Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata—khalani ndi Zolinga Zolemekeza Mulungu

Achinyamata—khalani ndi Zolinga Zolemekeza Mulungu

 Achinyamata​—khalani ndi Zolinga Zolemekeza Mulungu

‘Khala ndi chizolowezi chochita zinthu zokuthandiza kukhalabe wodzipereka kwa Mulungu.’​—1 TIMOTEYO 4:7.

1, 2. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Paulo anatamanda Timoteyo? (b) Kodi achinyamata masiku ano akutani kuti akhale ndi ‘chizolowezi chochita zinthu zowathandiza kukhalabe odzipereka kwa Mulungu’?

“NDILIBE wina wa mtima ngati iye amene angasamaledi za inu moona mtima. . . . Monga mwana ndi bambo wake, watumikira monga kapolo limodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino.” (Afilipi 2:20, 22) Mtumwi Paulo ananena mawu olimbikitsa amenewa m’kalata yake kwa Akhristu a ku Filipi. Kodi anali kunena za ndani? Anali kunena za Timoteyo, mnyamata amene ankayenda naye. Timoteyo ayenera kuti anasangalala kumva mawu amenewo osonyeza kuti Paulo anali kumukonda ndi kumukhulupirira.

2 Kuyambira kale, achinyamata okonda zinthu zauzimu ngati Timoteyo, akhala ofunika kwambiri pakati pa anthu a Yehova. (Salmo 110:3) Masiku ano, gulu la Mulungu lili ndi achinyamata ambiri amene ndi apainiya, amishonale, ogwira ntchito zomangamanga, ndi otumikira ku Beteli. Enanso amene akuchita bwino ndi achinyamata amene amalimbikira kugwira ntchito ndi mpingo ngakhale kuti ali ndi ntchito zawo zina. Achinyamata amenewa amasangalala chifukwa choyesetsa kukwaniritsa zolinga zawo zolemekeza Yehova, Atate wathu wakumwamba. Iwo alidi ndi ‘chizolowezi chochita zinthu zowathandiza kukhalabe odzipereka kwa Mulungu.’​—1 Timoteyo 4:7, 8.

3. Kodi m’nkhani ino tikambirana mafunso otani?

3 Kodi achinyamata inu, muli ndi zolinga zauzimu zimene mukuyesetsa kuzikwaniritsa? Kodi ndani amene angakuthandizeni ndi kukulimbikitsani? Kodi mungatani kuti musatengeke ndi mzimu wa dzikoli wokonda chuma? Kodi mungapeze madalitso otani ngati mutakhala ndi zolinga zolemekeza Mulungu? Kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa, tiyeni tikambirane za moyo ndi ntchito ya Timoteyo.

Moyo wa Timoteyo

4. Fotokozani mwachidule utumiki wa Timoteyo.

4 Timoteyo anakulira ku Lusitara, mzinda waung’ono m’chigawo cha Galatiya mu ufumu wa Roma. Ayenera kuti anamva za Chikhristu ali wachinyamata panthawi imene Paulo anakalalikira ku Lusitara cha m’ma 47 C.E. Pasanapite nthawi, Timoteyo anakhala ndi mbiri yabwino pakati pa abale achikhristu kumeneko. Patapita zaka ziwiri, Paulo anabwerera ku Lusitara ndipo atamva za kupita patsogolo kwa Timoteyo, anamusankha kukhala mmishonale mnzake. (Machitidwe 14:5-20; 16:1-3) Timoteyo atakhwima mwauzimu, anapatsidwa udindo wina waukulu, umene unafunanso kuti azichita ntchito yofunika kwambiri yolimbikitsa abale. Nthawi imene Paulo analembera Timoteyo kalata ali m’ndende ku Roma cha m’ma 65 C.E., Timoteyo anali mkulu mumpingo ku Efeso.

5. Malinga ndi 2 Timoteyo 3:14, 15, kodi ndi zinthu ziwiri ziti zimene zinathandiza Timoteyo kusankha kuchita zinthu zauzimu?

5 Ndi zoonekeratu kuti Timoteyo anasankha kuchita zinthu zauzimu. Kodi ndi chiyani chimene chinamulimbikitsa kuchita zimenezo?  M’kalata yake yachiwiri imene analembera Timoteyo, Paulo anatchula zinthu ziwiri zimene zinamuthandiza. Analemba kuti: “Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira utakhutira nazo, podziwa anthu amene anakuphunzitsa. Komanso, kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba opatulika.” (2 Timoteyo 3:14, 15) Tiyeni tikambirane kaye zimene Akhristu ena anachita kuti Timoteyo asankhe zimene anasankhazo.

Anthu Ena Angakulimbikitseni

6. Kodi Timoteyo anaphunzitsidwa chiyani, ndipo analabadira motani?

6 Timoteyo anakulira m’banja la makolo osiyana zipembedzo. Atate ake anali Mgiriki, ndipo amayi ake, a Yunike, ndi agogo ake, a Loisi, anali Ayuda. (Machitidwe 16:1) Yunike ndi Loisi anaphunzitsa Timoteyo choonadi cha m’Malemba Achiheberi kuyambira ali khanda. Atakhala Akhristu, iwo ayenera kuti anamuthandiza kukhutira ndi ziphunzitso zachikhristu n’kuzikhulupirira. Timoteyo anagwiritsa ntchito zimene anaphunzira. Paulo anaona zimenezi ndipo anati: “Ndikukumbukira chikhulupiriro chopanda chinyengo chimene chili mwa iwe, chimene chinakhazikika mwa agogo ako aakazi a Loisi, ndi amayi wako a Yunike choyamba, ndipo ndili wotsimikiza mtima kuti chilinso mwa iwe.”​—2 Timoteyo 1:5.

7. Kodi achinyamata ambiri ali ndi mwayi wotani, ndipo zimenezi zingawathandize bwanji?

7 Masiku ano, achinyamata ambiri ali ndi makolo ndi agogo oopa Mulungu, amene mofanana ndi Loisi ndi Yunike, amadziwa kufunika kokhala ndi zolinga zauzimu. Mwachitsanzo, Samira amakumbukirabe zimene ankakambirana ndi makolo ake ali mtsikana. Iye anati: “Bambo ndi mayi anga anandiphunzitsa kuona zinthu mmene Yehova amazionera ndi kuona ntchito yolalikira kukhala yofunika kwambiri. Ankandilimbikitsa kuyamba utumiki wa nthawi zonse.” Samira anamvera malangizo a makolo ake ndipo lero akutumikira ku Beteli m’dziko lakwawo. Ngati makolo anu amakulimbikitsani kukhala ndi zolinga zauzimu, ganizirani mofatsa malangizo awo. Iwo amakufunirani zabwino.​—Miyambo 1:5.

8. Kodi kukhala ndi mabwenzi achikhristu olimbikitsa kunamuthandiza bwanji Timoteyo?

8 Komanso mufunika kukhala ndi mabwenzi olimbikitsa pakati pa abale achikhristu. Timoteyo anali wodziwika kwambiri kwa akulu a mumpingo wake ndi a ku Ikoniyo, mzinda umene unali pa mtunda wa makilomita 30. (Machitidwe 16:1, 2) Anakhala bwenzi lapamtima la Paulo, amene anali munthu wokangalika. (Afilipi 3:14) Kalata za Paulo zimasonyeza kuti Timoteyo anali ndi mtima womvera malangizo ndipo sankachedwa kutsanzira anthu achikhulupiriro. (1 Akorinto 4:17; 1 Timoteyo 4:6, 12-16) N’chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Iwe wayesetsa kutsatira chiphunzitso changa, moyo wanga, cholinga changa, chikhulupiriro  changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga.” (2 Timoteyo 3:10) Zoonadi, Timoteyo anatsanzira kwambiri chitsanzo cha Paulo. Mabwenzi olimba mwauzimu mumpingo angakuthandizeni inunso kukhala ndi zolinga zabwino zauzimu.​—2 Timoteyo 2:20-22.

Phunzirani “Malemba Opatulika”

9. Kuwonjezera pa kukhala ndi mabwenzi abwino, kodi muyenera kuchita chiyani kuti mukhale ndi ‘chizolowezi chochita zinthu zokuthandizani kukhalabe wodzipereka kwa Mulungu’?

9 Kodi munthu akakhala ndi mabwenzi abwino ndiye kuti basi adzakwaniritsa zolinga zake zauzimu? Ayi, si choncho. Mofanana ndi Timoteyo, inunso muyenera kuphunzira “malemba opatulika” mosamala. Mwina simukonda kuwerenga, koma mofanana ndi Timoteyo, inunso mungaphunzire kukhala ndi ‘chizolowezi chochita zinthu zokuthandizani kukhalabe wodzipereka kwa Mulungu.’ Anthu ochita masewera ali ndi chizolowezi chokonzekera kwa miyezi yambiri kuti akwaniritse zolinga zawo. N’chimodzimodzinso zolinga zauzimu, zimafuna kudzipereka ndi khama. (1 Timoteyo 4:7, 8, 10) Mwina mungafunse kuti, ‘Kodi kuphunzira Baibulo kungandithandize bwanji kukwaniritsa zolinga zanga?’ Kungathandize m’njira zitatu. Tiyeni tione njira zimenezo.

10, 11. Kodi n’chifukwa chiyani Malemba angakulimbikitseni kukwaniritsa zolinga zanu zauzimu? Perekani chitsanzo.

10 Choyamba, Malemba amakulimbikitsani kuchita zinthu zoyenera. Amatiuza za umunthu wosangalatsa umene Atate wathu wakumwamba ali nawo ndi za njira yaikulu imene Mulungu anatisonyezera chikondi. Amatiuzanso za madalitso osatha amene wakonzera atumiki ake okhulupirika. (Amosi 3:7; Yohane 3:16; Aroma 15:4) Mukamaphunzira zambiri za Yehova, mumayamba kumukonda kwambiri ndipo mumafuna kudzipereka kwa iye.

11 Akhristu ambiri achinyamata akuti chizolowezi chophunzira Baibulo paokha chawathandiza kwambiri kukonda choonadi. Mwachitsanzo, Adele anakulira m’banja lachikhristu koma analibe zolinga zilizonse zauzimu. Iye anati: “Makolo anga ankapita nane ku Nyumba ya Ufumu koma pandekha sindinkaphunzira Baibulo kapena kumvetsera misonkhano.” Mchemwali wake atabatizidwa, Adele anayamba kuona choonadi kukhala chofunika kwambiri. Iye anati: “Ndinayamba kuwerenga Baibulo lonse. Ndimati ndikawerenga pang’ono, ndinkalemba mfundo za zimene ndawerengazo. Mfundo zimene ndinkalembazo ndidakali nazobe. Ndinawerenga Baibulo lonse chaka chimodzi.” Zimenezi zinamulimbikitsa Adele kudzipereka kwa Yehova. Ngakhale kuti ndi wolemala, iye tsopano ndi mpainiya, kapena kuti mlaliki wa nthawi zonse.

12, 13. (a) Kodi kuphunzira Baibulo kungathandize bwanji achinyamata kukonza umunthu wawo? (b) Kodi nzeru ya m’Mawu a Mulungu ingathandize achinyamata pazinthu zotani?

12 Chachiwiri, Baibulo lingakuthandizeni kukonza umunthu wanu. Paulo anauza Timoteyo kuti “malemba opatulika” ndi “opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo, kuti munthu  wa Mulungu akhale woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Mukamasinkhasinkha nkhani za Mawu a Mulungu ndi kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, mzimu wa Mulungu umakonza umunthu wanu kukhala wabwino kwambiri. Umakuthandizani kukhala ndi makhalidwe ofunika kwambiri monga kudzichepetsa, kupirira, khama, ndi kukonda kwambiri Akhristu anzanu. (1 Timoteyo 4:15) Timoteyo anali ndi makhalidwe amenewa, n’chifukwa chake anali wofunika kwambiri kwa Paulo ndi kumipingo imene anatumikirako.​—Afilipi 2:20-22.

13 Chachitatu, Mawu a Mulungu ndi nkhokwe ya nzeru. (Salmo 1:1-3; 19:7; 2 Timoteyo 2:7; 3:15) Angakuthandizeni kusankha anzanu mwanzeru, kusankha bwino zosangalatsa, ndi kuthana ndi mavuto osiyanasiyana. (Genesis 34:1, 2; Salmo 119:37; 1 Akorinto 7:36) Ngati mumasankha zinthu mwanzeru panopa, mudzatha kukwaniritsa zolinga zanu zauzimu.

“Menya Nkhondo Yabwino”

14. Kodi n’chifukwa chiyani ndi zovuta kukwaniritsa zolinga zauzimu?

14 Kukhala ndi zolinga zolemekeza Yehova ndi njira yanzeru koma si yophweka. Mwachitsanzo, posankha ntchito, mwina achibale, anzanu, ndi aphunzitsi okufunirani zabwino, angakuumirizeni kuti mukhale ndi maphunziro apamwamba ndi ntchito ya ndalama zambiri. Angatero chifukwa chakuti iwo amakhulupirira kuti zinthu zimenezi zingakuthandizeni kukhala ndi moyo wabwino ndi wachimwemwe. (Aroma 12:2) Monga Timoteyo, inunso muyenera ‘kumenya nkhondo yabwino yosunga chikhulupiriro’ kuti ‘mugwire zolimba moyo wosatha’ umene Yehova wakulonjezani.​—1 Timoteyo 6:12; 2 Timoteyo 3:12.

15. Kodi mwina Timoteyo anakumana ndi chiyeso chotani?

15 Ngati achibale anu osakhulupirira sakugwirizana ndi zimene mwasankha, mungakhale pa chiyeso chachikulu. Mwina Timoteyo anakumana ndi chiyeso ngati chimenechi. Buku lina limanena kuti ndi zotheka kuti banja la Timoteyo “linali la anthu ophunzira ndi olemera.” Mwina atate ake anafuna kuti iye akhale ndi maphunziro apamwamba kuti apitirize ntchito ya makolo ake. * Atate a Timoteyo ayenera kuti sanamvetse atamva kuti iye wasankha kugwira ntchito ya umishonale ndi Paulo, imene ikanaika moyo wake pangozi ndipo imene sakanaidalira kuti ingamupatse ndalama.

16. Kodi mnyamata wina anatani bambo ake atamutsutsa?

16 Masiku anonso Akhristu achinyamata amakumana ndi ziyeso ngati Timoteyo. Mwachitsanzo, Matthew, amene akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, akuti: “Nditayamba upainiya, bambo anakhumudwa kwambiri. Iwo anaona ngati maphunziro anga angopita pachabe chifukwa chakuti ndinapeza ntchito yosesa kuti izindithandiza pa utumiki wanga. Ankandinyoza ndi kundiuza kuti ndikanapeza ndalama zambiri ndikanakhala pa ntchito yolongosoka.” Kodi Matthew anatani atakumana ndi chiyeso chimenechi? “Ndinali ndi chizolowezi chowerenga Baibulo ndiponso kupemphera, makamaka ndikatsala pang’ono kupsa mtima.” Khama lake linapindula. Patapita nthawi, anayambanso kugwirizana ndi bambo ake. Ubwenzi wake ndi Yehova unalimba. Matthew akuti: “Yehova wakhala akundisamalira, kundilimbikitsa, ndi kundithandiza kuti ndisalakwitse posankha zinthu. Sindikanapeza zinthu zimenezi ndikanapanda kukhala ndi zolinga zauzimu.”

Musasiye Zolinga Zanu Zauzimu

17. Kodi ena mosadziwa amafoola bwanji anthu amene akufuna kuyamba utumiki wa nthawi zonse? (Mateyo 16:22)

17 Enanso amene angakugwetseni ulesi poyesetsa kukwaniritsa zolinga zanu zauzimu ndi  Akhristu anzanu. Mwina iwo anganene kuti, ‘N’chifukwa chiyani ukufuna kuchita upainiya? Utha kumalalikira bwinobwino popanda kuchita upainiya. Pezani ntchito yabwino kuti mukonze tsogolo.’ Zimenezi zingamveke ngati zanzeru, koma kodi mungati muli ndi chizolowezi chochita zinthu zokuthandizani kukhalabe wodzipereka kwa Mulungu ngati mwatsatira zimenezo?

18, 19. (a) Kodi mungachite chiyani kuti mtima wanu ukhale pa zolinga zauzimu? (b) Tchulani zinthu zina zimene achinyamatanu mukudzimana pa moyo chifukwa cha Ufumu.

18 Zikuoneka kuti Akhristu ena masiku a Timoteyo anali ndi maganizo ngati amenewa. (1 Timoteyo 6:17) Pofuna kuthandiza Timoteyo kuti aike mtima wake pa zolinga zauzimu, Paulo anamulimbikitsa kuti: “Msilikali amene ali pankhondo sachita zamalonda za moyo uwu pofuna kukondweretsa amene anam’lemba usilikali.” (2 Timoteyo 2:4) Msilikali amene ali pa ntchito satengeka ndi zinthu zina. Iye amakhala wokonzeka nthawi zonse kumvera mkulu wa asilikali chifukwa chakuti moyo wake ndi wa anthu ena umadalira iyeyo. Pokhala msilikali wa Khristu, inunso mtima wanu uyenera kukhala pa chinthu chimodzi kuti musamatanganidwe ndi zinthu zosafunika kwenikweni pamoyo, zimene zingakulepheretseni kukwaniritsa utumiki wanu wopulumutsa moyo.​—Mateyo 6:24; 1 Timoteyo 4:16; 2 Timoteyo 4:2, 5.

19 M’malo mofuna moyo watayale, khalani ndi mtima wodzipereka. “Konzekerani kudzimana zinthu zapamwamba, monga msilikali wa Khristu Yesu.” (2 Timoteyo 2:3, The English Bible in Basic English) Timoteyo anaphunzira chinsinsi chokhala wokhutira, ngakhale pamavuto, chifukwa choyenda ndi Paulo. (Afilipi 4:11, 12; 1 Timoteyo 6:6-8) Inunso mungatero. Kodi ndinu wokonzeka kudzimana zinthu zina pamoyo chifukwa cha Ufumu?

Madalitso Panopa ndi M’tsogolo

20, 21. (a) Tchulani ena a madalitso amene mungapeze ngati muli ndi zolinga zauzimu. (b) Kodi inuyo mwatsimikiza kuchita chiyani?

20 Timoteyo anayenda ndi Paulo kwa zaka pafupifupi 15. Iye anaona mipingo yatsopano ikupangidwa pamene uthenga wabwino unali kufalikira m’dera lonse la kumpoto kwa nyanja ya Mediterranean. Moyo wake unali waphindu ndi wosangalatsa kwambiri kusiyana ndi mmene ukanakhalira akanasankha moyo umene anthu amati ndiwo moyo wabwino. Mukakhala ndi zolinga zauzimu, inunso mudzapeza madalitso osaneneka auzimu. Ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimba ndipo Akhristu anzanu adzakukondani ndi kukulemekezani. M’malo mogwiritsidwa mwala pofunafuna chuma, mudzapeza chisangalalo chenicheni chifukwa chokhala ndi mtima wopatsa. Koposa zonse, ‘mudzagwira zolimba moyo weniweniwo,’ moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi.​—1 Timoteyo 6:9, 10, 17-19; Machitidwe 20:35.

21 Ngati simunakhalebe ndi chizolowezi chochita zinthu zokuthandizani kukhalabe wodzipereka kwa Mulungu, tikukulimbikitsani kuyamba panopo. Gwirizanani ndi ena mumpingo amene angakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zauzimu ndipo apempheni nzeru. Kuphunzira Mawu a Mulungu panokha kukhale chinthu choyamba pamoyo wanu. Kanani mzimu wa dzikoli wokonda chuma. Ndipo musaiwale kuti Mulungu, “amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale,” walonjeza kukupatsani madalitso panopa ndi m’tsogolo ngati mutakhala ndi zolinga zomulemekeza.​—1 Timoteyo 6:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Agiriki ankakonda kwambiri maphunziro apamwamba. Plutarch, amene anakhala ndi moyo nthawi imodzi ndi Timoteyo, analemba kuti: “Maphunziro apamwamba ndi gwero ndi muzu wa zinthu zonse zabwino. . . . Ndi maphunziro amenewa, amene amathandiza munthu kukhala ndi makhalidwe abwino kwambiri komanso chimwemwe. . . . Zinthu zina zonse ndi zopanda phindu ndi zachabechabe ndipo palibe chifukwa chovutikira nazo.”​—Moralia, I, “The Education of Children.”

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ndi chiyani chimene chingathandize achinyamata kukwaniritsa zolinga zauzimu?

• Kodi n’chifukwa chiyani kuphunzira Baibulo mosamala n’kofunika?

• Kodi achinyamata angatani kuti asatengeke ndi mzimu wa dzikoli wokonda chuma?

• Kodi kukhala ndi zolinga zauzimu kuli ndi madalitso otani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 24]

Timoteyo anali ndi zolinga zabwino

[Zithunzi patsamba 25]

Kodi ndani analimbikitsa Timoteyo?

[Zithunzi patsamba 26]

Kodi mukuyesetsa kukwaniritsa zolinga zauzimu?