Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tiyenera Kuopa Kubwera kwa Khristu?

Kodi Tiyenera Kuopa Kubwera kwa Khristu?

 Kodi Tiyenera Kuopa Kubwera kwa Khristu?

KODI mukuganiza kuti kubwera kwa Yesu Khristu kudzakhala kotani? Kodi mukuganiza kuti kudzabweretsa chiwonongeko, chisoni ndi kulanga anthu? Kodi kapena mukuganiza kuti kudzathetsa mavuto athu onse? Kodi tiyenera kuopa kubwera kwa Khristu? Kodi kapena tizikuyembekezera mwachidwi?

Ponena za kubwera kwa Khristu, Baibulo limati:“Taonani! Akubwera ndi mitambo, ndipo diso lililonse lidzamuona, . . . ndipo mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye.” (Chivumbulutso 1:7) Kubwera kumeneku kukutanthauza nthawi imene Yesu adzafika m’tsogolo kuti apereke mphoto kwa olungama ndi kulanga oipa.

M’malo moopa kubwera kwa Khristu kumeneku, mtumwi Yohane anakuyembekezera mwachidwi. Atadziwa za kubwera kumeneku ndi zimene zidzachitike pa dziko lapansi, Yohane anapemphera ndi mtima wonse kuti: “Bwerani, Ambuye Yesu.” (Chivumbulutso 22:20) Koma n’chifukwa chiyani “mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa . . . chifukwa cha iye”? Kodi “diso lililonse” lidzamuona motani? Kodi Khristu akabwera adzachita zinthu zotani? Kodi kukhulupirira kuti Khristu adzabwera kungatithandize motani panopo? Nkhani yotsatirayi iyankha mafunso amenewa.