Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinapeza Chuma Chimene Tinkafufuza

Tinapeza Chuma Chimene Tinkafufuza

 Mbiri ya Moyo Wathu

Tinapeza Chuma Chimene Tinkafufuza

Yosimbidwa ndi Dorothea Smith ndi Dora Ward

Kodi ndi chuma chotani chomwe tinkafufuza? Ine ndi mnzanga tinkafunitsitsa kumvera lamulo la Yesu lakuti: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyo 28:19) Apa n’kuti tili atsikana ang’onoang’ono. Tatilolani kuti tifotokoze za chuma chokhalitsa chomwe tinapeza pa kufufuzaku.

DOROTHEA: Ndinabadwa mu 1915, nkhondo yoyamba yapadziko lonse itangoyamba kumene, ndipo ndinali mwana wachitatu m’banja mwathu. Tinkakhala pafupi ndi mzinda wa Howell ku Michigan, m’dziko la United States. Bambo anga sanali m’chipembedzo chilichonse koma mayi anga anali munthu woopa Mulungu. Mayi ankatiphunzitsa mwakhama kutsatira Malamulo Khumi koma anali ndi nkhawa yoti ine, mchimwene wanga Willis, ndi mkulu wanga Viola sitinali m’chipembedzo chilichonse.

Ndili ndi zaka 12, mayi anga anaganiza zoti ndikabatizidwe ku mpingo wa Presbyterian. Ndimakumbukira bwinobwino zimene zinachitika pa tsiku la ubatizo. Ndinabatizidwa pamodzi ndi makanda awiri, omwe anawabatiza ali m’manja mwa mayi awo. Ndinachita manyazi kwambiri kubatizidwa pamodzi ndi makanda. Abusa anandidonthezera madzi pamutu kenaka n’kunena mawu enaake monong’ona. Mofanana ndi makandawo, ineyo sindinkadziwa chilichonse chokhudza tanthauzo la ubatizo.

Tsiku lina m’chaka cha 1932, kunyumba kwathu kunabwera anthu awiri pagalimoto ndipo mayi anga anapita kukawalonjera. Anthuwa ankapereka mabuku achipembedzo, ndipo winayo anati dzina lake ndi Albert Schroeder. Iye  anawasonyeza mayi anga mabuku ena a Mboni za Yehova, ndipo iwo analandira mabukuwo. Mabuku amenewa anathandiza mayi kuvomereza choonadi cha m’Mawu a Mulungu.

Chiyambi Chofufuza Chuma Chimenechi

Patapita nthawi ndinasamukira mu mzinda wa Detroit n’kumakhala ndi mkulu wanga. Kumeneko ndinakumana ndi mayi wina wachikulire amene ankabwera ku nyumba kwathuko kuti azidzam’phunzitsa mkulu wangayo Baibulo. Zimene ankakambirana zinandikumbutsa pulogalamu ya mlungu ndi mlungu ya pawailesi imene ndinkamvetsera ndi mayi. Pulogalamuyi inkakhala ndi nkhani ya mphindi 15 yofotokoza za m’Baibulo, yokambidwa ndi J. F. Rutherford, yemwe ankatsogolera Mboni za Yehova panthawiyo. Mu 1937 tinayamba kusonkhana ndi mpingo woyamba wa Mboni za Yehova ku Detroit. Ndinabatizidwa chaka chotsatira.

Chakumayambiriro kwa m’ma 1940 Mboni za Yehova zinalengeza kuti zitsegula sukulu yotchedwa Gileadi, ku South Lansing, mumzinda wa New York, n’cholinga chophunzitsa amishonale. Nditamva zoti ena mwa ophunzira a m’sukuluyi adzatumizidwa kunja, ndinangoti, ‘Umenewu ndi mwayi wanga.’ Motero ndinakhala ndi cholinga chopita ku Gileadi. Unalitu mwayi wapadera zedi kukafufuza “chuma,” kapena kuti anthu amene akufuna kukhala ophunzira a Khristu Yesu.​—Hagai 2:6, 7.

Ndinakwaniritsa Cholinga Changa

Mu April 1942, ndinasiya ntchito yanga kuti ndikhale mpainiya, kapena kuti mtumiki wa nthawi zonse. Uku kunali ku Ohio mumzinda wa Findlay. Ndinkachita ntchitoyi pamodzi ndi alongo ena asanu. Kunalibe mpingo wokhala ndi misonkhano yokhazikika, koma tinkalimbikitsana powerengera pamodzi nkhani za m’mabuku athu. M’mwezi woyamba ndinagawira mabuku 95 kwa anthu achidwi. Patapita pafupifupi chaka ndi theka, ndinapatsidwa ntchito yotumikira monga mpainiya wapadera m’tauni ya Chambersburg ku Pennsylvania. Kumeneko ndinakakhala pamodzi ndi gulu la apainiya ena asanu, kuphatikizapo Dora Ward, mlongo yemwe anali wochokera m’boma la Iowa. Dora anadzakhala mnzanga muutumiki. Tinabatizidwa chaka chimodzi, ndipo tonse tinkalakalaka titadzapita ku Sukulu ya Gileadi n’kukatumikira kunja monga amishonale.

Chakuyambiriro kwa m’ma 1944, tsiku losaiwalikali linafika. Tonse tinalandira kalata yotiitana ku kalasi yachinayi ya Gileadi ndipo mu August chaka chomwecho tinalowa sukuluyi. Koma ndisananene zambiri, lekani Dora akuuzeni mmene zinakhalira kuti afike pokhala mnzanga pantchito yofufuza chuma.

 Ndinkafunitsitsa Kuyamba Ulaliki Wanthawi Zonse

DORA: Mayi anga ankapemphera kwa Mulungu kuti awathandize kumvetsetsa Baibulo. Tsiku lina Lamlungu, tinkamvetsera wailesi limodzi ndi mayi ndipo panali nkhani ya J. F. Rutherford. Nkhaniyo itatha, mayiwo anati, “Choonadi n’chimenechi basi!” Posakhalitsa, tinayamba kuphunzira mabuku a Mboni za Yehova. Mu 1935, ndili ndi zaka 12, ndinapita kukamvetsera nkhani ya ubatizo yokambidwa ndi Mboni za Yehova, ndipo ndinayamba kulakalaka nditapereka moyo wanga kwa Yehova. Patadutsa zaka zitatu, ndinabatizidwa. Kudzipereka kwa Mulungu ndi kubatizidwa kunandithandiza kuti ndisaiwale zolinga zanga pa zaka zonse zimene zinatsala kuti ndimalize sukulu. Ndinkangofuna kuti ndimalize sukuluyo kuti ndiyambe kuchita upainiya.

Panthawiyo mpingo wathu unkasonkhana ku Fort Dodge, ku Iowa. Tinkafunika kuchita khama zedi kuti tizipita ku misonkhanoyi. Masiku amenewo nkhani zophunziridwa za mu Nsanja ya Olonda sizinkakhala ndi mafunso okambirana mu mpingo. Wofalitsa aliyense ankapereka mafunso amene wakonzekera, kwa m’bale wochititsa Nsanja ya Olonda. Lolemba madzulo, ine ndi mayi tinkakonzekera funso pa ndime iliyonse, ndipo tinkapereka mafunsowo kwa wochititsayo kuti asankhepo.

Nthawi zambiri kumpingo kwathu kunkafika woyang’anira woyendayenda. Mmodzi wa abalewa anali John Booth, ndipo ndiye anandiphunzitsa utumiki wa khomo ndi khomo ndili ndi zaka 12. Ndili ndi zaka 17, ndinam’pempha kuti andithandize kulemba zinthu zofunika pa fomu yaupainiya, ndipo anatero. Panthawiyi sindinkadziwa kuti tidzakumananso kutsogolo ndiponso kuti tidzagwirizana kwa moyo wathu wonse.

Muutumiki wanga waupainiya, nthawi zambiri ndinkalalikira ndi mlongo Dorothy Aronson, mlaliki wa nthawi zonse amene anali wamkulu kwa ine ndi zaka 15. Tinachitira limodzi ntchitoyi mpaka panthawi imene anaitanidwa kukachita nawo kalasi yoyamba ya Gileadi mu 1943. Zitatero, ndinapitiriza kuchita upainiya pandekha.

Otitsutsa Analephera

M’ma 1940 zinthu sizinali bwino chifukwa choti nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inapangitsa kuti anthu ayambe kuchita zinthu zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo. Nthawi zambiri tikamalalikira nyumba ndi nyumba, anthu ankatigenda ndi mazira owola, tomato, ndipo ngakhale miyala imene. Koma chiyeso chathu chachikulu n’chimene tinkakumana nacho mumsewu, pogawira magazini a Nsanja  ya Olonda ndi Consolation (imene tsopano ndi Galamukani!). Apolisi omwe anachita kutumidwa ndi atsogoleri a zipembedzo, anatilondola n’kunena kuti adzatimanga akadzationanso tikulalikira.

Komabe tinakana kusiya kulalikira, motero apolisi anatitenga kuti akatifunse mafunso kusiteshoni kwawo. Atatimasula, tinabwerera pamene anatimangirapo n’kuyamba kugawira magazini omwe aja. Potsatira malangizo a akulu, anthu otitsutsa tinkawawerengera lemba la Yesaya 61:1, 2. Nthawi ina wapolisi atandipeza, ndinamuuza malembawa mwamantha. N’zodabwitsa kuti iyeyo anangotembenuka n’kumapita. Ndikuona kuti angelo ankatiteteza.

Tsiku Losaiwalika

Mu 1941, ndinasangalala kwambiri kuchita nawo msonkhano wa Mboni za Yehova wa masiku asanu ku St. Louis, m’boma la Missouri. Pamsonkhanowo, M’bale Rutherford anapempha ana onse a zaka zapakati pa 5 ndi 18 kuti akhale cha pakati pa sitediyamuyo. Ndiye panasonkhana ana ochuluka zedi. M’bale Rutherford anatibayibitsa anafe ndi kansalu kawo kam’manja. Ndiye tonse tinawabayibitsanso. Atakamba nkhani kwa ola limodzi, iye anati: “Ndikupempha ana nonse amene mwavomera kuchita chifuniro cha Mulungu n’kuyamba kuchirikiza boma lake lolamulidwa ndi Khristu Yesu, kutanthauzanso kuti mwavomereza kumvera Mulungu ndi Mfumu yake, kuti muimirire.” Atatero, ana 15,000 anaimirira ndipo ineyo ndinali mmodzi mwa iwo. Kenaka m’baleyo anati: “Nonse amene mwatsimikiza kuti muyesetsa kuuza ena za Ufumu wa Mulungu ndi za madalitso amene udzabweretse, nena kuti Inde.” Tonse tinatero, ndipo m’bwalo monsemo munadzaza phokoso la kuwomba m’manja.

Iye anatulutsa buku lakuti Children (Ana), * ndipo ana anapanga mzere wautali wopita ku pulatifomu, komwe M’bale Rutherford anali kupereka buku latsopanoli kwa mwana aliyense. Zinali zosangalatsa zedi. Panopo anthu ambiri amene analandira buku limeneli akutumikirabe Yehova mwakhama padziko lonse, ndipo akuuza ena za Ufumu ndiponso chilungamo cha Mulungu.​—Salmo 148:12, 13.

Nditachita upainiya kwa zaka zitatu pandekha, ndinasangalala kwambiri kuikidwa kuti ndikakhale mpainiya wapadera ku Chambersburg. Kumeneko ndinakumana ndi Dorothea, ndipo posakhalitsa tinakhala paubwenzi wa ponda apa m’pondepo. Tinali tidakali atsikana amphamvu zathu motero tinali okonzeka kuwonjezera ntchito yathu yolalikira. Tinayamba ulendo wofufuza chuma womwe takhala tikuuyenda limodzi kwa moyo wathu wonse.​—Salmo 110:3.

Titachita utumikiwu kwa miyezi ingapo, tinakumana ndi Albert Mann, m’bale yemwe anali m’kalasi yoyamba ya sukulu ya Gileadi. Iyeyu anali pafupi kupita kudziko limene anatumizidwako. Anatilimbikitsa kuti tivomere kupita dziko lililonse limene tingatumizidweko.

Tinali Limodzi Kusukulu

DORA NDI DOROTHEA: Tangoganizani chisangalalo chomwe tinali nacho titayamba sukulu yophunzitsa amishonale. Tsiku loyamba m’bale Albert Schroeder, yemwe anapereka buku lotchedwa Studies in the Scriptures kwa mayi a Dorothea zaka 12 zapitazo, analemba mayina athu. John Booth analinso komweko. Iye ankatumikira pa famu ya Mboni za Yehova m’dera lomwe kunali sukuluyi. Kenaka onsewa anadzakhala m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.

Kusukulu ya Gileadi tinaphunzira mfundo zozama za choonadi cha m’Baibulo. Anali maphunziro abwino kwambiri. Tinali m’kalasi ya anthu 104 ndipo munali m’bale mmodzi wa ku Mexico, yemwe anali wophunzira woyamba wochokera kunja. Iye ankayesetsa kuphunzira Chingelezi pomwe ife tinkayesetsa kuphunzira Chisipanishi. Tinasangalala kwambiri tsiku limene m’bale Nathan H. Knorr amatiuza mayiko omwe tikatumikire. Ambiri anatumizidwa ku Central ndi ku South America koma ife tinatumizidwa ku dziko la Chile.

 Kufufuza Chuma M’dziko la Chile

Kuti tilowe m’dziko la Chile panafunika zikalata zoyenerera, choncho panapita nthawi ndithu tisananyamuke. Motero tinachita kaye upainiya ku Washington D.C. kwa chaka ndi theka titamaliza maphunziro athu mu January 1945. Titalandira zikalata zathu tinali m’gulu la amishonale 9 amene ankapita ku Chile. M’gululi, anthu 7 anali atamaliza maphunziro awo ife tisanapite kusukuluyo.

Pamene tinafika ku likulu la dzikoli lotchedwa Santiago abale angapo anatilandira. Mmodzi wa iwo anali Albert Mann, mmishonale yemwe anatilimbikitsa kwambiri kwa zaka zingapo mbuyomo. Apa n’kuti m’baleyu atatha chaka chimodzi ku Chile pamodzi ndi Joseph Ferrari yemwe anaphunzira m’kalasi yachiwiri ya Gileadi. Pamene timafika, ku Chile kunali Mboni zosakwana 100. Tinafunitsitsa kupeza chuma, kapena kuti anthu oona mtima, m’dera latsopanoli.

Tinapemphedwa kukatumikira ku nyumba ya amishonale ku Santiago. Kwa ife, kunali kuyamba kukhala m’banja lalikulu la amishonale. Mmishonale aliyense ankalalikira kwa maola angapo ndipo kamodzi pa mlungu ankaphika chakudya cha banja lonse. Ndiye nthawi ina tinachita manyazi kwambiri. Tinaphika masikono oti banja lathu lonse lidye pa chakudya cha m’mawa. Koma titawatulutsa mu uvuni, tinamva fungo linalake losakhala bwino. Zinali choncho chifukwa choti tinathiramo soda mosadziwa. Mmishonale wina anaika sodayo m’botolo la yisiti wofufumitsira masikono.

Tinkachitanso manyazi kwambiri chifukwa chosadziwa Chisipanishi. Anthu a m’banja linalake lalikulu limene tinkaphunzira nalo Baibulo anafika potsala pang’ono kusiya kuphunzira chifukwa choti sankamva zolankhula zathu. Koma anaphunzirabe choonadi n’kukhala Mboni pomawerenga Malemba amene tinkawasonyeza m’Baibulo. Masiku amenewo, amishonale sankakhala ndi kosi yowaphunzitsa chinenero. Tinkangoyamba kulalikira basi n’kumayesa kuphunzira chinenero kwa anthu amene tikuwalalikirawo.

Tinali ndi maphunziro ambiri a Baibulo ndipo ena mwa anthu amene tinkaphunzira nawo anapita patsogolo mwamsanga. Komabe ena ankafunika kuleza nawo mtima kwambiri. Mayi wina wachitsikana, dzina lake Teresa Tello, anamvetsera uthenga wa choonadi n’kunena kuti: “Mudzabwerenso.” Tinabwererako ka 12 koma osam’peza. Mpaka panatha zaka zitatu. Kenaka tinapita ku msonkhano wadera womwe unachitikira mu holo inayake ku Santiago. Lamlungu, tikuchoka pa msonkhano, ndinamva munthu wina akukuwa kuti: “Mayi Dora, Mayi Dora!” Titacheuka tinaona kuti anali Teresa. Iyeyu anabwera kwa mkulu wake, yemwe ankakhala cha pafupi ndipo anafika ku holoyo kuti adzaone kuti kukuchitika zotani. Tinasangalala kwambiri kukumana nayenso. Tinakonza zoyamba kuphunzira naye Baibulo, ndipo posakhalitsa anabatizidwa. Patsogolo pake anadzakhala mpainiya wapadera. Panopo patha zaka 45 Teresa akuchitabe utumiki wanthawi zonse wapaderawu.​—Mlaliki 11:1.

 Kufufuza Chuma “Mumchenga”

Mu 1959 tinatumizidwa ku mzinda wotchedwa Punta Arenas, kutanthauza kuti “Dera la Mchenga.” Mzindawu uli chakum’mwera kwenikweni kwa chigawo cha m’mphepete mwanyanja cha m’dziko la Chile, chomwe n’chachitali makilomita 4,300. Gawo la Punta Arenas n’lodabwitsa. M’nyengo yotentha, dzuwa sililowa mwamsanga moti limawalabe mpaka hafu pasiti leveni usiku. Motero tinkalalikira masiku ambiri, ngakhale kuti nthawi zina tinkakumana ndi zovuta chifukwa cha mphepo yamkuntho imene imawomba m’nyengoyi. Koma m’nyengo yozizira dzuwa silichedwa kulowa.

Ngakhale kuti panali mavuto oterewa, ku Punta Arenas kunali m’pokomera pake. M’chilimwe, mitambo ya mvula imakuta thambo lonse lakumadzulo. Nthawi zina mitamboyi imabweretsa mvula yamphamvu, yomwe imakunyowetsani koma kenaka kumabwera mphepo yomwe imakuumitsani. Zikatero kumwambaku kumayala utawaleza wokongola. Nthawi zina utawalezawu umakhala kwa maola ambiri ndipo umati pena kuzimiririka pena kutuluka malingana ndi kuwala kwa dzuwa podutsa m’mitambo yamvula.​—Yobu 37:14.

Panthawiyo ku Punta Arenas kunali ofalitsa ochepa chabe. Motero mumpingo waung’ono wa kumeneku tinkachititsa misonkhano ndi ifeyo. Yehova anadalitsa khama lathu. Patatha zaka 37, tinabwerera ku Punta Arenas kuti tikaoneko. Kodi tinapezako zotani? Tinapezako mipingo 6 ndi Nyumba za Ufumu zitatu zokongola. Tinasangalala kwambiri kuti Yehova anatilola kupeza chuma chauzimu m’dera lam’chengali.​—Zekariya 4:10.

Tinapeza Chuma Chinanso pa “Gombe Lalikulu”

Titatumikira ku Punta Arenas kwa zaka zitatu ndi theka, anatitumiza ku mzinda wa Valparaiso, womwe uli ndi doko. Mzindawu uli ndi timapiri 41 tating’ono ndipo tili kumaso kwa nyanja ya Pacific. Tinalalikira makamaka m’dera lozungulira kaphiri kamodzi, lotchedwa Playa Ancha, kutanthauza kuti “Gombe Lalikulu.” Kwa zaka 16 zimene tinakhala kumeneku, taona abale achinyamata ochuluka ndithu akukula mwauzimu moti panopo ndi oyang’anira oyendayenda ndiponso akulu m’mipingo yosiyanasiyana m’dziko la Chile.

Kenaka anatitumiza ku mzinda wa Viña del Mar. Tinatumikira kumeneku kwa zaka zitatu ndi theka mpaka pamene chivomezi chinawononga nyumba yathu ya amishonale. Tinabwerera ku Santiago, komwe tinayambira ntchito yathu yaumishonale zaka 40 zapitazo. Tinapeza zinthu zitasintha kwambiri. Anali atamanga ofesi yatsopano ya nthambi, ndipo yoyambayo inasanduka nyumba ya amishonale onse amene anatsala m’dzikomo. Patsogolo pake, nyumbayi anayamba kuigwiritsa ntchito ngati malo a Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Panthawiyo, Yehova anatisonyezanso kukoma mtima kwachikondi. Amishonale asanu okalambafe tinaitanidwa kuti tikakhale pa Beteli. Panthawi imene takhala tikutumikira ku Chile, tapatsidwapo magawo 15 ochitako utumiki. Taona ofalitsa akuwonjezeka kuchoka pa 100 kufika pa 70,000! Tasangalala kwambiri kufufuza chuma m’dziko la Chile kwa zaka 57!

Timaona kuti Yehova watidalitsa kwambiri potilola kupeza anthu ambiri chonchi, omwenso agwiritsidwa ntchito ndi gulu lake. Anthuwa ndi chuma chamtengo wapatali zedi. Pazaka zoposa 60 zimene takhala tikutumikira Yehova limodzi, tikuvomereza ndi mtima wonse mawu amene Mfumu Davide, inalemba, akuti: “Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu!”​—Salmo 31:19.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 24 Bukuli linkafalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tinasiya kulisindikiza.

[Zithunzi patsamba 9]

Uyu ndi Dorothea mu 2002 ndiponso akulalikira mu 1943

[Chithunzi patsamba 10]

Umu ndi mu 1942 tikulalikira mu msewu ku Fort Dodge, m’boma la Iowa

[Chithunzi patsamba 10]

Uyu ndi Dora, mu 2002

[Chithunzi patsamba 12]

Dorothea ndi Dora ali panja pa nyumba yawo yoyamba ya amishonale m’dziko la Chile, mu 1946