Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Munthu Wauzimu Ndi Wotani?

Kodi Munthu Wauzimu Ndi Wotani?

 Kodi Munthu Wauzimu Ndi Wotani?

PAULALIKI wake wa paphiri, Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyo 5:3) Mwina inunso mukuvomereza zimenezi. Anthu kulikonse amazindikira kufunika kokhala munthu wauzimu ndipo amaganiza kuti akatero, adzakhala anthu osangalala. Koma kodi munthu wauzimu ndi wotani?

Buku lina lotanthauzira mawu limati “munthu wauzimu amakonda kupembedza” ndipo “amakhala woopa Mulungu.” Choncho, mawu akuti “munthu wauzimu” amafanana ndi mawu akuti “munthu wokonda zauzimu.” Kuti timvetse bwino, tiyeni tiganizire chitsanzo ichi: Munthu waluso pamalonda amatchedwa munthu wokonda bizinesi. Munthunso amene amaona kufunika kwa zinthu zauzimu kapena kupembedza amatchedwa munthu wokonda zauzimu.

Nanga kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti akhaledi wauzimu? Ngakhale kuti chipembedzo chilichonse chimati chikudziwa mmene munthu angakhalire wauzimu, zipembedzo zimapereka malangizo ambiri osiyanasiyana. Apolotesitanti amanena za kupulumutsidwa pamisonkhano yawo yachitsitsimutso. Akatolika amafuna kuyanjanitsidwa ndi Mulungu pa Misa. Abuda amasinkhasinkha pofuna kuzindikira zinthu zauzimu. Ahindu amayesetsa kukhala odzikana kuti amasuke ku moyo wongobadwabadwa. Kodi ndi njira zonsezi, kapena ndi imodzi yokha pa zimenezi, imene ingathandize munthu kukhaladi wauzimu?

Ambiri amati yankho lake ndi ayi. Iwo amakhulupirira kuti kukhala munthu wauzimu kumatanthauza kukhulupirira mulungu popanda kukhala m’chipembedzo chilichonse. Ena amaganiza kuti kukhala munthu wauzimu sikukonda zachipembedzo, koma kukhala ndi mtima wofuna mtendere ndi kudziwa cholinga cha moyo. Iwo amati amene akufuna kukhala anthu auzimu safunikira n’komwe chipembedzo. Amati chipembedzo ndi mtima wa munthu. Munthu wina analemba kuti: “Kukhaladi munthu wauzimu kumadalira mmene munthuwe ukumvera mu mtima; mmene umakondera anthu ndi mmene umakhudzidwira ndi zinthu m’dzikoli. Sikukhala m’chipembedzo ayi.”

Apa ndi zoonekeratu kuti anthu amasiyana kwambiri maganizo ponena za munthu wauzimu. Pali mabuku ambiri amene amati angathandize munthu kukhala wauzimu, koma owerenga mabukuwa sakhutira ndi zimene awerengazo ndipo amangosokonezeka nazo maganizo. Ngakhale zili choncho, lilipo buku lina limene lili ndi malangizo odalirika pankhani zauzimu. Buku limeneli limapereka umboni wokwanira wakuti amene analiuzira ndi Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Tiyeni tione zimene bukulo, Baibulo, limaphunzitsa ponena za munthu wauzimu ndiponso kufunika kokhala munthu wotero.

 [Mawu a Chithunzi patsamba 2]

COVER: Background: © Mark Hamblin/​age fotostock