Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Anatipulumutsa ku Ulamuliro Wankhanza

Yehova Anatipulumutsa ku Ulamuliro Wankhanza

 Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Anatipulumutsa ku Ulamuliro Wankhanza

Yosimbidwa ndi Henry Kdornik

NDINABADWA mu 1926 ndipo makolo anga anali Akatolika olimbikira kwambiri pachipembedzo chawo. Ankakhala ku Ruda Slaska, tawuni yamigodi, kufupi ndi mzinda wa Katowice, kum’mwera kwa dziko la Poland. M’banja mwathu tinalimo ana anayi; ineyo, mkulu wanga Bernard ndi alongo anga aang’ono awiri, Róża ndi Edyta. Makolo athu anatiphunzitsa kupemphera ndi kupita ku tchalitchi, komwenso tinkakalapa.

Banja Lathu Linayamba Kuphunzira Choonadi

Tsiku lina mu January 1937, ndili ndi zaka 10, bambo anafika panyumba chimwemwe chitadzaza tsaya. Anabwera ndi buku lalikulu lomwe anapatsidwa ndi Mboni za Yehova. Iwo anati: “Ananu, taonani! Ndabweretsa Malemba Oyera.” Ndinali ndisanaonepo Baibulo.

Tchalitchi cha Katolika chinali ndi mphamvu kwambiri ku Ruda Slaska ndi m’madera ena ozungulira, ndipo izi zinachitika kwanthawi yaitali. Ansembe ankagwirizana kwambiri ndi enimigodi ndipo ankafuna kuti anthu ogwira ntchito m’migodiyo ndi mabanja awo aziwamvera kwambiri. Anthuwo akalephera kupita ku Misa kapena akakana kupita kokalapa, ankawaona kuti ndi achikunja ndipo ankatha kuwachotsa ntchito. Bambo nawonso akanatha kuchotsedwa ntchito chifukwa chakuti ankagwirizana ndi Mboni za Yehova. Koma tsiku lina wansembe atabwera kunyumba kwathu, bambo anaulula chinyengo chake chonse poyera. Iye anachita manyazi ndipo bambo sanachotsedwe ntchito chifukwa wansembeyu ankaopa kudziputira mavuto ena.

Kukangana kwa bambo ndi wansembeyu kunandilimbikitsa kufuna kudziwa zambiri za Baibulo.  Pang’ono ndi pang’ono, ndinayamba kukonda Yehova ndiponso ndinakhala naye paubwenzi. Patapita miyezi ingapo kuchokera pamene bambo analankhula ndi wansembe uja, tinapita nawo ku Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Tili kumeneku, bambo anadziwikitsidwa kwa anthu 30 ndi mawu akuti, “Uyu ndi wa Ayonadabu.” Kenako, ndinazindikira kuti “Ayonadabu” ndi Akhristu odzakhala pa dziko lapansi komanso kuti chiwerengero chawo chidzawonjezeka kwambiri. *​—2 Mafumu 10:15-17.

“Mnyamatawe, Kodi Ukudziwa Tanthauzo la Ubatizo?”

Bambo ataphunzira choonadi, anasiya kumwa mowa ndipo anakhala mwamuna ndiponso kholo labwino. Komabe, mayi sankagwirizana ndi zimene bambo anayamba kukhulupirira. Iwo ankanena kuti angakonde bambo atakhala mmene analili poyamba ndi kukhalabe Mkatolika. Komabe, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itayamba, mayi anaona kuti ansembe amene anapempherera Poland, dzikoli litaukiridwa ndi dziko la Germany, anayambanso kupemphera mapemphero othokoza chifukwa chakuti Hitler akupambana pankhondoyo. Kenako mu 1941, mayi nawonso anayamba kutumikira Yehova.

Zimenezi zisanachitike, ndinapempha kuti ndibatizidwe posonyeza kudzipereka kwa Mulungu, koma akulu mumpingo ankaona kuti ndine mwana kwambiri. Anandiuza kuti ndidikire kaye. Kenako, pa December 10, 1940, Konrad Grabowy (m’bale yemwe anamwalira ali wokhulupirika ku ndende yozunzirako anthu) anapita nane m’kachipinda kukandifunsa mafunso. Anandifunsa mafunso asanu ndipo ataona kuti ndayankha bwino, anandibatiza. Funso lake lina linali lakuti, “Mnyamatawe, kodi ukudziwa tanthauzo la ubatizo?” Lina linali lakuti, “Popeza kuti tsopano kuli nkhondo, kodi ukudziwa kuti ufunikira kusankha kukhala wokhulupirika kwa Hitler kapena kwa Yehova, ndiponso kuti zimene ungasankhe zingaike moyo wako pangozi?” Ndinayankha mosakayika kuti, “inde.”

Chizunzo Chinayamba

N’chifukwa chiyani Konrad Grabowy anafika pofunsa mafunso ngati amenewa? Asilikali a ku Germany anali atalanda Poland mu 1939, ndipo chikhulupiriro chathu chinayesedwa kwambiri. Tsiku lililonse zinthu zinkaipiraipira. Tinkamva kuti abale ndi alongo athu achikhristu amangidwa, ena atumizidwa kwawo, ndiponso ena aponyedwa m’ndende zozunzirako anthu. Tinadziwa kuti posachedwa nafenso tikumana ndi mavuto ngati amenewa.

Chipani cha Nazi chinafuna kuti achinyamata, kuphatikizapo ineyo ndi abale anga atatu, tikhale odzipereka ku ulamuliro wa Hitler. Bambo ndi mayi anakana kambirimbiri kusayina chikalata (chotchedwa Volkslist) chosonyeza kuti munthu wakhala, kapena akufuna kukhala nzika ya dziko la Germany. Zimenezi zinachititsa kuti asaloledwe kulera ana awofe. Bambo anatumizidwa ku ndende yozunzirako anthu ku Auschwitz. Mu February 1944, ine ndi mchimwene wanga anatiponya m’ndende yolangirako ana ku Grodków (kapena kuti ku Grottkau), kufupi ndi Nysa. Azichemwali athu anatumizidwa ku malo kokhala masisitere ku Czarnowąsy (kapena kuti ku Klosterbrück), kufupi ndi Opole. Cholinga chawo chinali choti tisiye kutsatira maganizo a makolo athu, amene akuluakulu a boma ankati ndi achinyengo. Mayi anatsala okha panyumba.

Kundendeko, m’mawa uliwonse akamakweza mbendera ya Nazi ankatilamula kukweza manja athu akumanja pochitira ulemu mbenderayo, n’kumati: “Hitler ndiye Mpulumutsi Wathu.” Chimenechi chinali chiyeso chachikulu, komabe ine ndi Bernard sitinagonje. Motero tinamenyedwa kwambiri chifukwa ankaganiza kuti tilibe ulemu. Anayesayesabe kutifoola koma analephera ndipo kenako asilikali a Nazi anatiuza kuti: “Musankhe, kusayina chikalata chovomereza kuti mukhala okhulupirika ku boma la Germany ndiponso mulowa  usilikali, apo ayi tikutumizani ku ndende yozunzirako anthu.”

Mu August 1944, akuluakulu a boma atagwirizana zoti atitumize ku ndende yozunzirako anthu, anati: “Anthu awa sangasinthe. Amasangalala kufera chikhulupiriro chawo. Amenewa ndi anthu ogalukira boma ndipo zimenezi zikhoza kusokoneza ndende yonse.” Ngakhale kuti cholinga changa sichinali kufera chikhulupiriro, ndinali wosangalala chifukwa chokhala wokhulupirika kwa Yehova pokumana ndi mavuto. (Machitidwe 5:41) Ndekha, sindikanatha kupirira mavuto amene ndinali kudzakumana nawo. Komabe, mapemphero ochokera pansi pamtima anandithandiza kuyandikira kwa Yehova, ndipo iye anakhala Mthandizi wodalirika.​—Aheberi 13:6.

M’ndende Yozunzirako Anthu

Posapita nthawi ananditumiza ku ndende yozunzirako anthu ya Gross-Rosen ku Silesia. Anandipatsa nambala ya mkaidi ndiponso kansalu kapepo, kondidziwikitsa kuti ndine wa Mboni za Yehova. Asilikali a Nazi anandiuza kuti ndingathe kutulutsidwa m’ndendeyo ndi kukhala mmodzi wa akuluakulu a asilikali ngati nditachita zimene iwo andiuze. Iwo anati: “Uyenera kusiya kutsatira ziphunzitso za Ophunzira Baibulo zomwe zimatsutsana kwambiri ndi ulamuliro wa Hitler.” Akaidi ena onse sanapatsidwe mwayi ngati umenewu. Mboni za Yehova zokha n’zomwe zinapatsidwa mwayi woti zitha kutuluka m’ndendezi. Komabe ine, mofanana ndi Mboni za Yehova zambiri, ndinakanitsitsa “mwayi” umenewu. Asilikaliwa anandiuza kuti: “Tayang’anitsitsa chumuni cha nyumba yowotcheramo anthuyo. Taganiza bwino, apo ayi ufulu wako uupeza kudzera m’chumunicho.” Ndinakanitsitsanso, ndipo nthawi imeneyi ndinali ndi “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira.”​—Afilipi 4:6, 7.

Ndinapemphera kuti ndithe kulankhula ndi okhulupirira anzanga m’ndendemo, ndipo Yehova anandithandiza kutero. Mmodzi wa Akhristuwa anali m’bale wokhulupirika dzina lake Gustaw Baumert, yemwe anandisamalira mwachikondi. Kunena zoona, Yehova anali “Tate wa chifundo chachikulu ndi Mulungu wa chitonthozo chonse” kwa ine.​—2 Akorinto 1:3.

Patatha miyezi ingapo, asilikali a Nazi ataona kuti asilikali a dziko la Russia ayandikira, anathawa pa ndendeyo. Pokonzekera kuchoka, abalefe tinaika moyo wathu pachiswe mwa kupita kumene ankasungirako alongo athu achikhristu kukawaona. Kumeneku kunali alongo pafupifupi 20 ndipo ena mwa iwo anali Elsa Abt ndi Gertrud Ott. * Atationa anatithamangira, ndipo titalimbikitsana kwa nthawi yochepa, alongowa anaimba pamodzi nyimbo ya Ufumu ya mawu akuti: “Yemwe ali wokhulupirika, sadzakhala ndi mantha.” * Tonse tinagwetsa misozi.

 Anatisamutsira ku Ndende Ina

Asilikali a Nazi anatipakira akaidi 100 mpaka 150 mu mabogi a sitima zamalasha, opanda chakudya kapena madzi, ndipo tinadutsa m’madera ozizira kwambiri ndiponso amvula. Tinavutika ndi ludzu ndiponso kuphwanya thupi. Kuthithikana kunayamba kuchepa m’sitimazi, pamene akaidi odwala ndiponso otopa, ankagwa ndi kufa. Miyendo yanga inatupa kwambiri moti sindinkatha kuimirira. Titayenda masiku 10, akaidi ochepa kwambiri omwe tinapulumuka tinafika ku ndende yozunzirako anthu ya Mittelbau-Dora mu mzinda wa Nordhausen, womwe uli kufupi ndi mzinda wa Weimar ku Thuringia. Zinali zodabwitsa kwambiri kuti panalibe m’bale amene anamwalira paulendo wovuta kwambiri umenewu.

Pasanapite nthawi yaitali titavutika ndi ulendo uja, m’ndendemo munabuka mliri wotsegula m’mimba ndipo ineyo ndi abale ena tinadwala matendawa. Tinalangizidwa kuti tisiye kaye kumwa supu ndipo tizingodya buledi wowotcha. Ndinatsatira malangizowa ndipo posapita nthawi ndinachira. Mu March 1945, tinamva kuti Lemba la chaka linali Mateyo 28:19 limene limati: “Choncho pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.” Zinali zoonekeratu kuti sipapita nthawi yaitali tisanamasulidwe ndi kuti uthenga wabwino upitiriza kulalikidwa. Zimenezi zinatisangalatsa ndiponso zinatipatsa chiyembekezo, chifukwa tinkaganiza kuti nkhondo yachiwiri ya padziko lonse idzatifikitsa ku Aramagedo. Yehova anatilimbikitsa kwambiri m’nthawi yovuta imeneyi.

Kutulutsidwa M’ndende

Pa April 1, 1945, mayiko olimbana ndi Germany anaphwasula malo a asilikali a Nazi ndiponso ndende ina yakufupi ndi yathu ndi mabomba. Anthu ambiri anafa ndipo ena anavulala. Tsiku lotsatira, anaphulitsa mabomba pandende yathu ndipo bomba lina lamphamvu kwambiri linandiponyera m’mwamba.

M’bale wina dzina lake Fritz Ulrich anabwera kudzandithandiza. Ngakhale kuti ndinali n’takwiririka, iye anafukula zimene zinandikwirirazo poganiza kuti ndili moyo. Kenako, anandipeza ndi kundikokapo. Nditatsitsimuka, ndinazindikira kuti ndinavulala kwambiri kumaso ndi m’thupi ndipo makutu anali atagontha. Phokoso la bomba lija linandiwononga m’makutu. Ndinavutika ndi makutuwa kwa zaka zambiri mpaka pamene ndinachira.

Akaidi ochepa anapulumuka bomba limeneli koma ambiri anafa. Abale ena anafanso ndipo mmodzi wa iwo anali Gustaw Baumert. Mabala omwe ndinali nawo, anandiputiranso matenda ena. Koma patatha nthawi yochepa, asilikali olimbana ndi dziko la Germany anatipeza n’kutimasula. Panthawi imodzimodziyo, matupi owola a akaidi omwe anafa okha kapena kuchita kuphedwa anayambitsa matenda enaake a pakhungu. Nanenso ndinadwala matenda amenewa. Ananditengera kuchipatala pamodzi ndi odwala ena. Madokotala anayesetsa, koma tinapulumuka anthu atatu okha. Ndinathokoza kwambiri Yehova chifukwa chondithandiza kukhalabe wokhulupirika m’nthawi ya mavuto imeneyi. Ndinathokozanso Yehova chifukwa chondipulumutsa mu “mthunzi” wa imfa.​—Salmo 23:4.

Kubwerera ku Nyumba

Dziko la Germany litagonja pankhondoyo, ndinaganiza kuti ndibwerera ku nyumba mwamsanga, koma sizinatero. Anthu omwe kale anali akaidi ndipo anali m’bungwe lina lotchedwa Catholic Action atandiona, anakuwa kuti, “Iphani ameneyo!” Ndipo anandigwetsera pansi n’kuyamba kundiponda. Munthu wina anabwera kudzandipulumutsa, koma panadutsa nthawi yaitali kuti ndichire chifukwa anandivulaza ndiponso matenda apakhungu aja anandifoola. Koma kenako, ndinabwereranso ku nyumba. Ndinasangalala kwambiri kuonananso ndi anthu a m’banja lathu. Onse anali osangalala kundiona chifukwa ankaganiza kuti ndafa.

Tinayambanso ntchito yolalikira ndipo anthu ambiri analabadira choonadi. Ndinapatsidwa ntchito yotumiza ku mipingo mabuku ofotokoza Baibulo. Ine ndi abale ena, tinali ndi  mwayi wopita ku Weimar, kukaonana ndi abale ochokera ku nthambi ya Germany. Ndipo pochokera kumeneko tinkabweretsa ku Poland magazini atsopano a Nsanja ya Olonda omwe anasindikizidwa nkhondo itatha. Anamasuliridwa ndi kusindikizidwa mwamsangamsanga. Ofesi yathu ya ku Lodz itayamba kuyang’anira ntchito yonse ku Poland, mabuku ofotokoza Baibulo anayamba kufika ku mipingo mokhazikika. Ndinakhala mpainiya wapadera, kapena kuti mlaliki wa nthawi zonse, ndipo ndinkalalikira ku dera lalikulu la Silesia. Panthawi imeneyo, mbali yaikulu ya derali inali m’dziko la Poland.

Posakhalitsa, Mboni za Yehova zinayambanso kuzunzidwa, koma panthawiyi ndi boma la Komyunizimu la Poland. Mu 1948, ndinalamulidwa kukakhala m’ndende zaka ziwiri chifukwa chosalowerera ndale. Ndili kumeneko, ndinathandiza akaidi ena ambiri kuyandikira kwa Mulungu. Mmodzi wa akaidiwa anayamba kuphunzira choonadi ndipo kenako anadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa.

Mu 1952, ndinaikidwanso m’ndende pondiganizira kuti ndine kazitape wa boma la United States. Podikira mlandu wanga, ananditsekera kwandekha ndipo ndinkafunsidwa mafunso usana ndi usiku. Komabe, Yehova anandipulumutsanso m’manja mwa ozunzawa, ndipo zaka zotsatira sindinakumanenso ndi zoterezi.

Zimene Zinandithandiza Kupirira

Ndikakumbukira zaka zonse zomwe ndinakumana ndi mayesero komanso mavuto, ndimaona zinthu zingapo zimene zinandilimbikitsa kwambiri. Choyamba, ndinalimbikitsidwa ndi Yehova ndiponso Mawu ake, Baibulo. Kupemphera mwakhama nthawi zonse kwa “Mulungu wa chitonthozo chonse” ndiponso kuwerenga Mawu ake tsiku lililonse, zinathandiza ine ndi anzanga kukhalabe okhulupirika. Magazini a Nsanja ya Olonda olembedwa pamanja anandithandizanso kwambiri. Ndili ku ndende zozunzirako anthu, ndinkalimbikitsidwa ndi okhulupirira anzanga achikondi kwambiri amene anali ofunitsitsa kundithandiza.

Mkazi wanga, Maria analinso dalitso limene Yehova anandipatsa. Tinakwatirana mu October 1950, ndipo tinakhala ndi mwana wamkazi, dzina lake Halina, yemwe tinam’phunzitsa kukonda ndiponso kutumikira Yehova. Maria ndi ine tinakhala m’banja zaka 35 mpaka pamene anamwalira atadwala nthawi yaitali. Ndinali wachisoni komanso wopwetekedwa mtima chifukwa cha imfa yake. Ngakhale kuti kwa kanthawi ndinamva ngati ‘ndinagwetsedwa pansi’ koma ‘sindinawonongeke.’ (2 Akorinto 4:9) Panthawi yovuta imeneyo, mwana wanga wamkazi, mwamuna wake ndiponso ana awo anandithandiza. Onsewa akutumikira Yehova mokhulupirika.

Kuyambira mu 1990, ndakhala ndikutumikira pa ofesi ya nthambi ya ku Poland. Tsiku lililonse, kukhala ndi Banja la Beteli lomwe ndi lapadera ndi dalitso lalikulu kwa ine. Panopa thupi langa likufooka, ndipo zimenezi zimandipangitsa kudziona ngati chiwombankhanga chofooka chomwe chikuuluka popanda kukupiza mapiko. Ngakhale zili choncho, sindikayikira zam’tsogolo, ndipo ‘ndimaimbira Yehova, pakuti akundichitirabe zokoma.’ (Salmo 13:6) Ndikuyembekezera nthawi imene Yehova, Mthandizi wanga, adzachotseratu zoipa zonse zimene ulamuliro wopondereza wa Satana ukuchititsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 1998, tsamba 13, ndime 6.

^ ndime 20 Onani nkhani ya moyo wa Elsa Abt mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1980, masamba 12 mpaka 15.

^ ndime 20 Nyimbo imeneyi inali nambala 101 m’buku la nyimbo la 1928 (la Songs of Praise to Jehovah), lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. M’buku la nyimbo la masiku ano nyimboyi ndi nambala 56.

[Chithunzi patsamba 10]

Kundende yozunzirako anthu anandipatsa nambala iyi ndi kansalu kapepo

[Chithunzi patsamba 12]

Ine ndi mkazi wanga, Maria, mu 1980