko. Tiyeni tione zimene tingaphunzire m’mafanizo awiriwa.

Dothi Losiyanasiyana

4, 5. Fotokozani mwachidule fanizo la Yesu la wofesa mbewu pozimwaza.

4 Pa Maliko 4:1-9, Yesu anafotokoza za wofesa mbewu amene anamwaza mbewu zimene zinagwera m’malo osiyanasiyana. Iye anati: “Tamverani. Wofesa mbewu anapita kukafesa. Pamene anali kufesa, mbewu zina zinagwera m’mbali mwa msewu, ndipo kunabwera mbalame ndi kuzidya. Mbewu zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira, ndipo mwamsanga zinamera chifukwa dothilo linali losazama. Koma dzuwa litakwera, zinawauka, ndipo popeza zinalibe mizu zinafota. Mbewu zina zinagwera paminga, ndipo mingayo inakula ndi kupinimbiritsa mbewuzo, moti sizinabale chipatso chilichonse. Koma zina zinagwera panthaka yabwino, ndipo zinamera ndi kukula, mwakuti zinayamba kubala zipatso, ina 30, ina 60, ndipo ina 100.”

5 M’nthawi za m’Baibulo, munthu akafuna kufesa mbewu ankachita kuzimwaza. Wofesayo anali kunyamula mbewuzo pachovala chake kapena m’kathumba, ndipo ankatapa mbewuzo ndi dzanja n’kuzimwaza uku ndi uku. Choncho, m’fanizo limeneli, wofesayo sakufesa dala mbewuzo m’dothi losiyanasiyana. Koma mbewu zomwazikazo zikugwera m’malo osiyanasiyana.

6. Kodi Yesu anafotokoza bwanji tanthauzo la fanizo la wofesa mbewu?

6 Sitikufunikira kulota tanthauzo la fanizo limeneli. Pa Maliko 4:14-20, Yesu anafotokoza tanthauzo  lake kuti: “Wofesayo amafesa mawu. Chotero anthu amenewa, ndiwo mbewu zimene zimagwera m’mphepete mwa msewu kumene mawu afesedwa; koma atangomva mawuwo, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu ofesedwa mwa iwo. Momwemonso, anthu amenewa ndiwo mbewu zofesedwa pamiyala: atangomva mawuwo, amawalandira ndi chimwemwe. Iwo amakhala opanda mizu mwa iwo okha, ndipo amapitirizabe kwa kanthawi; koma chisautso kapena mazunzo akangobuka chifukwa cha mawuwo, amapunthwa. Koma palinso mbewu zina zofesedwa paminga; zimenezi ndiwo anthu amene amamva mawu, koma nkhawa za m’dongosolo lino la zinthu, ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma, komanso zilakolako za zinthu zina, zimalowa ndi kupinimbiritsa mawuwo, ndipo sabala zipatso. Potsirizira pake, zimene zinafesedwa panthaka yabwino, ndiwo anthu amene amamvetsera mawu ndi kuwalandira bwino, ndipo amabala zipatso wina 30, wina 60, ndipo wina 100.”

7. Kodi mbewu ndiponso dothi losiyanasiyana zikuimira chiyani?

7 Onani kuti Yesu sakunena kuti mbewu zosiyanasiyana zikufesedwa. M’malomwake akunena za mtundu umodzi wa mbewu zimene zikugwera pa dothi losiyanasiyana, ndipo zotsatira zake zikukhala zosiyanasiyananso. Dothi loyamba ndi lolimba, lachiwiri ndi losazama, lachitatu pali minga, ndipo lachinayi ndi labwino, kapena kuti lachonde, ndipo likubala zipatso zambiri. (Luka 8:8) Kodi mbewuyo n’chiyani? Ndi uthenga wa Ufumu wopezeka m’Mawu a Mulungu. (Mat. 13:19) Nanga dothi losiyanasiyana likuimira chiyani? Likuimira anthu amitima yosiyanasiyana.​—Werengani Luka 8:12, 15.

8. (a) Kodi wofesa mbewu akuimira ndani? (b) N’chifukwa chiyani anthu amalabadira mosiyanasiyana ntchito yolalikira Ufumu?

8 Kodi wofesa mbewu akuimira ndani? Akuimira antchito anzake a Mulungu, anthu amene akulengeza uthenga wabwino wa Ufumu. Mofanana ndi Paulo komanso Apolo, iwo amabzala ndi kuthirira. Koma ngakhale agwire ntchito mwakhama, zotsatira zake zimakhala zosiyanasiyana. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mitima ya anthu amene amamva uthengawo imasiyanasiyana. M’fanizoli, wofesa mbewu satha kulamulira kakulidwe ka mbewuzo. Zimenezi n’zokhazika mtima pansi, makamaka kwa abale ndi alongo okhulupirika amene agwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali, mwinanso zaka makumi angapo, ndipo zotsatira zake sizioneka. * N’chifukwa chiyani mfundo imeneyi ili yokhazika mtima pansi?

9. Kodi ndi mfundo yokhazika mtima pansi yotani imene mtumwi Paulo ndiponso Yesu anatsindika?

 9 Zotsatira za ntchito ya wofesa mbewu si zimene zimaonetsa kuti iye ndi wokhulupirika kapena ayi. Paulo anasonyeza zimenezi pamene anati: “Aliyense payekha adzalandira mphoto yake mogwirizana ndi ntchito yake.” (1 Akor. 3:8) Munthu amalandira mphoto malinga ndi ntchito yake, osati zotsatira za ntchito yakeyo. Yesu anatsindikanso mfundo imeneyi, ophunzira ake atabwera kuchokera ku ulendo wolalikira. Iwo anasangalala kwambiri chifukwa chakuti ziwanda zinawagonjera atagwiritsa ntchito dzina la Yesu. Ngakhale kuti zimenezi zinali zosangalatsa, Yesu anawauza kuti: “Musakondwere ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjerani, koma kondwerani chifukwa maina anu alembedwa kumwamba.” (Luka 10:17-20) Ngakhale ngati wofesa mbewu ataona kuti anthu sakuwonjezereka chifukwa cha ntchito yake, sindiye kuti iye salimbikira kapenanso kuti ndi wosakhulupirika poyerekeza ndi ena. Mokulira, zotsatira za ntchito yake zimadalira mmene mitima ya anthu omva uthenga wakewo ilili. Koma mfundo ndi yakuti Mulungu ndi amene amakulitsa.

Udindo wa Anthu Amene Amamva Mawu

10. Kodi n’chiyani chimachititsa munthu amene amamva mawu kukhala ngati dothi labwino kapena loipa?

10 Bwanji za anthu amene amamva mawu? Kodi zinalembedweratu kuti iwo adzalabadira? Ayi. Zili kwa iwo kusankha kukhala ngati dothi labwino kapena loipa. Zoonadi, mtima wa munthu ungasinthe, n’kumuchititsa kulabadira kapena kusalabadira. (Aroma 6:17) M’fanizo lake, Yesu ananena kuti ena “atangomva” mawu, Satana amabwera ndi kuchotsa mawuwo. Koma n’zotheka kupewa zimenezi. Pa Yakobe 4:7, Akhristu akulimbikitsidwa ‘kutsutsa Mdyerekezi,’ ndipo akatero iye adzawathawa. Yesu akufotokoza kuti ena poyamba amalandira mawu ndi chimwemwe koma kenako amapunthwa chifukwa iwo “amakhala opanda mizu mwa iwo okha.” Koma atumiki a Mulungu akulangizidwa kuti ‘azike mizu ndi kukhazikika pa maziko,’ n’cholinga chakuti athe kudziwa bwino lomwe ‘m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama, ndi kuti adziwe chikondi cha Khristu chimene chiposa kudziwa zinthu konse.’​—Aef. 3:17-19; Akol. 2:6, 7.

11. Kodi munthu angapewe bwanji kulola nkhawa ndi chuma kupinimbiritsa mawu?

11 Ena amene amamva mawu, akufotokozedwa kuti amalola “nkhawa za m’dongosolo lino la zinthu, ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma” kulowa ndi kupinimbiritsa mawuwo. (1 Tim. 6:9, 10) Kodi iwo angapewe bwanji zimenezi? Mtumwi Paulo akuyankha kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo panthawiyo. Pakuti iye anati: ‘Mulimonse sindidzakusiyani, ngakhale kukutayani konse.’”​—Aheb. 13:5.

12. N’chifukwa chiyani anthu amene akuimiridwa ndi nthaka yabwino amabala zipatso mosiyanasiyana?

12 Pomaliza, Yesu akunena kuti mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino ‘zimabala zipatso zina 30, zina 60, ndipo zina 100.’ Ngakhale kuti ena amene amalabadira mawu ali ndi mtima wabwino ndipo amabala zipatso, zimene amakwanitsa kuchita polengeza uthenga wabwino zimasiyanasiyana chifukwa cha zinthu zina pamoyo wawo. Mwachitsanzo, chifukwa cha ukalamba kapena matenda, ena sangachite zambiri m’ntchito yolalikira. (Yerekezerani ndi Maliko 12:43, 44.) Apanso n’zovuta kapena n’zosatheka kuti wofesa mbewu alamulire zimenezi, koma amakondwera akaona kuti Yehova wakulitsa mbewuzo.​—Werengani Salmo 126:5, 6.

Wofesa Mbewu Amene Amagona

13, 14. (a) Fotokozani mwachidule fanizo la Yesu la munthu womwaza mbewu. (b) Kodi wofesayu ndiponso mbewu zikuimira chiyani?

13 Pa Maliko 4:26-29, tikupezapo fanizo lina lonena za wofesa mbewu. Fanizoli limati: “Chotero ufumu wa Mulungu uli ngati mmene munthu amamwazira mbewu panthaka, ndipo amagona usiku n’kumadzuka kukacha. Mbewuzo zimamera ndi kukula. Koma kwenikweni mmene zimenezi zimachitikira, mwini wakeyo sadziwa ayi. Payokha nthaka ija imabala zipatso m’kupita kwa nthawi, choyamba mmera umabiriwira, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera m’ngalamo. Koma zipatso  zikacha, iye amamweta ndi chikwakwa, chifukwa nthawi yokolola yakwana.”

14 Kodi wofesa mbewu ameneyu ndani? Anthu ena m’Matchalitchi Achikhristu amakhulupirira kuti wofesayo ndi Yesu mwini wakeyo. Koma kodi n’zomveka kunena kuti Yesu amagona ndipo sadziwa kakulidwe ka mbewu? Kunena zoona, Yesu amadziwa kakulidwe ka mbewu. Choncho wofesayu, mofanana ndi wa m’fanizo loyamba lija, akuimira olengeza Ufumu, amene amafesa mbewu za Ufumu kudzera m’ntchito yolalikira imene amaigwira mwachangu. Mbewu imene amamwaza pa nthaka ndi mawu amene iwo amalalikira. *

15, 16. Kodi ndi mfundo yotani yokhudza kukula kwa mbewu ndi kukula kwauzimu imene Yesu anafotokoza m’fanizo lake la wofesa mbewu?

15 Yesu akufotokoza kuti wofesayo “amagona usiku n’kumadzuka kukacha.” Zimenezi sizikutanthauza kuti wofesayo akunyalanyaza mbewuzo. Zikungosonyeza zimene zimachitika pa moyo wa anthu ambiri. Mawu a m’vesi limeneli akusonyeza zinthu zochitika mobwerezabwereza kwa nthawi yaitali, kugwira ntchito kukacha ndi kugona usiku. Yesu akufotokoza zimene zimachitika pa nthawiyo. Iye akuti: “Mbewuzo zimamera ndi kukula.” Kenako akuwonjezera kuti: “Koma kwenikweni mmene zimenezi zimachitikira, mwini wakeyo sadziwa ayi.” Apa akutsindika mfundo yakuti kukulako kumachitika ‘pakokha.’ *

16 Kodi mfundo ya Yesu pamenepa ndi yotani? Onani kuti iye akutsindika za kukula kwa mbewu ndiponso kuti kukulako kumachitika pang’onopang’ono. “Payokha nthaka ija imabala zipatso m’kupita kwa nthawi, choyamba mmera umabiriwira, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera m’ngalamo.” (Maliko 4:28) Kukulako kumachitika pang’onopang’ono, chinthu chimodzi panthawi yake. Palibe amene angakakamize kapena kufulumizitsa kukulako. Zimateronso ndi kukula kwauzimu. Kukulako kumachitika panthawi yake pamene Yehova akulola choonadi kukula mu mtima wa munthu amene ali ndi maganizo oyenerera.​—Mac. 13:48; Aheb. 6:1.

17. Kodi ndani amasangalala nawo mbewu ya choonadi ikabala zipatso?

17 Kodi wofesayo amakolola nawo bwanji “zipatso zikacha”? Yehova akakulitsa choonadi cha  Ufumu m’mitima ya ophunzira atsopano, m’kupita kwa nthawi iwo amafika poti chikondi chawo pa Mulungu chimawalimbikitsa kupereka moyo wawo kwa iye. Amasonyeza kudzipereka kwawoko mwa kubatizidwa m’madzi. M’kupita kwa nthawi, abale amene amapitirizabe kukula mpaka kukhwima mwauzimu amatha kukhala ndi maudindo ena mumpingo. Zipatso za Ufumu zimakololedwa ndi wofesa uja ndiponso ndi olengeza Ufumu ena amene mwina sanafese nawo mbewu imene yabala wophunzira ameneyo. (Werengani Yohane 4:36-38.) Inde, ‘wofesa mbewu ndi wokolola amasangalalira pamodzi.’

Zimene Tikuphunzirapo Masiku Ano

18, 19. (a) Kodi nkhani ya mafanizo a Yesu imeneyi yakulimbikitsani bwanji inuyo panokha? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

18 Kodi taphunzirapo chiyani pa mafanizo awiriwa a m’chaputala 4 cha Maliko? Taphunzira kuti tilidi ndi ntchito yoti tigwire, ntchito yofesa. Tisalole zifukwa zina ndi zina komanso mavuto ongowaganizira kutilepheretsa kugwira ntchito imeneyi. (Mlal. 11:4) Tadziwa kuti tili ndi mwayi waukulu kukhala antchito anzake a Mulungu. Yehova ndi amene amakulitsa munthu mwauzimu, podalitsa khama lathu ndi khama la anthu amene amalandira uthenga. Tadziwa kuti sitingakakamize munthu kukula mwauzimu. Komanso sitifunika kugwa ulesi kapena kutaya mtima ngati munthu akuchedwa kukula kapena sakukula n’komwe. N’zokhazika mtima pansi kwambiri kudziwa kuti zimene zimasonyeza kuti tikuchita bwino, ndi kukhulupirika kwathu kwa Yehova komanso pantchito imene watipatsa yolalikira “uthenga wabwino . . . wa ufumu . . . kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse.”​—Mat. 24:14.

19 Kodi Yesu akutiphunzitsanso chiyani zokhudza kukula kwa ophunzira atsopano ndi zokhudza ntchito ya Ufumu? Yankho la funso limeneli likupezeka m’mafanizo ena olembedwa m’Mauthenga Abwino. M’nkhani yotsatira, tidzaona bwinobwino ena mwa mafanizo amenewa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Mwachitsanzo, onani nkhani yofotokoza za utumiki wa M’bale Georg Fjölnir Lindal ku Iceland mu Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 2005, masamba 210-211, komanso onani Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 1988, masamba 82-99, kuti mumve nkhani za atumiki okhulupirika amene analalikira kwa zaka zambiri ku Ireland ngakhale kuti zotsatira zake zinatenga nthawi.

^ ndime 14 M’mbuyomu magazini ino inafotokoza kuti mbewu ikuimira makhalidwe a munthu ofunikira kukula mpaka kukhwima, ndipo kakulidwe ka makhalidwewo kamakhudzidwa ndi zinthu monga malo ndi anthu okhala nawo. Komabe, onani kuti m’fanizo la Yesu mbewu sikusintha kukhala yoipa kapena yovunda. Ikungokula mpaka kukhwima.​—Onani Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya June 15, 1980, masamba 17-19.

^ ndime 15 Malo enanso pamene pamapezeka mawuwa ndi pa Machitidwe 12:10 basi, pamene pamati chipata chachitsulo chinatseguka “chokha.”

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi pali kufanana kotani pakati pa kufesa mbewu ndi kulalikira uthenga wa Ufumu?

• Kodi Yehova amaona chiyani kuti anene kuti mlaliki wa Ufumu ndi wokhulupirika?

• Kodi ndi kufanana kotani pakati pa kukula kwa mbewu ndi kukula kwauzimu kumene Yesu anatsindika?

• Kodi ‘wofesa mbewu ndi wokolola amasangalalira pamodzi’ motani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 13]

N’chifukwa chiyani Yesu anayerekezera mlaliki wa Ufumu wa Mulungu ndi wofesa mbewu?

[Zithunzi patsamba 15]

Anthu oimiridwa ndi nthaka yabwino amalalikira za Ufumu ndi mtima wonse, malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wawo

[Zithunzi patsamba 16]

Mulungu ndi amene amakulitsa