Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi “nkhondo ya . . . Mulungu Wamphamvuyonse” pa Haramagedo n’chiyani, ndipo idzatha bwanji?​—Chivumbulutso 16:14, 16.

Kunena mwachidule, nkhondo ya Haramagedo ndi nkhondo imene idzachitika m’tsogolo pa dziko lonse lapansi pamene Yesu Khristu, Mfumu yosankhidwa ndi Yehova, adzawononge adani a Mulungu. Baibulo limafotokoza kuti adani amenewa, omwe ndi “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu,” asonkhanitsidwa ndi “mauthenga ouziridwa ndi ziwanda” ndipo akusonkhanitsidwira “ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse . . . kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.”​—Chivumbulutso 16:14, 16.

Sikuti magulu omenyanawa asonkhana ku malo enieni ayi. Dzina lakuti Haramagedo, limene m’Mabaibulo ena analimasulira kuti “Aramagedo,” limatanthauza “Phiri la Megido.” (Chivumbulutso 16:16) Sikunakhalepo phiri lomwe linali ndi dzina limenelo. Kuwonjezera apo, sizingatheke kuti “mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo” asonkhanedi pa malo amodzi. (Chivumbulutso 19:19) M’malo mwake, ‘malowo’ akutanthauza zochitika zimene atsogoleri andale a dziko lapansi ndi otsatira awo akupititsidwako. Ndipo zochitikazi ndi zotsutsana ndi Yehova ndi “magulu ankhondo amene anali kumwamba” otsogozedwa ndi mkulu wa asilikali yemwe ndi “Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye,” Yesu Khristu.​—Chivumbulutso 19:14, 16.

N’zochititsa chidwi kuti, mawu akuti “Haramagedo” akugwirizana ndi mzinda wa Isiraeli wakale, wa Megido. Mzindawu unali pamalo abwino kwambiri omwe anali kum’mawa kwa phiri la Karimeli, ndipo unali pakatikati pa njira zikuluzikulu zomwe kunkadutsa amalonda ndiponso asilikali ankhondo m’nthawi imeneyo. Komanso kunachitikira nkhondo zikuluzikulu. Mwachitsanzo, kunali “ku madzi a Megido” kumene Woweruza wa Isiraeli, Baraki, anagonjetsa gulu lankhondo lamphamvu la Akanani lotsogozedwa ndi Mkulu Wankhondo Sisera. (Oweruza 4:12-24; 5:19, 20) Komanso kufupi ndi malo omwewo, Woweruza Gidiyoni anagonjetseratu Amidyani. (Oweruza 7:1-22) Choncho pogwirizanitsa Megido ndi nkhondo imene ikubwera, Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu, kudzera mwa Mwana wake, adzagonjetseratu adani ake onse.

Kodi zidzatha bwanji? Nkhondo ya Haramagedo idzathetseratu chinyengo ndi kuipa konse padziko lapansi. Idzakhala chiyambi cha nyengo yabwino kwambiri m’mbiri yonse ya anthu. (Chivumbulutso 21:1-4) Moyang’aniridwa ndi Ufumu wa Mulungu wachikondi, dziko lapansi lidzasinthidwa n’kukhala paradaiso mmene anthu olungama adzakhalemo kosatha.​—Salmo 37:29.