Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu a Yehova Amakwaniritsidwa Nthawi Zonse

Mawu a Yehova Amakwaniritsidwa Nthawi Zonse

 Mawu a Yehova Amakwaniritsidwa Nthawi Zonse

“Pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu.”​—YOSWA 23:14.

1. Kodi Yoswa anali ndani, ndipo anachita chiyani chakumapeto kwa moyo wake?

YOSWA anali mtsogoleri wa asilikali wamphamvu, wolimba mtima, wachikhulupiriro komanso wokhulupirika. Iye ankayenda ndi Mose ndipo Yehova anamusankha kuti atsogolere Aisiraeli podutsa m’chipululu choopsa, n’kukalowa m’dziko loyenda mkaka ndi uchi. Chakumapeto kwa moyo wake, Yoswa, amene ambiri ankamupatsa ulemu, analankhula mawu olimbikitsa potsanzikana ndi akuluakulu a Isiraeli. Mosakayikira, chikhulupiriro cha anthu amene anamva mawu akewo chinalimba. Ndipo mawuwo angalimbitsenso chikhulupiriro chanu.

2, 3. Kodi Yoswa analankhula zotani ndi akuluakulu a Isiraeli, ndipo kodi zinthu zinali bwanji ndi mtundu wa Isiraeli panthawiyo?

2 Yerekezani kuti mukuona zochitika zimene Baibulo limafotokoza motere: “Atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Isiraeli kwa adani awo onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri; Yoswa anaitana Aisiraeli onse, akuluakulu awo, ndi akulu awo, ndi oweruza awo, ndi akapitawo awo, nanena nawo, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri.”​—Yoswa 23:1, 2.

3 Apa n’kuti Yoswa atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 110 zakubadwa. Nthawi imene iye anakhala ndi moyo inali imodzi mwa nthawi zosangalatsa kwambiri m’mbiri ya anthu a Mulungu. Iye anaona zinthu zamphamvu zimene Mulungu anachita ndipo anaonanso kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova. Chifukwa cha zimenezi, iye anatha kunena mosakayikira kuti: “Mudziwa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasowapo mawu amodzi.”​—Yoswa 23:14.

4. Kodi Yehova anawalonjeza chiyani Aisiraeli?

4 Kodi ndi mawu a Yehova ati amene anakwaniritsidwa m’nthawi ya Yoswa? Tikambirana malonjezo atatu amene Yehova anapereka kwa Aisiraeli. Lonjezo loyamba linali lakuti iye adzawapulumutsa ku ukapolo. Lachiwiri linali lakuti adzawateteza. Ndipo lachitatu linali lakuti adzawasamalira. Yehova waperekanso malonjezo ngati amenewa kwa anthu ake masiku ano ndipo taona kukwaniritsidwa kwa mawu ake. Koma tisanakambirane zimene Yehova wachita masiku ano, tiyeni choyamba tione zimene Iye anachita m’nthawi ya Yoswa.

Yehova Anapulumutsa Anthu Ake

5, 6. Kodi Yehova anapulumutsa Aisiraeli motani ku Iguputo, ndipo zimenezi zinasonyeza chiyani?

5 Ali mu ukapolo ku Iguputo, Aisiraeli anafuulira Yehova ndipo iye anamva kulira kwawo. (Eksodo 2:23-25) Pachitsamba choyaka moto, Yehova anauza Mose kuti: ‘Nditsikira kuwalanditsa [anthu anga] m’manja a anthu a Aiguputo, ndi kuwatulutsa m’dziko lija akwere nalowe m’dziko labwino ndi lalikulu, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.’ (Eksodo 3:8) Zinalitu zosangalatsa kwambiri kuona Yehova akukwaniritsa lonjezo limeneli. Farao atakana kulola Aisiraeli kuchoka mu Iguputo, Mose anamuuza kuti Mulungu asandutsa madzi a mumtsinje wa Nile kukhala magazi. Ndipo mawu a Yehova amenewa anakwaniritsidwa. Madzi a mumtsinje wa Nile anasandukadi magazi. Nsomba zonse zinafa ndipo anthu sakanatha kumwa madziwo. (Eksodo 7:14-21) Koma Farao sanasinthe ndipo Yehova anachititsa miliri ina 9, ndipo asanachititse mliri uliwonse ankayamba wafotokozeratu za mliriwo.  (Eksodo chaputala 8 mpaka 12) Pambuyo pa mliri wachikhumi umene unapha ana oyamba kubadwa a ku Iguputo, Farao analamula kuti Aisiraeli anyamuke ndipo ananyamukadi.​—Eksodo 12:29-32.

6 Kupulumutsidwa kumeneko kunachititsa kuti Aisiraeli akhale mtundu wosankhidwa ndi Yehova. Zimenezi zinasonyeza kuti Yehova amakwaniritsa malonjezo ake, ndipo mawu ake onse amakwaniritsidwa. Zinaonetsanso kuti Yehova ndi wamphamvu kuposa milungu ya anthu amitundu ina. Chikhulupiriro chathu chimalimba tikamawerenga za kupulumutsidwa kumeneku. Tangoganizani mmene anthuwo anamvera atapulumutsidwa ndi Yehova. Yoswa sanakayikire kuti Yehova ndi “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”​—Salmo 83:18.

Yehova Anateteza Anthu Ake

7. Kodi Yehova anateteza motani Aisiraeli ku magulu ankhondo a Farao?

7 Nanga bwanji za lonjezo lachiwiri loti Yehova adzateteza anthu ake? Lonjezo lakuti Yehova adzapulumutsa anthu ake kuchoka ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa linaphatikizapo lonjezo la kuwateteza. Kumbukirani kuti Farao atakwiya analondola Aisiraeli ndi magaleta ambiri a asilikali ake amphamvu. Farao anaona kuti zinthu zimuyendera bwino pamene Aisiraeli ankaoneka kuti apanikizika pakati pa mapiri ndi nyanja. Tsopano Mulungu anachitapo kanthu kuti ateteze anthu ake. Anachititsa kuti pakhale mtambo pakati pa Aisiraeli ndi Aiguputo. Kumbali ya Aiguputo kunali mdima pamene kumbali ya Aisiraeli kunali kowala. Pamene mtambo unatsekereza Aiguputo, Mose anamenya madzi ndi ndodo yake ndipo madzi a Nyanja Yofiira anagawikana. Izi zinapereka mpata woti Aisiraeli adutse komanso malo oti Aiguputo aferepo. Yehova anawonongeratu ankhondo amphamvu a Farao, motero anateteza anthu ake kuti asagonjetsedwe.​—Eksodo 14:19-28.

8. Kodi Aisiraeli anatetezedwa motani (a) m’chipululu (b) atalowa m’Dziko Lolonjezedwa?

8 Atawoloka Nyanja Yofiira, Aisiraeli anayendayenda m’dera lomwe Baibulo limafotokoza kuti linali, ‘chipululu chachikulu ndi choopsa, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi.’ (Deuteronomo 8:15) Yehova anatetezanso anthu ake m’chipululumo. Nanga bwanji polowa m’Dziko Lolonjezedwa? Kutsogolo kwawo kunali magulu ankhondo amphamvu a ku Kanani. Koma Yehova anauza Yoswa kuti: “Tauka tsono, nuwoloke Yordano uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m’dzikomo ndili kuwapatsa, ndiwo ana a Isiraeli. Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.” (Yoswa 1:2, 5) Mawu a Yehova amenewa anakwaniritsidwa. Pamene zaka pafupifupi 6 zinkatha,  Yoswa anali atagonjetsa mafumu 31 ndipo anali atalanda mbali yaikulu ya Dziko Lolonjezedwa. (Yoswa 12:7-24) Yehova akanapanda kuwateteza, iwo sakanatha kugonjetsa mafumuwo.

Yehova Anasamalira Anthu Ake

9, 10. Kodi Yehova anasamalira motani anthu ake m’chipululu?

9 Taganiziraninso za lonjezo lachitatu loti Yehova adzasamalira anthu ake. Atangotuluka mu Iguputo, Yehova analonjeza Aisiraeli kuti: “Ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake.” Mulungu anawapatsadi ‘mkate wochokera kumwamba’ malinga ndi lonjezo lake. Baibulo limati: “Pamene ana a Isiraeli anakaona, anati wina ndi mnzake, N’chiyani ichi?” Anali mana, mkate umene Yehova anawalonjeza.​—Eksodo 16:4, 13-15.

10 Pa zaka 40 zimene Aisiraeli anali m’chipululu, Yehova anawasamalira powapatsa chakudya ndi madzi. Komanso, iye anaonetsetsa kuti zovala zawo sizikutha ndiponso mapazi awo asamatupe. (Deuteronomo 8:3, 4) Yoswa ankaona zonsezi. Yehova anapulumutsa, kuteteza ndiponso kusamalira anthu ake malinga ndi malonjezo ake.

Mmene Yehova Wapulumutsira Anthu Ake Masiku Ano

11. N’chiyani chinachitika ku Brooklyn, New York, mu 1914, ndipo pamenepa inali nthawi ya chiyani?

11 Nanga bwanji masiku ano? M’mawa wa Lachisanu, pa October 2, 1914, Charles Taze Russell, yemwe anali mtsogoleri wa Ophunzira Baibulo panthawiyo, analowa m’chipinda chodyera cha Beteli ku Brooklyn, mumzinda wa New York. Atangolowa, anapereka moni kwa onse mwansangala. Ndiyeno asanakhale pansi ananena mosangalala kuti: “Nthawi za Akunja zatha; tsiku la mafumu awo latha.” Apanso nthawi inali itakwana yoti Yehova, Mfumu ya chilengedwe chonse, achitepo kanthu pofuna kupulumutsa anthu ake, ndipotu anachitadi zimenezo.

12. Kodi anthu a Mulungu anapulumutsidwa motani mu 1919, ndipo zimenezi zinakhala ndi zotsatirapo zotani?

12 Patangotha zaka zisanu chichitikireni zimenezi, Yehova anapulumutsa anthu ake mu “Babulo Wamkulu” womwe ndi ufumu wamphamvu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga. (Chivumbulutso 18:2) Ambiri a ife sitinaone ndi maso athu zochitika zosangalatsa zimenezo. Koma tikutha kuona zotsatira zake. Yehova wabwezeretsa kulambira koyera ndipo wagwirizanitsa anthu amene akufunitsitsa kumulambira. Izi n’zimene mneneri Yesaya analosera kuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.”​—Yesaya 2:2.

13. Kodi inuyo mwaona kuwonjezeka kotani kwa chiwerengero cha anthu a Yehova?

13 Mawu a Yesaya amenewa anakwaniritsidwa. Mu 1919, otsalira odzozedwa anayamba ntchito ya padziko lonse yochitira umboni molimba  mtima, ndipo zimenezi zachititsa kuti kulambira Mulungu woona kukhale kokwezeka. M’ma 1930, zinadziwika kuti “nkhosa zina” zinali zitayamba kusonkhanitsidwa. (Yohane 10:16) Nthawi imeneyo, anthu masauzande ankagwirizana m’kulambira koyera koma panopa chiwerengero chawo chafika mamiliyoni. M’masomphenya amene mtumwi Yohane anaona, iwo anafotokozedwa kuti ndi “khamu lalikulu limene munthu sanathe kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse, fuko, mtundu, ndi lilime lililonse.” (Chivumbulutso 7:9) Nanga kodi inuyo mwaonapo zotani m’moyo wanu? Kodi pamene inuyo munkayamba choonadi n’kuti Mboni za Yehova zilipo zochuluka bwanji padziko lonse? Masiku ano anthu oposa 6,700,000 akutumikira Yehova. Choncho, mwa kupulumutsa anthu ake mu Babulo Wamkulu, Yehova anatsegula njira yoti chiwerengero cha atumiki ake padziko lonse chiwonjezeke mochititsa chidwi.

14. Kodi ndi kupulumutsidwa kotani kumene tikuyembekezera?

14 Yehova adzapulumutsanso anthu m’njira imene idzakhudza munthu wina aliyense padziko lapansi. Iye adzasonyeza mphamvu zake m’njira yodabwitsa kwambiri. Adzawonongeratu onse amene amatsutsa ulamuliro wake ndipo adzapulumutsa anthu ake, n’kuwalowetsa m’dziko latsopano mmene mudzakhala chilungamo. Zidzakhalatu zosangalatsa kwabasi kuona zoipa zonse zikuthetsedwa ndiyeno, n’kuona kuyambika kwa nthawi yabwino kwambiri m’mbiri yonse ya anthu.​—Chivumbulutso 21:1-4.

Mmene Yehova Akutetezera Anthu Ake Masiku Ano

15. Kodi n’chifukwa chiyani tikufunikira chitetezo cha Yehova masiku ano?

15 Monga momwe taonera, Aisiraeli a m’nthawi ya Yoswa anafunikira chitetezo cha Yehova. N’chimodzimodzinso ndi anthu a Yehova masiku ano. Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Anthu adzakuperekani ku chisautso ndipo adzakuphani. Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa.” (Mateyo 24:9) Kwa zaka zambiri, Mboni za Yehova zapirira potsutsidwa kwambiri komanso pozunzidwa mwankhanza. Koma Yehova wakhala akuthandiza anthu ake. (Aroma 8:31) Mawu ake amatitsimikizira kuti ‘palibe chida chosulidwira ife’ chimene chingaletse ntchito yathu yolalikira za Ufumu ndi kuphunzitsa anthu.​—Yesaya 54:17.

16. Kodi inu mwaona umboni wotani wosonyeza kuti Yehova amateteza anthu ake?

16 Chiwerengero cha anthu a Yehova chikuwonjezekabe ngakhale kuti dzikoli limawada. Ntchito ya Mboni za Yehova ikupita patsogolo m’mayiko 236, ndipo umenewu ndi umboni wakuti Yehova akutiteteza kwa anthu amene amafuna kutiwononga kapena kutiletsa kulalikira.  Kodi inuyo mukukumbukira mayina a atsogoleri andale kapena achipembedzo omwe azunza kwambiri anthu a Mulungu m’nthawi yanu? Kodi chinawachitikira n’chiyani? Kodi lero ali kuti? Ambiri a iwo kulibe monga m’mene zinakhalira ndi Farao m’nthawi ya Mose ndi Yoswa. Nanga bwanji za atumiki a Mulungu amasiku ano amene akhala okhulupirika kufikira imfa? Iwo ndi otetezeka chifukwa Yehova akuwakumbukira ndipo zimenezi n’zoposa chitetezo china chili chonse. Apatu, n’zoonekeratu kuti mawu a Yehova oti adzateteza anthu ake akwaniritsidwa.

Yehova Akusamalira Anthu Ake Masiku Ano

17. Kodi Yehova analonjeza chiyani pankhani ya chakudya chauzimu?

17 Yehova anasamalira anthu ake m’chipululu ndipo akusamaliranso anthu ake masiku ano. Timalandira chakudya chauzimu kuchokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyo 24:45) Tikudziwa choonadi chonena za Mulungu chimene chakhala chosadziwika kwa zaka zambiri. Mngelo wina anauza Danieli kuti: “Tsekera mawu awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimariziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.”​—Danieli 12:4.

18. N’chifukwa chiyani tinganene kuti masiku ano chidziwitso chonena za Mulungu chachuluka?

18 Tsopano tikukhala m’nthawi ya mapeto ndipo chidziwitso chonena za Mulungu chachulukadi. Padziko lonse mzimu woyera ukuthandiza anthu ofuna choonadi kudziwa zoona zenizeni za Mulungu ndi zolinga zake. Masiku ano Baibulo likupezeka padziko lonse, ndipo pali mabuku ambiri othandiza anthu kumvetsa choonadi chamtengo wapatali chopezeka m’Baibulo. Tangoganizani nkhani zimene zili m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * Mwa zina, m’bukuli muli nkhani zakuti: “Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?,” “Kodi Akufa Ali Kuti?,” “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?,” ndiponso “N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?” Anthu akhala akudzifunsa mafunso amenewa kwa zaka zambiri. Tsopano n’zosavuta kupeza mayankho a mafunso amenewa. Ngakhale kuti padutsa zaka zambiri anthu akungokhala, osadziwa choonadi, ndiponso chipembedzo chonyenga chikuphunzitsa mabodza, Mawu a Mulungu apambana ndipo anthu ofuna kutumikira Yehova akusamaliridwa.

19. Kodi ndi malonjezo ati amene inuyo mwaona akukwaniritsidwa ndipo mwatsimikizira za chiyani?

19 Apatu, malinga ndi zimene taona, tinganene kuti: “Pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasowapo mawu amodzi.” (Yoswa 23:14) Yehova amapulumutsa, kuteteza ndiponso kusamalira atumiki ake. Kodi mungathe kunena lonjezo lina lililonse limene iye sanakwaniritse pa nthawi yake? Simungathe kutero. Choncho, ndi bwino kukhulupirira Mawu a Mulungu omwe ndi odalirika.

20. N’chifukwa chiyani sitingakayikire chilichonse ponena za m’tsogolo?

20 Nanga bwanji za m’tsogolo? Yehova watilonjeza kuti ambirife tidzakhala m’dziko lapansi, litakonzedwa bwino kukhala paradaiso wokongola. Anthu ochepa chabe akuyembekezera kukalamulira limodzi ndi Khristu kumwamba. Kaya tikuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, kaya kupita kumwamba, tili ndi zifukwa zomveka zokhalira okhulupirika ngati Yoswa. Nthawi ina, zonse zimene tikuyembekezera zidzakwaniritsidwa. Ndiyeno tikadzakumbukira zonse zimene Yehova anatilonjeza, nafenso tidzatha kunena kuti: ‘Zonse zachitika.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi Yoswa anaona kukwaniritsidwa kwa malonjezo ati a Yehova?

• Kodi inuyo mwaona kukwaniritsidwa kwa malonjezo ati a Mulungu?

• Ponena za mawu a Mulungu, kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Yehova anachitapo kanthu kuti apulumutse anthu ake

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi Yehova anateteza anthu ake motani pa Nyanja Yofiira?

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi Yehova anasamalira anthu ake motani m’chipululu?

[Zithunzi patsamba 25]

Yehova amasamalira anthu ake masiku ano