Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaona Anthu Mmene Yehova Amawaonera?

Kodi Mumaona Anthu Mmene Yehova Amawaonera?

 Kodi Mumaona Anthu Mmene Yehova Amawaonera?

“Thupi lisakhale logawikana . . . Ziwalo zake zipatsane chisamaliro chofanana.”​—1 AKOR. 12:25.

1. Kodi munamva bwanji nthawi yoyamba imene munalowa mu paradaiso wauzimu?

TITACHOKA ku dziko loipali ndi kuyamba kugwirizana ndi anthu a Yehova, mosakayikira tinasangalala kwambiri kuona mmene iwo amakonderana ndi kusamalirana. Anali osiyana kwambiri ndi anthu amwano, odana ndi okonda ndewu amene Satana akuwalamulira m’dzikoli. Nthawi imeneyo tinalowa mu paradaiso wauzimu, wodzala mtendere ndi umodzi.​—Yes. 48:17, 18; 60:18; 65:25.

2. (a) Kodi n’chiyani chingatichititse kusintha mmene timaonera ena? (b) Nanga tingachite chiyani?

2 Ngakhale zili choncho, m’kupita kwa nthawi tingasinthe ndi kuyamba kuona abale athu molakwika chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu. Chifukwa cha kupanda ungwiroko,  tingayambe kuyang’ana kwambiri zolakwa za abale athuwo m’malo moyang’ana makhalidwe awo abwino auzimu. Mwachidule, tinganene kuti timaiwala ndi kusiya kuona abale athu mmene Yehova amawaonera. Ngati zimenezi zachitika, ndi nthawi yakuti tidziunike ndi kusintha maganizo athu kuti afanane ndi a Yehova.​—Eks. 33:13.

Mmene Yehova Amaonera Abale Athu

3. Kodi Baibulo limayerekeza mpingo wachikhristu ndi chiyani?

3 Pa 1 Akorinto 12:2-26, mtumwi Paulo anayerekeza mpingo wa Akhristu odzozedwa ndi thupi la munthu lomwe limakhala ndi “ziwalo zambiri.” Monga mmene ziwalo za thupi zimakhalira zosiyana, mumpingo anthu amakhalanso osiyana kwambiri makhalidwe ndi luso lawo. Koma Yehova amalandira onse. Amakonda ndi kuwerengera munthu aliyense. N’chifukwa chake Paulo akutilangiza kuti ziwalo za mpingo ziyenera ‘kupatsana chisamaliro chofanana.’ Zimenezi zingakhale zovuta chifukwa chakuti umunthu wa ena ungakhale wosiyana ndi wathu.

4. N’chifukwa chiyani tingafunike kusintha mmene timaonera abale athu?

4 Mwina tingamakonde kuyang’ana kwambiri zofooka za abale athu. Tikamatero, timakhala ngati tikungoona mbali yochepa ya chithunzi. Koma tingati Yehova amaona chithunzi chonse. Ife timakonda kuyang’ana mbali yoipa ya munthuyo, pamene Yehova amayang’ana munthu yense ndi makhalidwe ake onse abwino. Tikamayesetsa kukhala ngati Yehova, timalimbikitsa kwambiri mzimu wa chikondi ndi umodzi mumpingo.​—Aef. 4:1-3; 5:1, 2.

5. Kodi n’chifukwa chiyani si nzeru kuweruza anzathu?

5 Yesu anali kudziwa bwino kuti anthu opanda ungwiro amakonda kuweruza anzawo. Iye analangiza kuti: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.” (Mat. 7:1) Onani kuti Yesu sananene kuti “musaweruze” koma anati “lekani kuweruza.” Iye anali kudziwa kuti omvera ake ambiri anali ndi chizolowezi choweruza anzawo. Kodi nafenso tili ndi chizolowezi chimenechi? Ngati tili nacho, tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tisinthe poopera kuti tingaweruzidwe koopsa. Ndife ndani kuti tiziweruza munthu amene Yehova wamupatsa udindo kapena kunena kuti iye asakhale mumpingo? Inde, m’bale angakhale ndi zofooka zina, koma ngati Yehova akumugwiritsabe ntchito, kodi chingakhale chanzeru kuti ife timukane? (Yoh. 6:44) Kodi timakhulupiriradi kuti Yehova akutsogolera mpingo wa anthu ake ndiponso kuti ngati pakufunika kusintha zinthu zina, iye adzatero panthawi yake?​—Werengani Aroma 14:1-4.

6. Kodi Yehova amawaona bwanji atumiki ake?

6 Yehova ndi wodabwitsa chifukwatu amatha kudziwa mtundu wa munthu amene Mkhristu aliyense adzakhala, akadzakhala wangwiro m’dziko latsopano. Iye amadziwanso zimene munthuyo wasintha ndi pamene wafika pamoyo wake wauzimu. Choncho, savutika ndi kuyang’ana chofooka chilichonse cha munthu. Pa Salmo 103:12, timawerenga kuti: “Monga kum’mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.” Tiyenera  kuthokoza kuti iye amationa motero.​—Sal. 130:3.

7. Kodi Yehova anamuona bwanji Davide, ndipo ife tikuphunzirapo chiyani?

7 M’Malemba, timapeza umboni wakuti Yehova ali ndi luso lodabwitsa loyang’ana zabwino za munthu aliyense. Ponena za Davide, Mulungu anati: “Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wake wonse kuchita zolunjika zokhazokha pamaso panga.” (1 Maf. 14:8) Tikudziwa kuti Davide anachita zinthu zina zolakwa, koma Yehova anasankha kuyang’ana zabwinozo chifukwa anadziwa kuti mtima wa Davide unali wowongoka.​—1 Mbiri 29:17.

Onani Abale Anu Mmene Yehova Amawaonera

8, 9. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tifanane ndi Yehova? (b) Kodi mungafanizire zimenezi ndi chiyani, ndipo tikuphunzirapo chiyani?

8 Mosiyana ndi ife, Yehova amatha kudziwa zimene zili mu mtima wa munthu. Pachifukwachi, sitiyenera kuweruza ena. Ife sitidziwa zolinga zonse za munthu. Tiziyesetsa kutsanzira Yehova posayang’ana zolakwa za anzathu, zimene sizidzakhalakonso m’tsogolo. Kodi simukuona kuti ndi bwino kukhala ndi cholinga chotsanzira Yehova pankhani imeneyi? Kuchita zimenezi kudzatithandiza kwambiri kukhala mwamtendere ndi abale ndiponso alongo athu.​—Aef. 4:23, 24.

9 Tiyerekeze chonchi. Nyumba ina ndi yowonongeka. Tsindwi lake ndi lakutha, mawindo osweka ndipo pansi m’pokumbikakumbika. Anthu ambiri oona nyumbayo akunena kuti ndi bwino kungoigwetsa chifukwa sikuoneka bwino. Kenako pakubwera munthu amene maganizo ake ndi osiyana ndi amenewa. Iye sakuyang’ana vuto limene likuonekalo koma akuona kuti nyumbayo ndi yolimba ndipo angathe kuikonza. Iye akugula nyumbayo ndi kuyamba kuikonza mpaka kuoneka bwino. Ndiye anthu odutsa, akunena kuti ndi yokongola kwambiri. Kodi ife tingakhale ngati munthu uyu amene anayesetsa kukonza nyumbayi? M’malo moyang’ana zolakwa zoonekeratu za abale athu, bwanji osayang’ana makhalidwe awo abwino ndi kuona kuti iwo atha kupita patsogolo mwauzimu? Tikatero, ndiye kuti tidzayamba kuwakonda kwambiri abale athuwo chifukwa cha kukongola kwawo kwauzimu, ngati mmene Yehova amachitira.​—Werengani Aheberi 6:10.

10. Kodi uphungu wa pa Afilipi 2:3, 4 ungatithandize bwanji?

10 Mtumwi Paulo anapereka uphungu umene ungatithandize kugwirizana ndi anthu onse mumpingo. Iye anauza Akhristu kuti: “Musachite kanthu kalikonse ndi mzimu wandewu kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, mukumaona ena kukhala okuposani. Musasamale zofuna zanu zokha, koma musamalenso zofuna za ena.” (Afil. 2:3, 4) Kudzichepetsa kudzatithandiza kuwaona bwino anzathu. Kusamala zofuna za anzathu komanso kuona zabwino zawo, kudzatithandizanso kuwaona mmene Yehova amawaonera.

11. Kodi kusintha kwa zinthu masiku ano kwakhudza motani mipingo ina?

11 Masiku ano anthu ambiri akusamukira ku mayiko ena. M’mizinda ina, muli anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Anthu ena amene ndi alendo kudera lathu achita chidwi ndi choonadi cha Baibulo, ndipo agwirizana nafe pakulambira Yehova. Anthu amenewa ndi ‘ochokera m’dziko lililonse, fuko, mtundu, ndi lilime lililonse.’ (Chiv. 7:9) Choncho, mipingo yathu yambiri ili ndi anthu ochokera mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi.

12. Kodi tisasiye kuona anzathu m’njira yotani, nanga n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kungativute nthawi zina?

12 Mumpingo mwathu, tiyenera kuyesetsa kuti tisasiye kuona anzathu moyenera. Zimenezi zimafuna kuti tizikumbukira uphungu wa mtumwi Petulo wakuti tikhale ndi “chikondi chaubale chopanda chinyengo” ndi ‘kukondana kwambiri kuchokera mu mtima.’ (1 Pet. 1:22) Kukhala ndi chikondi chenicheni pamene pali anthu ochokera mayiko osiyanasiyana ndi kovuta. Chikhalidwe cha olambira anzathu chingakhale chosiyana kwambiri ndi  chathu. Tingakhalenso osiyana maphunziro, chuma ndi fuko. Kodi zimakuvutani kumvetsa mmene anzanuwo amaganizira kapena mmene amachitira zinthu? Iwonso angavutike kukumvetsani. Ngakhale zili choncho, tonsefe tikulangizidwa kuti: “Kondani gulu lonse la abale.”​—1 Pet. 2:17.

13. Kodi ndi maganizo ati amene tifunika kusintha?

13 Mwina tingafunike kusintha mmene timaganizira kuti tifutukule chikondi chathu pa abale athu onse. (Werengani 2 Akorinto 6:12, 13.) Kodi nthawi zina timapezeka tikulankhula kuti “Sikuti ndikukondera ayi, koma kungoti . . . ” kenako n’kuyamba kufotokoza makhalidwe oipa amene timaganiza kuti ndi ofala kwa anthu a fuko lina? Maganizo otero angasonyeze kuti tidakali ndi tsankho mumtima mwathu ndipo tifunika tisinthe. Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ine ndimayesetsa kuwadziwa bwino anthu achikhalidwe china?’ Kudzifufuza kumeneku kungatithandize kusintha ndi kuyamba kukonda abale athu apadziko lonse.

14, 15. (a) Perekani zitsanzo za anthu omwe anasintha mmene ankaonera anthu ena. (b) Kodi tingawatsanzire bwanji?

14 M’Baibulo muli zitsanzo zabwino za anthu amene anasintha mmene anali kuganizira, ndipo mmodzi wa iwo ndi mtumwi Petulo. Popeza Petulo anali Myuda, iye ayenera kuti anali kupewa kulowa m’nyumba za anthu akunja. Kodi mukuganiza kuti iye anamva bwanji atauzidwa kuti apite kunyumba ya Koneliyo, yemwe anali munthu wakunja ndiponso wosadulidwa? Petulo anasintha maganizo ake n’kuyamba kuona kuti cholinga cha Mulungu ndi chakuti anthu amitundu yonse akhale mumpingo wachikhristu. (Mac. 10:9-35) Saulo yemwe anadzakhala mtumwi Paulo, anasinthanso maganizo ake n’kusiya tsankho. Iye anavomereza kuti anali kudana kwambiri ndi Akhristu mpaka “[anachita] kunyanya kuzunza mpingo wa Mulungu ndi kuuwononga mopitirizabe.” Komabe, Ambuye Yesu atadzudzula Paulo, iye anasintha kwambiri mpaka anayamba kutsatira malangizo ochokera kwa anthu amene poyamba anali kuwazunza.​—Agal. 1:13-20.

15 Ifenso sitikukayikira kuti mzimu wa Yehova ungatithandize kusintha mmene timaganizira. Ngati tikudziwa kuti tili ndi tsankho mumtima mwathu, tiyeni tiyesetse kulithetsa ndi “kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwa mtendere monga chomangira chotigwirizanitsa.” (Aef. 4:3-6) Baibulo limatilimbikitsa ‘kuvala chikondi, pakuti ndicho chomangira umodzi changwiro.’​—Akol. 3:14.

Tsanzirani Yehova Muutumiki Wanu

16. Kodi Mulungu amafuna kuti anthu azichita chiyani?

16 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu alibe tsankho.” (Aroma 2:11) Cholinga cha Yehova  ndi chakuti anthu amitundu yonse azimulambira. (Werengani 1 Tim. 2:3, 4.) N’chifukwa chake wakonza zakuti “uthenga wabwino wosatha” ulengezedwe “ku dziko lililonse, fuko, lilime, ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6) Yesu anati: “Munda ndiwo dziko.” (Mat. 13:38) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa inuyo ndi anthu a pabanja panu?

17. Kodi tingathandize bwanji anthu amtundu uliwonse?

17 Si anthu onse amene angakwanitse kupita ku madera a kutali kukalalikira uthenga wa Ufumu. Komabe, tingathe kulalikira anthu ochokera mayiko osiyanasiyana amene amakhala m’gawo lathu. Kodi timagwiritsa ntchito mpata uliwonse kulalikira anthu amtundu uliwonse, osati chabe amene takhala tikuwalalikira nthawi yaitali? Bwanji osakhala ndi cholinga cholalikira anthu amene sanalalikidwepo bwinobwino?​—Aroma 15:20, 21.

18. Kodi Yesu anali ndi mtima wotani kwa anthu?

18 Yesu anali ndi mtima wofuna kuthandiza anthu onse. Iye sanalalikire dera limodzi lokha. Nkhani ina ya m’Baibulo imatiuza kuti iye “anayamba ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse.” Ndipo kenako, “poona chikhamu cha anthu, anawamvera chisoni,” ndipo anafuna kuwathandiza.​—Mat. 9:35-37.

19, 20. Kodi ndi njira ziti zimene tingasonyezere chidwi chimene Yehova ndi Yesu ali nacho pa anthu amtundu uliwonse?

19 Kodi mungasonyeze mtima umenewu m’njira ziti? Ena ayesetsa kulalikira malo ena a gawo lawo amene anthu salalikirako kawirikawiri. Malowa angakhale monga ogulitsira malonda, mapaki, kokwerera mabasi, kapena mumsewu pafupi ndi nyumba zovuta kulowa. Ena ayesetsa kuphunzira chinenero chatsopano kuti alalikire anthu achinenero china amene tsopano akukhala m’gawo lawo kapena anthu amene sanayambe alalikidwapo. Kuphunzira kuwapatsa moni m’chinenero chawo kungawasonyeze kuti timawakonda. Ngati sitingathe kuphunzira chinenero china, kodi tingalimbikitse anthu amene akutero? Tisafooketse kapena kunyoza anthu amene akuyesetsa kulalikira anthu ochokera kumayiko ena. Anthu onse ndi amtengo wapatali pamaso pa Mulungu ndipo nafenso tifunika kuwaona mmene Mulungu amawaonera.​—Akol. 3:10, 11.

20 Kuona anthu mmene Mulungu amawaonera kumafunanso kuti tizilalikira anthu onse, kaya anthuwo akhale otani. Ena angakhale opanda nyumba, ena auve ndipo ena amachita kuonekeratu kuti ndi achiwerewere. Anthu ena akatichitira nkhanza, si chifukwa chakuti ife tikhale ndi maganizo akuti anthu a dziko lonselo kapena fuko lonselo ndi oipa. Anthu ena anachitira nkhanza Paulo, koma iye sanalole zimenezo kumusiyitsa kulalikira anthu amtundu umenewo. (Mac. 14:5-7, 19-22) Iye anali ndi chikhulupiriro chakuti ena adzamvetsera ndi kulabadira uthengawo.

21. Kodi kuona anthu mmene Yehova amawaonera kungakuthandizeni motani?

21 Apa ndi zoonekeratu kuti tikamachita zinthu ndi abale akwathu, abale ochokera mayiko ena ndi anthu amene timawalalikira, tifunika kukhala ndi maganizo oyenera owaona mmene Yehova amawaonera. Ngati tiyesetsa kwambiri kukhala ndi maganizo a Yehova amenewa, tidzalimbikitsa kwambiri mtendere ndi umodzi. Ndiponso tidzatha kuthandiza ena kukonda Yehova, amene ndi Mulungu “wosasamalira nkhope” ndipo amakonda anthu onse, chifukwa “onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.”​—Yobu 34:19.

Kodi Mungayankhe?

• Kodi tizipewa kuona motani abale athu?

• Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pankhani ya mmene timaonera abale athu?

• Kodi inuyo mwaphunzirapo chiyani za mmene timaonera abale athu apadziko lonse?

• Tikakhala mu utumiki, kodi tingatsanzire bwanji mmene Yehova amaonera anthu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi mungadziwane bwanji ndi anthu achikhalidwe china?

[Zithunzi patsamba 28]

Kodi mungalalikire bwanji uthenga wabwino kwa anthu ambiri?