Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’mabuku a Obadiya, Yona, ndi Mika

Mfundo Zazikulu za M’mabuku a Obadiya, Yona, ndi Mika

 Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’mabuku a Obadiya, Yona, ndi Mika

“MASOMPHENYA a Obadiya.” (Obadiya 1) Awa ndi mawu oyambirira a buku la m’Baibulo la Obadiya. M’bukuli, lomwe analilemba mu 607 B.C.E., mneneriyu sananenepo chilichonse chokhudza iyeyo, kupatulapo dzina lake basi. M’buku lina limene linamalizidwa zaka zoposa 200 Obadiya asanalembe buku lake, mneneri Yona anasimba nkhani yosabisa kanthu ya zimene anakumana nazo pantchito yake yaumishonale. Mika anachita ntchito yauneneri zaka 60, kuchokera mu 777 B.C.E. mpaka mu 717 B.C.E., ndipo nthawiyi n’kuti Yona atamaliza kale utumiki wake koma Obadiya anali asanachite. Mika nayenso sananene zambiri zokhudza iyeyo, anangotchulapo kuti iyeyo anali “wa ku [mudzi wa] Morese” ndiponso kuti mawu a Yehova anam’fikira “masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya,” omwe anali mafumu a Yuda. (Mika 1:1) Mafanizo amene mneneri Mika anagwiritsa ntchito pofuna kugogomezera mfundo za uthenga wake akuonetsa kuti mneneriyu ankadziwa bwino moyo wakumudzi.

EDOMU ‘ADZAWONONGEDWA KU NTHAWI ZONSE’

(Obadiya 1-21)

Ponena za Edomu, Obadiya anati: “Chifukwa cha chiwawa unam’chitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzawonongeka ku nthawi yonse.” Mneneriyu akukumbukira bwinobwino chiwawa chimene Aedomu anali atangochitira kumene ana a Yakobo, Aisiraeli. Mu 607 B.C.E., Ababulo atawononga Yerusalemu, Aedomu ‘anaima padera’ n’kukhala mbali ya anthu “achilendo” obwerera nkhondowo.​—Obadiya 10, 11.

Mosiyana ndi Edomu, nyumba ya Yakobo ikuyembekezera kudzabwezeretsedwa. Ulosi wa Obadiya unati: “M’phiri la Ziyoni mudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika.”​—Obadiya 17.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

5-8—Kodi n’chifukwa chiyani kuwonongedwa kwa Edomu anakusiyanitsa ndi kubwera kwa akuba usiku ndiponso kubwera kwa anthu otchera mphesa? N’chifukwa choti ku Edomu kukanati kubwere akuba, akanangotenga zimene akufuna basi, osati chilichonse. Ndipo kukanati kubwere anthu okolola, akanasiyako mbewu zina kuti anthu adzakunkhe. Komatu anthu odzawonongawo adzaseseratu chuma chake chonse ndipo Edomu adzalandidwa chilichonse ndi ‘anthu amene akupangana naye,’ omwe ndi Ababulo.​—Yeremiya 49:9, 10.

10—Kodi Edomu ‘anawonongedwa ku nthawi yonse’ m’njira yotani? Monga mmene ulosi unanenera, mtundu wa Edomu unatha, chifukwa choti panopo kulibe boma lililonse, kapena anthu aliwonse odziwika kuti ndi Aedomu. Mfumu ya ku Babulo Nabonidasi, inalanda Edomu cha m’ma 550 B.C.E. Pofika m’ma 300 B.C.E., ku Edomu kunkakhala Anebayoti, ndipo Aedomu anathawira chakum’mwera kwa Yudeya, dera lomwe linadzayamba kutchedwa Idumeya. Aroma atawononga Yerusalemu mu 70 C.E., mtundu wa Edomu unatha.

 Zimene Tikuphunzirapo:

3, 4N’kutheka kuti Aedomu ankadzithemba n’kumaganiza kuti n’ngotetezeka chifukwa choti ankakhala m’dera lovuta kufikako; lamapiri ataliatali ndi zigwembe zakuya. Koma chiweruzo cha Yehova sichithawika.

8, 9, 15. Nzeru ndiponso mphamvu za anthu sizidzawateteza pa “tsiku la Yehova.”​—Yeremiya 49:7, 22.

12-14. Aedomu ndi chitsanzo chochenjeza aliyense amene amasangalala anthu a Mulungu akamavutika. Yehova saona mopepuka nkhani ya kuzunzika kwa anthu ake.

17-20. Ulosi wonena za kubwezeretsedwa kwa ana a Yakobo umenewu unayamba kukwaniritsidwa pamene anthu otsalira anabwerera ku Yerusalemu kuchoka ku Babulo mu 537 B.C.E. Mawu a Yehova amakwaniritsidwa nthawi zonse. Tisakayike ngakhale pang’ono za malonjezo a Yehova.

“NINEVE ADZAPASUKA”

(Yona 1:1–4:11)

M’malo momvera lamulo la Mulungu lakuti “pita ku Nineve, mudzi waukuluwo, nulalikire [uthenga wachiweruzo] motsutsana nawo,” Yona anathawa n’kulowera kwina. Potumiza “chimphepo chachikulu panyanja” ndiponso pogwiritsira ntchito “chinsomba chachikulu,” Yehova anam’bweza Yonayo n’kumutumanso kachiwiri kuti apite ku likulu la dziko la Asuri.​—Yona 1:2, 4, 17; 3:1, 2.

Yona anafika ku Nineve n’kuyamba kupereka uthenga wosapita m’mbali wakuti: “Atsala masiku makumi anayi ndipo Nineve adzapasuka.” (Yona 3:4) Anthuwo anasintha chifukwa cha uthenga wake, koma iye “anapsa mtima” kwambiri chifukwa choti sanayembekezere zimenezi. Yehova anagwiritsira ntchito “msatsi” pophunzitsa Yona, kukhala wachifundo.​—Yona 4:1, 6.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

3:3​—Kodi mzinda wa Nineve unalidi waukulu kukwana “ulendo wa masiku atatu”? Inde. Zikuoneka kuti kalekale dzina loti Nineve linkaphatikizapo madera ena kuchokera ku Khorsabad, kumpoto kwa Nineve, mpaka kukafika ku Nimrud, kummwera kwake. Kuzungulira midzi yonse ya ku Nineve unali mtunda wa makilomita 100.

3:4​—Kodi Yona anafunika kuphunzira chinenero cha Asuri kuti alalikire anthu a ku Nineve? N’kutheka kuti Yona ankadziwa kale chinenerocho, apo ayi anapatsidwa mphamvu zozizwitsa zom’thandiza kulankhula chinenerocho. N’kuthekanso kuti uthenga wosapita m’mbaliwo anaupereka m’Chiheberi, ndipo anali ndi munthu wina womasulira ndipotu ngati zinali choncho, ndiye kuti mawu akewo ayenera kuti anachititsa anthu chidwi kwabasi.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:1-3. Kuchita dala zinthu zina n’cholinga chopewa kuchita nawo bwinobwino ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira kumasonyeza kuti munthuwe ulibe zolinga zabwino. Munthu amene amachita zimenezi amakhala ngati kuti akuthawa ntchito imene Mulungu wam’patsa.

1:1, 2; 3:10. Yehova sasonyeza chifundo chake kwa anthu amtundu kapena fuko limodzi lokha ayi. Sasonyezanso chifundo chake kwa kagulu kenakake kokha ka anthu. “Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.”​—Salmo 145:9.

1:17; 2:10. Yona anakhala m’mimba mwa chinsomba masiku atatu ndipo zimenezi zinkalosera imfa ndi kuukitsidwa kwa Yesu.​—Mateyo 12:39, 40; 16:21.

1:17; 2:10; 4:6. Yehova anapulumutsa Yona panyanja yolusa. Mulungu yemweyonso “anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kum’landitsa m’nsautso yake.” Atumiki a Yehova masiku ano asamakayike ngakhale pang’ono kuti Mulungu wawo n’ngokoma mtima ndipo angathe kuwateteza ndi kuwalanditsa.​—Salmo 13:5; 40:11.

2:1, 2, 9, 10. Yehova amamva mapemphero a atumiki ake ndipo amamvera zopempha zawo.​—Salmo 120:1; 130:1, 2.

3:8, 10. Mulungu woona “analeka choipa,”  kapena kuti anasintha maganizo ake, pa zoopsa zimene ananena kuti adzachitira mzinda wa Nineve, ndipo ‘sanazichite.’ N’chifukwa chiyani anatero? N’chifukwa choti anthu a ku Nineve ‘anabwerera kuleka njira yawo yoipa.’ N’chimodzimodzinso masiku ano. Munthu wochimwa angathe kupewa kulangidwa ndi Mulungu ngati atasonyeza kulapa kwenikweni.

4:1-4. Palibe munthu amene angachititse Mulungu kuika malire a chifundo Chake. Tizisamala kuti tisamaweruze njira zachifundo za Yehova.

4:11. Yehova waleza mtima kuti uthenga wa Ufumu ulalikidwe pa dziko lonse chifukwa choti iyeyo amachitira chisoni anthu “osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere,” monga anachitira ndi anthu 120,000 a ku Nineve. Kodi nafenso sitingachite bwino kumvera chisoni anthu am’dera lathu pochita mwakhama ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira?​—2 Petulo 3:9.

‘DAZI LAWO LIDZAKULITSIDWA’

(Mika 1:1–7:20)

Mika ananena poyera za machimo a Isiraeli ndi Yuda, analosera zoti malikulu awo adzawonongedwa, ndipo analonjeza zoti adzabwezeretsedwa. Samariya adzakhala “ngati mulu wa miyala ya m’munda.” Chifukwa cha kulambira mafano, Isiraeli ndi Yuda n’ngoyenerera “dazi,” kapena kuti kuchititsidwa manyazi. Potumizidwa ku ukapolo, dazi lawo lidzakulitsidwa “ngati la muimba,” mbalame yometeka m’mutu. Yehova analonjeza kuti: “Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo.” (Mika 1:6, 16; 2:12) Chifukwa cha atsogoleri achinyengo ndiponso aneneri osamvera Mulungu, Yerusalemu naye ‘adzasanduka miunda.’ Koma Yehova ‘adzasonkhanitsa anthu ake.’ Ku “Betelehemu Efrata” kudzachokera “wina wakudzakhala woweruza m’Isiraeli.”​—Mika 3:12; 4:12; 5:2.

Kodi Yehova anawalakwira Aisiraeli powalanga chonchi? Kodi zimene Yehova amafuna kuti anthu azichita n’zovuta kwambiri kuzikwanitsa? Ayi. Yehovatu amangofuna kuti atumiki ake ‘azichita cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wawoyu.’ (Mika 6:8) Komatu anthu a m’masiku a Mika anafika poipa kwambiri moti “wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wawo aipa koposa mpanda waminga,” womwe umabaya munthu aliyense wouyandikira. Komano mneneriyu akufunsa kuti: “Ndani Mulungu wofanana ndi [Yehova]?” Mulungu adzasonyezanso chifundo kwa anthu ake ndipo ‘adzataya zochimwa zawo zonse m’nyanja yakuya.’​—Mika 7:4, 18, 19.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

2:12​—Kodi ulosi wonena za ‘kusonkhanitsa otsala a Isiraeli’ unakwaniritsidwa liti? Unakwaniritsidwa koyamba mu 537 B.C.E. pamene Ayuda otsalira anabwerera kwawo kuchoka ku ukapolo ku Babulo. Masiku ano, ulosiwu umakwaniritsidwa mwa “Isiraeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) Kuyambira mu 1919, Akhristu odzozedwa asonkhanitsidwa “ngati nkhosa” m’khola. Kufika kwa “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” makamaka kuyambira mu 1935, kwachititsa kuti ‘achite phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.’ (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Magulu awiriwa akuchitira pamodzi mwakhama ntchito yolimbikitsa kulambira koona.

4:1-4​—Kodi mu “masiku otsiriza” ano, Yehova akukwaniritsa motani mawu akuti “adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali”? Mawu akuti “mitundu yambiri ya anthu” ndiponso akuti “amitundu amphamvu” satanthauza mitundu yeniyeni kapena mayiko ayi. Koma amatanthauza anthu osiyanasiyana omwe ali ochokera m’mitundu yonse ya anthu, ndipo ayamba kulambira Yehova. Iye amawaweruza ndi kuwadzudzula mwauzimu.

 Zimene Tikuphunzirapo:

1:6, 9; 3:12; 5:2. Samariya anawonongedwa ndi Asuri mu 740 B.C.E., Mika adakali moyo. (2 Mafumu 17:5, 6) Asuri anafika mpaka ku Yerusalemu panthawi ya ulamuliro wa Hezekiya. (2 Mafumu 18:13) Mzinda wa Yerusalemu unayatsidwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E. (2 Mbiri 36:19) Monga ulosi unanenera, Mesiya anabadwira ku “Betelehemu Efrata.” (Mateyo 2:3-6) Mawu aulosi a Yehova salephera kukwaniritsidwa.

2:1, 2N’zoopsa kwambiri ngati timanena kuti tikutumikira Mulungu komano panthawi yomweyo n’kumayamba kufunafuna kaye chuma osati “kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake.”​—Mateyo 6:33; 1 Timoteyo 6:9, 10.

3:1-3, 5Yehova amafuna kuti abale amaudindo pakati pa anthu ake azichita zinthu mwachilungamo.

3:4. Ngati tikufuna kuti Yehova aziyankha mapemphero athu, tisamachite zochimwa kapena kukhala moyo wachiphamaso.

3:8. Sitingakwanitse ntchito imene tapatsidwa yolalikira uthenga wabwino, womwenso uli wachiweruzo, popanda kulimbikitsidwa ndi mphamvu ya mzimu woyera wa Yehova.

5:5. Ulosi wonena za Mesiyawu umatitsimikizira kuti anthu a Mulungu akamazunzidwa ndi adani awo, Mulungu amautsa “abusa asanu ndi awiri,” kutanthauza kuti okwanira ndi “akalonga asanu ndi atatu,” kutanthauza kuti amuna ochuluka ndithu, n’cholinga choti atsogolere anthu a Yehova.

5:7, 8Anthu ambiri amaona kuti Akhristu odzozedwa masiku ano ali ngati “mame ochokera kwa Yehova,” kutanthauza madalitso ochokera kwa Mulungu. Zili choncho chifukwa chakuti Yehova amagwiritsira ntchito Akhristu odzozedwa polengeza uthenga wa Ufumu. A “nkhosa zina” amathandiza nawo kutsitsimula anthu mwauzimu pogwira ntchito yolalikira limodzi ndi Akhristu odzozedwa. (Yohane 10:16) Kuchita nawo ntchito imeneyi ndi mwayi waukulu kwambiri chifukwa ikutsitsimula anthu kwabasi.

6:3, 4Tizitsanzira Yehova Mulungu pokhala okoma mtima ndi achifundo ngakhale kwa anthu ovuta kuchita nawo zinthu kapena ofooka mwauzimu.

7:7. Tisamataye mtima chifukwa cha mavuto amene tikukumana nawo kumapeto kwa dongosolo la zinthu loipali. M’malo mwake, tizikhala ngati Mika ‘polindirira Mulungu’ wathu.

7:18, 19. Yehova ndi wokonzeka kutikhululukira zolakwa zathu, motero nafenso tizikhala okonzeka kukhululukira anthu amene atilakwira.

Pitirizani ‘Kuyenda M’dzina la Yehova’

Amene amalimbana ndi Mulungu komanso anthu ake ‘adzawonongedwa ku nthawi zonse.’ (Obadiya 10) Koma Yehova angasiye kutikwiyira ngati timvera chenjezo lake, ‘n’kuleka njira zoipa.’ (Yona 3:10) Mu “masiku otsiriza” ano, kulambira koona kwakwezedwa pamwamba pa kulambira konse konyenga ndipo anthu omvera akukhamukirako. (Mika 4:1; 2 Timoteyo 3:1) Motero tiyeni tiyesetse kuyenda “m’dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yomka muyaya.”​—Mika 4:5.

Mabuku a Obadiya, Yona, ndiponso Mika amatiphunzitsa zinthu zofunikira kwambiri. Ngakhale kuti analembedwa zaka zoposa 2,500 zapitazo, uthenga wawo ndi ‘wamoyo ndi wamphamvu,’ ngakhale masiku ano.​—Aheberi 4:12.

[Chithunzi patsamba 13]

Obadiya analosera kuti: ‘[Edomu] adzawonongedwa ku nthawi yonse’

[Chithunzi patsamba 15]

Mika ‘anasonyeza mtima wolindirira Yehova,’ ndipo nanunso mungatero

[Chithunzi patsamba 16]

Tiziona kuti ndi mwayi waukulu zedi kwa ifeyo kuchita ntchito yolalikira