Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Wanzeru ndi Womvetsa Zinthu Ndani Pakati pa Inu?”

“Kodi Wanzeru ndi Womvetsa Zinthu Ndani Pakati pa Inu?”

 “Kodi Wanzeru ndi Womvetsa Zinthu Ndani Pakati pa Inu?”

“Kodi wanzeru ndi womvetsa zinthu ndani pakati pa inu? Mwa khalidwe lake labwino, aonetse ntchito zake mwa kufatsa kumene kumachokera mu nzeru.”​—YAK. 3:13.

1, 2. Kodi tinganene chiyani za anthu ambiri amene amaonedwa kuti ndi anzeru?

KODI inu mumati munthu wanzeru kwambiri ndani? Kodi mumaganiza kuti ndi makolo anu, munthu wokalamba, kapena mphunzitsi wa kukoleji? Mmene mumaonera munthu wanzeru, zimadalira mmene munakulira ndi zochitika pamoyo wanu. Koma atumiki a Mulungu amaona kuti munthu wanzeru ndi amene Mulunguyo amati ndi wanzeru.

2 Pa anthu amene dzikoli limawaona kuti ndi anzeru, si onse amene Mulungu amawaona kuti ndi anzerudi. Mwachitsanzo, polankhula ndi anthu amene anali kudziona kuti akulankhula zanzeru, Yobu anati: “Sindipeza mwa inu wanzeru.” (Yobu 17:10) Ponena za anthu amene anakana nzeru ya Mulungu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngakhale anali kunenetsa kuti ndi anzeru, iwo anakhala opusa.” (Aroma 1:22) Ndipo kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova mwiniyo ananena motsindika kuti:“Tsoka kwa iwo amene adziyesera anzeru ndi ochenjera!”​—Yes. 5:21.

3, 4. Kodi chofunika ndi chiyani kuti munthu akhaledi wanzeru?

3 N’zoonekeratu kuti tikufunikira kudziwa zimene zimachititsa munthu kukhaladi wanzeru kuti ayanjidwe ndi Mulungu. Lemba la Miyambo 9:10 limatiuza kuti: “Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova; kudziwa Woyerayo ndiko luntha.” Anthu anzeru amafunika kuopa Mulungu moyenerera ndi kutsatira malamulo ake. Komabe, zambiri zimafunika osati chabe kungodziwa kuti Mulungu aliko ndipo ali ndi malamulo. Wophunzira Yakobe amatithandiza kuganizira nkhani imeneyi. (Werengani Yakobe 3:13.) Mawu ake amati: “Aonetse ntchito zake mwa kufatsa kumene kumachokera mu nzeru.” Nzeru yeniyeni iyenera kuonekera pa zochita ndi zolankhula zathu tsiku ndi tsiku.

4 Nzeru yeniyeni imatanthauza kuganiza bwino ndi kugwiritsa ntchito m’njira yothandiza zimene munthu ukudziwa ndi kuzimvetsetsa. Kodi ndi zinthu ziti zimene ife tingachite posonyeza kuti tili ndi nzeru? Yakobe anatchula zinthu zingapo zimene anthu anzeru amachita. * Kodi iye anatchula zinthu ziti zimene zingatithandize kukhala bwino ndi okhulupirira anzathu, ndiponso anthu akunja?

Munthu Amene Ndi Wanzerudi Amadziwika ndi Zochita Zake

5. Kodi munthu amene ndi wanzerudi, amaonetsetsa kuti khalidwe lake likugwirizana ndi chiyani?

5 Pajatu Yakobe anasonyeza kuti nzeru imayendera limodzi ndi khalidwe labwino. Popeza kuti chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova, munthu wanzeru amaonetsetsa kuti khalidwe lake likugwirizana ndi njira za Mulungu ndi malamulo ake. Ife sitibadwa ndi nzeru yeniyeni. Koma tingaipeze mwa kuphunzira Baibulo  nthawi zonse ndi kusinkhasinkha. Zimenezi zidzatithandiza kuchita zimene lemba la Aefeso 5:1 limanena. Limati: “Khalani otsanzira Mulungu.” Khalidwe lathu likamafanana kwambiri ndi la Yehova, nazonso zochita zathu zidzasonyeza kwambiri kuti ndife anzeru. Njira za Yehova ndi zapamwamba kwambiri kuposa za anthu. (Yes. 55:8, 9) Choncho tikamatsanzira Yehova pochita zinthu, anthu akunja adzaona kuti ndife osiyana ndi iwo.

6. N’chifukwa chiyani kufatsa ndi umboni wakuti munthu akutsanzira Mulungu, ndipo munthu wofatsa amakhala wotani?

6 Yakobe akusonyeza kuti njira ina imene munthu angakhalire wofanana ndi Yehova ndiyo “kufatsa kumene kumachokera mu nzeru.” Ngakhale kuti Mkhristu wofatsa amakhala wodekha, iye amakhalanso wolimba mtima, ndipo zimenezi zimamuthandiza kuchita zinthu mwanzeru. Ngakhale kuti mphamvu zake zilibe malire, Mulungu ndi wofatsa ndipo sitiopa kumuyandikira. Nayenso Mwana wa Mulungu anali wofatsa ngati Atate ake, motero anatha kunena kuti: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu.”​—Mat. 11:28, 29; Afil. 2:5-8.

7. N’chifukwa chiyani Mose ndi chitsanzo chabwino cha munthu wofatsa?

7 Baibulo limatiuza za anthu ena amene anali kudziwika ndi kufatsa, kapena kuti kudzichepetsa. Mmodzi wa iwo ndi Mose. Iye anali ndi udindo waukulu kwambiri, koma amanenedwa kuti anali “wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi.” (Num. 11:29; 12:3) Komanso Yehova anapatsa Mose mphamvu kuti achite chifuniro chake. Inde, Yehova anali kusangalala kugwiritsa ntchito anthu ofatsa kukwaniritsa cholinga chake.

8. Kodi anthu opanda ungwiro angasonyeze bwanji “kufatsa kumene kumachokera mu nzeru”?

8 Apa ndi zoonekeratu kuti anthu opanda ungwiro atha kusonyeza “kufatsa kumene kumachokera mu nzeru.” Nanga bwanji ifeyo? Kodi tingachite chiyani kuti tizisonyeza kwambiri khalidwe limeneli? Kufatsa ndi chimodzi mwa zipatso za mzimu woyera wa Yehova. (Agal. 5:22, 23) Tiyenera kupempherera mzimu wake ndi kuyesetsa kusonyeza zipatso za mzimuwo. Tichite zimenezi ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu adzatithandiza kukhala ofatsa kwambiri. Wamasalmo akutipatsa chifukwa champhamvu chochitira zimenezi ponena kuti: “[Mulungu] adzaphunzitsa ofatsa njira yake.”​—Sal. 25:9.

9, 10. Kodi chofunika ndi chiyani kuti ife tikhale ofatsadi? Perekani chifukwa.

9 Komabe, pamafunika khama kuti tichite bwino pambali imeneyi. Chifukwa cha mmene tinakulira, enafe zingativute kukhala ofatsa. Ndiponso anthu amene timacheza nawo angafune kuti tisakhale ofatsa. Iwo angakolezere moto potilimbikitsa kukhala ndi mtima wobwezera. Koma kodi imeneyi ndi nzerudi? Ngati moto wochepa wabuka m’nyumba mwanu, kodi mungayese kuuzimitsa ndi mafuta kapena ndi madzi? Kuthira mafuta pamotopo kungangowonjezera motowo, koma kuthirapo madzi kungauzimitse. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limatilangiza kuti: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu owawitsa aputa msunamo.” (Miy. 15:1, 18) Ngati pangabuke vuto pakati pa ife ndi munthu wina mumpingo kapena kunja, tingasonyeze kuti tili ndi nzeru yeniyeni mwa kuchita zinthu mofatsa.​—2 Tim. 2:24.

10 Monga taonera, anthu ambiri amene ali ndi mzimu wa dziko sakhala odekha ndi amtendere. Koma amakhala opupuluma, ankhanza ndi odzikuza. Yakobe anali kudziwa zimenezi, ndipo anachenjeza anthu mumpingo kuti asaipitsidwe ndi mzimu umenewo. Kodi n’chiyaninso chimene uphungu wake ukutiphunzitsa?

Zochita za Anthu Opanda Nzeru

11. Kodi ndi makhalidwe ati amene amasemphana ndi nzeru yeniyeni?

11 Yakobe analemba mosapita m’mbali zochita zimene zimasemphana ndi nzeru yeniyeni.  (Werengani Yakobe 3:14.) Nsanje ndiponso ndewu ndi makhalidwe athupi, osati auzimu. Taonani zimene zimachitika anthu akamayendera maganizo aumunthu. Magulu 6 amene amadzitenga kuti ndi Akhristu amayang’anira mbali zawo za Tchalitchi cha Manda Opatulika ku Yerusalemu, ndipo amati tchalitchicho chinamangidwa pa malo amene anaphera Yesu ndi kumuika m’manda. Maguluwa sagwirizana. Mu 2006, magazini ya Time inafotokoza kuti m’mbuyomo panali nkhondo pakati pa abusa kumeneko ndipo “anamenyana kwa nthawi yaitali, . . . kugogodana ndi zoikamo makandulo zikuluzikulu.” Iwo sakhulupirirana ngakhale pang’ono motero kuti amasungitsa makiyi a tchalitchicho kwa Msilamu.

12. Ngati anthu alibe nzeru, kodi chingachitike ndi chiyani?

12 Ndewu zoopsa ngati zimenezi siziyenera kuchitika mumpingo wa Akhristu oona. Koma nthawi zina, kupanda ungwiro kwachititsa anthu ena kuumirira maganizo awo. Zimenezo zingayambitse mikangano ndi ndewu. Mtumwi Paulo anaona zimenezi mumpingo wa ku Korinto, ndipo analemba kuti: “Ngati mukuchitirana nsanje ndi kukangana nokhanokha, kodi sindiye kuti ndinu a kuthupi ndipo mukuyenda monga anthu?” (1 Akor. 3:3) Khalidwe lomvetsa chisoni limeneli linalimo mumpingowu kwa nthawi ndithu. Choncho, tifunika kusamala kuti mzimu umenewu usapezeke mu mpingo masiku ano.

13, 14. Perekani zitsanzo za mmene munthu angasonyezere maganizo oipa aumunthu.

13 Kodi mzimu umenewu ungayambe bwanji? Ungayambe pang’onopang’ono. Mwachitsanzo, pomanga Nyumba ya Ufumu abale angakhale ndi maganizo osiyana a mmene angachitire zinthu. M’bale wina angachite makani ngati anthu sakuvomereza maganizo ake, ndipo mwina angayambe kutsutsa mwavoko zimene abale ena agwirizana. Iye mwina angafike posiya kugwira nawo ntchitoyo. M’bale wochita zimenezi amaiwala kuti ntchito za pampingo zimayenda bwino ngati mu mpingowo muli mtendere osati chifukwa cha njira imene akugwirira ntchitoyo. Yehova amadalitsa mzimu wofatsa osati wandewu.​—1 Tim. 6:4, 5.

14 Chitsanzo china chingakhale chakuti, akulu mumpingo aona kuti mkulu mnzawo amene watumikira kwa nthawi yaitali, tsopano sakukwanitsa ziyeneretso za m’Malemba. Woyang’anira dera atadziwa kuti m’baleyo wakhala akupatsidwa uphungu m’mbuyomo koma sakusintha, akugwirizana ndi akulu ena n’kuvomereza kuti munthuyo asiye kukhala mkulu. Kodi iye angaione bwanji nkhaniyi? Kodi iye adzavomereza modzichepetsa komanso mofatsa uphungu wawo wa m’Malemba ndi zimene akuluwo agwirizana? Ndipo kodi adzayesetsa kukwaniritsa ziyeneretso za m’Malemba kuti adzatumikirenso m’tsogolo? Kapena kodi adzasunga chakukhosi ndi kumachita nsanje chifukwa chakuti iye si mkulunso? Kodi ndi zomveka kuti m’bale aziumirira kukhala mkulu pamene akulu ena onse akuona kuti sakuyenerera? Ndi nzeru ndithu kukhala wodzichepetsa ndi womvetsa zinthu.

15. N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti uphungu wouziridwa umene uli pa Yakobe 3:15, 16 ndi wofunika kwambiri?

15 Komatu, pali njira zinanso zimene munthu  angasonyezere mtima umenewu. Mulimonse mmene zingakhalire, tiyenera kuyesetsa kupewa makhalidwe amenewa. (Werengani Yakobe 3:15, 16.) Wophunzira Yakobe ananena kuti makhalidwe amenewa ndi a “padziko lapansi” chifukwa ndi akuthupi, osati auzimu. Ndipo ndi ‘aumunthu,’ kapena kuti auchinyama, chifukwa chakuti amachokera m’maganizo a anthu, ndipo amafanana ndi makhalidwe a nyama chifukwa nyamazo siziganiza. Komanso makhalidwe amenewa ndi ‘auchiwanda’ chifukwa chakuti amasonyeza maganizo a ziwanda zomwe ndi adani a Mulungu. Ndiyetu, Mkhristu sayenera kukhala ndi makhalidwe amenewo ngakhale pang’ono.

16. Kodi tingafunikire kusintha motani, ndipo tingathe bwanji kuchita zimenezo?

16 Aliyense mumpingo ayenera kudzifufuza pa nkhaniyi ndipo akapeza kuti ali ndi makhalidwe oipa amenewa, ayesetse kusintha. Popeza oyang’anira ndi aphunzitsi mumpingo, iwo ayenera kukumbukira kuti afunika kupewa makhalidwe oipa. Zimenezi n’zovuta chifukwa chakuti ndife anthu opanda ungwiro ndiponso tikukhala m’dziko loipa. Kuchita zimenezi kuli ngati kukwera phiri la matope ndi loterera. Ngati palibe chinthu chakuti tigwire, tingamaterereke ndi kubwerera m’mbuyo. Koma ngati tigwira zolimba uphungu wopezeka m’Baibulo, ndiponso thandizo la mpingo wa Mulungu wa padziko lonse, tingapite patsogolo.​—Sal. 73:23, 24.

Makhalidwe Amene Anthu Anzeru Amayesetsa Kukhala Nawo

17. Kodi anthu anzeru amachita chiyani akamayesedwa kuti achite zoipa?

17 Werengani Yakobe 3:17. Timapindula kwambiri tikamaganizira za makhalidwe ena amene munthu amakhala nawo chifukwa cha “nzeru yochokera kumwamba.” Kukhala woyera kumatanthauza kukhala osadetsedwa pa zochita ndi zolinga zathu. Tifunika kukana zinthu zoipa nthawi yomweyo. Tizichita zimenezi mofulumira ngati mmene munthu mwachibadwa amachitira akaona zoopsa. Munthu wina akafuna kukutosani m’maso ndi chala chake, inu nthawi yomweyo mumathawitsa mutu wanu kapena kutchinga chala chakecho ndi dzanja lanu. Zimenezi zimangochitika mwachibadwa popanda inu kuzindikira. Tikamayesedwa kuti tichite zoipa tifunika kuchitanso chimodzimodzi. Ngati ndife oyera ndiponso ngati chikumbumtima chathu ndi chophunzitsidwa Baibulo, tidzakana zoipazo nthawi yomweyo. (Aroma 12:9) Baibulo lili ndi zitsanzo za anthu amene anachita zimenezi, monga Yosefe ndi Yesu.​—Gen. 39:7-9; Mat. 4:8-10.

18. Kodi mawu akuti (a) kukhala amtendere, amatanthauza chiyani? (b) nanga akuti kukhala odzetsa mtendere?

 18 Nzeru yochokera kwa Mulungu imafunanso kuti tikhale amtendere. Izi zikutanthauza kupewa kukhala anthu aukali, okonda mikangano kapena ochita zinthu zimene zingasokoneze mtendere. Yakobe anafotokoza zambiri pa mfundoyi pamene ananena kuti: “Chilungamo ndicho chipatso cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.” (Yak. 3:18) Taganizirani za mawu akuti “odzetsa mtendere.” Kodi ifeyo timadziwika monga odzetsa mtendere kapena osokoneza mtendere mumpingo? Kodi timakangana kawirikawiri ndi anthu ena, kukwiya msanga kapena kukwiyitsa ena? Kodi timaumirira kuti ife ndi mmene tilili ndipo anthu ena azitimvetsa, kapena timayesetsa modzichepetsa kusintha ndi kusiya makhalidwe amene amakhumudwitsa anthu ena? Kodi timadziwika monga anthu amene timayesetsa kulimbikitsa mtendere, kukhululuka msanga ndiponso kusasunga chakukhosi? Tingachite bwino kudzifufuza n’kuona ngati tikufunika kusintha pa nkhani imeneyi kuti tisonyeze nzeru yochokera kwa Mulungu.

19. Kodi munthu wololera amadziwika bwanji?

19 Yakobe ananenanso za kulolera pofotokoza nzeru yochokera kumwamba. Kodi timadziwika kuti ndife ololera maganizo a ena ngati mfundo za m’Malemba sizikuphwanyidwa? Kodi timadziwika ngati munthu amene sakonda kuumirira kuti anthu atsatire mfundo zake? Kodi timadziwika kuti ndife odekha ndiponso ochezeka? Ngati ndi choncho, ndiye kuti taphunzira kukhala ololera.

20. Kodi chimachitika ndi chiyani tikamasonyeza makhalidwe abwino amene takambiranawa?

20 Zinthu zimayenda bwino kwambiri mumpingo ngati abale ndi alongo amayesetsa kusonyeza makhalidwe abwino amene Yakobe analemba. (Sal. 133:1-3) Kukhala ofatsa, amtendere, ndiponso ololerana wina ndi mnzake, kudzatithandiza kukhala ogwirizana ndipo zimenezi zidzasonyeza kuti tili ndi “nzeru yochokera kumwamba.” M’nkhani yotsatira tidzaphunzira kuti tikamaona ena mmene Yehova amawaonera, zidzatithandiza kukhala ndi makhalidwe amenewa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Nkhani yonse imene Yakobe anali kufotokoza imasonyeza kuti iye polemba, anali kuganiza makamaka za akulu, kapena kuti “aphunzitsi” mumpingo. (Yak. 3:1) Inde, amuna amenewa ayenera kupereka chitsanzo chabwino chakuti ali ndi nzeru yeniyeni. Ngakhale ndi choncho, tonsefe tingapindule ndi uphungu wake.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi Mkhristu amadziwika bwanji kuti ndi wanzerudi?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisonyeze kwambiri nzeru yeniyeni?

• Kodi anthu amene alibe “nzeru yochokera kumwamba” amakhala ndi makhalidwe otani?

• Kodi ndi makhalidwe ati amene mukufuna kukhala nawo kwambiri?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi mikangano ingayambe bwanji masiku ano?

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi mumakana zoipa mukangoziona?