Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Jonatani Anachita Zinthu Mothandizidwa ndi Mulungu

Jonatani Anachita Zinthu Mothandizidwa ndi Mulungu

Jonatani Anachita Zinthu Mothandizidwa ndi Mulungu

MWANA wa mfumu yoyamba ya Isiraeli anapita kukaona munthu wina amene ankakhala mobisala. Anauza munthu wokhala mobisalayo kuti: “Usaopa; chifukwa dzanja la Sauli atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe.”​—1 Samueli 23:17.

Mlendoyu anali Jonatani, ndipo munthu wokhala mobisalayo anali Davide. Jonatani akanapanda kufa msanga, akanakhala munthu wodalirika kwambiri kwa Davide.

Mgwirizano wa anthu awiriwa unali wochititsa chidwi kwambiri. Ndipotu, Jonataniyo anali munthu wochititsa chidwi. Nawonso anthu a m’nthawi yake anaona chimodzimodzi, chifukwa ananena kuti: “Iye anagwirizana ndi Mulungu,” kutanthauza kuti Jonatani anachita zinthu mothandizidwa ndi Mulungu. (1 Samueli 14:45) Kodi n’chifukwa chiyani anthuwa ananena zimenezi? Kodi Jonatani anali ndi makhalidwe otani? Ndipo kodi nkhani yake ingakuthandizeni bwanji?

Aisiraeli ‘Anapsinjika’

Pamene Baibulo linatchula koyamba za Jonatani, n’kuti Aisiraeli ‘atapsinjika.’ Afilisti anali atawalanda dziko ndiponso analibe mpata uliwonse wodzitetezera.​—1 Samueli 13:5, 6, 17-19.

Koma Yehova anafotokoza kuti sadzasiya anthu ake, ndipo Jonatani ankakhulupirira zimenezi. Pofotokoza za Sauli amene anali bambo ake, Mulungu ananena kuti: ‘Adzapulumutsa anthu anga m’manja a Afilisti.’ Jonatani sankakayikira mfundo imeneyi. Iye anali atatsogolerapo Aisiraeli 1,000, omwe analibe zida zokwanira, n’kugonjetsa Afilisti. Tsopano ankafuna kuti athetseretu mantha onse amene Aisiraeli anali nawo chifukwa cha Afilistiwo.​—1 Samueli 9:16; 12:22; 13:2, 3, 22.

Analimba Mtima N’kuukira Adani

Jonatani anafuna kulimbana ndi Afilisti pamsasa umene unali pafupi ndi malo olowera ku Mikimasi. (1 Samueli 13:23) Kuti akafike ku msasawo, iye anafunika kukwera mtunda “chokwawa.” Komatu, zimenezi sizinam’gwetse ulesi. Jonatani anaganiza zokaukira msasawo ali awiriwiri ndi womunyamulira zida, ndipo anamuuza kuti: “Kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chom’letsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.”​—1 Samueli 14:6, 13.

Aisiraeli awiriwa anafuna chizindikiro chochokera kwa Yehova. Iwo anakonza zoti akadzionetse okha kwa asilikali a mumsasawo. Afilistiwo akananena kuti: “Baimani kufikira titsikira kwa inu,” Jonatani ndi wonyamula zidayo sakanamenyana nawo. Koma ngati akananena kuti: “Kwerani kuno kwa ife,” zikanasonyeza kuti Yehova athandiza Jonatani ndi wonyamula zidayo kuti agonjetse adaniwo. Jonatani akanapita ku msasawo ndi kukamenya nkhondo ngati akanakhala ndi chikhulupiriro choti Mulungu am’thandiza.​—1 Samueli 14:8-10.

Kodi anthu awiri angamenyane bwanji ndi msasa wonse wa asilikali? Taganizirani izi: Kodi Yehova sanathandize Woweruza Ehudi pamene anatsogolera Aisiraeli polimbana ndi Amoabu? Kodi Mulungu sanathandize Samagara, mpaka kupha Afilisti 600 ndi mtoso wa ng’ombe? Ndipo kodi Yehova sanapatse Samsoni mphamvu pamene ankalimbana ndi Afilisti yekhayekha? Jonatani ankakhulupirira kuti Mulungu am’thandiza nayenso.​—Oweruza 3:12-31; 15:6-8, 15; 16:29, 30.

Ataona Aisiraeli awiriwo, Afilisti anafuula kuti: “Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu.” Jonatani ndi womunyamulira zida uja anakweradi. Iwo analimba mtima, n’kumenyana ndi asilikaliwo mpaka kupha adani pafupifupi 20, zomwe zinasokoneza msasawo. Mwina Afilistiwo ankaganiza kuti asilikali ambiri achiisiraeli akubwera kutsatira asilikali awiriwo. Kenako, nkhaniyo imati, ‘kunali kunthunthumira . . . pakati pa anthu onse a ku kaboma . . . ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.’ Chifukwa cha chivomezi chimene Mulungu anachititsa, Afilisti anayamba kulowera kwina ndi kwina, moti “munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga.” Asilikali a Aisiraeli ataona zimenezi analimba mtima. Mothandizidwa ndi Aisiraeli amene anali atabisala ndiponso Aisiraeli amene anagwirizana ndi Afilisti, Jonatani ndi womunyamulira zida uja “anakantha Afilisti . . . kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ajaloni.”​—1 Samueli 14:11-23, 31.

Anthu Apulumutsa Jonatani

Mfumu Sauli inanena mosaganiza bwino kuti msilikali aliyense amene adye kanthu, iwo asanapambane nkhondo yomwe anali kumenya, akhale wotembereredwa. Jonatani sanadziwe za lumbiro limeneli, ndipo anadya. Iye anatosa chisa cha uchi ndi ndodo, n’kudyako uchiwo. Zikuoneka kuti izi zinam’thandiza kupeza nyonga zopitirizira nkhondoyo.​—1 Samueli 14:24-27.

Sauli atamva kuti Jonatani wadya kanthu, analamula kuti aphedwe. Jonatani sanaope imfa ndipo anati: “Onani ndiyenera kufa.” Baibulo limati: “Ndipo anthuwo ananena ndi Sauli, Kodi Jonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi m’Isiraeli? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pa mutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Jonatani kuti angafe.”​—1 Samueli 14:38-45.

Inuyo, monga mtumiki wamakono wa Mulungu simufunikira kumenya nkhondo yeniyeni. Komabe, nthawi zina mungafunike kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima. Mwina kungakhale kovuta kuchita zinthu zoyenera pamene anthu ena onse akuchita zinthu zolakwika. Koma Yehova adzakulimbikitsani ndiponso kudalitsa mtima wanu wofuna kutsatira mfundo zake zolungama. N’kutheka kuti mungafunike kulimba mtima kuti muchite utumiki winawake m’gulu la Yehova, monga kuwonjezera utumiki wanu, kulandira utumiki watsopano, kapena kusamukira ku dera lomwe kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Mwina mungadzikayikire ngati ndinu woyenera utumiki umenewo. Koma dziwani kuti ngati mwadzipereka kuti Yehova akugwiritsireni ntchito mmene iye akufunira, ndiye kuti mukuchita bwino kwambiri. Kumbukirani kuti Jonatani anachita zinthu mothandizidwa ndi Mulungu.

Jonatani ndi Davide

Patatha zaka pafupifupi 20, Davide anapha Goliati, chimphona cha Afilisti chimene chinanyoza asilikali a Aisiraeli. Ngakhale kuti Jonatani ndi Davide ankasiyana ndi zaka pafupifupi 30, anthu awiriwa anali ndi makhalidwe ofanana. * Kulimba mtima kumene Jonatani anasonyeza ku Mikimasi kunaonekeranso mwa Davide. Koma koposa zinthu zonsezi, Davide ankakhulupiriranso kuti Yehova amapulumutsa, ndipo n’chifukwa chake analimba mtima kukamenyana ndi Goliati pamene Aisiraeli ena onse ankachita mantha. Choncho, “mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anam’konda iye monga moyo wa iye yekha.”​—1 Samueli 17:1–18:4.

Ngakhale kuti mphamvu za Davide zinapangitsa Mfumu Sauli kumuona monga mdani wake, Jonatani sanam’chitire nsanje m’pang’ono pomwe. Iye anagwirizana kwambiri ndi Davide, ndipo n’zosakayikitsa kuti pokambirana nkhani zawo zachinsinsi, Jonatani anadziwa zoti Davide anadzozedwa kuti adzakhale mfumu yotsatira ya Isiraeli. Jonatani anagwirizana ndi zimene Mulungu anasankha.

Mfumu Sauli italankhula ndi mwana wake ndiponso atumiki ake zopha Davide, Jonatani anachenjeza Davide za nkhaniyi. Jonatani anatsimikizira Sauli kuti panalibe chifukwa choopera Davide. Ndipo sikuti Davide anali atachimwira mfumuyo ayi. Komanso Davideyo anali ataikapo moyo wake pachiswe kuti amenyane ndi Goliati. Mtima wa Sauli unakhala m’malo chifukwa cha pempho la Jonatani lochokera pansi pamtima. Komabe, patangotha nthawi yochepa, maganizo oipa a mfumuyo anabweranso, ndipo inayesanso kupha Davide, moti iye anathawa.​—1 Samueli 19:1-18.

Jonatani anakhalabe wokhulupirika kwa Davide. Anthu awiriwa anakumana kuti agwirizane zochita. Pokhala wokhulupirika kwa mnzakeyo ndiponso poyesetsabe kukhala wokhulupirika kwa bambo ake, Jonatani anauza Davide kuti: “Usatero iyayi, sudzafa.” Komabe, Davide anauza Jonatani kuti: “Pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.”​—1 Samueli 20:1-3.

Kenako, Jonatani ndi Davide anapeza njira yodziwira zolinga za Sauli. Ngati mfumu idzazindikire kuti Davide sanabwere kudzadya ndi mfumu, Jonatani adzauza bambo ake kuti Davide wapempha kuti akakhale ndi abale ake pamwambo wopereka nsembe. Ngati Sauli adzakwiye ndi zimenezi, chimenecho chidzakhala chizindikiro cha maganizo ake oipa pa Davide. Jonatani anadalitsa Davide n’kuvomereza zoti adzakhala mfumu, pamene ananena kuti: “Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.” Anthu awiriwa analumbirirana kuti aliyense akhala wokhulupirika kwa mnzake ndiponso anauzana mmene Jonatani adzadziwitsire Davide maganizo a Sauli.​—1 Samueli 20:5-24.

Sauli atazindikira kuti Davide palibe panthawi ya chakudya, Jonatani anafotokoza kuti Davide anam’pempha kuti: “Ngati wandikomera mtima undilole ndichoke, ndikaone abale anga.” Jonatani sanachite mantha kuvomereza kuti anakomera mtima Davide. Mfumu inakwiya kwambiri! Inanyoza Jonatani ndi kulankhula mokalipa kuti Davide ankafuna kulepheretsa kuti mwana wakeyo adzalowe ufumu. Sauli analamula Jonatani kuti am’bweretsere Davide chifukwa choti ndi woyenera kufa. Jonatani anayankha kuti: “Aphedwe chifukwa ninji? anachitanji?” Atapsa mtima, Sauli anaponya mkondo kuti alase mwana wakeyo. Jonatani anazinda ndipo sanavulale, koma anamva chisoni kwambiri chifukwa cha Davide.​—1 Samueli 20:25-34.

Apatu Jonatani anasonyeza kuti anali wokhulupirika kwambiri. Malinga n’kuona kwa anthu, Jonatani sakanapindula chifukwa chogwirizana ndi Davide, m’malo mwake akanangotaya zinthu zambiri. Komabe, Yehova anali atadzoza Davide kuti adzalowe ufumu wa Sauli ndipo zimene Yehova anakonza zinali zothandiza kwa Jonatani ndi anthu ena onse.

Analira Potsanzikana

Jonatani anazemba n’kupita kukauza Davide zomwe zinachitika. Apa zinali zoonekeratu kuti Davide sadzalowanso m’nyumba ya Sauli. Anthu awiriwa analira ndi kukumbatirana. Kenako Davide anapita kukabisala.​—1 Samueli 20:35-42.

Jonatani anaonananso ndi Davide kamodzi kokha pamene Davideyo ankabisala “m’chipululu cha Zifi m’nkhalango,” pothawa Sauli. Panthawiyi m’pamene Jonatani analimbikitsa Davide ndi mawu akuti: “Usaopa; chifukwa dzanja la Sauli atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Sauli atate wanga achidziwa.” (1 Samueli 23:15-18) Patangopita nthawi yochepa, Jonatani ndi Sauli anafa pa nkhondo yolimbana ndi Afilisti.​—1 Samueli 31:1-4.

Anthu amene amakonda Mulungu angachite bwino kuganizira za moyo wa Jonatani. Kodi mumavutika kusankha kuti mukhala wokhulupirika kwa ndani? Ndiyetu kumbukirani kuti Sauli analimbikitsa Jonatani kuti achite zinthu zongokomera iyeyo basi. Koma Jonatani analemekeza ndi kugonjera Yehova ndi mtima wonse ndiponso anasangalala kuti munthu amene Mulungu anasankha ndiye adzakhale mfumu yotsatira ya Isiraeli. Zoonadi, Jonatani anathandiza Davide ndipo anakhala wokhulupirika kwa Yehova.

Jonatani anali ndi makhalidwe abwino kwambiri, ndipo tingachite bwino kum’tsanzira. Tikatero, pofotokoza za ifeyo, anthu adzanena ngati zimene ananenera Jonatani kuti, ‘Anachita zinthu mothandizidwa ndi Mulungu.’​—1 Samueli 14:45.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Jonatani anali wazaka zosachepera 20 pamene anatchulidwa koyamba monga woyang’anira gulu lankhondo, chakumayambiriro kwa ulamuliro wa zaka 40 wa Sauli. (Numeri 1:3; 1 Samueli 13:2) Motero, pamene Jonatani ankamwalira cha m’ma 1078 B.C.E., ayenera kuti anali ndi zaka pafupifupi 60. Popeza kuti panthawiyi Davide anali ndi zaka 30, zikuoneka kuti Jonatani ankasiyana zaka pafupifupi 30 ndi Davide.​—1 Samueli 31:2; 2 Samueli 5:4.

[Chithunzi patsamba 19]

Jonatani sanachitire nsanje Davide