Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Gonjerani Ulamuliro wa Yehova

Gonjerani Ulamuliro wa Yehova

 Gonjerani Ulamuliro wa Yehova

“Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake; ndipo malamulo akewo si olemetsa.”​—1 YOH. 5:3.

1, 2. (a) Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano amaipidwa ndi nkhani yogonjera ulamuliro? (b) Kodi anthu omwe safuna kugonjera ena ndi odziimiradi paokha? Fotokozani.

ANTHU ambiri masiku ano amadana ndi ulamuliro. Ambiri amaipidwa ndi kugonjera munthu wina. Anthu amene safuna kugonjera ena, amakhala ndi maganizo akuti, “Sindifuna wina kundiuza chochita.” Koma kodi ndi zoona kuti anthu amenewa ndi odziimira paokha? Kutalitali! Ambiri amatsatira mfundo za anthu omwe ‘amatengera nzeru za dongosolo lino la zinthu.’ (Aroma 12:2) M’malo modziimira paokha, iwo ndi “akapolo a chivundi,” tikatengera mawu a mtumwi Petulo. (2 Pet. 2:19) Anthuwa amayenda “mogwirizana ndi dongosolo la zinthu la m’dzikoli, momveranso wolamulira wa mphamvu ya mumpweya,” Satana Mdyerekezi.​—Aef. 2:2.

2 Munthu wina wolemba mabuku ananena monyada kuti: “Sindilola makolo, kaya wansembe, kaya m’busa . . . kapena Baibulo kundiuza chochita.” Ndi zoona kuti anthu ena angagwiritse ntchito mphamvu zawo molakwika ndipo sangayenerere kuwamvera. Koma kodi kukaniratu kuti sitifunikira munthu wina kutipatsa malangizo kumathandiza? Yankho lake likupezeka mu nkhani zimene zimatuluka m’manyuzipepala. Nkhani zakezo zimakhala zomvetsa chisoni zokhazokha. Panthawi ino anthu akufunika kwambiri malangizo. Koma mwatsoka, ambiri safuna malangizowo.

Mmene Ife Timaonera Ulamuliro

3. Kodi Akhristu oyambirira anasonyeza bwanji kuti sanangomvera zilizonse zimene olamulira aumunthu anawalamula?

3 Akhristufe timaona ulamuliro mosiyana ndi  mmene dzikoli limaonera. Izi sizikutanthauza kuti timangochita chilichonse chimene tauzidwa kuchita. Nthawi zina timakana kugonjera zofuna za ena, kaya akhale ndi ulamuliro wotani. Umu ndi mmenenso Akhristu oona oyambirira anachitira. Mwachitsanzo, atumwi atalamulidwa kuti asiye kulalikira, sanagonjere mkulu wa ansembe ndi akuluakulu ena amene anali m’Bungwe Lalikulu la Ayuda. Iwo sanasiye kuchita zabwino kuti amvere olamulira aumunthu.​—Werengani Machitidwe 5:27-29.

4. Kodi ndi zitsanzo ziti m’Malemba Achiheberi zomwe zikusonyeza kuti anthu ambiri a Mulungu sanatsatire zimene ena ankachita?

4 Nawonso atumiki a Mulungu amene anakhalako Chikhristu chisanayambe, anasonyeza kulimba mtima. Mwachitsanzo, Mose “anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao, nasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu,” ngakhale kuti kuchita zimenezi kunautsa mkwiyo wa “mfumu.” (Aheb. 11:24, 25, 27) Yosefe anakana kugona ndi mkazi wa Potifara, ngakhale kuti mkaziyo anali ndi mphamvu yomulanga mwina kumukonzera chiwembu. (Gen. 39:7-9) Danieli ali ku Babulo “anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu,” ngakhale kuti zofuna zakezo zinali zovuta kuti mkulu wa adindo a kunyumba ya mfumu azivomereze. (Dan. 1:8-14) Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti kuyambira kale, anthu a Mulungu akhala osasunthika pochita zabwino, ngakhale pamene kuchita zimenezi kukanawabweretsera mavuto. Iwo sanagonjere anthu pofuna kuti awakonde. Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi.

5. Kodi mmene timaonera ulamuliro, zimasiyana bwanji ndi mmene dziko limauonera?

5 Kusagonja kumeneku sikutanthauza kuti ndife aliuma kapena amakani, ndipo sitili ngati anthu ena amene amapanduka pofuna kusonyeza kuti sakusangalala ndi mmene ndale zikuyendera. Ife timafuna kugonjera ulamuliro wa Yehova kuposa wa munthu wina aliyense. Lamulo la munthu likatsutsana ndi lamulo la Mulungu, sitivutika kusankha chochita. Mofanana ndi atumwi, timamvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.

6. Kodi n’chifukwa chiyani ndi bwino nthawi zonse kumvera malamulo a Yehova?

6 Kodi n’chifukwa chiyani ifeyo timagonjera ulamuliro wa Mulungu? N’chifukwa chakuti timamvera mawu a pa Miyambo 3:5, 6 akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” Timakhulupirira kuti chilichonse chimene Mulungu amafuna kuti tichite, chimapindulitsa ife tomwe. (Werengani Deuteronomo 10:12, 13.) Pajatu Yehova anauza Aisiraeli kuti: ‘Ine ndine amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.’ Ndipo anawonjezera kuti: “Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.” (Yes. 48:17, 18) Ife timakhulupirira mawu amenewa. Sitikayika ngakhale pang’ono kuti tikamamvera malamulo a Mulungu, timapindula nthawi zonse.

7. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati sitikumvetsa lamulo linalake lopezeka m’Mawu a Mulungu?

7 Timagonjera ulamuliro wa Yehova ndi kumumvera ngakhale pamene sitikumvetsa lamulo linalake lopezeka m’Mawu ake. Timachita zimenezi chifukwa chomudalira, osati kungokhulupirira zinthu popanda maziko. Zimenezi zimasonyeza kuti timakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova amadziwa zinthu zabwino kwa ife. Kumvera kwathu kumasonyezanso kuti timamukonda. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.” (1 Yoh. 5:3) Koma palinso mbali ina ya kumvera imene sitiyenera kuinyalanyaza.

Kuphunzitsa Luntha Lathu la Kuzindikira

8. Kodi ‘kuphunzitsa luntha lathu la kuzindikira’ kungatithandize bwanji kugonjera ulamuliro wa Yehova?

8 Baibulo limatilangiza kuti tiyenera ‘kuphunzitsa luntha lathu la kuzindikira, kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.’ (Aheb. 5:14) Choncho, sitifunika kumvera malamulo a Mulungu mongotengeka, popanda kuganizira. M’malomwake, tifunika kuti tizitha “kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika,” malinga ndi mfundo za  Yehova. Tifunika kuona ubwino wa njira za Yehova, kuti tigwirizane ndi wamasalmo amene anati: ‘Malamulo anu ali m’kati mwa mtima wanga.’​—Sal. 40:8.

9. Kodi tingachite chiyani kuti chikumbumtima chathu chigwirizane ndi mfundo za Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani tifunika kuchita zimenezi?

9 Kuti tione kufunika kwa malamulo a Mulungu monga wamasalmoyu, tifunika kusinkhasinkha zimene timawerenga m’Baibulo. Mwachitsanzo, tikaphunzira lamulo linalake la Yehova, tingadzifunse kuti: ‘Kodi n’chifukwa chiyani lamuloli kapena mfundo imeneyi ndi yanzeru? Kodi kumvera lamulo limeneli kuli ndi ubwino wotani? Kodi anthu amene amanyalanyaza malangizo a Mulungu pankhani imeneyi, amagwera m’mavuto otani?’ Ngati chikumbumtima chathu chimagwirizana ndi njira za Yehova, mosakayikira tidzapanga zosankha zogwirizana ndi chifuniro chake. Tidzatha ‘kupitiriza kuzindikira chifuniro cha Yehova’ ndi kuchita chifuniro chakecho mwa kukhala omvera. (Aef. 5:17) Koma nthawi zina kuchita zimenezi ndi kovuta.

Satana Amayesetsa Kupeputsa Ulamuliro wa Mulungu

10. Tchulani njira imodzi yosonyeza kuti Satana wakhala akuyesetsa kupeputsa ulamuliro wa Mulungu.

10 Satana wakhala akuyesetsa kupeputsa ulamuliro wa Mulungu kuyambira kale. Ndipo mzimu wake wodziimira payekha umaonekera mwa anthu m’njira zambiri. Mwachitsanzo, anthu salemekeza mfundo za Mulungu pankhani ya ukwati. Ena amakhalira limodzi popanda kukwatirana mwalamulo, pamene enanso amafunafuna njira zothetsera ukwati wawo n’cholinga choti amasuke. Magulu onsewa ayenera kuti amagwirizana ndi zimene mayi wina, yemwe ndi katswiri wa mafilimu, ananena motsindika kuti: “N’zosatheka kukhala ndi mwamuna kapena mkazi mmodzi yekha.” Iye ananenanso kuti: “Sindikudziwa munthu aliyense wapabanja amene ali wokhulupirika kapena amene amafuna kutero.” Katswiri winanso wa mafilimu, yemwe anakhalapo ndi akazi osiyanasiyana, ananena kuti: “Ndikukayikira ngati tinalengedwa kuti tizikhala ndi mkazi kapena mwamuna mmodzi moyo wathu wonse.” Ndiyeno tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimagonjera ulamuliro wa Yehova pankhani ya ukwati, kapena ndili ndi maganizo a dzikoli osalemekeza ukwati?’

11, 12. (a) N’chifukwa chiyani kungakhale kovuta kuti achinyamata agonjere ulamuliro wa Yehova? (b) Fotokozani chitsanzo chosonyeza kuti kunyalanyaza malamulo ndi mfundo za Yehova n’kupusa.

11 Kodi ndinu wachinyamata ndipo muli m’gulu la Yehova? Ngati zili choncho, Satana akufunitsitsa kuti muzipeputsa ulamuliro wa Yehova. Chifukwa cha “zilakolako za unyamata” ndiponso anzanu, mungayambe kuganiza kuti malamulo a Mulungu ndi olemetsa. (2 Tim. 2:22) Koma musalole zimenezi. M’malomwake yesetsani kuona ubwino wa mfundo za Mulungu. Mwachitsanzo, Baibulo limakulamulani kuti, “thawani dama.” (1 Akor. 6:18) Apanso dzifunseni kuti: ‘Kodi n’chifukwa chiyani lamuloli lili lanzeru? Kodi kumvera lamulo limeneli kuli ndi ubwino wotani?’ Muyenera kuti mukudziwa anthu ena omwe ananyalanyaza malangizo a Mulungu ndipo anagwera m’mavuto aakulu chifukwa cha tchimo lawo. Kodi panopa iwo akusangalaladi? Kodi iwo ali ndi moyo wabwino kuposa umene anali nawo ali m’gulu la Yehova? Kodi kapena iwo apezadi chinsinsi cha chimwemwe chimene atumiki ena onse a Mulungu sakuchipeza?​—Werengani Yesaya 65:14.

12 Tamverani zimene mlongo wina, dzina lake Sharon, ananena m’mbuyomu. Iye anati: “Chifukwa chosamvera malamulo a Yehova, ndinatenga  matenda oopsa a Edzi. Ndimati ndikakumbukira, ndimaona kuti ndinkasangalala kwambiri zaka zonse zimene ndinali kutumikira Yehova.” Sharon anazindikira kuti anapusa posamvera malamulo a Yehova ndipo akanachita bwino akanawalemekeza kwambiri. Ndithudi malamulo a Yehova amatiteteza. Patangopita milungu 7 atalemba mawu amenewa, Sharon anamwalira. Nkhani yomvetsa chisoni imeneyi ikusonyeza kuti palibe chinthu chabwino chilichonse chimene Satana angapatse anthu amene amakhala mbali ya dongosolo loipali. Popeza iye ndi “tate wake wa bodza,” amalonjeza zinthu zambirimbiri koma zimene amalonjezazo zimangopita ndi mphepo, ngati mmene zinachitikira ndi Hava. (Yoh. 8:44) Kunena zoona, ndi bwino nthawi zonse kugonjera ulamuliro wa Yehova.

Pewani Mzimu Wofuna Kudziimira Panokha

13. Kodi tingafunike kupewa mzimu wofuna kudziimira patokha pankhani ina iti?

13 Kuti tigonjere ulamuliro wa Yehova, timafunika kupewa mzimu wofuna kudziimira patokha. Ngati tili ndi mtima wodzikuza, tingayambe kuganiza kuti sitikufunikira kupatsidwa malangizo ndi wina aliyense. Mwachitsanzo, tingakane uphungu woperekedwa ndi anthu amene akutsogolera m’gulu la Mulungu. Mulungu wakhazikitsa dongosolo lakuti kapolo wokhulupirika ndi wanzeru azipereka chakudya chauzimu panthawi yoyenera. (Mat. 24:45-47) Modzichepetsa, tiyenera kuzindikira kuti Yehova akugwiritsa ntchito njira imeneyi posamalira anthu ake masiku ano. Tikhale ngati atumwi okhulupirika aja. Ophunzira ena atakhumudwa, Yesu anafunsa atumwiwo kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” Petulo anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.”​—Yoh. 6:66-68.

14, 15. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera uphungu wa m’Baibulo modzichepetsa?

14 Kugonjera ulamuliro wa Yehova kumaphatikizapo kulabadira uphungu wa m’Mawu ake. Mwachitsanzo, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wakhala akutichenjeza kuti “tikhalebe maso ndi kusunga maganizo athu.” (1 Ates. 5:6) Uphungu umenewu ndi woyenereradi masiku otsiriza ano pamene anthu ambiri ndi “odzikonda, okonda ndalama.” (2 Tim. 3:1, 2) Kodi zingatheke kuti ife n’kutengera maganizo ofala amenewa? Inde. Tingayambe kuwodzera mpaka kugona mwauzimu chifukwa chofunafuna zinthu za dzikoli, kapena tingayambe kukonda zinthu zakuthupi. (Luka 12:16-21) Choncho, ndi nzeru kumvera uphungu wa m’Baibulo ndi kupewa moyo wodzikonda umene wafala m’dziko la Satanali.​—1 Yoh. 2:16.

15 Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amagwiritsa ntchito akulu kupereka chakudya chauzimu m’mipingo. Baibulo limatilangiza kuti: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankha mlandu. Teroni kuti achite ntchito yawo mwa chimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuwonongani.” (Aheb. 13:17) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti akulu mumpingo salakwa? Ayi, amalakwa. Ndipo Mulungu amaona zolakwa zawo zonse kuposa munthu aliyense. Komabe, iye amafuna kuti ife tiziwagonjera. Tikamagwirizana ndi akulu, ngakhale kuti ndi opanda ungwiro, timasonyeza kuti timagonjera ulamuliro wa Yehova.

Kudzichepetsa N’kofunika

16. Kodi tingasonyeze motani kuti timalemekeza Yesu, Mutu wa mpingo wachikhristu?

16 Nthawi zonse tiyenera kukumbukira kuti Yesu ndiyedi Mutu wa mpingo. (Akol. 1:18)  Chimenechi ndi chifukwa china chimene chimatichititsa kumvera modzichepetsa malangizo a akulu, ndi kuwapatsa “ulemu wowirikiza.” (1 Ates. 5:12, 13) Nawonso akulu mumpingo angasonyeze mtima wogonjera mwa kuonetsetsa kuti akupereka uthenga wa Mulungu kumpingo, osati maganizo awoawo. Iwo ‘sapitirira zinthu zolembedwa’ kuti alimbikitse mfundo za m’mutu mwawo.​—1 Akor. 4:6.

17. N’chifukwa chiyani mzimu wokhumba udindo uli woopsa?

17 Tonse mumpingo tiyenera kusamala kuti tipewe kufunafuna ulemu. (Miy. 25:27) Zikuoneka kuti ili ndi vuto limene wophunzira wina amene mtumwi Yohane anakumana naye anali nalo. Yohane analemba kuti: “Diotirefe, wokonda kukhala woyamba uja pakati pawo, salandira chilichonse mwaulemu kwa ife. Ndiye chifukwa chake ndikadzabwera, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene akuchitirachitirabe, pomatijeda ndi mawu oipa.” (3 Yoh. 9, 10) Apa pali phunziro kwa ife masiku ano. Tikupezapo chifukwa chabwino chochotseratu maganizo okhumba udindo amene tingakhale nawo. Baibulo limatichenjeza kuti: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.” Anthu amene amagonjera ulamuliro wa Mulungu ayenera kupewa msampha wodzikuza, chifukwa ngati satero adzachititsidwa manyazi.​—Miy. 11:2; 16:18.

18. Kodi n’chiyani chingatithandize kugonjera ulamuliro wa Yehova?

18 Ndiyetu, chikhale cholinga chanu kukana mzimu wa dzikoli wofuna kudziimira pawekha komanso chikhale cholinga chanu kugonjera ulamuliro wa Yehova. Nthawi ndi nthawi, muzisinkhasinkha za mwayi waukulu umene muli nawo wotumikira Yehova. Kukhala kwanu pakati pa anthu a Mulungu ndi umboni wakuti iye anakukokani ndi mzimu wake woyera. (Yoh. 6:44) Musapeputse ubale wanu ndi Mulungu. Yesetsani m’zochita zanu zonse kusonyeza kuti mukukana mzimu wodziimira panokha ndiponso kuti mumagonjera ulamuliro wa Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timagonjera ulamuliro wa Yehova?

• Kodi kuphunzitsa luntha lathu la kuzindikira kungatithandize bwanji kugonjera ulamuliro wa Yehova?

• Kodi Satana amayesetsa kupeputsa ulamuliro wa Mulungu m’njira ziti?

• N’chifukwa chiyani kudzichepetsa n’kofunika kuti tigonjere ulamuliro wa Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

“Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu”

[Chithunzi patsamba 20]

Ndi bwino nthawi zonse kutsatira mfundo za Mulungu