Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata Mumasangalatsa Mtima wa Makolo Anu

Achinyamata Mumasangalatsa Mtima wa Makolo Anu

 Achinyamata Mumasangalatsa Mtima wa Makolo Anu

“PALIBE chondisangalatsa koposa zinthu zimenezi, kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi,” anatero mtumwi wokalamba Yohane. (3 Yohane 4) Ngakhale kuti ana amene atchulidwa m’vesili ndi ophunzira achikhristu, kholo loopa Mulungu limamvanso chimodzimodzi ngati ana ake akuyendabe m’choonadi. Monga mmene zochita za makolo zimakhudzira ana, zochita za ananso zimakhudza kwambiri makolo awo.

Mfumu Solomo ya Isiraeli inkadziwanso kuti zochita za ana zimakhudza kwambiri makolo awo. Inalemba kuti: “Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.” (Miyambo 10:1) Choncho ana onse, ndi aakulu omwe, amachita bwino kuganizira mmene zochita zawo zimakhudzira bambo ndi mayi awo. N’chifukwa chiyani zimenezi ndi zofunika kwambiri?

Tangoganizani zimene makolo anu oopa Mulungu akuchitirani kuyambira muli khanda. Iwo anayamba kukuderani nkhawa ndi kukupemphererani musanabadwe. Mutabadwa, bambo ndi mayi anu anayamba kukukondani ndipo n’kutheka kuti anathokoza Mulungu chifukwa cha mwayi ndi udindo wokhala kholo. Nthawi imeneyo, anakhala ndi udindo wosamalira kakhanda kobadwa kumene ndipo monga atumiki a Yehova, udindowo sanauone mopepuka.

Popeza kuti makolo anu ndi Akhristu enieni, anayamba kuwerenga kwambiri Baibulo ndi mabuku olifotokoza kuti apeze malangizo odalirika okulererani, ndipo anapempha nzeru kwa makolo amene analera bwino ana awo. Anapitirizanso kupempha Mulungu kuti awathandize kukulerani. (Oweruza 13:8) Pamene mumakula, makolo anu ankadziwa zinthu zimene munkachita bwino ndi zolakwa zanu zomwe. (Yobu 1:5) Mutafika zaka zaunyamata, panabuka mavuto ena. Nthawi zina, mwina munkapulupudza ndipo makolo anu ankapemphera kwambiri, kuwerenga kwambiri, ndi kuganizira kwambiri kuti akuthandizani bwanji kupitiriza kulambira Yehova, Atate wanu wakumwamba.

Bambo ndi mayi anu sasiya kukhala makolo. Ngakhale mutakula, makolo anu amadabe nkhawa za thanzi lanu, moyo wanu wauzimu, ndipo amafuna kuti muzisangalalabe. Nthawi  yonseyi, makolo anu saiwala kuti muli ndi ufulu wodzisankhira zochita ndipo sadziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani. Zoti moyo wanu udzakhala wotani, zikudalira inuyo.

Ngati ‘palibe chosangalatsa koposa zinthu zimenezi’ kuti makolo amve kuti ana awo “akuyendabe m’choonadi,” kodi si zomvekanso kuti makolo amakhumudwa kwambiri akamva kuti ana awo ‘asiya kuyenda m’choonadi’? Zoonadi, ana opusa amapweteka makolo awo mtima. Solomo anati: “Mwana wopusa achititsa atate wake chisoni, namvetsa zowawa amake wom’bala.” (Miyambo 17:25) Zimakhaladi zopweteka kwa makolo, mwana akasiya kulambira Mulungu woona.

Ndithudi, zochita zanu zimakhudza kwambiri banja lanu ndi anthu enanso. Khalidwe lanu limakhudza kwambiri mtima wa makolo anu. Mukafulatira Mulungu ndi mfundo zake, makolo anu amakhumudwa kwambiri. Koma mukapitiriza kukhulupirika ndi kumvera Yehova, makolo anu amasangalala kwambiri. Musasiye kusangalatsa mtima wa makolo anu. Kodi pali mphatso imene mungapatse makolo anu amene akukulerani, kukutetezani, ndi kukukondani yoposa kuwamvera?