Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tinali Osiyana Zinenero Koma Chikondi Chinatigwirizanitsa”

“Tinali Osiyana Zinenero Koma Chikondi Chinatigwirizanitsa”

 “Tinali Osiyana Zinenero Koma Chikondi Chinatigwirizanitsa”

Kwa zaka zambiri, anthu akhala akufuna kuwomboledwa ku mavuto awo. Akhala akufuna ufulu ndi chipulumutso. Kodi tingathane nawo bwanji mavuto athu? Kodi chipulumutso chidzafikadi? Nanga chidzafika bwanji?

ZIMENEZI ndi nkhani zimene zinakambidwa pa msonkhano wachigawo wamasiku atatu wa Mboni za Yehova, umene unayamba mu May 2006. Mutu wake unali wakuti “Chipulumutso Chayandikira.”

Pamisonkhano ina 9 panali anthu zikwizikwi ochokera ku mayiko osiyanasiyana. Misonkhano imeneyi inachitika kuyambira mu July mpaka August 2006, ku Prague, likulu la dziko la Czech Republic; Bratislava, likulu la dziko la Slovakia; Chorzow ndi Poznan, ku Poland; * ndi m’mizinda isanu ya ku Germany iyi: Dortmund, Frankfurt, Hamburg, Leipzig, ndi Munich. Kumisonkhano yonseyi kunali anthu oposa 313,000.

Kodi pamisonkhanoyi panali zochitika zotani? Kodi anthu ananena zotani zokhudza misonkhano imeneyi? Ndipo kodi osonkhanawo anamva bwanji misonkhanoyi itatha?

Kukonzekera

Alendo ndiponso Mboni zakomweko zinali kuyembekezera mwachidwi msonkhanowo podziwa kuti udzakhala wosaiwalika ndi wolimbikitsa mwauzimu. Panali ntchito yaikulu yopezera alendo malo ogona. Mwachitsanzo, kumsonkhano wa ku Chorzow, ku Poland, Mboni zinalandira alendo pafupifupi 13,000 m’nyumba zawo ochokera ku mayiko a kum’mawa kwa Ulaya. Alendowo anachokera ku Armenia, Belarus, Estonia, Georgia, Kazakhstan, Kyrgyzstan, Latvia, Lithuania, Moldova, Russia, Tajikistan, Turkmenistan, Ukraine, United States, ndi Uzbekistan.

Ambiri anayamba kukonzekera ulendo wawo kudakali miyezi yambiri. Mwachitsanzo, Tatiana, mlaliki wa nthawi zonse ku Kamchatka, dera la Russia kumpoto koma chakum’mawa kwa Japan, anayamba kusunga ndalama zoyendera kudakali chaka chathunthu. Anayenda makilomita pafupifupi 10,500. Anayamba kuyenda maola asanu pandege, masiku atatu pasitima ya pamtunda, ndiponso maola 30 pabasi kukafika ku Chorzow.

Anthu zikwizikwi anadzipereka kugwira ntchito yokonzekera msonkhano, yoyeretsa mabwalo a masewera kuti akhale oyenera kulambiriramo. (Deuteronomo 23:14) Kungotchulapo chitsanzo chimodzi, ku Leipzig  Mboni zinagwira ntchito yotamandika yoyeretsa bwalo la masewera, ndipo zinalonjeza kukonzanso malowo msonkhano ukatha. Akuluakulu oyang’anira bwalolo ataona zimenezi, anawauza kuti pandalama zolipirira malowo achotserapo ndalama zambiri zoyeretsera.

Ntchito Yoitana Anthu

Mipingo padziko lonse inalengeza kwambiri za msonkhano wachigawo wakuti “Chipulumutso Chayandikira.” Anthu amene anali kukonzekera kupita ku misonkhano yapadera imeneyi anachita khama pantchito yoitanira anthu kumsonkhano. Anapitiriza kulengeza za misonkhanoyo mpaka usiku woti mawa lake misonkhano iyamba. Kodi khama lawo linabala zipatso zilizonse?

Bogdan, Mboni ya ku Poland, anakumana ndi mwamuna wina wachikulire amene anafuna kupita nawo kumsonkhano koma analibe ndalama zokwanira kuyenda ulendo wa makilomita 120 kukafika ku Chorzow. Koma mwamwayi, m’basi imene mpingo unachita hayala munatsala malo a munthu mmodzi. Bogdan anati: “Tinamuuza mkuluyo kuti atha kupita nafe osalipira ngati atakapezeka pa malo okwerera basiyo nthawi ya 5:30 m’mawa.” Munthuyo anavomera ndipo anapita nawo kumsonkhano. Kenako anawalembera abalewo kalata kuwauza kuti: “Kuchokera pa msonkhano uja, ndikuyesetsa kukhala munthu wabwino.”

Ku Prague mwamuna wina amene anali kukhala ku hotela komwe kunali alendo ochokera ku Britain anauza alendowo tsiku lina madzulo kuti nayenso anapita nawo kumsonkhanowo. N’chiyani chinamuchititsa kupita nawo? Mwamunayo anati atalandira timapepala toitanira anthu kumsonkhano kwa ofalitsa 10 mumsewu, anaona kuti anafunikira kupita basi. Anasangalala kwambiri ndi msonkhanowo ndipo anafuna kuphunzira zambiri.​—1 Timoteyo 2:3, 4.

Nkhani Zauzimu Zolimbikitsa

Pamsonkhanopo panakambidwa nkhani zosonyeza zimene tingachite tikakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Panaperekedwa malangizo a m’Malemba osapita m’mbali othandiza kuthana ndi mavuto kapena kupirira.

Anthu ovutika ndi ukalamba, matenda, imfa ya achibale kapena mavuto ena analandira malangizo olimbikitsa a m’Baibulo owathandiza kupirira. (Salmo 72:12-14) Anthu apabanja ndi makolo anamva malangizo a m’Baibulo onena za mmene angakhalire ndi banja losangalala ndi mmene angalerere bwino ana awo. (Mlaliki 4:12; Aefeso 5:22, 25; Akolose 3:21) Akhristu achinyamata amene amalangizidwa za Mawu a Mulungu kunyumba ndi kumpingo koma amene akakhala ku sukulu, anzawo amawanyengerera kuchita zinthu zoipa, analandira malangizo owathandiza kuti asanyengeke ndi anzawo koma kuti ‘athawe zilakolako za unyamata.’​—2 Timoteyo 2:22.

Uwu Ndiyedi Ubale wa Padziko Lonse

Mboni za Yehova zikakhala pamisonkhano yawo, zimalandira malangizo abwino a m’Malemba. (2 Timoteyo 3:16) Koma misonkhano yachigawo imeneyi inali yapadera chifukwa chakuti kunali anthu ochokera ku mayiko osiyanasiyana. Kumisonkhano yonseyi kunakambidwa  nkhani zofanana koma m’zinenero zosiyanasiyana. Tsiku lililonse, abale a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ankakamba nkhani, komanso panali kuperekedwa malipoti osangalatsa ochokera ku mayiko ena. Nkhani ndi malipoti amenewa ankazimasulira kuti anthu azinenero zosiyanasiyana athe kumva.

Osonkhanawo ankafunitsitsa kuonana ndi abale ndi alongo ochokera ku mayiko ena. Mmodzi wa iwo anati: “Kusiyana zinenero sikunali vuto. M’malo mwake, kunachititsa kuti msonkhano ukhale wosangalatsa. Chikhalidwe cha alendowo chinali chosiyanasiyana, koma tonse tinali ogwirizana pa chikhulupiriro chimodzi.” Anthu amene anasonkhana ku Munich anati: “Tinali osiyana zinenero koma chikondi chinatigwirizanitsa.” Kaya anali ochokera kuti, kaya anali achinenero chanji, onsewo anaona kuti anali mabwenzi enieni, inde, abale ndi alongo auzimu.​—Zekariya 8:23.

Mawu Oyamikira

Kumisonkhano ya ku Poland nyengo sinali bwino ndipo panafunika chikhulupiriro ndi kupirira kuti munthu akhalepo. Nthawi zambiri kunkagwa mvula ndipo kunkazizira kwambiri. M’bale wina wa ku United States anati: “Sindinaonepo nyengo yoipa ndi yozizira kwambiri ngati imeneyi pamsonkhano, ndipo nkhani zambiri sindinazimve bwinobwino. Komabe ndinasangalala kuona abale ochokera ku mayiko osiyanasiyana, mgwirizano wabwino, ndi mtima wosasimbika wochereza alendo. Msonkhano umenewu unali wosaiwalika!”

Chinthu china chosaiwalika kwa anthu olankhula Chipolishi pamsonkhanopo chinali kutulutsidwa kwa buku lakuti Insight on the Scriptures m’chinenero chawo. Amenewa anali ngati malipiro a kupirira kwawo mvula ndi kuzizira. Ndiponso, pamisonkhano yonse yakuti “Chipulumutso Chayandikira,” anthu anasangalala ndi kutulutsidwa kwa buku lakuti Live With Jehovah’s Day in Mind.

Ambiri amene anapitako ali ndi zifukwa zina zimene sadzaiwalira msonkhanowo. Mwachitsanzo, Kristina, mlongo wachitcheki amene anadzipereka kuperekeza basi ya alendo ochokera kunja, anati: “Potsazikana, mlongo wina ananditengera pambali, kundikumbatira, ndi kundiuza kuti: ‘Komatu mwatisamalira! Munali kutibweretsera chakudya ndi madzi akumwa mpaka kumipando yathu. Zikomo kwambiri chifukwa cha chikondi ndi kudzipereka kwanu.’” Apa mlongoyo anali kunena za chakudya chamasana cha alendo ochokera kunja. M’bale wina anafotokoza kuti: “Ntchito yosamalira alendo chonchi sitinaichitepo. Tsiku lililonse tinkagawira chakudya anthu pafupifupi 6,500. Zinali zosangalatsa kuona kuti anthu ambiri, kuphatikizapo ana, anadzipereka pa ntchitoyi.”

Mlongo wina amene anapita ku msonkhano wa ku Chorzow kuchokera ku Ukraine anati: “Tachita chidwi kwambiri ndi chikondi, chisamaliro komanso ndi mmene okhulupirira anzathu anatilandirira bwino. Tikusowa mawu othokozera.” Mtsikana wina wa zaka 8 dzina lake Annika wa ku Finland analembera kalata ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Poland kuti: “Sindinayembekezere kuti msonkhano ungakhale wabwino chonchi. Ndi chinthu chabwino kukhala m’gulu la Yehova chifukwa munthu umakhala ndi anzako padziko lonse.”​—Salmo 133:1.

Ndemanga za Anthu Ena

Misonkhano isanayambe, alendo ena anaperekezedwa kukaona malo. Atafika ku midzi  ya ku Bavaria, alendowo anaima pa Nyumba za Ufumu, kumene analandiridwa bwino ndi Mboni zakomweko. Woperekeza alendo wina yemwe sanali wa Mboni anachita chidwi kwambiri ndi ubale umenewu. Mlendo wina ananena kuti: “Tili m’basi kubwerera ku hotela, woperekeza alendo ananena kuti tinali osiyana kwambiri ndi magulu ena okaona malo. Anati tinavala bwino ndipo sitinavutane ndi amene ankatitsogolera. Panalibe kutukwana kapena chisokonezo. Anadabwa kwambiri kuona kuti anthu oti sanaonanepo n’kukhala mabwenzi atangokumana.”

M’bale wina amene anagwira ntchito ku Dipatimenti ya Nkhani za M’nyuzi ku msonkhano wa ku Prague anati: “Lamlungu m’mawa, mkulu wa apolisi omwe anaikidwa kuti ayang’anire msonkhanowo anabwera ku malo amsonkhano. Anaona kuti pamsonkhanopo panali bata ndipo anati alibe ntchito yoti agwire. Ananenanso kuti anthu apafupi ndi malowo ankafunsa kuti adziwe zimene zinali kuchitika pamalopa. Mkuluyo akayankha kuti umenewu unali msonkhano wa Mboni za Yehova, anthuwo anali kuda nkhawa. Kenako mkuluyo anali kuwauza kuti: ‘Ngati anthu akanati ayese ngakhale pang’ono kukhala ngati a Mboni za Yehova, apolisi sakanakhalako.’”

Ambiri Amasuka Kale

Baibulo, Mawu a Mulungu, lili ngati mlatho wogwirizanitsa anthu azikhalidwe zosiyanasiyana ndipo limagwirizanitsa Akhristu kuti akhale mumtendere ndi umodzi. (Aroma 14:19; Aefeso 4:22-24; Afilipi 4:7) Misonkhano yapadera imeneyi ya “Chipulumutso Chayandikira” inatsimikizira mfundo imeneyi. Mboni za Yehova zamasuka kale ku mavuto ambiri a m’dzikoli. Kusagwirizana, ziwawa, ndi tsankho, kungotchula zochepa chabe, zathetsedwa ndithu pakati pawo, ndipo Mbonizo zikuyembekezera dziko lopandiratu mavuto amenewa.

Anthu amene anapita ku misonkhano imeneyi anadzionera okha umodzi umene ulipo pakati pa Mboni za ku mayiko osiyanasiyana komanso zachikhalidwe chosiyanasiyana. Zimenezi zinaonekera bwino kumapeto kwenikweni kwa misonkhanoyi. Onse anali kuomba m’manja, kukumbatirana, ndi kujambulitsa zithunzi zotsazikirana. (1 Akorinto 1:10; 1 Petulo 2:17) Ali osangalala komanso ali ndi chikhulupiriro chakuti atsala pang’ono kupulumutsidwa ku mavuto awo, osonkhanawo anabwerera ku nyumba ndi kumipingo kwawo atapezanso mphamvu zokapitirizira kugwiritsitsa ‘mawu a Mulungu a moyo.’​—Afilipi 2:15, 16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Misonkhano 6 ku Poland ndi umodzi ku Slovakia inalumikizidwa ndi misonkhano ina ya kumene kunali nkhani zokambidwa ndi alendo ochokera ku mayiko ena ndipo anthuwo ankazionerera pa TV.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]

Unali Mgwirizano wa Anthu Olankhula Zinenero 26

Kumisonkhano yonse 9, nkhani zinakambidwa mu zinenero zakomweko. Ku Germany, nkhani zinakambidwa mu zinenero zinanso 18. Ku Dortmund, nkhani zinakambidwa mu zinenero izi: Chiarabu, Chifasi, Chipwitikizi, Chisipanishi, ndi Chirasha; msonkhano wa ku Frankfurt unali mu Chingelezi, Chifalansa, ndi Chisebiya/​Chikolowesha; msonkhano wa ku Hamburg unali mu Chidanishi, Chidatchi, Chiswidishi, ndi Chitamiwu; msonkhano wa ku Leipzig unali mu Chitchaina, Chipolishi, ndi Chitheki; msonkhano wa ku Munich unali mu Chigiriki, Chitaliyana, ndi Chinenero Chamanja cha ku Germany. Msonkhano wa ku Prague unali ndi nkhani zonse mu Chitcheki, Chingelezi, ndi Chirasha. Ku Bratislava, nkhani zinakambidwa mu Chingelezi, Chihangare, Chisilovaki, ndi Chinenero Chamanja cha ku Slovakia. Ku Chorzow msonkhano unali mu Chipolishi, Chirasha, Chiyukireniya, ndi m’Chinenero Chamanja cha ku Poland. Ndipo ku Poznan, msonkhano unali mu Chipolishi ndi Chifinishi.

Zinenero zonse zinalipo 26. N’zoona kuti anthu pamisonkhanoyo anali osiyana zinenero koma chikondi chinawagwirizanitsa.

[Chithunzi patsamba 9]

Ku Frankfurt, anthu olankhula Chikolowesha anasangalala kulandira “Baibulo la Dziko Latsopano” m’chinenero chawo