Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Zimene Baibulo Limaphunzitsa Kwenikweni

Phunzitsani Zimene Baibulo Limaphunzitsa Kwenikweni

 Phunzitsani Zimene Baibulo Limaphunzitsa Kwenikweni

“Mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse . . . [ndi] kuwaphunzitsa.”​—MATEYO 28:19, 20.

1. Kodi tinganene chiyani za kupezeka kwa Baibulo?

MAWU A YEHOVA, Baibulo Loyera, ndi limodzi mwa mabuku akale kwambiri komanso ofalitsidwa kwambiri pa dziko lonse lapansi. Mbali za Baibulo zamasuliridwapo m’zinenero zoposa 2,300. Anthu 90 pa anthu 100 alionse padziko lapansi ali ndi Baibulo m’chinenero chawo.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani anthu amasokonezeka pa nkhani ya zimene Baibulo limaphunzitsa? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

2 Anthu mamiliyoni ambiri amawerenga Baibulo tsiku lililonse. Ena aliwerengapo lonse lathunthu nthawi zambirimbiri. Zipembedzo zambiri zimati zimaphunzitsa zinthu zochokera m’Baibulo, koma zipembedzozo sizigwirizana pa zimene Baibulo limaphunzitsa. Pakati pa anthu achipembedzo chimodzi pamakhalanso kusagwirizana kwakukulu, ndipo zimenezi zimangowonjezera chisokonezo chimene chilipo kale. Ena amalikayikira Baibulo lenilenilo, ndipo amakayikiranso za kumene linachokera, ndi phindu lake. Ena amaliona ngati buku longogwiritsidwa ntchito mwamwambo polumbira kapena pofuna kulonjeza kuti anena zoonadi m’khoti.

3 Komatu, Baibulo lili ndi mawu, kapena kuti uthenga wamphamvu wa Mulungu kwa anthu. (Aheberi 4:12) Choncho, ife monga Mboni za Yehova tikufuna anthu aphunzire zimene Baibulo limaphunzitsa. Timasangalala kugwira ntchito imene Yesu Khristu anapatsa otsatira ake pamene ananena kuti: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse . . . [ndi] kuwaphunzitsa.” (Mateyo 28:19, 20) Tikamalalikira, timapeza anthu a mtima wabwino amene akhumudwa ndi chisokonezo chimene chafala m’zipembedzo za m’dzikoli. Amafuna kudziwa zoona zake za Mlengi wathu ndiponso amafunitsitsa kuphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza cholinga cha moyo. Tiyeni tikambirane mafunso atatu amene anthu ambiri amakhala nawo. Pa funso lililonse, tiona zinthu zabodza zimene atsogoleri a zipembedzo amanena, kenaka tiona zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni. Mafunso ake ndi akuti: (1) Kodi Mulungu amasamala za ife? (2) N’chifukwa chiyani tili padziko pano? (3) N’chiyani chimatichitikira tikafa?

Kodi Mulungu Amasamala za Ife?

4, 5. N’chifukwa chiyani anthu amaganiza kuti Mulungu sasamala za ife?

4 Tiyeni tiyambe ndi funso lakuti, Kodi Mulungu amasamala za ife? N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amaganiza kuti yankho lake n’loti ayi, sasamala. N’chifukwa chiyani amaganiza choncho? Chifukwa chimodzi n’choti akukhala m’dziko lodzadza ndi chidani, nkhondo, ndi kuvutika. Choncho amaganiza kuti, ‘Kodi Mulungu akanati azisamaladi za ife, si bwenzi ataletsa zinthu zoipazi kuti zisamachitike?’

5 Chifukwa china chimene anthu amaganizira kuti Mulungu sasamala za ife n’chakuti atsogoleri a zipembedzo awachititsa kuganiza choncho. Kodi atsogoleri a zipembedzo nthawi zambiri amati chiyani pakachitika zinthu zoipa? Ana awiri aang’ono a mayi wina atamwalira pa ngozi ya galimoto, abusa a tchalitchi cha mayiyo anati:  “N’chifuniro cha Mulungu. Mulungu amafuna angelo ena awiri.” Atsogoleri a zipembedzo akamanena zinthu ngati zimenezo, amakhala akumuloza chala Mulungu kuti ndi amene wachititsa zinthu zoipazo. Koma wophunzira Yakobe analemba kuti: “Pokhala pa mayesero, munthu asanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobe 1:13) Yehova Mulungu sachititsa zinthu zoipa. Ndipotu, “n’kutali ndi Mulungu kuchita choipa.”​—Yobu 34:10.

6. Kodi ndani amachititsa zinthu zoipa ndi mavuto m’dzikoli?

6 Nangano n’chifukwa chiyani pali zinthu zoipa ndi mavuto ambirimbiri? Chifukwa chimodzi n’choti anthu akana kuti Mulungu akhale Wolamulira wawo, ndipo safuna kugonjera malamulo ndi mfundo zake zolungama. Mosadziwa, anthu agonjera Mdani wa Mulungu, Satana, chifukwa “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kudziwa mfundo imeneyi kumatithandiza kuti tisavutike kumvetsa chifukwa chake zinthu zoipa zimachitika. Satana ndi woipa, wachidani, wachinyengo, ndi wankhanza. Choncho tiyenera kuyembekezera dzikoli kuchita zinthu zofanana ndi khalidwe la wolamulira wake. Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti pali zoipa zambirimbiri!

7. Kodi n’zifukwa zina ziti zimene zimachititsa kuti anthu azivutika?

7 Kupanda ungwiro kwa anthu n’chifukwa china chimene chimachititsa kuti tizivutika. Anthu ochimwa nthawi zambiri amalimbirana ulamuliro, ndipo zimenezo nthawi zambiri zimabweretsa nkhondo, kuponderezana, ndi kuvutika. Lemba la Mlaliki 8:9 limafotokoza bwino mfundo imeneyi, kuti: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” Chifukwa china chimene chimachititsa kuti tizivutika ndicho zinthu ‘zotigwera m’nthawi mwake.’ (Mlaliki 9:11) Nthawi zambiri anthu amakumana ndi tsoka chifukwa choti ali pa malo olakwika pa nthawi yolakwika.

8, 9. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amasamaladi za ife?

8 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova sayambitsa kuvutika. Koma kodi Mulungu amakhudzidwadi ndi zimene zikuchitika pamoyo wathu? Yankho lake n’loti inde, ndipo zimenezi n’zosangalatsadi! Tikudziwa kuti Mulungu amakhudzidwa chifukwa Mawu ake ouziridwa amatiuza chifukwa chimene walolera anthu kuchita zoipa. Mulungu watero chifukwa cha nkhani ziwiri: ulamuliro wake ndi kukhulupirika kwa anthu. Popeza Yehova ndi Mlengi wamphamvuyonse, atafuna akhoza osatiuza chifukwa chimene amalolera anthu kuvutika. Komabe, watiuza chifukwa choti amasamala za ife.

9 Taonani umboni winanso woti Mulungu amasamala za ife. Iye “anavutika m’mtima mwake” pamene kuipa kunadzadza pa dziko lapansi m’masiku a Nowa. (Genesis 6:5, 6) Kodi Mulungu amamvabe chimodzimodzi masiku ano? Inde, chifukwa iye sasintha. (Malaki 3:6) Iye amadana kwambiri ndi kupanda chilungamo ndipo zimamuipira akaona anthu akuvutika. Baibulo limaphunzitsa  kuti posachedwapa Mulungu adzakonza zinthu zonse zimene zawonongeka chifukwa cha ulamuliro wa anthu ndi zochita za Mdyerekezi. Kodi umenewo si umboni wokwanira woti Mulungu amasamala za ife?

10. Kodi Yehova amamva bwanji akamaona anthu akuvutika?

10 Atsogoleri a zipembedzo amamuipitsira mbiri Mulungu akamanena kuti zinthu zoipa zimene zikutichitikira ndi chifuniro chake. Mosiyana ndi zimenezi, Yehova akufunitsitsa kuthetsa mavuto a anthu. Lemba la 1 Petulo 5:7 limati, “amasamala za inu.” Zimenezo n’zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni!

N’chifukwa Chiyani Tili Padziko Pano?

11. Kodi zipembedzo za m’dzikoli nthawi zambiri zimati chiyani za moyo wa anthu padziko pano?

11 Tsopano tiyeni tikambirane funso lachiwiri limene anthu ambiri amadzifunsa loti, N’chifukwa chiyani tili padziko pano? Zipembedzo za m’dzikoli nthawi zambiri zimayankha kuti anthu ali padziko pano mongoyembekezera chabe. Amaona dziko lathuli ngati malo ongowolokera, kapena kuti njira yopitira ku moyo wina. Atsogoleri ena a zipembedzo amaphunzitsa bodza loti tsiku lina Mulungu adzawononga dziko lapansili. Chifukwa cha ziphunzitso zimenezi, anthu ambiri amaganiza kuti ndi bwino kuti ayesetse kupeza zonse zomwe angathe m’moyo uno chifukwa pamapeto pake adzafa basi. Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani kwenikweni za chifukwa chomwe tilili padziko pano?

12-14. Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani za cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi ndi anthu?

12 Mulungu ali ndi cholinga chabwino kwambiri chokhudza dziko lapansi ndi anthu. Iye “sanalilenga [dziko lapansi] mwachabe” koma “analiumba akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Komanso, Yehova “anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthawi yonse.” (Salmo 104:5) Kuphunzira zinthu zimenezi zokhudza cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi ndi anthu kungatithandize kumvetsa chifukwa chomwe tilili padziko pano.

13 Machaputala 1 ndi 2 a Genesis amasonyeza kuti Yehova anakonza bwino kwambiri dziko lapansili kuti anthu akhalemo. Pamapeto pa nyengo yolenga dziko lathuli, zonse “zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Mulungu anaika mwamuna ndi mkazi oyamba, Adamu ndi Hava, m’munda wokongola wa Edene ndipo anawapatsa chakudya chabwino cha mwanaalirenji. Anthu awiri oyambawo anauzidwa kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” Ntchito yawo inali yoti akhale ndi ana angwiro, akulitse munda womwe ankakhalamo mpaka ufike dziko lonse, ndi kuti alamulire zinyama mwachikondi.​—Genesis 1:26-28.

14 N’cholinga cha Yehova kuti anthu angwiro akhale pa dziko lapansi kosatha. Mawu a Mulungu amati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Indedi, anthu anapangidwa kuti akhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso pa dziko lapansi. Chimenecho ndiye cholinga cha Mulungu, ndipo n’zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni!

N’chiyani Chimatichitikira Tikafa?

15. Kodi zipembedzo zambiri m’dzikoli zimaphunzitsa kuti n’chiyani chimatichitikira tikafa?

15 Tsopano tiyeni tikambirane funso lachitatu limene anthu ambiri amakhala nalo.  Funso lake n’loti, N’chiyani chimatichitikira tikafa? Zipembedzo zambiri m’dzikoli zimaphunzitsa kuti munthu ali ndi chinachake m’kati mwake chimene chimakhalabe ndi moyo thupi likafa. Zipembedzo zina zimaphunzitsabe kuti Mulungu amalanga anthu oipa mwa kuwazunza kwamuyaya m’moto wa helo. Koma kodi zimenezo n’zoona? Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani kwenikweni za imfa?

16, 17. Malinga ndi zimene Baibulo limanena, kodi akufa chimawachitikira n’chiyani?

16 Mawu a Mulungu amati: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, sadzalandira mphoto.” Popeza “akufa sadziwa kanthu bi,” sangamve, kuona, kulankhula, kumva kukhudza, kapena kuganiza. Salandira mphoto, kapena kuti malipiro alionse. Angalandire bwanji, popeza sangathe kugwira ntchito iliyonse? Komanso, “chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano,” chifukwa sakhudzidwa mtima ndi chilichonse.​—Mlaliki 9:5, 6, 10.

17 Zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi n’zomveka bwino. Munthu akafa sakhalanso ndi moyo kwina kulikonse. Tikafa, palibe chimene chimachoka m’thupi mwathu n’kumakhalabe ndi moyo kuti chidzabadwenso m’thupi lina, ngati zimene anthu ena amakhulupirira. Tikhoza kupereka chitsanzo ichi: Moyo umene tili nawo uli ngati lawi la kandulo. Lawilo likazima, silipita kulikonse. Limakhala kulibeko basi.

18. Wophunzira Baibulo akaphunzira kuti akufa sadziwa kalikonse, kodi angazindikirenso mfundo zina ziti?

18 Tangoganizirani mmene mfundo ya choonadi yosavuta kumva koma yamphamvu imeneyo ingakhudzire munthu. Wophunzira Baibulo akaphunzira kuti akufa sadziwa chilichonse, sizingam’vute kuzindikira kuti makolo ake amene anafa sangam’vutitsenso, kaya anali ndi chidani chotani pamoyo wawo. Angamvetsenso msanga mfundo yoti okondedwa ake amene anafa sangathenso kumva, kuona, kulankhula, kumva kukhudza, kapena kuganiza. Choncho, sangakhale akusungulumwa ku puligatoriyo kapena kuzunzika kumoto. Koma Baibulo limaphunzitsa kuti akufa amene ali m’chikumbumtima cha Mulungu adzaukitsidwa. Chimenechi n’chiyembekezo chosangalatsa kwabasi!​—Yohane 5:28, 29.

Buku Latsopano Loti Tizigwiritsa Ntchito

19, 20. Kodi Akhristufe tili ndi udindo wotani, ndipo ndi buku liti lophunzirira Baibulo limene analikonza makamaka kuti tizigwiritsa ntchito mu utumiki wathu?

19 Tangokambirana mafunso atatu okha amene anthu ambiri amakhala nawo. Pa funso lililonse, zimene Baibulo limaphunzitsa n’zomveka bwino. Zimakhala zosangalatsa kwambiri kukambirana mfundo zoona zimenezi ndi anthu amene akufuna kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa! Koma palinso mafunso ena ambiri ofunika amene anthu a mtima wabwino amafuna atayankhidwa mokhutiritsa. Akhristufe tili ndi udindo wowathandiza kupeza mayankho a mafunso amenewo.

20 Zimakhala zovuta kuphunzitsa choonadi cha m’Malemba momveka bwino komanso mom’fika pamtima wophunzirayo. Kuti atithandize kuchita zimenezi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anakonza buku limene ntchito yake kwenikweni ndi kuphunzitsira anthu mu utumiki wathu wachikhristu. (Mateyo 24:45-47) Buku lake ndi la masamba 224 ndipo mutu wake ndi wakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

21, 22. Kodi mbali zina zabwino kwambiri za buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? n’ziti?

 21 Bukuli linatulutsidwa pa Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova mu 2005, ya mutu wakuti “Kumvera Mulungu,” ndipo lili ndi mbali zingapo zabwino kwambiri. Mwachitsanzo, lili ndi mawu oyamba a masamba asanu amene akuthandiza kwambiri poyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Mosakayikira simungavutike kukambirana zithunzi ndi malemba amene ali m’mawu oyambawa. Mukhozanso kugwiritsa ntchito zomwe zili m’chigawo chimenechi pophunzitsa ophunzira kupeza machaputala ndi mavesi m’Baibulo.

22 Bukuli analilemba m’njira yosavuta kumva. Anayesetsa kuti am’fike pamtima wophunzirayo mwa kum’limbikitsa kunena zimene akuganiza. Mutu uliwonse uli ndi mafunso angapo koyambirira ndipo pamapeto pake pali bokosi la mutu wakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa.” Bokosilo limakhala ndi mayankho a m’Malemba a mafunso a koyambirira aja. Zithunzi zabwino kwambiri ndi mawu ofotokozera zithunzizo, komanso mafanizo a m’buku limeneli angathandize wophunzira kumvetsa mfundo zatsopano. Ngakhale kuti nkhani za m’mitu ya m’bukuli azilemba mofewa, pali za kumapeto zomwe zikufotokoza mozama mitu 14 yofunika. Mungagwiritse ntchito za kumapetozi ngati wophunzira akufuna kudziwa mfundo zina zowonjezera.

23. Kodi paperekedwa malangizo otani a momwe mungagwiritsire ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pochititsa maphunziro a Baibulo?

23 Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani analikonza kuti litithandize kuphunzitsa anthu a maphunziro ndi zipembedzo zosiyanasiyana. Ngati wophunzira sadziwa chilichonse cha m’Baibulo, mwina mungafunike kuphunzira mutu umodzi maulendo angapo. Musafulumire n’cholinga choti mungomaliza mutuwo, koma yesetsani kum’fika pamtima wophunzirayo. Ngati sakumvetsa fanizo linalake la m’bukuli, lifotokozeninso kapena gwiritsani ntchito fanizo lina. Muzikonzekera bwino, muziyesetsa kugwiritsa ntchito bwino bukuli, ndipo pempherani kuti Mulungu akuthandizeni kuti muthe ‘kuwalondoloza bwino mawu a choonadi.’​—2 Timoteyo 2:15.

Yamikirani Mwayi Wanu Wamtengo Wapatali

24, 25. Kodi Yehova wapatsa anthu ake mwayi wamtengo wapatali wotani?

24 Yehova wapatsa anthu ake mwayi wamtengo wapatali. Watithandiza kuphunzira zoona zake za iyeyo. Sitiyenera kupeputsa mwayi umenewu. Pajatu Mulungu wabisa zolinga zake kwa anthu odzitukumula koma waziulula kwa anthu odzichepetsa. Pa nkhani imeneyi, Yesu anati: “Ndikutamanda inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwazivumbula kwa tiana.” (Mateyo 11:25) Ndi mwayi wapadera kwambiri kukhala pakati pa anthu odzichepetsa amene akutumikira Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, Yehova.

25 Mulungu watipatsanso mwayi wophunzitsa anthu ena za iyeyo. Kumbukirani kuti mbiri yake yaipitsidwa ndi anthu amene amaphunzitsa zinthu zomunamizira. Choncho anthu ambiri ali ndi chithunzi cholakwika kwambiri cha Yehova, ndipo amaganiza kuti samvera ena chisoni ndiponso kuti ndi wouma mtima. Kodi inuyo ndinu wokonzeka komanso wofunitsitsa kumuchotsera mbiri yoipayi? Kodi mukufuna kuti anthu a mtima wabwino kulikonse adziwe zoona za Mulungu? Ngati mukufuna, sonyezani kuti mumamvera Mulungu mwa kulalikira mwakhama ndi kuphunzitsa ena zimene Malemba amanena pa nkhani zofunika kwambiri. Anthu amene akufunafuna choonadi akufunika kuphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu amasamala za ife?

• N’chifukwa chiyani tili padziko pano?

• N’chiyani chimatichitikira tikafa?

• Kodi ndi mbali ziti za buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani zimene mumakonda kwambiri?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 22]

Baibulo limaphunzitsa kuti kuvutika kudzatha

[Mawu a Chithunzi]

Top right, girl: © Bruno Morandi/​age fotostock; left, woman: AP Photo/​Gemunu Amarasinghe; bottom right, refugees: © Sven Torfinn/​Panos Pictures

[Chithunzi patsamba 23]

Olungama adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso