Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?

N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?

N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?

BAIBULO limati: “Yehova [Mulungu] ali wolungama m’njira zake zonse.” (Salmo 145:17; Chivumbulutso 15:3) Mose analemba kuti, Mulungu “ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Lemba la Yakobe 5:11 limati: “Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” Mulungu sachititsa zoipa ndipo sangatero n’komwe.

Wophunzira Yakobe analembanso kuti: “Pokhala pa mayesero, munthu asanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobe 1:13) Yehova Mulungu sayesa anthu ndi zoipa kapena kuwachititsa kuchita zinthu zoipa. Nanga ndani amachititsa zinthu zoipa ndiponso kuti anthu azivutika?

Ndani Amachititsa Zoipa?

Wolemba Baibulo, Yakobe, anasonyeza kuti anthu ndi amene amachititsa mwa zinthu zoipa zina. Analemba kuti: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako cha iye mwini. Ndiye chilakolako chikatenga pathupi, chimabala tchimo; nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.” (Yakobe 1:14, 15) Nthawi zina anthu amachita zinthu zoipa chifukwa cha zilakolako zawo. Ndiponso anthu amabadwa ndi uchimo umene umakulitsa zilakolakozo n’kuwapangitsa kuchita zinthu zoipa kwambiri. (Aroma 7:21-23) N’zoona, uchimo wobadwa nawo wakhala ukulamulira anthu “monga mfumu,” n’kuwachititsa kukhala akapolo a zoipa zimene zimabweretsa mavuto aakulu. (Aroma 5:21) Komanso, anthu oipa angakope ena kuti azichita zoipa.​—Miyambo 1:10-16.

Koma wochititsa zoipa wamkulu ndi Satana Mdyerekezi. Iye ndiye anabweretsa zoipa padziko lapansi. Yesu Khristu anamutchula kuti “woipayo” ndiponso “wolamulira wa dziko,” kapena kuti wa anthu oipa. Pafupifupi anthu onse akumvera Satana ndipo akutsatira zofuna zake zoti anthu anyalanyaze njira zabwino za Yehova Mulungu. (Mateyo 6:13; Yohane 14:30; 1 Yohane 2:15-17) Lemba la 1 Yohane 5:19 limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Ndipotu Satana ndi angelo ake “akusocheretsa dziko lonse lapansi,” n’kubweretsa “tsoka” lokhalokha. (Chivumbulutso 12:9, 12) Choncho, tiyenera kuloza chala Satana Mdyerekezi kuti ndiye makamaka akuchititsa zoipa.

Lemba la Mlaliki 9:11 limavumbula chinthu china chimene chikuchititsa zoipa, ponena kuti: “Yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.” Yesu Khristu ananena za tsoka limene linachitikira anthu 18, omwe anafa nsanja itawagwera. (Luka 13:4) Anthuwa anakumana ndi tsoka limeneli chifukwa chakuti anali pa malo olakwika, panthawinso yolakwika. Zinthu zofanana ndi zimenezi zimachitikanso masiku ano. Mwachitsanzo, njerwa ingagwe kuchoka pamwamba pa nyumba n’kugwera munthu pansi. Kodi tingati Mulungu ndiye wachititsa zimenezi? Ayi. Zinangochitika basi. Tinganenenso chimodzimodzi panyumba pakagwa matenda ndi imfa n’kusiya mkazi ndi ana amasiye.

Choncho, n’zoonekeratu kuti Mulungu sachititsa zoipa ndiponso kuvutika kwa anthu. M’malo mwake, Yehova ali ndi cholinga chochotseratu zoipa ndiponso amene amazichititsa. (Miyambo 2:22) Ndipo Mulungu adzachita zinanso zambiri. Malemba amanena kuti, Mulungu ali ndi cholinga choti “awononge ntchito za Mdyerekezi” kudzera mwa Khristu. (1 Yohane 3:8) Dongosolo la zinthu lilipoli lodzaza ndi dyera, udani, ndi ntchito zoipa, lidzatha. Mulungu “adzapukuta msozi uliwonse m’maso [mwa anthu onse].” (Chivumbulutso 21:4) Kumeneku kudzakhala kutha kwa kuvutika konse. Koma mungafunse kuti: ‘Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu sanachite zimenezi kale? N’chifukwa chiyani walola zoipa ndi kuvutika kwa anthu kupitirirabe mpaka pano?’ Yankho lake limapezeka mu nkhani ya m’Baibulo ya Adamu ndi Hava.

Nkhani Yaikulu Kwambiri

Chifukwa chimene Mulungu walolera zoipa kupitirirabe mpaka pano chikukhudzana ndi zimene zinachitika Mulungu atangolenga kumene anthu. Zimene zinachitika nthawi imeneyo zinayambitsa nkhani yaikulu kwambiri yokhudza Mlengi, yomwe sikanathetsedwa mwamsanga ndiponso mosavuta. Tiyeni tione bwinobwino zimene zinachitikazo.

Yehova Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi omwe anali angwiro, ndipo anawaika m’Paradaiso. Anawapatsa ufulu wosankha zochita ndipo chifukwa cha mphatso imeneyi, anthuwa anali osiyana ndi zinyama. (Genesis 1:28; 2:15, 19) Ndi ufulu umenewu, Adamu ndi Hava anali ndi mwayi wosankha kukonda Mlengi wawo, kum’tumikira ndi kumumvera kapena kusankha kudziimira paokha ndi kusamumvera.

Kuti apereke mwayi kwa Adamu ndi Hava wosonyeza chikondi chawo pa iye, Mulungu anawaletsa kuchita chinthu chimodzi. Anauza Adamu kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Kuti Adamu ndi Hava apitirizebe kuyanjidwa ndi Mulungu komanso kuti iwo ndi ana awo zinthu ziwayendere bwino, anafunikira kupewa kudya zipatso za mtengo umene anawaletsawo. Kodi iwo anamvera?

Baibulo limatiuza zimene zinachitika. Polankhula kudzera mwa njoka, Satana Mdyerekezi anafunsa Hava kuti: “Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Hava atauza Satana zimene Mulungu analamula, Satana anati: “Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” Ndipo Hava ataona kuti mtengowo unali wokoma m’maso, “anatenga zipatso zake, nadya.” Nkhaniyo imapitiriza kuti mkaziyo ‘anapatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso.’ (Genesis 3:1-6) Choncho, Adamu ndi Hava anagwiritsa ntchito molakwika ufulu wawo wosankha zochita ndipo anachimwa chifukwa sanamvere Mulungu.

Kodi mukuona kuopsa kwa zimene zinachitikazi? Mdyerekezi anatsutsa zimene Mulungu anauza Adamu. Satana anasonyeza kuti Adamu ndi Hava sanafunikire kudalira Yehova pankhani yosankha chabwino ndi choipa. Mwa kutero, Satana anayambitsa kukayikira zoti Yehova ali ndi ufulu wolamulira anthu. Choncho, nkhani yaikulu imene Satana anayambitsa inali yakuti, Yehova si woyenera kulamulira anthu. Kodi Mulungu woonayo anatani kuti athetse nkhani imeneyi?

Panafunika Nthawi Yaitali

Yehova anali ndi mphamvu zowononga opanduka onse atatuwo Satana, Adamu ndi Hava. Palibe amene angakayikire kuti Mulungu anali ndi mphamvu kwambiri kuposa onsewa. Koma Satana sanatsutse mphamvu za Mulungu. Iye anatsutsa zoti Yehova ali ndi ufulu wolamulira. Nkhani imeneyi inakhudza anthu ndi angelo, omwe ali ndi ufulu wosankha zochita. Iwo anafunikira kuzindikira kuti ufulu wawo wosankha zochita uyenera kugwiritsidwa ntchito bwino. Zosankha zawo zinayenera kugwirizana ndi malamulo a Mulungu okhudza chilengedwe, makhalidwe ndi moyo wauzimu. Kulephera kutsatira malamulo amenewa kumachititsa mavuto aakulu, monga mmene zimakhalira munthu akadumpha kuchokera pamwamba pa nyumba yaitali popanda kuganizira zotsatirapo zake. (Agalatiya 6:7, 8) Angelo ndiponso anthu, anayenera kuona zimene zimachitika ena akasankha kusadalira Mulungu. Zimenezi zinafunika nthawi.

Mungamvetse kuti nkhani zina zimafuna nthawi kuti zithetsedwe poganizira chitsanzo ichi: Bambo wa banja lina akuderera bambo wa banja linanso kuti alibe mphamvu. Nkhaniyi ingathetsedwe mwamsanga. Mwina akhoza kungonyamula miyala, ndipo amene anganyamule mwala wolemera kwambiri ndiye wamphamvu. Koma tayerekezerani kuti nkhani yake inali yakuti ndi bambo uti amene amakonda kwambiri ana ake, ndiponso amene ana akewo amamukonda. Kapenanso kuti ndi bambo uti amene amasamalira bwino banja lake? Mphamvu kapena mawu sizingathetse nkhani imeneyi. Pangafunike nthawi yokwanira, kuonetsetsa zimene zikuchitika, ndiyeno nkhaniyo ingathetsedwe moyenera.

Nthawi Yayankha

Papita zaka pafupifupi 6,000 kuchokera pamene Satana anatsutsa zoti Mulungu ali ndi ufulu wolamulira anthu. Kodi nthawi imeneyi yasonyeza chiyani? Taganizirani zinthu ziwiri zimene Satana ananena potsutsa Mulungu. Satana anauza Hava mopanda mantha kuti: “Kufa simudzafai.” (Genesis 3:4) Ponena kuti Adamu ndi Hava saafa akadya zipatso zoletsedwa, kwenikweni Satana ankanena kuti Yehova ndi wabodza. Imeneyi inali nkhani yaikulu kwabasi! Ngati Mulungu ananamadi, kodi tingam’khulupirire bwanji pa zinthu zina zonse? Komano kodi nthawi yonse imene yadutsayi yasonyeza chiyani?

M’kupita kwa nthawi, Adamu ndi Hava anayamba kudwala, kuvutika, kukalamba ndipo anafa. Baibulo limati: “Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anayi, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.” (Genesis 3:19; 5:5) Ndipo Adamu anapatsira anthu onse mavuto amenewa. (Aroma 5:12) Nthawi yonseyi yatsimikizira kuti Satana ndi “wabodza komanso tate wake wa bodza” ndiponso kuti Yehova ndi “Mulungu wa choonadi.”​—Yohane 8:44; Salmo 31:5.

Satana anauzanso Hava kuti: “Adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya [mtengo woletsedwawo], adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:5) Ndi mawu aukathyali amenewo, Satana ananyengerera anthu kuti atha kudzilamulira okha. Pofuna kuwasocheretsa, Satana anachititsa anthu kuganiza kuti zinthu zingawayendere bwino popanda kudalira Mulungu. Kodi nthawi imene yadutsayi yasonyeza kuti zimenezi n’zoona?

Kuyambira kalekale, maufumu ambiri akhala akubwera ndi kupita. Anthu ayesera mitundu yosiyanasiyana ya maboma. Koma panthawi yonseyi, anthu akhala akukumana ndi zinthu zoipa. Zaka pafupifupi 3,000 zapitazo wolemba Baibulo wina ananena mwanzeru kuti: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Mneneri Yeremiya nayenso analemba kuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Mawu amenewa ndi olondolabe ngakhale kuti sayansi ndi luso la zopangapanga zapita patsogolo kwambiri masiku ano. Kupita kwa nthawi kwangotsimikizira kuti zimenezi ndi zoona.

Kodi Inu Muli Mbali Iti?

Nthawi imene Mulungu wapereka yatsimikizira kuti Satana ndi wabodza ndi kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira anthu. Yehova Mulungu ndiye wolamulira wamkulu wachilengedwe chonse. Ali ndi ufulu wolamulira ndipo iye ndi wolamulira wabwino. Angelo, amene akhala akulamulidwa ndi Yehova kwa zaka zambiri, amadziwa bwino mfundo imeneyi ndipo amalengeza kuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu, kulandira ulemerero, ndi ulemu, ndi mphamvu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo chifukwa cha chifuniro chanu, zinakhalapo, inde zinalengedwa.”​—Chivumbulutso 4:11.

Kodi inuyo muli mbali iti pankhani ya ulamuliro wa Mulungu? Kodi mumavomereza kuti Mulungu ndiye woyenera kukulamulirani? Ngati mumatero, muyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi ulamuliro wake. Mungachite zimenezi mwa kutsatira malangizo ndi mfundo zamtengo wapatali za choonadi, zimene zimapezeka m’Mawu ake, Baibulo. “Mulungu ndiye chikondi” ndipo anapereka malamulo ake chifukwa chokonda zolengedwa zake. (1 Yohane 4:8) Yehova sabisira aliyense zabwino. Choncho mungachite bwino kumvera malangizo a m’Baibulo akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”​—Miyambo 3:5, 6.

[Chithunzi patsamba 7]

Mungasankhe ulamuliro wa Mulungu mwa kuphunzira Baibulo ndi kugwiritsa ntchito zimene limanena pamoyo wanu

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

© Jeroen Oerlemans/​Panos Pictures