Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi lemba la Miyambo 22:6 limatsimikizira kuti ana achikhristu akaphunzitsidwa bwino, ndiye kuti basi sadzasiya njira ya Yehova?

Lembali limati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” Mofanana ndi mfundo yakuti kuwongola mtengo m’poyamba, ana amene amaphunzitsidwa bwino nthawi zambiri amapitiriza kutumikira Yehova atakula. Kholo lililonse limadziwa kuti kuphunzitsa ana koteroko kumafuna nthawi ndi khama. Makolo amayenera kuphunzitsa, kulangiza, kulimbikitsa ndiponso kulanga ana awo mwachifatse limodzi ndi kuwapatsa chitsanzo chabwino, kuti anawo akhale ophunzira a Khristu. Ayenera kuchita zimenezi nthawi zonse ndiponso mwachikondi kwa zaka zambiri.

Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti mwana akasiya kutumikira Yehova ndiye kuti makolo sanam’phunzitse bwino? Nthawi zina, makolo zingawavute kulera bwino ana awo m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake. (Aefeso 6:4) Koma lemba la Miyambo limeneli silikutsimikizira kuti makolo akamaphunzitsa bwino ana awo ndiye kuti nthawi zonse adzakhala okhulupirika kwa Mulungu. Makolo sangapangitse mwana wawo kuti azichita chilichonse chimene iwowo akufuna. Mofanana ndi achikulire, ana ali ndi ufulu wosankha zochita ndipo iwowo ndi amene adzayenera kusankha zimene adzachite pa moyo wawo. (Deuteronomo 30:15, 16, 19) Ngakhale kuti makolo angayesetse kuphunzitsa bwino ana awo, ana ena amasiya kukhala okhulupirika, monga mmene Solomo yemwe analemba vesili anachitira. Ngakhale Yehova anali ndi ana omwe anasiya kukhala okhulupirika.

Motero, lembali silikutanthauza kuti nthawi zonse mwana “sadzachokamo” m’njira imene makolo anam’phunzitsa koma kuti nthawi zambiri adzakhala wokhulupirika. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri kwa makolo. Ndipo makolo angasangalale kudziwa kuti akamayesetsa kuphunzitsa ana awo m’njira ya Yehova adzakhala ndi zotsatirapo zabwino. Popeza kuti zimene makolo amachita n’zomwe zimathandiza kwambiri ana awo, iwowo ayenera kuona udindo wawo kukhala wofunika kwambiri.​—Deuteronomo 6:6, 7.

Ngakhale kuti ana angasiye kutumikira Yehova, makolo omwe anayesetsa kuphunzitsa bwino ana awo angakhale ndi chiyembekezo choti nthawi ina adzabwerera kwa Yehova. Ndipotu, choonadi cha m’Baibulo n’champhamvu kwambiri ndipo ana sangaiwale mwamsanga zimene makolo awo anawaphunzitsa.​—Salmo 19:7.