Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Chenjerani ndi Kusirira kwa Nsanje kwa Mtundu Uliwonse”

“Chenjerani ndi Kusirira kwa Nsanje kwa Mtundu Uliwonse”

 “Chenjerani ndi Kusirira kwa Nsanje kwa Mtundu Uliwonse”

“Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”​—LUKA 12:15.

1, 2. (a) Kodi mwaona kuti anthu ali ndi maganizo otani masiku ano? (b) Kodi ifeyo tingakhudzidwe motani ndi maganizo oterowo?

TAGANIZIRANI zinthu izi: Ndalama, katundu, ulemu, ntchito yapamwamba, ndiponso banja. Izi ndi zina mwa zinthu zimene anthu ambiri amaziona kuti n’zotsimikizira kuti munthu ali ndi moyo wabwino kapena tsogolo lodalirika. N’zoonekeratu kuti m’mayiko olemera ndi osauka omwe, maganizo a anthu ambiri ali pa kupeza chuma ndiponso kukhala moyo wotukuka. Koma chidwi chawo pazinthu zauzimu chikucheperachepera.

2 Izi zikungofanana ndi zimene Baibulo linalosera. Linanena kuti: “M’masiku otsiriza, idzafika nthawi yovuta yoikika. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma mphamvu ya kulambira Mulungu siitha kuwasintha.” (2 Timoteyo 3:1-5) Popeza kuti tikukhala ndi anthu oterewa, ife Akhristu oona tiyenera kuyesetsa nthawi zonse kuti tisatengere maganizo ndi moyo umenewu. Kodi n’chiyani chingathandize kuti dzikoli ‘lisatikanikizire m’chikombole chake’?​—Aroma 12:2, The New Testament in Modern English, lomasuliridwa ndi J. B. Phillips.

3. Kodi tsopano tiganizira malangizo otani amene Yesu anapereka?

3 Monga “Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu,” Yesu Khristu anatipatsa phunziro lamphamvu kwambiri pankhani imeneyi. (Aheberi 12:2) Nthawi inayake, Yesu akulankhula ndi gulu la anthu pankhani zina zauzimu, munthu wina anam’dula mawu, n’kupempha kuti: “Mphunzitsi, mundiuzireko m’bale wanga kuti andigawireko cholowa.” Poyankha, Yesu anapereka malangizo amphamvu kwa munthuyo ndiponso kwa anthu ena onse omwe anali kumvetsera. Anachenjeza mwamphamvu za kusirira kwa nsanje ndipo anatsindika chenjezolo ndi fanizo logwira mtima kwambiri. Tiyeni tiganizire mofatsa zimene Yesu ananena pa nthawiyo ndiponso mmene tingapindulire pozigwiritsira ntchito m’moyo wathu.​—Luka 12:13-21.

Pempho Losayenera

4. Kodi n’chifukwa chiyani munthu uja sanayenera kum’dula mawu Yesu?

4 Munthu uja asanam’dule mawu, Yesu ankafotokozera ophunzira ake ndiponso anthu ena za kupewa chinyengo, kufunika koti munthu azilimba mtima n’kuvomereza kuti ndi wogwirizana ndi Mwana wa munthu, ndiponso za kuthandizidwa ndi mzimu woyera. (Luka 12:1-12) Kunena zoona, izi ndi mfundo zofunika kwambiri zimene ophunzirawo sanafunike kuzinyalanyaza. Koma Yesu ali m’kati mofotokoza zinthu zogwira mtimazi, munthu uja anam’dula mawu, n’kumupempha kuti awaweruze pa kusamvana kumene anali nako ndi m’bale wake pankhani ya chuma. Pankhani imeneyi pali mfundo zofunika kwambiri zimene tingaphunzirepo.

5. Kodi pempho la munthu uja linasonyeza zinthu zotani zimene zinali mu mtima mwake?

5 Anthu amati, “khalidwe lenileni la munthu limaonekera m’zinthu zimene amaganizira pamene iye akumvetsera malangizo auzimu.” Yesu ali m’kati molankhula zinthu zofunika kwambiri zauzimu, zikuoneka kuti munthu uja anali kuganizira njira zoti apezere chuma. Baibulo silifotokoza ngati munthuyo anali ndi zifukwa zomveka zodandaulira  pankhani ya cholowacho. N’kutheka kuti iye ankafuna kupezerapo mwayi pa udindo wa Yesu ndiponso mbiri yake yoweruza mwanzeru zochita za anthu. (Yesaya 11:3, 4; Mateyo 22:16) Mulimonse mmene zinalili, pempho lake linasonyeza kuti iye anali ndi vuto lalikulu mumtima mwake, losayamikira zinthu zauzimu ngakhale pang’ono. Pamenepa tikuonapo kufunika koti tizidziunika mumtima mwathu nthawi zonse. Mwachitsanzo, pamisonkhano yachikhristu, n’zosavuta kulekerera maganizo athu kuyamba kuyendayenda. M’malo mwake, tiyenera kumvetsera mwatcheru zimene zikunenedwa ndi kuona mmene tingazigwiritsire ntchito. Ndipo tizichita zimenezi n’cholinga choti zitithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, komanso ndi Akhristu anzathu.​—Salmo 22:22; Maliko 4:24.

6. N’chifukwa chiyani Yesu anakana pempho la munthu uja?

6 Sitikudziwa zimene zinachititsa munthu uja kupempha Yesu kuti amuweruzire nkhani yake, koma Yesu anakana kutero. M’malo mwake, Yesu anam’funsa kuti: “Munthu iwe, ndani anandiika ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma chanu?” (Luka 12:14) Apa, Yesu ananena za zinthu zimene anthuwo ankazidziwa bwino kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti malinga ndi Chilamulo cha Mose, m’mizinda munkaikidwa anthu oweruza nkhani zoterezi. (Deuteronomo 16:18-20; 21:15-17; Rute 4:1, 2) Komanso ntchito yofunika kwambiri kwa Yesu inali yolengeza choonadi cha Ufumu ndi kuphunzitsa anthu chifuniro cha Mulungu. (Yohane 18:37) Potsatira chitsanzo cha Yesu, timagwiritsira ntchito nthawi ndi mphamvu zathu kulalikira uthenga wabwino ndi ‘kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse,’ m’malo motanganidwa ndi zinthu zosafunikira kwenikweni.​—Mateyo 24:14; 28:19.

Chenjerani ndi Kusirira kwa Nsanje

7. Kodi ndi mfundo yogwira mtima iti imene Yesu anatchula?

7 Popeza kuti Yesu ankatha kudziwa zinthu za mumtima mwa munthu, iye anazindikira kuti munthu uja anali ndi maganizo olakwika pom’pempha kuti alowerere nkhani yosam’khudza. Motero m’malo mongokana pempho lake, Yesu anatchula vuto lenileni limene munthu uja anali nalo. Iye anati: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwa mtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”​—Luka 12:15.

8. Kodi kusirira kwa nsanje n’kutani, ndipo kungakhale ndi zotsatirapo zotani?

8 Malinga ndi zimene limanena buku lina lotanthauzira mawu, kusirira kwa nsanje ndi “mtima wofunitsitsa chuma kapena katundu kapenanso kulakalaka zinthu zamwini zitakhala zako.” Izi zingaphatikizepo kulakalaka zinthuzo ndi mtima wadyera kapenanso waumbombo, n’cholinga chongofuna kukhala nazo basi. Ndipotu munthu wa mtima umenewu saganizira za ena. Zochita ndiponso maganizo ake zimangokhala pa chinthu chimene akufunacho, moti tinganene kuti chimakhala mulungu wake. Kumbukirani kuti mtumwi Paulo ananena kuti munthu waumbombo ndi wofanana ndi munthu wopembedza mafano, amene sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.​—Aefeso 5:5; Akolose 3:5.

9. Kodi mtima wosirira mwansanje ungaonekere motani? Perekani zitsanzo.

9 N’zochititsa chidwi kuti Yesu anachenjeza za “kusirira kwa nsanje kwa mtundu uliwonse.” Pali mitundu yosiyanasiyana ya kusirira kwa nsanje. Lamulo lomaliza pa Malamulo Khumi limanena ina mwa mitundu imeneyi. Lamuloli limati: “Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.” (Eksodo 20:17) M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anachita machimo akuluakulu chifukwa cha mitundu yosiyanasiyana ya kusirira kwa nsanje. Satana ndi munthu woyamba amene anasirira mwansanje chinthu chamwini. Iye anasirira ulemerero, ulemu, ndi udindo wa Yehova. (Chivumbulutso 4:11) Hava anasirira ufulu wodzilamulira, ndipo chifukwa choti iye  ananyengedwa pankhani imeneyi, anthu tonse timachimwa ndi kufa. (Genesis 3:4-7) Ziwanda ndi angelo amene sanakhutitsidwe ndi “malo awo oyambirira.” Iwo “anasiya malo awo okhala” pofuna zinthu zimene sanayenera kukhala nazo. (Yuda 6; Genesis 6:2) Taganiziraninso za Balamu, Akani, Gehazi, ndi Yudasi. Anthu amenewa, m’malo mokhutitsidwa ndi zinthu zimene anali nazo, analolera kugwiritsira ntchito molakwa udindo wawo chifukwa cholakalaka chuma. Mtima umenewu unawalowetsa m’mavuto aakulu kwambiri.

10. Kodi tiyenera kutani kuti ‘tikhale maso,’ mogwirizana ndi malangizo a Yesu?

10 M’pake kuti poyamba kuchenjeza za kusirira kwa nsanje, Yesu ananena kuti “khalani maso.” N’chifukwa chiyani anatero? Chifukwa chakuti anthu savutika kuona kuti munthu wina wayamba mtima waumbombo kapena kusirira kwa nsanje, koma sikawirikawiri pamene amavomereza kuti iwowo ali ndi vuto limeneli. Komatu, mtumwi Paulo ananena kuti “kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.” (1 Timoteyo 6:9, 10) Wophunzira Yakobe anafotokoza kuti chilakolako choipa, “chikatenga pathupi, chimabala tchimo.” (Yakobe 1:15) Mogwirizana ndi malangizo a Yesu, tiyenera ‘kukhala maso,’ osati n’cholinga choona ngati ena ali ndi mtima wosirira mwansanje, koma kuti tizidziunika kuti tione zimene zili mu mtima mwathu. Tikatero, tidzatha kupewa “kusirira kwa nsanje kwa mtundu uliwonse.”

Moyo Wokhala ndi Zochuluka

11, 12. (a) Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani ponena za kusirira kwa nsanje? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera chenjezo limeneli?

11 Pali chifukwa chinanso chopewera kusirira kwa nsanje. Taonani zimene Yesu ananena pambuyo pake: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Imeneyitu ndi mfundo yofunika kuiganizira kwambiri makamaka m’nthawi yathu ino pamene anthu ambiri ali ndi mtima wokonda chuma, ndipo amaona kuti munthu angakhale wosangalala ndiponso wopambana ngati ali wolemera. Pamenepa Yesu anasonyeza kuti kukhala ndi moyo watanthauzo ndiponso wosangalala sikudalira chuma chimene munthu ali nacho, ngakhale chitakhala chochuluka motani.

12 Komabe, anthu ena angatsutse zimenezi. Iwo anganene kuti chuma n’chofunika chifukwa chimathandiza munthu kukhala ndi moyo wabwino ndiponso watanthauzo. Choncho, iwo angathere nthawi yochuluka akuchita zinthu zimene zingawathandize kupeza katundu ndiponso zipangizo zonse zamakono zimene akufuna. Iwo amaganiza  kuti kupeza zinthu zimenezi kungawathandize kukhala ndi moyo wawofuwofu. Komatu akamaganiza choncho, amakhala akusemphana ndi mfundo imene Yesu anaphunzitsa.

13. Kodi tiyenera kuuona motani moyo ndiponso chuma?

13 M’malo mofotokoza kuti kukhala ndi chuma chambiri n’kulakwa kapena ayi, Yesu anali kutsindika mfundo yoti moyo wa munthu suchokera “m’zinthu zimene ali nazo,” kutanthauza zinthu zimene munthuyo ali nazo kale. Pankhani imeneyi, tonse tikudziwa bwino kuti kukhala ndi moyo, kapena kuusamalira, sikudalira kwenikweni kukhala ndi zinthu zambiri. Pamangofunika zakudya zochepa, chovala, ndiponso pogona basi. Anthu olemera amakhala ndi zinthu zimenezi zambiri, pamene osauka angavutikire kupeza zinthu zofunikira pamoyo. Koma paimfa sipakhala kusiyana kulikonse pakati pa osauka ndi olemera, chifukwa zonse zimathera pomwepo. (Mlaliki 9:5, 6) Choncho, kuti moyo ukhale watanthauzo, sikuti zimangodalira chuma chimene munthu angapeze kapena chimene ali nacho. Mfundo imeneyi ikuonekera bwino kwambiri tikaganizira mofatsa za moyo umene Yesu anatchula.

14. Kodi tingaphunzire zotani pamawu akuti “moyo” opezeka m’Baibulo?

14 Yesu anati ‘moyo suchokera m’zinthu zimene [munthu] ali nazo.’ Mawu akuti “moyo” m’buku la Uthenga Wabwino wa Luka (m’Chigiriki, zo·eʹ), satanthauza mmene munthu akukhalira pamoyo wake, koma amatanthauza moyo weniweniwo. * Apa mfundo ya Yesu inali yakuti, anthufe tilibe mphamvu zonse zotalikitsira moyo wathu kapena zotsimikizira kuti tsiku lotsatira tikhale ndi moyo. Zimenezi zili choncho kwa munthu aliyense, kaya ndi wolemera kapena wosauka. Mu ulaliki wake wa paphiri, Yesu anati: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?” (Mateyo 6:27) Baibulo limanena momveka bwino kuti Yehova yekha ndiye “chitsime cha moyo,” ndipo ndi iye yekha amene angapatse anthu okhulupirika “moyo weniweniwo,” kapena kuti “moyo wosatha,” kaya ndi kumwamba kapena padziko lapansi.​—Salmo 36:9; 1 Timoteyo 6:12, 19.

15. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amadalira chuma?

15 Zimene Yesu ananenazi zikusonyeza kuti anthu angasokonezeke mosavuta pamfundo ya mmene amaonera moyo. Kaya ndi olemera kapena osauka, anthu onse n’ngopanda ungwiro ndipo zimene zimawachitikira pamapeto a moyo n’zofanana. Kale kwambiri, Mose anati: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.” (Salmo 90:10; Yobu 14:1, 2; 1 Petulo 1:24) Choncho, anthu amene sali paubwenzi ndi Mulungu kawirikawiri amakhala ndi mtima womwe mtumwi Paulo anatchula, woti “tiyeni tidye ndi kumwa, popeza mawa tifa.” (1 Akorinto 15:32) Anthu ena poona kuti moyo n’ngwaufupi ndiponso wosinthasintha, amaganiza kuti chuma chingadzawathandize kukhala ndi moyo wabwino ndiponso wokhazikika. Choncho, iwo amagwira ntchito mwakhama kuti apeze chuma ndi katundu wambiri.​—Salmo 49:6, 11, 12.

 Tsogolo Lodalirika

16. Kodi moyo watanthauzo sudalira chiyani?

16 N’kutheka kuti kukhala ndi zakudya zambiri, zovala zambiri, nyumba yabwino, ndiponso zinthu zina zamakono zosangalatsa, kungam’thandize munthu kukhala ndi moyo wabwinopo. Kapena zingam’thandizenso kupeza chithandizo chabwino chamankhwala, moti angathe kukhala moyo wotalikirapo. Komabe, kodi moyo woterowo ndi watanthauzodi ndiponso wodalirika? Kutalika kwa moyo wa munthu ndiponso kuchuluka kwa chuma chake, sikuthandiza kudziwa kuti iye ali ndi moyo watanthauzo. Mtumwi Paulo anatchula za vuto limene limakhalapo ngati munthu akudalira kwambiri chuma. Anauza Timoteyo kuti: “Lamula achuma m’dongosolo ili la zinthu kuti asakhale odzikweza, ndi kuti asadalire chuma chosadalirika, koma adalire Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.”​—1 Timoteyo 6:17.

17, 18. (a) Pankhani yokhala ndi chuma, kodi ndi zitsanzo zabwino ziti zimene tifunika kutsanzira? (b) M’nkhani yotsatira, kodi tikambirana fanizo liti limene Yesu anapereka?

17 Kudalira chuma n’kupanda nzeru chifukwa chuma ‘n’chosadalirika.’ Yobu anali wolemera kwambiri, koma pamene anakumana ndi tsoka mwadzidzidzi, chuma chake sichinam’thandize. Chuma chake chonse chinatheratu nthawi yomweyo. Koma kukhala paubwenzi wolimba ndi Mulungu, n’komwe kunam’thandiza kupirira mayesero ndiponso mavuto onsewo. (Yobu 1:1, 3, 20-22) Abulahamu anali wolemera kwambiri, koma sanalole kuti chuma chake chimulepheretse kuvomera utumiki wovuta umene Yehova anam’patsa. Chifukwa cha zimenezi, iye anadalitsidwa n’kukhala “atate wa khamu la mitundu.” (Genesis 12:1, 4; 17:4-6) Anthu amenewa ndiponso zitsanzo zina ndi oyenera kuti tiwatsanzire. Tonsefe, ana ndi akulu omwe, tiyenera kumadziunika kuti tione zinthu zomwe tikuona kuti n’zofunika kwambiri m’moyo wathu ndiponso zomwe timadalira.​—Aefeso 5:10; Afilipi 1:10.

18 Kunena zoona, tapindula kwambiri ndi mawu ochepa amene Yesu ananena pa nkhani ya kusirira kwa nsanje ndiponso kuona moyo moyenerera. Komabe, Yesu analinso ndi malangizo ena, ndipo anapereka fanizo logwira mtima, lokhuza munthu wina wachuma wopanda nzeru. Kodi fanizo limenelo n’lothandiza motani masiku ano, ndipo lingatiphunzitse chiyani? Nkhani yotsatira iyankha mafunso amenewa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Mawu ena a Chigiriki omwe amamasuliridwa kuti “moyo” ndi biʹos. Mawu amenewa amatanthauza “nyengo yokhala ndi moyo,” “kakhalidwe ka moyo,” ndiponso “zinthu zochirikiza moyo.”​—Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words.

 Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yesu anachita pokana pempho la munthu wina?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuchenjera ndi kusirira kwa nsanje, ndipo tingachite bwanji zimenezo?

• N’chifukwa chiyani moyo suchokera m’zinthu zimene munthu ali nazo?

• Kodi n’chiyani chomwe chingapangitse moyo kukhala watanthauzo ndiponso wodalirika?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Kusirira kwa nsanje kungalowetse munthu m’mavuto aakulu kwambiri

[Chithunzi patsamba 23]

N’chifukwa chiyani Yesu anakana pempho la munthu wina?

[Zithunzi patsamba 25]

Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankaona chuma moyenerera?