Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupulumutsidwa ku Misampha ya Wosaka Mbalame

Kupulumutsidwa ku Misampha ya Wosaka Mbalame

 Kupulumutsidwa ku Misampha ya Wosaka Mbalame

“[Yehova] adzakuwonjola ku msampha wa msodzi [“wosaka mbalame,” NW].”​—SALMO 91:3.

1. Kodi “wosaka mbalame” ndani, ndipo n’chifukwa chiyani ali woopsa kwambiri?

AKHRISTU onse amalimbana ndi mdani wanzeru ndiponso wochenjera kwambiri kuposa anthu. Palemba la Salmo 91:3, mdaniyu akutchedwa “wosaka mbalame.” Kodi mdani ameneyu ndani? Kuyambira mu Nsanja ya Olonda, ya June 1, 1883, mdani ameneyu wakhala akudziwika kuti ndi Satana Mdyerekezi. Mdani wamphamvu ameneyu amayesetsa mochenjera kwambiri kusocheretsa ndi kukola anthu a Yehova monga mmene wosaka mbalame amachitira.

2. N’chifukwa chiyani Satana amayerekezedwa ndi wosaka mbalame?

2 Kalekale, anthu ankagwira mbalame chifukwa cha nyimbo zake zokoma, kukongola kwake, pofuna kukapereka nsembe, komanso monga chakudya. Komabe, mbalame n’zochenjera kwambiri ndipo zimavuta kukola. Motero, wosaka mbalame wa m’nthawi zotchulidwa m’Baibulo ankafunika kuyamba waphunzira bwino kwambiri makhalidwe ndiponso zochita za mbalame zimene akufuna kutchera. Akatero, ankapeza njira zabwino kwambiri zokolera mbalamezo. Poyerekezera Satana ndi wosaka mbalame, Baibulo limatithandiza kumvetsa njira zimene iye amagwiritsa ntchito. Mdyerekezi amaphunzira munthu aliyense payekhapayekha. Iye amaona zochita ndiponso makhalidwe athu ndipo akatero amatchera misampha yobisika pofuna kutikola amoyo. (2 Timoteyo 2:26) Kukodwa ndi Satana kungawonongetse ubwenzi wathu ndi Mulungu ndipo pamapeto pake tingadzawonongedwe kotheratu. Motero, kuti tikhale otetezeka, ndi bwino kudziwa njira zosiyanasiyana zimene ‘wosaka mbalameyu’ amagwiritsa ntchito.

3, 4. Kodi Satana amatiukira monga mkango kapena mphiri motani?

3 Wamasalmo anayerekezera bwino kwambiri njira zimene Satana amagwiritsa ntchito ndi zochita za mkango kapena mphiri. (Salmo 91:13) Mofanana ndi mkango, Satana amaukira anthu a Yehova mwachindunji pogwiritsa ntchito chizunzo kapena malamulo a maboma. (Salmo 94:20) Ndipo anthu ena angasiye Yehova chifukwa cha kuukiridwa kotereku. Komabe, nthawi zambiri kuukira mwachindunji kumeneku kumagwirizanitsa anthu a Mulungu m’malo mowachititsa kuti asiye Yehova. Nangano, kodi Satana amatiukira mochenjera ngati mphiri m’njira ziti?

4 Mdyerekezi amagwiritsa ntchito nzeru zake zoposa za anthu, poukira anthu a Mulungu mochenjera ndiponso mochititsa mantha kwambiri, mofanana ndi njoka yaululu woipa kwambiri imene yabisala. Mwanjira imeneyi, iye wasokoneza maganizo a anthu a Mulungu, n’kuwasocheretsa mpaka kuyamba kuchita zofuna zake m’malo mochita chifuniro cha Yehova, ndipo zotsatirapo zake zimakhala zoopsa kwambiri. Koma n’zosangalatsa kuti timadziwa machenjera a Satana. (2 Akorinto 2:11) Tsopano, tiyeni tione misampha inayi yoopsa kwambiri imene ‘wosaka mbalameyu’ amagwiritsa ntchito.

Kuopa Anthu

5. N’chifukwa chiyani msampha wa “kuopa anthu” ndi woopsa kwambiri?

5 ‘Wosaka mbalameyu’ amadziwa kuti mwachibadwa anthufe timafuna kuti ena azitikonda. Akhristu sanyalanyaza maganizo a anthu ena, ndiponso mmene anthuwo angawaonere, ndipo Mdyerekezi amapezerapo mwayi pa zimenezo. Mwachitsanzo, iye amakola ena mwa anthu a Mulungu pogwiritsa ntchito msampha wa “kuopa anthu.” (Miyambo 29:25) Ngati chifukwa choopa anthu, atumiki a Mulungu amagwirizana ndi anthu ena pochita zinthu zimene Yehova amaletsa  kapena sakuchita zimene Mawu a Mulungu amawauza kuti achite, ndiye kuti iwo akodwa mu msampha wa “wosaka mbalame.”​—Ezekieli 33:8; Yakobe 4:17.

6. Kodi ndi chitsanzo chotani chimene chikusonyeza mmene wachinyamata angakodwere mu msampha wa “wosaka mbalame”?

6 Mwachitsanzo, wachinyamata wina angayambe kusuta fodya chifukwa choonera anzake amene akuphunzira nawo sukulu. N’kutheka kuti popita ku sukulu tsiku limenelo iye samaganiza n’komwe zosuta fodya. Koma, pasanathe nthawi, mnyamatayu akuchita zinthu zimene angadwale nazo ndiponso zosakondweretsa Mulungu. (2 Akorinto 7:1) Kodi n’chiyani chamuchititsa zimenezi? N’kutheka kuti wakopeka ndi anzake a maganizo oipa ndipo waopa kuwakhumudwitsa. Tikukupemphani achinyamatanu kuti musalole ‘wosaka mbalameyu’ kukunyengererani ndi kukukolani. Kuti musagwidwe amoyo, chenjerani ndi zinthu ngakhale zing’onozing’ono. Tsatirani chenjezo la m’Baibulo lopewa mayanjano oipa.​—1 Akorinto 15:33.

7. Kodi Satana angachititse bwanji makolo kusokonezeka mwauzimu?

7 Makolo achikhristu amayesetsa kukwaniritsa udindo wawo wa m’Malemba wosamalira mwakuthupi mabanja awo. (1 Timoteyo 5:8) Koma Satana amafuna kuti asokoneze maganizo a Akhristu pankhani imeneyi. N’kutheka kuti Akhristu ena amaphonya misonkhano kawirikawiri chifukwa chomvera mabwana awo akawapempha kugwira ovataimu. Mwina angachite mantha kupempha tchuthi kuti adzakhale nawo pazigawo zonse za msonkhano wachigawo ndi kulambira Yehova pamodzi ndi abale awo. ‘Kukhulupirira Yehova’ n’kumene kungathandize kwambiri kupewa msampha umenewu. (Miyambo 3:5, 6) Komanso, kukumbukira kuti tonsefe ndife a m’nyumba ya Yehova ndiponso kuti iye amatisamalira kungatithandize kuti tisasokonezeke maganizo pankhaniyi. Makolo, kodi mumakhulupirira kuti Yehova angakuthandizeni mwanjira inayake pamodzi ndi banja lanu mukamachita chifuniro chake? Kapena kodi Mdyerekezi adzakugwirani amoyo n’kuyamba kukugwiritsani ntchito pazofuna zake chifukwa choopa anthu? Tikukupemphani kuti muganizire mafunso amenewa mwapemphero.

Msampha Wokonda Chuma

8. Kodi Satana amagwiritsa ntchito msampha wokonda chuma m’njira iti?

8 Njira ina imene Satana amagwiritsanso ntchito kuti atikole ndiyo kukonda chuma. Dongosolo la zamalonda m’dzikoli, limalimbikitsa anthu kutsatira njira zachinyengo kuti alemere mwamsanga. Izi zingachitikirenso anthu a Mulungu. Nthawi zina munthu angauzidwe kuti: “Ingolimbikirani kugwira ntchito ndipo mukadzapeza chuma chambiri, mukhoza kuyamba kusangalala ndi moyo ngakhale kuyambanso upainiya.” Mawu otere angachokere kwa abale kapena alongo osaganiza bwino amene amapezerapo mwayi pachuma chimene anzawo mumpingo ali nacho. Ndi bwino kuganizira bwino pankhani imeneyi. Kodi sizingafanane ndi maganizo a munthu wachuma “wopanda nzeru” wa m’fanizo la Yesu?​—Luka 12:16-21.

9. Kodi n’chiyani chimene chachititsa Akhristu ena kukodwa ndi chilakolako chofuna katundu?

9 Satana akulamulira dongosolo loipali m’njira yoti anthu azilakalaka zinthu. Kenako, chilakolako  chimenechi chingalowe m’moyo wa Mkhristu n’kupinimbiritsa mawu, ndipo “sabala zipatso.” (Maliko 4:19) Baibulo limatilimbikitsa kukhala wokhutira ndi chakudya ndiponso zovala. (1 Timoteyo 6:8) Koma anthu ambiri amakoledwa ndi “wosaka mbalame” chifukwa chakuti satsatira malangizo amenewa. Kodi kungakhale kudzikuza kumene kumawachititsa kuti azifuna kukhala ndi moyo wapamwamba? Nanga bwanji ifeyo? Kodi kulakalaka kukhala ndi katundu kumachititsa kuti tiziona kulambira kwathu kukhala kosafunika kwenikweni? (Hagai 1:2-8) N’zomvetsa chisoni kuti m’nthawi za mavuto a zachuma, ena asokoneza moyo wawo wauzimu n’cholinga chopitiriza kukhala ndi moyo umene anauzolowera. “Wosaka mbalame” amasangalala ndi mtima wokonda chuma umenewu.

Msampha Wosangalala ndi Zinthu Zoipa

10. Kodi Mkhristu aliyense ayenera kudzifufuza pankhani iti?

10 Kusokoneza maganizo achibadwa a anthu pankhani ya kusiyanitsa chabwino ndi choipa ndi njira ina imene ‘wosaka mbalameyu’ amagwiritsa ntchito. Masiku ano, mafilimu ambiri amasonyeza maganizo amene anthu a ku Sodomu ndi Gomora anali nawo. Nazonso nkhani za pa TV ndi m’magazini, zimalimbikitsa ziwawa ndiponso chilakolako cha kugonana. Zinthu zimene anthu amasangalala nazo m’nyuzipepala ndiponso pawailesi zimawalepheretsa “kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.” (Aheberi 5:14) Komabe, kumbukirani zimene Yehova analankhula kudzera mwa mneneri Yesaya, kuti: “Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa.” (Yesaya 5:20) Kodi “wosaka mbalame” waipitsa maganizo anu ndi zinthu zoipa zoterezi? Ndi bwino kudzifufuza pankhaniyi.​—2 Akorinto 13:5.

11. Kodi ndi chenjezo lotani limene magazini ya Nsanja ya Olonda inapereka pankhani ya masewero omwe amaonetsa pa TV?

11 Pafupifupi zaka 25 zapitazo, magazini a Nsanja ya Olonda anachenjeza atumiki oona a Mulungu pankhani ya masewero omwe amaonetsa pa TV. * Magaziniwa anafotokoza za kuopsa kwa masewero otchuka kwambiri a pa TV, kuti: “Anthu amaona kuti sikulakwa kuchita chilichonse chifukwa chofunafuna chikondi. Mwachitsanzo, m’sewero lina, mtsikana wina yemwe anali woyembekezera koma asanakwatiwe, anauza mnzake kuti: ‘Victor ndimam’konda. Ndipo sindikudandaula. . . . Ndikufunitsitsa kwambiri n’takhala ndi mwana wake.’ Nyimbo zimene zimamveka chapansipansi sewerolo lili m’kati, zingachititse munthu kuganiza kuti zochita za mtsikanayu n’zabwino. Munthu woonera seweroli angakopekenso ndi Victor. Angayambe kumvera chisoni mtsikanayo ndiponso kugwirizana ndi khalidwe lake loipalo. Mayi wina amene anaonera seweroli koma kenako anazindikira kuipa kwake anati: ‘N’zodabwitsa kuti munthu umayamba kudzikhululukira. N’zoona, timadziwa kuti chiwerewere n’choipa. . . . Koma ndinazindikira kuti m’maganizomu ndinkagwirizana ndi anthu achiwerewere.’”

12. N’chiyani chikusonyeza kuti chenjezo lokhudza mapulogalamu ena a pa TV n’loyenera masiku ano?

 12 Kuchokera nthawi yomwe nkhani zimenezi zinasindikizidwa, mapulogalamu oipa oterewa awonjezeka kwambiri. M’madera ambiri, mapologalamu oterewa amaulutsidwa masana ndiponso usiku wonse. Abambo ndi amayi komanso achinyamata ambiri amaipitsa maganizo ndi mitima yawo ndi zinthu zimenezi. Koma ife sitiyenera kudzinyenga ndi maganizo olakwika. N’kulakwa kuganiza kuti zinthu monga mapulogalamu a pa TV si zoopsa kwenikweni kusiyana ndi zochitika zenizeni. Mkhristu sangayerekeze m’pang’ono pomwe kusangalatsidwa ndi anthu amene sangawaitane n’komwe kunyumba kwake.

13, 14. Kodi anthu ena anafotokoza motani phindu limene anapeza chifukwa cha chenjezo lokhudza mapulogalamu a pa TV?

13 Anthu ambiri anapindula chifukwa chotsatira chenjezo limene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anapereka panthawiyo. (Mateyo 24:45-47) Anthu ena atawerenga malangizo achindunji a m’Baibulo amenewa analemba makalata onena mmene nkhanizo zinawathandizira. * Mayi wina analemba kuti: “Ndakhala ndikuonera masewero a pa TV zaka 13, ndipo ndinkawakonda kwambiri. Ndinkaona kuti sangandisokoneze mwauzimu malinga ngati ndikupita ku misonkhano yachikhristu ndiponso kuchita utumiki wa kumunda mwa apo ndi apo. Koma ndinayamba kutengera maganizo a m’masewero a pa TV akuti ngati mwamuna wako akukuzunza kapena ngati ukuona kuti sakukukonda, si polakwika kuchita chigololo, vuto ndi lake. Motero, nditaona kuti pali chifukwa chokwanira, ndinachita chigololo, ndipo ndinachimwira Yehova ndiponso mwamuna wanga.” Mayiyu anachotsedwa mu mpingo. M’kupita kwa nthawi, iye anavomereza tchimo lake, n’kulapa, ndipo anabwezeretsedwa. Chenjezo lokhudza masewero omwe amaonetsa pa TV limene nkhanizo zinapereka, linathandiza mayiyu kupeza mphamvu zokana kuonera zinthu zimene Yehova amadana nazo.​—Amosi 5:14, 15.

14 Munthu wina amene anakhudzidwa mtima kwambiri atawerenga nkhanizi anati: “Ndinalira nditatha kuwerenga, chifukwa ndinazindikira kuti sindinkatumikira Yehova ndi mtima wonse. Ndinalonjeza Mulungu kuti sindidzakhalanso kapolo wa masewero amenewa.” Mlongo wina wachikhristu atafotokoza mawu ake oyamikira nkhanizi, ananenanso kuti ankakonda kwambiri kuonerera masewero ndipo analemba kuti: “Sindinkadziwa . . . kuti zingakhudze ubwenzi wanga ndi Yehova. Zinali zosatheka kukhala paubwenzi ndi ochita masewerowa komanso n’kukhala bwenzi la Yehova.” Ngati masewero a pa TV amenewa anawononga maganizo a anthu zaka 25 zapitazo, nanga bwanji masiku ano? (2 Timoteyo 3:13) Tiyenera kukhala maso ndi msampha wa Satana wosangalala ndi zinthu zoipa, kaya kudzera m’masewero a pa TV, masewera a pakompyuta, kapena mavidiyo a nyimbo zoipa.

Msampha wa Kusemphana Maganizo

15. Kodi ena akodwa motani amoyo ndi Mdyerekezi?

15 Satana amagwiritsa ntchito kusemphana maganizo ngati msampha kuti anthu a Yehova akhale osagwirizana. Tingathe kukodwa mu  msampha umenewu mosasamala kanthu za utumiki womwe tikuchita. Ena akodwa amoyo ndi Mdyerekezi chifukwa cholola kuti kusemphana maganizo kusokoneze mtendere ndi umodzi ndiponso kupita patsogolo kwa gulu la Mulungu kumene Yehova wachititsa.​—Salmo 133:1-3.

16. Kodi Satana wakhala akuyesetsa motani kuti asokoneze umodzi wathu?

16 Pankhondo yoyamba ya padziko lonse, Satana anayesa kufafaniza mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova mwa kuliukira mwachindunji, koma analephera. (Chivumbulutso 11:7-13) Kuyambira nthawi imeneyo, iye wakhala akuyesetsa mochenjera kwambiri kuti asokoneze umodzi wathu. Tikalola kuti kusemphana maganizo kutigawanitse, ndiye kuti tapereka mpata kwa “wosaka mbalame.” Tikatero, tingachititse kuti mzimu woyera usamagwire bwino ntchito m’moyo wathu komanso mumpingo. Satana angasangalale kwambiri ngati zimenezi zitachitika, chifukwa chakuti kusokonezeka kwa mtendere ndi umodzi wa mpingo kungasokonezenso ntchito yolalikira.​—Aefeso 4:27, 30-32.

17. Kodi n’chiyani chingathandize anthu amene asemphana maganizo kuthetsa mavuto awo?

17 Kodi mungachite chiyani ngati mwasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzanu? N’zoona kuti palibe vuto lofanana ndi linzake. Komabe, ngakhale kuti pangakhale zifukwa zambiri zoyambitsa mavuto, palibe chifukwa chilichonse chosathetsera mavutowo. (Mateyo 5:23, 24; 18:15-17) Malangizo a m’Mawu a Mulungu ndi ouziridwa, ndiponso angwiro. Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo n’kothandiza kwambiri.

18. Kodi kutsanzira Yehova kungatithandize bwanji kuthetsa kusemphana maganizo?

18 Yehova “ndi wokhululukira.” (Salmo 86:5; 130:4) Tikamatsanzira Yehova, timasonyeza kuti ndife ana ake okondedwa. (Aefeso 5:1) Tonse ndife ochimwa ndipo timafuna kuti Yehova azitikhululukira. Choncho, tiyenera kusamala ngati tili ndi mtima wosakhululukira ena. Apo ayi, tingakhale ngati kapolo amene Yesu anam’tchula m’fanizo lake. Kapoloyu sanafune kukhululukira mnzake amene anabwereka kwa iye ndalama zochepa poyerekezera ndi zimene iyeyo anabwereka kwa mbuye wake. Atadziwa zimenezo, mbuyeyo anapereka kapolo wopanda chifundoyo kundende. Yesu anamaliza fanizo lakelo ndi mawu akuti: “Momwemonso Atate wanga wa kumwamba adzathana ndi inu ngati simukhululukira aliyense m’bale wake ndi mtima wonse.” (Mateyo 18:21-35) Kusinkhasinkha za fanizo limeneli ndi kuganizira zinthu zimene Yehova amatikhululukira kungathandize pamene tikufuna kuthetsa kusemphana maganizo ndi m’bale wathu.​—Salmo 19:14.

Khalani Otetezeka “M’ngaka Yake ya Wam’mwambamwamba”

19, 20. Kodi tiyenera kuona motani ‘ngaka’ ndi “mthunzi” wa Yehova m’masiku oopsa ano?

19 Panopa tikukhala m’masiku oopsa. Akanakhala kuti Yehova sakutiteteza mwachikondi, Satana akanatiwononga tonsefe. Choncho, kuti tisagwidwe ndi “wosaka mbalame” tiyenera kukhalabe m’malo ophiphiritsa achitetezo, “m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba” ndi kugona “mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.”​—Salmo 91:1.

20 Tiyenera kuona kuti malangizo ndi zikumbutso za Yehova zimatiteteza osati kutipanikiza. Tonsefe tikulimbana ndi mdani yemwe ali ndi nzeru zoposa za anthu. Popanda thandizo lachikondi la Yehova palibe aliyense amene angapewe kukodwa. (Salmo 124:7, 8) Choncho, tiyeni tizipemphera kuti Yehova atipulumutse ku misampha ya “wosaka mbalame”!​—Mateyo 6:13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya December 1, 1982, masamba 3 mpaka 7.

^ ndime 13 Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya December 1, 1983, tsamba 23.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani msampha wa “kuopa anthu” ndi woopsa kwambiri?

• Kodi Mdyerekezi amagwiritsa ntchito motani msampha wokonda chuma?

• Kodi Satana wakola bwanji anthu ena mumsampha wosangalala ndi zinthu zoipa?

• Kodi Mdyerekezi amagwiritsa ntchito msampha uti pofuna kusokoneza umodzi wathu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 27]

Ena akodwa mu msampha wa “kuopa anthu”

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi mumasangalala ndi zinthu zimene Yehova amadana nazo?

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi mungatani ngati mwasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzanu?