Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Omaliza Maphunziro a Gileadi Akulimbikitsidwa Kuti “Ayambe Kukumba”

Omaliza Maphunziro a Gileadi Akulimbikitsidwa Kuti “Ayambe Kukumba”

 Kalasi ya 123 ya Omaliza Maphunziro a Gileadi

Omaliza Maphunziro a Gileadi Akulimbikitsidwa Kuti “Ayambe Kukumba”

LOWERUKA, pa September 8, 2007, anthu 6,352 ochokera kumayiko 41, anasonkhana pa mwambo womaliza maphunziro wa kalasi ya 123 ya Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo. Itakwana 10 koloko m’mawa, tcheyamani wa pulogalamu, Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira, analonjera anthuwo. Atalonjera omvera ndi mawu ochepa, anaitana Gary Breaux wa m’Komiti ya Nthambi ya United States kuti akambe nkhani yoyamba.

M’bale Breaux anatsimikizira ophunzirawo kuti kaya akuoneka motani, anthu amene amachita chifuniro cha Yehova ndi okongola kwa Iye. (Yer. 13:11) Analimbikitsa ophunzirawo kusungabe kukongola kwawo. Kenako, Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira anatsindika mfundo yakuti sikulakwa kuyembekezera mphoto tikamatumikira Yehova. (Aheb. 11:6) Komabe, tiyenera kumutumikira chifukwa cha chikondi chopanda dyera.

Woyang’anira Dipatimenti ya Sukulu za Mulungu, William Samuelson, analimbikitsa ophunzirawo kuti asasiye ntchito yawo yolemekezeka yolengeza Mfumu imene ikulamulira ndiponso kudzisungira ulemu mwa kukhala ndi khalidwe labwino. * Sam Roberson, wachiwiri kwa woyang’anira Dipatimenti ya Sukulu za Mulungu, analimbikitsa ophunzirawo kuti aziona zabwino mwa ena nthawi zonse. Akatero, ophunzirawo adzatha ‘kukonda gulu lonse la abale.’​—1 Pet. 2:17.

Pambuyo pa nkhani zolimbikitsa zimenezo, mlangizi wa Sukulu ya Gileadi, Mark Noumair, anafunsa ophunzira angapo ndipo iwo anafotokoza zimene anakumana nazo muutumiki wa kumunda panthawi imene anali kuphunzira ku Gileadiko. Atamaliza, omvera onse anatha kuona kuti ophunzirawo amakondadi utumiki ndipo ali ndi mtima wofuna kuthandiza ena. Kent Fischer wa mu Ofesi ya Osamalira Banja la Beteli ku Patterson, anafunsa abale a m’Komiti ya Nthambi ochokera kumayiko atatu kumene kuli amishonale. Zimene abale okhulupirika amenewa ananena zinalimbikitsa omvera ndi makolo a ophunzirawo, kudziwa kuti amishonale atsopano amasamalidwa bwino pautumiki wawo. Kenako Izak Marais wa ku Dipatimenti Yothandiza Otembenuza, anafunsa amene akhala amishonale kwa nthawi yaitali, ndipo zimene iwo anakumana nazo zinathandiza ophunzirawo kuona chisangalalo chimene adzakhala nacho.

Nkhani yaikulu papulogalamuyi inakambidwa ndi Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira, ndipo mutu wake unali wakuti “Kodi Tsopano Mudzachita Chiyani ndi Zonse Zimene Mwamva?” M’bale Jackson, amene anali mmishonale ku South Pacific kwa zaka pafupifupi 25, anafotokoza mbali yomaliza ya ulaliki wa paphiri. Paulaliki umenewo, Yesu analankhula za amuna awiri, wina wochenjera ndi wina wopusa, amene anamanga nyumba. M’baleyo  anafotokoza kuti mwina nyumbazo zinali m’dera limodzi. Koma munthu wopusa anamanga nyumba yake pamchenga, pamene wochenjera uja anakumba pansi mpaka atapeza thanthwe monga maziko ndi kumangapo nyumba yake. Kutagwa mvula yamkuntho, nyumba yomangidwa pathanthwe sinagwe koma ija yomangidwa pamchenga inagwa yonse.​—Mat. 7:24-27; Luka 6:48.

Yesu anafotokoza kuti munthu wopusa anafanana ndi anthu amene anamva zimene Yesu anaphunzitsa koma osachita. Munthu wanzeru anafanana ndi anthu amene anamvera mawu a Yesu ndi kutsatira. M’bale Jackson anauza ophunzirawo kuti, “Paumishonale wanu mukamachita zimene mwaphunzira m’Baibulo, mudzakhala ngati munthu wochenjera.” Pomaliza, analimbikitsa ophunzirawo kuti “ayambe kukumba” pantchito yawo yaumishonale.

Kenako, omaliza maphunzirowo analandira zikalata zosonyeza kuti amaliza maphunziro awo ndipo anauzidwa kumene adzapita. M’bale Morris anapereka malangizo omaliza. Analimbikitsa ophunzirawo kutsatira Yesu nthawi zonse ndi kuti asaleke kudalira mphamvu ya Yehova. Apa ndi pamene pulogalamu yonse inathera.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Dipatimenti ya Sukulu za Mulungu imayang’aniridwa ndi Komiti Yophunzitsa, ndipo dipatimentiyi imayang’anira Gileadi, sukulu ya Makomiti a Nthambi, ndi sukulu ya oyang’anira oyendayenda.

[Bokosi patsamba 31]

ZA OPHUNZIRAWO

Chiwerengero cha mayiko amene ophunzira achokera: 10

Chiwerengero cha mayiko amene atumizidwa: 24

Chiwerengero cha ophunzira: 56

Avereji ya zaka za kubadwa: 33.5

Avereji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 17.9

Avereji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 13.8

[Chithunzi patsamba 32]

Kalasi ya 123 ya Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pam’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliwonse.

(1) Esparza, E.; Papaya, S.; Bilal, A.; Suárez, M.; Evers, E.; Dimichino, K. (2) Rosa, M.; Fujii, R.; Ratey, O.; Leveton, J.; Van Leemputten, M. (3) Boscaino, A.; Beck, K.; Budanov, H.; Braz, C.; Peltz, K.; Siaw, A. (4) Leveton, S.; Santikko, H.; Conte, S.; Wilson, J.; Rylatt, J.; Pierce, S.; Fujii, K. (5) Rosa, D.; Boscaino, M.; Austin, V.; Rodiel, P.; Bilal, P.; Dimichino, P. (6) Ratey, B.; Czyzyk, D.; Clarke, C.; Riedel, A.; Esparza, F.; Siaw, P.; Van Leemputten, T.(7) Rodiel, J.; Evers, J.; Green, J.; Czyzyk, J.; Santikko, M.; Rylatt, M. (8) Peltz, L.; Austin, D.; Riedel, T.; Beck, M.; Pierce, W.; Conte, S.; Green, S. (9) Suárez, J.; Clarke, J.; Papaya, S.; Budanov, M.; Wilson, R.; Braz, R.