Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezekieli—Gawo 2

Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezekieli—Gawo 2

 Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezekieli​—Gawo 2

MFUMU ya Babulo inayamba kuzinga komaliza Yerusalemu mwezi wa December mu 609 B.C.E. Uthenga wa Ezekieli kwa anthu omwe anali mu ukapolo ku Babulo kwenikweni unali kunena za kugwa ndi kuwonongedwa kwa Yerusalemu, mzinda umene anthuwo ankaukonda. Koma kenako uthenga wa Ezekieli unasintha n’kuyamba kunena za tsoka la mitundu imene sinkalambira Yehova yomwe inkasangalala chifukwa cha mavuto omwe anagwera anthu a Mulungu. Patapita miyezi 18 Yerusalemu atawonongedwa, uthenga wa Ezekieli unasinthanso n’kumanena zakuti kulambira koona kudzayambiranso ndipo anthu adzasangalala.

Pa Ezekieli 25:1 mpaka 48:35 pali maulosi onena za mitundu yozungulira Isiraeli ndiponso kulanditsidwa kwa anthu a Mulungu. * Nkhani yonse inafotokozedwa motsatira mitu ndiponso ndondomeko ya nthawi, kusiyapo Ezekieli 29:17-20. Mavesi anayiwa analembedwa motsatira mitu. Buku la Ezekieli lili mbali ya Malemba ouziridwa ndipo uthenga wake ndi ‘wamoyo ndi wamphamvu.’​—Aheberi 4:12.

‘DZIKO ILI LIDZASANDUKA NGATI MUNDA WA EDENE’

(Ezekieli 25:1–39:29)

Ataoneratu mmene mitunduyo idzachitire Yerusalemu akadzawonongedwa, Yehova kudzera mwa mneneri Ezekieli anapereka ulosi wotsutsa Amoni, Moabu, Edomu, Filistiya, Turo ndi Sidoni ndipo Iguputo anali kudzafunkhidwa. “Farao mfumu ya Aigupto ndi aunyinji ake” anawayerekezera ndi mkungudza womwe udzadulidwa ndi “lupanga la mfumu ya ku Babulo.”​—Ezekieli 31:2, 3, 12; 32:11, 12.

Pambuyo pa miyezi 6 Yerusalemu atawonongedwa mu 607 B.C.E., munthu amene anapulumuka anapita kwa Ezekieli n’kumuuza kuti: “Wakanthidwa mudzi.” Motero, mneneriyo ‘anatsegula pakamwa’ kuti anenere kwa omwe anali mu ukapolo. (Ezekieli 33:21, 22) Iye anali ndi maulosi onena kuti anthu a Yehova adzabwerera kwawo. Yehova ‘adzaziutsira mbusa mmodzi; . . . mtumiki wake Davide.’ (Ezekieli 34:23) Edomu adzakhala bwinja ndipo Yuda ‘adzasanduka ngati munda wa Edene.’ (Ezekieli 36:35) Yehova analonjeza kuti adzateteza anthu ake obwerera kwawo kuti “Gogi” asawaukire.​—Ezekieli 38:2.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

29:8-12—Kodi ndi liti pamene Iguputo anasanduka bwinja kwa zaka 40? Yerusalemu atawonongedwa mu 607 B.C.E., Ayuda otsala anathawira ku Iguputo ngakhale kuti mneneri Yeremiya anali atawachenjeza kuti asadzatero. (Yeremiya 24:1, 8-10; 42:7-22) Mwakuchita zimenezi, iwo sanathawe Ababulo chifukwa Nebukadinezara anagonjetsanso Iguputo. Ndipo kuyambira nthawi imene anagonjetsedwa ndi Babulo, Iguputo anakhala bwinja kwa zaka 40. Ngakhale kuti palibe umboni wa zimenezi m’mabuku a mbiri, tikutsimikiza kuti zinachitikadi chifukwa Yehova amakwaniritsa maulosi.​—Yesaya 55:11.

29:18—Kodi zinatheka bwanji kuti ‘mitu yonse ichite dazi ndi mapewa onse anyuke’? Kuzinga mzinda wa Turo kunali kovuta kwambiri ndiponso kotopetsa moti asilikali a Nebukadinezara anachita dazi chifukwa zisoti zimakwecha m’mutu mwawo. Ndipo mapewa awo ananyuka chifukwa chonyamula zinthu  zomangira nsanja ndi malinga.​—Ezekieli 26:7-12.

Zimene Tikuphunzirapo:

29:19, 20. Mfumu Nebukadinezara analandira zinthu zochepa zochokera ku Turo chifukwa choti anthu a kumeneku anathawira ku mzinda wawo wa pachilumba ndi chuma chawo chambiri. Ngakhale kuti Nebukadinezara anali wonyada ndiponso wolamulira wosapembedza ndi wosafuna kumva za wina, Yehova anam’patsa Iguputo monga “mphoto ya khamu lake” chifukwa cha ntchito imene anaichita. Kodi si zoona kuti nafenso tiyenera kutsanzira Mulungu woona mwa kulipira misonkho ku maboma chifukwa cha zimene amatichitira? Kaya olamulira akhale ndi khalidwe lotani, kaya ndalama zamisonkho akuzigwiritsa ntchito mu njira yotani, ife sitifunikira kusiya kulipira misonkho.​—Aroma 13:4-7.

33:7-9. Akhristu odzozedwa omwe ndi gulu la makono la mlonda limodzi ndi a nkhosa zina, safunikira kulephera kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kuchenjeza anthu za “chisautso chachikulu” chomwe chikubwera.​—Mateyo 24:21.

33:10-20. Tikasiya njira zoipa ndi kuchita zimene Mulungu amafuna m’pamene tingapulumutsidwe. Ndithudi, njira ya Yehova ndi ‘yoyenera.’

36:20, 21. Aisiraeli anaipitsa dzina la Mulungu pakati pa mitundu chifukwa sanachite zofuna za Yehova monga anthu ake. Tisalambire Yehova mwa dzina lokha.

36:25, 37, 38. Mu paradaiso wauzimu amene ife tilimo masiku ano muli “nkhosa za nsembe” kapena kuti gulu la anthu oyera. Choncho, tiyenera kuyesetsa kukhala anthu oyera.

38:1-23. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova adzalanditsa anthu ake poukiridwa ndi Gogi wa kudziko la Magogi. Gogi ndi dzina la “wolamulira wa dzikoli,” yemwe ndi Satana Mdyerekezi. Anapatsidwa dzina limeneli kuchokera pamene anachotsedwa kumwamba. Dziko la Magogi ndi malo kumene Satana ndi ziwanda zake ali.​—Yohane 12:31; Chivumbulutso 12:7-12.

‘UIKE MTIMA WAKO PA ZONSE NDIDZAKUONETSA IWE’

(Ezekieli 40:1–48:35)

Chinali chaka cha 14 kuchokera pamene Yerusalemu anawonongedwa. (Ezekieli 40:1) Apa n’kuti kutatsala zaka 56 zokhala muukapolo. (Yeremiya 29:10) Panthawiyi Ezekieli anali ndi zaka pafupifupi 50 ndipo mwa masomphenya anatengeredwa ku dziko la Isiraeli. Ndipo anauzidwa kuti: “Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m’makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe.” (Ezekieli 40:2-4) Ezekieli anasangalala kwambiri kuona masomphenya a kachisi watsopano.

Kachisi waulemerero amene Ezekieli anaona anali ndi zipata 6, zipinda zodyera 30, malo opatulika, malo opatulikitsa, guwa la nsembe la mtengo ndi guwa la nsembe zopsereza. Kuchokera ku kachisiyo kunayenda mtsinje umene madzi ake ankachulukirachulukira  kufikira ku chidikha. (Ezekieli 47:1) Ezekieli anaonanso masomphenya a malo omwe mafuko onse anagawiridwa. Gawo lililonse linali kuyambira ku m’mawa mpaka kumadzulo ndipo pakati pa malire a Yuda ndi malire a Benjamini panali kachigawo ka oyang’anira. “Malo opatulika a Yehova” ndiponso “mudzi” zinali pa kachigawo kameneka.​—Ezekieli 48: 9, 10, 15, 35.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

40:3–47:12—Kodi Kachisi wa m’masomphenya a Ezekieli akuimira chiyani? Kachisi wamkulu kwambiri amene Ezekieli anaona m’masomphenya sanamangidwe padziko lapansi. Anaimira kachisi wauzimu wa Mulungu kutanthauza dongosolo lake la kulambira koyera masiku ano, lomwe ndi lofanana ndi kachisi. (Ezekieli 40:2; Mika 4:1; Aheberi 8:2; 9:23, 24) Masomphenya a kachisiyu akukwaniritsidwa “m’masiku otsiriza,” pamene ansembe akuyeretsedwa. (2 Timoteyo 3:1; Ezekieli 44:10-16; Malaki 3:1-3) Koma kukwaniritsidwa komaliza kudzachitika m’Paradaiso. Kachisi wa m’masomphenyayo anapatsa Ayuda amene anali mu ukapolo chiyembekezo chakuti kulambira koyera kudzayambiranso akadzabwerera kwawo ndipo banja lililonse lidzakhala ndi malo ake.

40:3–43:17—Kodi kuyesa kachisi kukutanthauzanji? Kuyesa kachisi ndi chizindikiro chakuti cholinga cha Yehova chokhudza kulambira koyera chidzakwaniritsidwadi.

43:2-4, 7, 9—Kodi “mitembo ya mafumu awo” yomwe inafunika kuchotsedwa m’kachisi inali chiyani? Zikuoneka kuti mitemboyo inali mafano. Olamulira a ku Yerusalemu ndi anthu awo anaipitsa kachisi wa Mulungu ndi mafano moti mafanowo anali ngati mafumu awo.

43:13-20—Kodi guwa la nsembe m’masomphenya a Ezekieli likuimira chiyani? Guwa la nsembe lophiphiritsa likuimira chifuniro cha Mulungu mogwirizana ndi nsembe ya dipo ya Yesu Khristu. Chifukwa cha nsembeyi, odzozedwa amayesedwa olungama ndipo “khamu lalikulu” limayeretsedwa pamaso pa Mulungu. (Chivumbulutso 7:9-14; Aroma 5:1, 2) Mwina n’chifukwa chake “thawale lamkuwa” la m’kachisi wa Solomo silikupezeka m’kachisi wa m’masomphenya a Ezekieli. Thawale lamkuwa limeneli linali chibeseni chachikulu chomwe ansembe ankagwiritsa ntchito posamba.​—1 Mafumu 7:23-26.

44:10-16—Kodi ansembe akuimira ndani? Ansembe akuimira gulu la Akhristu odzozedwa masiku ano. Iwo anayeretsedwa mu 1918 pamene Yehova anayamba “kuyenga ndi kuyeretsa” m’kachisi wake wauzimu. (Malaki 3:1-5) Amene anali oyera kapena kuti omwe analapa anapitiriza utumiki wawo. Kenako anayesetsa kukhala ‘opanda thotho la dziko,’ motero anakhala chitsanzo chabwino kwa “khamu lalikulu” limene likuimiridwa ndi mitundu yomwe sinali ya ansembe.​—Yakobe 1:27; Chivumbulutso 7:9, 10.

45:1; 47:13–48:29—Kodi “dziko” ndi magawidwe ake zikuimira chiyani? Dziko likuimira malo amene anthu a Mulungu amachitirako utumiki wawo. Kulikonse kumene wolambira Yehova angakhale, iye amakhalabe m’dzikolo malinga ngati akuchirikiza kulambira koyera. Ndipo magawidwe a dziko adzakwaniritsidwa komaliza m’dziko latsopano  pamene munthu aliyense wokhulupirika adzapatsidwa malo ake.​—Yesaya 65:17, 21.

45:7, 16—Kodi chopereka cha anthu kwa ansembe ndi akalonga chikutanthauzanji? M’kachisi wauzimu, chopereka chimenechi kwenikweni chikutanthauza thandizo limene anthu anali kupereka ndiponso mzimu wogwirizanika womwe anali nawo.

47:1-5—Kodi madzi a mumtsinje wa m’masomphenya a Ezekieli akuimira chiyani? Madzi akuimira zinthu zopatsa moyo zimene Yehova wakonza monga nsembe ya dipo ya Yesu Khristu ndi malangizo a Mulungu opezeka m’Baibulo. (Yeremiya 2:13; Yohane 4:7-26; Aefeso 5:25-27) Madzi a mumtsinjewu akuchulukirachulukira kuti anthu atsopano omwe akubwera athe kuyamba kulambira koona. (Yesaya 60:22) Mumtsinjewu mudzayenda madzi amphamvu kwambiri opatsa moyo m’kati mwa zaka 1,000, ndipo madziwo adzaphatikizapo kuphunzira mfundo zina za m’mipukutu yomwe idzafunyululidwe.​—Chivumbulutso. 20:12; 22:1, 2

47:12—Kodi mitengo yobala zipatso ikuimira chiyani? Mitengo yophiphiritsa ikuimira zinthu zauzimu zimene Mulungu wakonza kuti zidzathandize anthu kukhalanso angwiro.

48:15-19, 30-35—Kodi mudzi wa m’masomphenya a Ezekieli ukuimira chiyani? Mudziwu uli m’malo “wamba” zomwe zikusonyeza kuti ukuimira zinthu za padziko lapansi. Motero, zikuoneka kuti mudziwu ukuimira uyang’aniro wa padziko lapansi umene ukuthandiza anthu odzakhala mu “dziko latsopano” lolungama. (2 Petulo 3:13) Mudziwu uli ndi zipata mbali zonse ndipo zimenezi zikusonyeza kuti ndi wosavuta kulowamo. Choncho oyang’anira m’gulu la Mulungu ayenera kukhala omasuka kucheza ndi anthu ena.

Zimene Tikuphunzirapo:

40:14, 16, 22, 26. Mitengo yosema ya kanjedza yomwe ili pamakoma pakhomo la kachisi ikusonyeza kuti, anthu amakhalidwe abwino okha ndi amene amaloledwa kulowamo. (Salmo 92:12) Zimenezi zikutiphunzitsa kuti Yehova amavomereza kulambira kwathu kokha ngati tili ndi makhalidwe abwino.

44:23. Ndife oyamikira kwambiri chifukwa cha utumiki umene gulu la ansembe amakono akuchita. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akutsogolera pa ntchito yopereka chakudya cha panthawi yake. Chakudya chimenenchi chimatithandiza kuzindikira kusiyana kwa zinthu zoyera ndi zosayera pamaso pa Yehova.​—Mateyo 24:45.

47:9, 11. Mbali yaikulu ya madzi ophiphiritsa ndi kudziwa Mulungu komwe kwakhala kothandiza kwambiri masiku ano. Kulikonse kumene anthu amadziwa Mulungu amakhala amoyo mwauzimu. (John 17:3) Koma anthu amene amakana madzi opatsa moyo adzawonongedwa. N’chifukwa chake n’kofunika kuti tichite zonse zimene tingathe ‘kulondoloza bwino mawu a choonadi.’​—2 Timoteyo 2:15.

“Ndidzazindikiritsa Dzina Langa Lalikulu”

Mfumu yomaliza m’mzere wa Davide itachotsedwa, Mulungu woona analola kuti papite nthawi yaitali asanabwezeretse ufumu kwa munthu yemwe ndi “mwini chiweruzo.” Koma Mulungu sanaswe pangano lake ndi Davide. (Ezekieli 21:27; 2 Samueli 7:11-16) Ulosi wa Ezekieli umanena kuti “mtumiki wanga Davide” adzakhala “mbusa” ndiponso “mfumu.” (Ezekieli 34:23, 24; 37:22, 24, 25) Ameneyu si wina ayi koma Yesu Khristu mu Ufumu wake. (Chivumbulutso 11:15) Ndipo kudzera mu Ufumu wa Mesiya, Yehova ‘adzazindikiritsa dzina lake lalikulu.’​—Ezekieli 36:23.

Posachedwapa onse amene amadetsa dzina loyera la Mulungu adzawonongedwa. Koma amene amaliyeretsa mwa kulambira Yehova m’njira yoyenera adzalandira moyo wosatha. Motero tiyeni tigwiritse ntchito kwambiri madzi opatsa moyo amene akuyenda masiku ano ndipo tiike patsogolo kulambira koona m’moyo wathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Nkhani yofotokoza Ezekieli 1:1 mpaka 24:27 mungaipeze mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2007 pamutu wakuti, “Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezekieli​—Gawo 1.”

[Chithunzi patsamba 9]

Uyu ndiye kachisi waulemerero amene Ezekieli anaona m’masomphenya

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi mtsinje wa madzi a moyo m’masomphenya a Ezekieli ukuimira chiyani?

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.