Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandizidwa ndi “Mulungu Amene Amapatsa Anthu Mphamvu Kuti Athe Kupirira”

Kuthandizidwa ndi “Mulungu Amene Amapatsa Anthu Mphamvu Kuti Athe Kupirira”

 Kuthandizidwa ndi “Mulungu Amene Amapatsa Anthu Mphamvu Kuti Athe Kupirira”

PAFUPIFUPI zaka 2,000 zapitazo, Paulo analemba kuti Yehova ndi “Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu kuti athe kupirira.” (Aroma 15:5) Popeza kuti Baibulo limatiuza kuti Mulungu sasintha, sitikayika kuti iye amaperekabe mphamvu kwa anthu om’tumikira kuti apirire. (Yakobe 1:17) Kwenikweni, Baibulo limasonyeza kuti Yehova amapereka mphamvu zoterezi m’njira zosiyanasiyana. Kodi zina mwa njirazi n’zotani? Mulungu amapereka mphamvu kwa anthu amene amapemphera kwa iye kuti awathandize. Amalimbikitsanso Akhristu oona kuti azitonthoza okhulupirira anzawo. Yehova waperekanso nkhani zolimbikitsa m’Baibulo zomwe zimatonthoza anthu amene mwana wawo anamwalira. Tiyeni tione bwinobwino njira zitatu zimenezi.

Yehova Anamumva

Ponena za Mlengi wathu Yehova, Mfumu Davide inalemba kuti: “Khulupirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu. Tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.” (Salmo 62:8) N’chifukwa chiyani Davide ankakhulupirira Yehova motere? Ponena za iye mwini, Davide analemba kuti: “Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nam’pulumutsa m’masautso ake onse.” (Salmo 34:6, 7) Davide nthawi zonse ankapemphera kwa Mulungu kuti am’thandize pa mavuto ake, ndipo Yehova ankamuthandizadi. Davide ankadziwa kuti Mulungu am’thandiza kuti apirire mavuto ake chifukwa choti Mulunguyo anam’chitirapo zimenezi m’mbuyomo.

Makolo amene anaferedwa ayenera kudziwa  kuti Yehova adzawatonthoza pa chisoni chawo chachikulu monga anachitira ndi Davide. Iwo angam’fikire Mulungu, yemwe ndi “wakumva pemphero” wamkulu ali ndi chikhulupiriro choti adzawathandiza. (Salmo 65:2) William, yemwe tam’tchula m’nkhani yapita ija anati: “Nthawi zambiri ndinkaganiza kuti sindingathenso kukhala popanda mwana wanga ndipo ndakhala ndikupempha Yehova kuti anditonthoze. Iye wandilimbikitsa kwambiri kuti ndizitha kukhala bwinobwino.” Inunso mutapemphera kwa Yehova mwachikhulupiriro, Mulungu wamkulu wakumwamba adzakuthandizani. Ndipotu Yehova Mulungu amalonjeza anthu onse amene amayesetsa kum’tumikira kuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.”​—Yesaya 41:13

Kuthandizidwa ndi Anzanu Apamtima

Makolo omwe mwana wawo anamwalira nthawi zambiri amafuna kukhala paokha kuti ayese kuchepetsako chisoni chawo. Komabe sibwino kudzipatula kwa nthawi yaitali. Lemba la Miyambo 18:1 limati, “wopanduka [kapena kuti wodzipatula]” amatha kugwa m’vuto. Motero anamalira azisamala kuti asamadzipatule.

Anzanu oopa Mulungu angathe kukuthandizani mukaferedwa. Lemba la Miyambo 17:17 limati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” Lucy amene tam’tchulanso m’nkhani yoyamba ija, analimbikitsidwa ndi anzake panthawi imene mwana wake anamwalira. Ponena za anzake a mumpingo iye anati: “Ngakhale kuti nthawi zina sankanena zambiri akabwera kudzandiona, ndinkalimbikitsidwa kwambiri chifukwa cha kubwera kwawo. Mnzanga wina ankakonda kubwera masiku amene ndinkakhala ndekhandekha. Iye ankadziwa kuti panthawiyi ndimangokhala ku nyumba n’kumalira, motero nthawi zambiri ankabwera n’kumalira nane limodzi. Mnzanga winanso ankandiimbira foni tsiku lililonse kuti azindilimbikitsa. Ndipo ena ankatiitana ku nyumba zawo kuti tikadye nawo chakudya, ndipo akupitirizabe kuchita zimenezi.”

Ngakhale kuti makolo saiwala msanga ululu umene amakhala nawo mwana wawo akamwalira, pemphero ndiponso kulimbikitsidwa ndi Akhristu anzawo zimawatonthoza. Makolo  ambiri achikhristu amene mwana wawo anamwalira amaona kuti Yehova akuwathandiza. Inde Yehova “achiritsa osweka mtima, namanga mabala awo.”​—Salmo 147:3.

Nkhani za M’Baibulo Zolimbikitsa

Kuphatikiza pa kupemphera ndi kulimbikitsidwa ndi Akhristu anzawo, Mawu olembedwa a Mulungu amalimbikitsanso anamalira. Nkhani za m’Baibulo zimasonyeza kuti Yesu amafunitsitsa ndiponso angathe kutonthozeratu anamalirawa powaukitsira ana awo. Nkhani zoterezi zimalimbikitsa kwambiri anamalira. Tiyeni tione nkhani ziwiri zoterezi.

Nkhani ya mu Luka chaputala 7 imafotokoza zimene zinachitika pamene Yesu anakumana ndi gulu la anthu limene linali kupita ku manda mumzinda wa Naini. Anthuwo ankapita kukaika maliro a mwana wamwamuna wa mayi wina wamasiye. Uyu anali mwana yekhayo wa mayiyu. Vesi 13 limati: “Pamene Ambuye anaona mayiyo, anamumvera chifundo, ndipo anati kwa iye: ‘Lekani kulira mayi.’”

Anthu ambiri sangayerekeze dala kuuza mayi kuti asiye kulira pa maliro a mwana wake. Nanga n’chifukwa chiyani Yesu ananena zimenezi? N’chifukwa choti iye ankadziwa kuti chisoni chonse chimene mayiyo anali nacho chitha posachedwa. Nkhaniyo imapitirira motere: “[Yesu] anayandikira ndi kugwira chithathacho, pamenepo onyamulawo anangoima chilili, ndipo iye anati: ‘Mnyamatawe, ndikunena ndi iwe, Tadzuka!’ Pamenepo wakufayo anadzuka nakhala tsonga, ndi kuyamba kulankhula. Kenako anam’pereka kwa mayi wake.” (Luka 7:14, 15) Panthawiyo, mayiyo ayenera kuti analiranso, komano uku kunali kulira kwachisangalalo.

Panthawi ina, munthu wina dzina lake Yairo  anapempha Yesu kuti athandize mwana wake wamkazi wa zaka 12, amene anali kudwala mwakayakaya. Posakhalitsa kunabwera uthenga wakuti mwanayo wamwalira. Uthenga umenewu unam’foola kwambiri Yairo, koma Yesu anamuuza kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi.” Kenaka Yesu anapita ku nyumba kwa Yairo n’kufika pamene panagona mtembo wa mwanayo. Ndiye anam’gwira mwanayo padzanja n’kunena kuti: “Buthuwe, ndikunena ndi iwe Dzuka!” Kodi atatero chinachitika n’chiyani? “Nthawi yomweyo buthulo linadzuka ndi kuyamba kuyenda.” Zitatero taonani zimene makolo ake anachita. Iwo “anasangalala kwadzaoneni.” Yairo ndi mkazi wake anakumbatira mwana wawoyo ali ndi chimwemwe chodzadza tsaya. Ankangoona ngati n’kutulo.​—Maliko 5:22-24, 35-43.

Nkhani za m’Baibulo zoterezi, zomwe zinafotozedwa mwatsatanetsatane, zimalimbikitsa makolo amene ana awo anamwalira powapatsa chithunzi cha zimene zidzachitike m’tsogolo. Yesu anati: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Cholinga cha Yehova n’chakuti Mwana wake adzaukitse anthu amene anamwalira. Ana ochuluka mosaneneka amene anamwalira “adzamva mawu ake” akadzawauza kuti: “Ndikunena ndi iwe Dzuka!” Ana amenewa adzauka, n’kuyamba kuyenda ndi kulankhula bwinobwino. Ndipo monga anachitira Yairo ndi mkazi wake, makolo a ana amenewo ‘adzasangalala kwadzaoneni.’

Ngati mwana wanu anamwalira, ndithu musakayike kuti Yehova angathe kudzakuchotserani chisoni chanu chonse poukitsa mwana wanuyo. Kuti mudzalandire nawo madalitso osasimbikawa, mverani mawu a wamasalmo akuti: “Funani Yehova, ndi mphamvu yake; funsirani nkhope yake nthawi zonse. Kumbukirani zodabwiza zake adazichita; zizindikiro zake.” (Salmo 105:4, 5) Inde, muzitumikira Yehova, yemwe ndi Mulungu woona ndipo muzimulambira m’njira yoyenerera.

Kodi mumapindula bwanji pakali pano chifukwa ‘chofuna Yehova’? Mumalimbikitsidwa popemphera kwa Mulungu, poona kuti Akhristu anzanu akukuganizirani, ndiponso powerenga Mawu a Mulungu. Kuphatikizanso pamenepa, posachedwapa mudzaona ‘zodabwitsa ndi zizindikiro’ zimene Yehova adzachite pofuna kuti moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu amene anamwalira udzakhale wabwino kosatha.

[Bokosi patsamba 5]

“Mukabwere ndi Mayi Amene Ana Ake Awiri Anamwalira Uja”

Kehinde ndi mkazi wake Bintu, ndi Mboni za Yehova za ku Nigeria. Ana awo awiri anamwalira pa ngozi yagalimoto. Kuchokera pa nthawiyo, imfa imeneyi yakhala ikuwapweteka mtima kwambiri. Komabe, iwowa amalimba mtima chifukwa chodalira Yehova, ndipo amauza ena uthenga wa m’Baibulo wachiyembekezo.

Anthu ena anaona chikhulupiriro ndi kulimba mtima kwa Kehinde ndi Bintu. Tsiku lina Mayi Ukoli anauza mnzake wa Bintu kuti: “Mukabwere ndi mayi amene akulalikirabe uja, ngakhale kuti ana ake awiri anafa tsiku limodzi. Ndikufuna ndidziwe kuti n’chiyani chimamulimbikitsa.” Bintu atafika kwa Mayi Ukoli, mayiyu anati: “Ndikufuna kudziwa kuti ukutha bwanji kumalalikirabe za Mulungu amene anakuphera ana ako. Ineyo Mulungu ananditengera mwana wanga wamkazi yekhayo amene ndinali naye. Kuchokera pa nthawiyi, za Mulungu ndilibe nazo ntchito.” Bintu anatenga Baibulo n’kufotokoza zimene zimachititsa kuti anthu azifa komanso umboni wotsimikizira kuti abale athu amene anamwalira adzaukitsidwa.​—Machitidwe 24:15; Aroma 5:12.

Ndiyeno Mayi Ukoli anati: “Inetu ndinkangoti Mulungu ndiye amachititsa kuti anthu azifa. Ayi, zikomo tsopano ndadziwa zoona zake.” Iye anaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova pofuna kudziwa zambiri zokhudza malonjezo a Mulungu.

[Bokosi patsamba 6]

‘Ndikufuna Kuthandizapo, Koma Ndikusowa Poyambira’

Makolo ndiponso abale ake a mwana womwalirayo amakhala ndi chisoni chachikulu. Koma nthawi zina anzawo amasowa chochita. Iwowa amafuna kuthandizapo koma amaopa kuti ngati atanena kapena kuchita zinazake molakwika angaipitse zinthu kwambiri. Malangizo otsatirawa angathandize anthu amene amaganiza kuti: ‘Ndikufuna kuthandizapo, koma ndikusowa poyambira.’

❖ Musapewe anamfedwawo chifukwa chosowa chonena kapena chochita. Kubwera kwanuko pakokha kumawalimbikitsa. Kodi mukusowa chonena? Kungowakumbatira ndi kuwauza kuti “pepani” n’kokwanira kuti iwowa adziwe kuti mumawaganizira. Kapena mukuopa kuti mukayamba kulira mungawonjezere chisoni chawo? Baibulo limati: “Lirani ndi anthu amene akulira.” (Aroma 12:15) Misozi yanu imasonyeza kuti nanunso ndinu achisoni, ndipotu zimenezi zimawalimbikitsa.

❖ Yesetsani kuchitapo kanthu. Kodi mungathe kukonzera banjalo chakudya? Kodi mungawatsukire mbale? Kodi mungawatumikire pa ntchito zina ndi zina zapakhomopo? Pewani kunena kuti: “Kodi mmene zililimu pali chilichonse choti ndingathandizepo ngati?” Ngakhale mutanena zimenezi mochokera pansi pa mtima, anamalira ambiri amaona kuti mulibe nthawi yowathandiza. Motero ndi bwino kunena kuti: “Kodi zakutizakuti zilipo? Nanga zakutizakuti achita kale?” Mukatero chitani zimene zikufunikazo. Koma pewani kulowerera kwambiri za pabanjapo.

❖ Pewani kunena kuti: “Ndikudziwa mmene mukumvera.” Si kuti anthu onse amene ana awo amwalira amamva chimodzimodzi. Ngakhale zitakhala kuti inunso mwana wanu anamwalira, simungadziwe ndendende mmene anzanuwo akumvera.

❖ Pamatenga nthawi kuti chisoni cha anthu a m’banjamo chiyambe kuchepa. Pitirizani kuwathandiza m’njira iliyonse imene mungakwanitse. Maliro akangochitika chakumene, pamakhala anthu ambiri ofuna kuthandizapo, koma pakapita nthawi othandiza amachepa. Yesetsani kuona zimene banjalo likufunikira ngakhale patatha milungu kapena miyezi ingapo chichitikireni malirowo. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 29 Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene mungathandizire makolo amene akulira maliro a mwana wawo, onani mutu wakuti “Kodi Ena Angathandize Motani?” pa tsamba 20 mpaka 24 m’kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Zithunzi patsamba 7]

Nkhani za m’Baibulo zimasonyeza kuti Yesu ali ndi mphamvu zoukitsa anthu ndipo amafuna kudzaukitsa ana athu