Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tikukondwera Chifukwa ‘Anapambana Limodzi ndi Mwanawankhosa’

Tikukondwera Chifukwa ‘Anapambana Limodzi ndi Mwanawankhosa’

 Tikukondwera Chifukwa ‘Anapambana Limodzi ndi Mwanawankhosa’

M’CHAKA cha 1971, Carey W. Barber analemba kalata yofotokoza zimene anachita m’zaka 50 akutumikira Mulungu woona. Iye anati: “Zaka zimene ndakhala ndikutumikira Yehova zinali zosangalatsa kwambiri. Ndakhala ndikucheza ndi anthu a Mulungu, ndipo ndatetezedwa kwa anthu oipa m’dziko la Satanali. Ndakhalanso ndikuyembekeza kupambana limodzi ndi Mwanawankhosa, Yesu Khristu, ndiponso ndaona kuti Yehova ndi wachikondi. Zonsezi, zandithandiza kukhala pa mtendere komanso kukhala wokhutira, ndipo izi zateteza mtima wanga ndiponso zandipatsa chiyembekezo chodalirika cha kupambana komaliza.”

Patapita zaka 6 kuchokera pamene analemba kalatayi, M’bale Barber, yemwe anali Mkhristu wodzozedwa ndi mzimu, anayamba kutumikira m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Atatumikira zaka 30 paudindowu, iye anali akuyembekezerabe “kupambana limodzi ndi Mwanawankhosa.” Ndipo anakwanitsadi kuchita zimenezi mwa kukhala wokhulupirika mpaka imfa. Iye anamwalira Lamlungu, pa April 8, 2007, ali ndi zaka 101.​—1 Akorinto 15:57.

Carey Barber anabadwira ku England mu 1905 ndipo anabatizidwa mu 1921, ku Winnipeg, m’dziko la Canada. Patatha zaka ziwiri atabatizidwa, iye pamodzi ndi mchimwene wake Norman, anasamukira ku Brooklyn, mu mzinda wa New York, kukathandiza pa ntchito ina yomwe inali itangoyamba kumene. Panthawiyi n’kuti anthu a Yehova atatsala pang’ono kuyamba kusindikiza mabuku awo ogwiritsa ntchito polalikira uthenga wabwino wa Ufumu “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyo 24:14) Imodzi mwa ntchito zoyambirira zimene M’bale Barber anapatsidwa inali yosindikiza mabuku pogwiritsa ntchito makina aang’ono. Zina mwa zinthu zimene ankasindikiza zinali zikalata za mfundo za milandu yopita ku Khoti Lapamwamba la ku United States. Kenako M’bale Barber anakatumikira m’Dipatimenti ya Utumiki, yomwe imayang’anira nkhani zokhudza mipingo komanso ntchito yolalikira m’dziko lonse la United States.

Zonsezi zinathandiza kuti M’bale Barber atumikire bwino kwambiri pamene anakhala mtumiki woyendayenda mu 1948, ndipo ankayendera misonkhano ndi mipingo yonse ya kumadzulo kwa dziko la United States. Iye ananena kuti ankasangalala akamayendayenda polalikira. Utumiki umenewu unachititsa kuti M’bale Barber adziwane ndi abale komanso alongo ambiri. Iye ankaganiza mwamsanga ndipo anali wachangu muutumiki. Zimenezi zinamuthandiza kwambiri pamene analowa kalasi la 26 la Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo. Kusukuluko anakumana ndi wophunzira wina wochokera ku Canada, dzina lake Sydney Lee Brewer. Atangomaliza sukuluyo anakwatirana, ndipo pambuyo pa mwambo wa ukwati wawo anapita kukatumikira ku mipingo ya ku mzinda wa Chicago, ku Illinois. Mlongo Barber anathandiza ndi kulimbikitsa kwambiri mwamuna wake, pazaka 20 zimene anachita utumiki woyendayenda.

Anthu amene anadziwana ndi M’bale Barber, pamene ankatumikira monga woyang’anira chigawo kapena woyang’anira dera, kapenanso m’zaka 30 zimene anakhala akutumikira ndi kuyendayenda monga wa m’Bungwe Lolamulira, sadzaiwala nkhani ndiponso ndemanga zake zolimbikitsa. Tiyeneradi kukondwera chifukwa iye ‘wapambana limodzi ndi Mwanawankhosa.’