Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsatirani Chikumbumtima Chanu

Tsatirani Chikumbumtima Chanu

 Tsatirani Chikumbumtima Chanu

“Zinthu zonse n’zoyera kwa anthu oyera. Koma kwa anthu oipitsidwa ndi opanda chikhulupiriro kulibe choyera.”​—TITO 1:15.

1. Kodi Paulo anachita zotani zokhudzana ndi mipingo ya ku Kerete?

MTUMWI PAULO atayenda maulendo ake atatu aumishonale, anamangidwa kenako n’kutumizidwa ku Roma, komwe anakakhalako zaka ziwiri. Kodi anachita chiyani atamasulidwa? Panthawi ina, iye limodzi ndi Tito anapita ku chilumba cha Kerete. Kenako analembera Tito kuti: “Ndinakusiya ku Kerete kuti ukonze zinthu zosalongosoka ndi kuti uike akulu.” (Tito 1:5) Tito anafunika kuthandiza anthu amene chikumbumtima chawo sichinkagwira bwino ntchito.

2. Kodi ndi vuto lotani limene Tito anafunika kuthetsa pa chilumba cha Kerete?

2 Paulo analangiza Tito za ziyeneretso za akulu m’mipingo ndipo kenako anamuuza kuti ku Kerete kunali “anthu ambiri osaweruzika, olankhula zopanda pake, ndi opotoza maganizo a ena.” Anthu amenewa ‘ankawononga mabanja athunthu mwa kuphunzitsa zinthu zimene sanayenere kuphunzitsa,’ ndipo Tito anafunika ‘kupitiriza kuwadzudzula.’ (Tito 1:10-14; 1 Timoteyo 4:7) Paulo ananena kuti maganizo ndiponso chikumbumtima chawo zinali ‘zoipitsidwa.’ Pamenepa iye anagwiritsa ntchito mawu otanthauza kuthimbirira, ngati mmene zimakhalira ndi chovala. (Tito 1:15) N’kutheka kuti ena mwa anthu amenewa anali Ayuda, chifukwa chakuti ‘anali kusungabe mdulidwe.’ Mipingo masiku ano sikuwonongedwa ndi anthu olimbikitsa mdulidwe ayi; koma tingaphunzire zambiri zokhudza chikumbumtima mwa kuona malangizo amene Paulo anapereka kwa Tito.

Anthu Achikumbumtima Choipitsidwa

3. Kodi Paulo anamuuza zotani Tito pankhani ya chikumbumtima?

3 Taonani nkhani imene Paulo anatchulamo za chikumbumtima. Iye anati: “Zinthu zonse n’zoyera kwa anthu oyera. Koma kwa anthu oipitsidwa ndi opanda chikhulupiriro kulibe choyera, m’malo mwake maganizo awo ndi chikumbumtima chawo n’zoipa. Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu, koma amam’kana ndi ntchito zawo.” N’zoonekeratu kuti anthu ena panthawiyo anafunika kusintha zina ndi zina kuti akhale ndi “chikhulupiriro cholimba.” (Tito 1:13, 15, 16) Iwo sankatha kusiyanitsa zoyera ndi zodetsedwa chifukwa cha chikumbumtima chawo.

4, 5. Kodi Akhristu ena anali ndi vuto lotani, ndipo kodi zinawakhudza bwanji?

4 Zaka zoposa 10 izi zisanachitike, bungwe lolamulira lachikhristu linaona kuti mdulidwe sunali wofunika kuti munthu akhale wolambira woona, ndipo linadziwitsa mipingo za nkhaniyi. (Machitidwe 15:1, 2, 19-29) Koma Akhristu ena ku Kerete ‘anali kusungabe mdulidwe.’ Iwo anatsutsa poyera zimene bungwe lolamulira linanena, ‘n’kumaphunzitsa zinthu zimene sanayenere kuphunzitsa.’ (Tito 1:10, 11) Chifukwa cha maganizo olakwika amenewa, n’kutheka kuti iwo ankalimbikitsa ena kutsatira zinthu za m’Chilamulo pankhani ya chakudya ndiponso kudziyeretsa  mwamwambo. N’kuthekanso kuti ankawonjezera pa zimene Chilamulo chinanena, monga momwe makolo awo a m’nthawi ya Yesu ankachitira. Komanso mwina ankalimbikitsa nthano za Chiyuda ndi malamulo a anthu.​—Maliko 7:2, 3, 5, 15; 1 Timoteyo 4:3.

5 Maganizo amenewa anasokoneza chikumbumtima chawo. Paulo analemba kuti: “Kwa anthu oipitsidwa ndi opanda chikhulupiriro kulibe choyera.” Chikumbumtima chawo chinasokonezeka kwambiri moti sichinalinso chodalirika pa zosankha ndi zoganiza zawo. Komanso iwo ankaweruza Akhristu anzawo pankhani zimene Mkhristu aliyense angasankhe yekha zochita ndipo mwina angasankhe zosiyana ndi Mkhristu mnzake. Apatu, zinthu zimene Akhristu a ku Kerete ankaona kuti n’zodetsedwa sizinali zodetsedwadi. (Aroma 14:17; Akolose 2:16) Ngakhale kuti iwo ankanena kuti amadziwa Mulungu, ntchito zawo zinali zoipa.​—Tito 1:16.

“Zoyera kwa Anthu Oyera”

6. Kodi Paulo anatchula magulu awiri ati a anthu?

6 Kodi ifeyo tingapindule motani ndi zinthu zimene Paulo anauza Tito? Taonani mmene mfundo iyi ikusiyanitsira magulu awiri a anthu: “Zinthu zonse n’zoyera kwa anthu oyera. Koma kwa anthu oipitsidwa ndi opanda chikhulupiriro kulibe choyera, m’malo mwake maganizo awo ndi chikumbumtima chawo n’zoipa.” (Tito 1:15) Paulo sankatanthauza kuti kwa Akhristu akhalidwe loyera, chilichonse n’choyera ndiponso chovomerezeka. Zimenezi n’zoona chifukwa chakuti m’kalata ina, Pauloyo anali atanena kuti munthu wadama, wopembedza mafano, wokhulupirira mizimu, ndiponso wamakhalidwe ena oipa “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (Agalatiya 5:19-21) Motero, tingaone kuti Paulo ankanena za magulu awiri a anthu. Gulu loyamba ndi la anthu oyera mwamakhalidwe ndiponso mwauzimu ndipo lachiwiri ndi la anthu odetsedwa.

7. Kodi lemba la Aheberi 13:4 limaletsa chiyani, nanga ndi funso lotani limene lingakhalepo?

7 Zinthu zimene Mkhristu woona ayenera kupewa sikuti ndi zokhazo zimene Baibulo limaletsa mwachindunji. Mwachitsanzo, taonani mfundo iyi: “Ukwati ukhale wolemekezeka pakati pa onse, ndi kama wa ukwati akhale wosaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweruza achiwerewere ndi achigololo.” (Aheberi 13:4) Ngakhale anthu amene si Akhristu ndiponso amene sadziwa n’komwe Baibulo anganene kuti vesi limeneli likuletsa chigololo. Malinga ndi vesili ndiponso mavesi ena a m’Baibulo, n’zoonekeratu kuti Mulungu safuna kuti munthu wapabanja agonane ndi wina amene sanakwatirane naye mwalamulo. Nanga bwanji ngati anthu awiri osakwatirana akugonana m’kamwa? Achinyamata ambiri amati palibe vuto lililonse kuchita zimenezi. Ndiyeno, kodi ndi bwino kuti Mkhristu aziganiza kuti kugonana m’kamwa n’koyenera?

8. Pankhani ya kugonana m’kamwa, kodi Akhristu amasiyana motani ndi anthu ambiri m’dzikoli?

8 Pa Aheberi 13:4 ndi 1 Akorinto 6:9 timauzidwa kuti Mulungu amadana ndi chigololo ndiponso dama (m’Chigiriki, por·neiʹa). Kodi dama n’chiyani? Mawu a Chigiriki omasuliridwa kuti dama amatanthauza kugwiritsa ntchito ziwalo zoberekera, mwachibadwa kapena m’njira yachilendo, ndi cholinga chokhutiritsa chilakolako  chogonana m’njira yolakwika. Amaphatikizapo zachiwerewere zamtundu uliwonse zochitika pakati pa anthu amene si okwatirana mogwirizana ndi Malemba. Motero dama limaphatikizapo kugonana m’kamwa, ngakhale kuti achinyamata ambiri padziko lonse akhala akuuzidwa kapena kuganiza kuti kuchita zimenezi sikolakwika. Akhristu oona satsatira maganizo a anthu “olankhula zopanda pake, ndi opotoza maganizo a ena.” (Tito 1:10) Iwo amatsatira mfundo zapamwamba kwambiri za m’Malemba Oyera. M’malo moganiza kuti kugonana m’kamwa n’koyenera, iwo amadziwa kuti malinga ndi Malemba kuchita zimenezi ndi dama, kapena kuti por·neiʹa, ndipo amaphunzitsa chikumbumtima chawo kudana ndi zimenezi. *​—Machitidwe 21:25; 1 Akorinto 6:18; Aefeso 5:3.

Zosankha Zimasiyana Malinga N’kusiyananso kwa Chikumbumtima

9. Ngati “zinthu zonse n’zoyera,” kodi chikumbumtima chili ndi ntchito yanji?

9 Koma kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti “zinthu zonse n’zoyera kwa anthu oyera”? Paulo ankanena za Akhristu amene maganizo ndi chikumbumtima chawo n’chogwirizana ndi mfundo za Mulungu, zimene timawerenga m’Mawu ake ouziridwa. Iwo amadziwa kuti pankhani zambiri zimene Mulungu saletsa mwachindunji, Akhristu angasankhe zinthu mosiyana. M’malo moweruza anzawo, iwo amaona kuti zinthu zimene Mulungu saletsa ndi “zoyera.” Iwo sayembekezera kuti pankhani zimene Baibulo sililetsa mwachindunji, anthu ena onse angaganize mofanana ndendende ndi mmene iwo amaganizira. Tiyeni tione zitsanzo za nkhani zoterezi.

10. Kodi mwambo wa ukwati (kapena maliro) ungabweretse mavuto otani?

10 Pali mabanja ambiri amene mwamuna kapena mkazi yekha ndiye Mkhristu. (1 Petulo 3:1; 4:3) Izi zingabweretse mavuto osiyanasiyana, mwachitsanzo pakakhala mwambo wa ukwati kapena maliro a wachibale. Taganizirani mmene zingakhalire ndi mlongo amene mwamuna wake si Mboni. Wachibale wa mwamuna wakeyo akukamangitsa ukwati kutchalitchi. (Kapena wachibale, mwinamwake kholo la mwamunayo, wamwalira, ndipo mwambo wake ukachitikira m’tchalitchi.) Iwo aitanidwa ku mwambowo, ndipo mwamunayo akufuna kuti mkazi wakeyo apite nawo. Kodi chikumbumtima cha mlongoyo chingamulole kuti apite? Kodi angachite chiyani pamenepa? Pali zinthu ziwiri zimene angachite.

11. Pankhani yopita ku mwambo wa ukwati kutchalitchi, kodi mlongo wina wokwatiwa angaganizire zotani, ndipo angasankhe kuchita chiyani?

11 Mlongo wina, dzina lake Loisi, akuganizira kwambiri lamulo la m’Baibulo lakuti: ‘Tulukani m’Babulo Wamkulu,’ yemwe ndi ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga. (Chivumbulutso 18:2, 4) Poyamba iye anali m’chipembedzo chomwecho ndipo akudziwa kuti anthu onse pamwambowo adzapemphedwa kuchita zinthu monga kupemphera, kuimba ndiponso kuchita zizindikiro zina zachipembedzo. Iye sakufuna m’pang’ono pomwe kuchita nawo zinthu zimenezi, ndipo wasankha kuti asapite n’cholinga choti akhalebe wokhulupirika kwa Mulungu. Loisi amalemekeza mwamuna wake chifukwa Malemba amati mwamunayo ndi mutu wa banja. Komabe sakufuna kuphwanya mfundo za m’Malemba. (Machitidwe 5:29) Ndiyeno akufotokozera mwamuna wakeyo mwanzeru kuti sapita ku tchalitchiko. Akumuuza kuti atati apite, koma n’kukakana kuchita nawo zinthu zina kumeneko zingakakhale zochititsa manyazi mwamuna wakeyo, choncho akuona kuti ndi bwino kuti asapite. Zimene wasankhazo zikumuchititsa kukhala ndi chikumbumtima choyera.

12. Kodi munthu wina ataitanidwa ku mwambo wa ukwati m’tchalitchi, angaganizire kaye mfundo ziti ndipo angachite zotani?

12 Rute nayenso wakumana ndi vuto lofanana  ndi la Loisi. Iye amalemekeza mwamuna wake, amafunitsitsa kukhala wokhulupirika kwa Mulungu, ndiponso amalabadira zimene chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo chimamuuza. Ataganizira mfundo ngati zimene Loisi anaganizira, Rute akuganizira mwapemphero mfundo za m’nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2002. Iye akukumbukira kuti Aheberi atatu aja anamvera lamulo lakuti akakhale nawo pamalo amene anthu akalambire fano, koma anakhalabe okhulupirika chifukwa sanalole kulambira nawo fanolo. (Danieli 3:15-18) Choncho, iye wasankha zoti apite limodzi ndi mwamuna wakeyo koma sakachita nawo chilichonse chokhudza kulambira, ndipo pochita zimenezi iye akutsatira chikumbumtima chake. Rute akufotokozera mwamuna wakeyo mwanzeru zinthu zimene chikumbumtima chake chingamulole kuchita ndiponso zimene sichingamulole. Iye akukhulupirira kuti mwamunayo aona kusiyana kwa chipembedzo choona ndi chipembedzo chonyenga.​—Machitidwe 24:16.

13. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa Akhristu awiri akasankha zinthu mosiyana?

13 Popeza kuti Akhristu awiri angasankhe zinthu mosiyana, kodi zimenezi zikutanthauza kuti zosankha zilizonse zilibe vuto kapena kuti mmodzi wa iwo ali ndi chikumbumtima chofooka? Ayi, si choncho. Poganizira kuti kale ankamvera nyimbo ndiponso ankachita nawo miyambo yosiyanasiyana ya tchalitchicho, Loisi angaone kuti si bwino kukapezeka pa mwambowo. N’kutheka kuti zimene iye ndi mwamuna wake ankachita pankhani za chipembedzo zakhudza chikumbumtima chake. Motero iye akukhulupirira kuti wasankha bwino kwambiri.

14. Kodi Akhristu ayenera kukumbukira chiyani pankhani ya zosankha za munthu payekha?

14 Koma kodi tinganene kuti Rute wasankha molakwika? Sitingatero ayi. Palibe munthu amene ayenera kumuweruza kapena kum’dzudzula chifukwa choti wasankha zoti akakhale nawo pamwambowo koma osakachitapo chilichonse chokhudza kupembedza. Tisaiwale malangizo amene Paulo anapereka okhudza zosankha za munthu payekha pankhani ya zakudya. Iye anati: “Amene amadya, asanyoze amene sadya, ndipo wosadyayo asaweruze amene amadya . . . Iye adzaimirira kapena kugwa pamaso pa mbuyake. Komatu, adzaimirira, chifukwa Yehova atha kumuimiritsa.” (Aroma 14:3, 4) Choncho, n’zoonekeratu kuti Mkhristu woona sangalimbikitse munthu wina aliyense kuti anyalanyaze zimene chikumbumtima chake chikumuuza. Chifukwa zimenezo zingachititse kunyalanyaza uthenga womwe ungapulumutse moyo.

15. N’chifukwa chiyani m’pofunika kuganizira kwambiri chikumbumtima ndiponso maganizo a anthu ena?

15 Pankhani yomwe ija, alongo awiri aja ayenera kuganiziranso zinthu zina. Mwa zina, ayenera kuganizira mmene zochita zawo zingakhudzire anthu ena. Paulo anatilangiza kuti: “Khalani otsimikiza mtima kusaikira m’bale chokhumudwitsa kapena chopunthwitsa.” (Aroma 14:13) N’kutheka kuti Loisi akudziwa kuti zochitika ngati zimenezi zinayambitsapo mavuto aakulu mumpingo  kapena m’banja mwake, ndiponso kuti zimene angachite zingakhudze kwambiri ana ake. Mosiyana ndi Loisi, n’kutheka kuti Rute akudziwa kuti zinthu ngati zimenezi sizinakhumudwitsepo ena mumpingo kapena m’dera limene iye akukhala. Alongo awiriwa, kuphatikizaponso tonsefe, tiyenera kudziwa kuti chikumbumtima chophunzitsidwa bwino chimaganizira mmene zosankha zathu zingakhudzire ena. Yesu anati: “Aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa aang’ono awa amene amakhulupirira mwa ine, zingam’khalire bwino kwambiri kum’mangirira chimwala cha mphero m’khosi mwake, ngati chimene bulu amayendetsa, ndi kum’miza m’nyanja yaikulu.” (Mateyo 18:6) Ngati munthu anyalanyaza mfundo ya kusakhumudwitsa ena, chikumbumtima chake chingayambe kuipitsidwa, ngati mmene zinalili ndi Akhristu ena a ku Kerete.

16. Kodi tingayembekezere kuti Mkhristu asintha chiyani m’kupita kwanthawi?

16 Popeza kuti Mkhristu ayenera kupitirizabe kukula mwauzimu, ayeneranso kutero pankhani yomvera ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chake. Tiyerekeze kuti Maliko ndi Mkhristu wongobatizidwa kumene. Chikumbumtima chake chikumuuza kuti asamachite nawo zinthu zina zotsutsana ndi Malemba zimene ankachita nawo kalekale, mwina zokhudza mafano kapena magazi. (Machitidwe 21:25) Ndipo panopa akuyesetsa kwambiri kupewa zinthu zimene zingaoneke zofananako ndi zimene Mulungu amaletsa. Koma, iye samvetsa chifukwa chimene anthu ena amakanira zinthu zimene iye amaona kuti zilibe vuto, monga mapulogalamu ena a pa TV.

17. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti chikumbumtima cha Mkhristu chingasinthe m’kupita kwanthawi komanso chifukwa cha kukula mwauzimu.

17 M’kupita kwanthawi, Maliko akudziwa zinthu zambiri komanso akuyandikira kwambiri kwa Mulungu. (Akolose 1:9, 10) Izi zikuchititsa kuti chikumbumtima chake chiphunzitsidwe bwino. Tsopano Maliko akutha kumvera chikumbumtima chake komanso kuganizira mosamala mfundo za m’Malemba. Ndipo wazindikira kuti zina mwa zinthu zimene ankaona kuti ndi zolakwika si zotsutsana kwenikweni ndi maganizo a Mulungu. Kuwonjezera pamenepo, popeza kuti Maliko amatsatira mfundo za m’Baibulo ndiponso amafunitsitsa kuchita zimene chikumbumtima chake chophunzitsidwa bwino chamuuza, iye saoneranso mapulogalamu a pa TV amene kale ankawaona kuti alibe vuto. Zoonadi, tsopano ali ndi chikumbumtima chophunzitsidwa bwino.​—Salmo 37:31.

18. Kodi tili ndi mwayi wamtengo wapatali uti?

18 M’mipingo yambiri muli anthu osiyanasiyana. Ena angoyamba kumene choonadi ndipo n’kutheka kuti chikumbumtima chawo sichiwatsutsa pa zinthu zina, koma chimawatsutsa kwambiri pa zina. Anthu oterowo angafunike kuthandizidwa ndipo m’kupita kwanthawi angayambe kutsatira malangizo a Yehova ndiponso kuchita zimene chikumbumtima chawo chimawauza. (Aefeso 4:14, 15) N’zosangalatsa kuti m’mipingoyi mulinso anthu odziwa zinthu zambiri, odziwa bwino kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, ndiponso achikumbumtima chogwirizana kwambiri ndi maganizo a Mulungu. Ndi mwayi wamtengo wapatali kukhala ndi “anthu oyera.” Anthu amenewa amaona zinthu zolandirika pamaso pa Ambuye kuti ‘n’zoyera’ mwamakhalidwe ndiponso mwauzimu. (Aefeso 5:10) Tiyeni tonse tikhale ndi cholinga cha kukula mwauzimu, n’kukhala ndi chikumbumtima chogwirizana ndi mfundo zolondola za choonadi ndiponso chogwirizana ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu.​—Tito 1:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Nsanja ya Olonda ya September 1, 1983, pamasamba 31 ndi 32, ili ndi mfundo zimene mwamuna ndi mkazi wake ayenera kuziganizira. Mwa zina, magaziniyi inati: “Adzachita bwino kukulitsa chidani pa chinthu chirichonse chimene chiri chodetsedwa pamaso pa Yehova, kuphatikizapo mikhalidwe imene mwachiwonekere iri yoluluza ya kugonana. Awiri okwatirana ayenera kuchita mwa njira imene idzawasiya ali ndi chikumbu mtima choyera . . . akumakumbukira makamaka kuti kugonana kuyenera kukhala kolemekezeka, kosaluluzika, chisonyezero cha chikondi chokoma mtima. Zimenezi zowonadi siziyenera kuphatikiza chirichonse chimene chikanyansa kapena kubvulaza mnzake wa mu ukwati wa munthuyo.​—Aefeso 5:28-30; 1 Petro 3:7.”

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani Akhristu ena a ku Kerete anali ndi chikumbumtima choipitsidwa?

• N’chifukwa chiyani Akhristu awiri achikumbumtima chophunzitsidwa bwino angasankhe kuchita zinthu mosiyana?

• Kodi chikumbumtima chathu chiyenera kusintha motani m’kupita kwanthawi?

[Mafunso]

[Mapu patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Sisile

GIRISI

Kerete

ASIA MINOR

Kupuro

NYANJA YA MEDITERRANEAN

[Chithunzi patsamba 28]

Pazochitika zofanana, Akhristu awiri angasankhe kuchita zinthu mosiyana