Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudzichepetsa Sikophweka

Kudzichepetsa Sikophweka

 Kudzichepetsa Sikophweka

PALI anthu ambiri amene amaona kuti khalidwe lodzichepetsa n’lachikale. Anthu ambiri aulemu wawo ndiponso omwe amaoneka kuti zinthu zikuwayendera kwambiri, amakhala odzitama, onyada, komanso ongoganizira zawo zokha basi. Pali anthu ambiri amene amakhumbira moyo wa anthu olemera ndi otchuka, koma osati wa anthu odzichepetsa ndi ofatsa. Nthawi zambiri, m’malo modzichepetsa, anthu olemerawa amadzitama, n’kumanena kuti chuma chawo chonsecho anachita kuchivutikira okha.

Wofufuza wina wa ku Canada anati m’dzikolo mwabweranso khalidwe lina lomangoganizira zako zokha basi. Palinso anthu ena amene akuona kuti anthu ambiri padzikoli amangokhalira kusangalala ndi kuchita zinthu mosaganizira kaye bwinobwino. Iwo amanena kuti anthu ambiri masiku ano akungoganizira zawo zokha basi. N’chifukwa chake masiku ano kudzichepetsa sikukuoneka ngati khalidwe labwino.

Komabe anthu ambiri angavomereze mfundo yakuti ndi bwino kuti anthu ena azikhala odzichepetsa, chifukwa choti anthu odzichepetsa savuta kuchita nawo zinthu. Komabe m’dziko lokonda kupikisanali, anthu ena sadzichepetsa poopa kuti akatero, anthu ayamba kuwaona kuti ndi ofooka.

Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, linalosera kuti m’nthawi yathu ino anthu adzakhala “odzimva, odzikweza.” (2 Timoteyo 3:1, 2) Kodi mukuona kuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa? Nanga kodi mumaona kuti kukhala wodzichepetsa kuli ndi ubwino uliwonse? Kapena mumaganiza kuti anthu amaona kuti munthu wodzichepetsa ndi wofooka, wosavuta kumudyera masuku pamutu?

Baibulo limapereka zifukwa zomveka zosonyeza kuti khalidwe lodzichepetsa n’lofunika kwambiri. Limatithandiza kumvetsa bwino khalidweli ndi ubwino wokhala nalo, ndipo limasonyeza kuti kudzichepetsa kwenikweni si kufooka kapena mantha ayi. Nkhani yotsatirayi ifotokoza zifukwa zake.

[Chithunzi patsamba 3]

Kodi tiyenera kumva bwanji tikachita zinthu zinazake zotamandika?