Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mtumwi Paulo ananena kuti “Isiraeli yense adzapulumuka.” (Aroma 11:26) Kodi iye anatanthauza kuti panthawi inayake Ayuda onse adzatembenuka n’kukhala Akhristu?

Ayi, si zimene Paulo anatanthauza. Mtunduwo, umene unali mbadwa za Abulahamu, unakana kulandira Yesu monga Mesiya. Ndipo Yesu atamwalira, zinaonekeratu kuti monga mtundu, si Ayuda onse amene adzatembenuka n’kukhala Akhristu. Komabe, mawu a Paulo akuti “Isiraeli yense adzapulumuka” anali oona. N’chifukwa chiyani tikutero?

Yesu anauza atsogoleri achipembedzo cha Chiyuda kuti: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu ndi kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.” (Mat. 21:43) Popeza kuti mtundu wonse wa Isiraeli unakana Yesu, Yehova anasankha mtundu watsopano wauzimu. Paulo anatcha mtunduwo “Isiraeli wa Mulungu.”​—Agal. 6:16.

Mavesi ena m’Malemba Achigiriki Achikristu amasonyeza kuti “Isiraeli wa Mulungu” wapangidwa ndi Akhristu odzozedwa ndi mzimu okwanira 144,000. (Aroma 8:15-17; Chiv. 7:4) Lemba la Chivumbulutso 5:9, 10, limatsimikizira kuti gululi limaphatikizapo anthu amene si Ayuda, chifukwa limati Akhristu odzozedwa akuchokera “mu fuko lililonse, lilime, mtundu, ndi dziko lililonse.” Anthu amene amapanga Isiraeli wauzimu anasankhidwa kuti akhale “ufumu ndi ansembe . . . , mwakuti adzalamulira dziko lapansi monga mafumu.” Ngakhale kuti Yehova anakana mtundu wake wa Isiraeli, ena mwa iwo akanatha kuyanjidwanso ndi iye. Izi n’zimene zinachitika ndi atumwi ndi Akhristu ena ambiri oyambirira. Komabe, Ayuda amenewo, mofanana ndi anthu ena onse, anafunikira kuwomboledwa ndi magazi a Yesu Khristu.​—1 Tim. 2:5, 6; Aheb. 2:9; 1 Pet. 1:17-19.

Ayuda ambiri m’nthawi ya Yesu anataya mwayi wokalamulira limodzi naye, koma zimenezi sizinalepheretse cholinga cha Mulungu. Cholinga cha Mulungu sichilephereka, chifukwa Yehova, kudzera mwa mneneri wake, anati: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”​—Yes. 55:11.

Mogwirizana ndi mawuwa, cholinga cha Mulungu chakuti anthu 144,000 akalamulire limodzi ndi Mwana wake kumwamba, sichingalephereke. Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu adzadzoza anthu okwana 144,000. Sipadzaperewera ngakhale mmodzi.​—Chiv. 14:1-5.

Motero, pamene Paulo anati “Isiraeli yense adzapulumuka,” sanali kunena kuti mtundu wonse wa Ayuda udzatembenuka n’kulowa Chikhristu. Koma iye anatanthauza kuti cholinga cha Mulungu chakuti anthu 144,000 omwe akupanga Isiraeli wauzimu akalamulire ndi Mwana wake Yesu Khristu kumwamba, chidzakwaniritsidwa. Nthawi ya Mulungu ikadzakwana, “Isiraeli yense,” osasiyako ndi mmodzi yemwe, adzapulumuka ndipo adzalamulira ngati mafumu ndi ansembe mu Ufumu wa Mesiya.​—Aef. 2:8.

[Zithunzi patsamba 28]

Odzozedwa akuchokera “mu fuko lililonse, lilime, mtundu, ndi dziko lililonse”