Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungafutukule Chikondi Chanu?

Kodi Mungafutukule Chikondi Chanu?

 Kodi Mungafutukule Chikondi Chanu?

TCHENI cha nangula wa sitima yapamadzi chiyenera kukhala cholimba kwambiri kuti sitimayo isasunthe. Koma zimenezi zimatheka kokha ngati malo olumikizirana tchenicho ali osasunthasuntha ndi olimba. Apo ayi, tchenicho chikhoza kuduka.

N’chimodzimodzinso ndi mpingo wachikhristu. Kuti mpingo ukhale wolimba ndi waumoyo, anthu a mumpingomo ayenera kukhala ogwirizana. Kodi n’chiyani chimawagwirizanitsa? Ndi chikondi, chomwe ndi chinthu champhamvu kwambiri chogwirizanitsira anthu. Choncho n’zosadabwitsa kuti Yesu Khristu anauza ophunzira ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana wina ndi mnzake. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana wina ndi mnzake. Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” Indedi, chikondi chimene chimakhalapo pakati pa Akhristu oona n’champhamvu kuposa chikondi cha mabwenzi wamba kapena anthu amene amangolemekezana. Akhristu oona amakhala ndi chikondi chololera kuvutikira ena.​—Yohane 13:34, 35.

Kulemekeza Akhristu Anzathu

M’mipingo yambiri muli anthu osiyana misinkhu, mafuko, mitundu, zikhalidwe, zinenero, ndi kakulidwe. Aliyense amakhala ndi zinthu zimene amakonda ndi zomwe sakonda, zimene amayembekezera ndi zimene amaopa, ndipo nthawi zambiri aliyense amakhala ndi mtolo wolemetsa winawake umene wanyamula, monga matenda kapena mavuto azachuma. Kusiyana kumeneku kukhoza kusokoneza mgwirizano wachikhristu. Choncho, kodi n’chiyani chingatithandize kufutukula chikondi chathu n’kukhalabe ogwirizana ngakhale pali kusiyana kotereku? Kulemekeza ndi mtima wonse anthu onse mumpingo kungatithandize kukulitsa chikondi chathu pa Akhristu anzathu.

Koma kodi tingalemekeze bwanji anthu ena? Ngati timalemekeza abale ndi alongo athu, timaganizira zosowa zawo, timawaona kuti ndi a mtengo wapatali, timazindikira ubwino wawo, ndipo timayamikira kuti timalambira nawo limodzi. Chifukwa chochita zimenezi, timayamba kuwakonda kwambiri. Kuona mwachidule zimene mtumwi Paulo analembera Akhristu oyambirira a ku Korinto kungatithandize kuona momwe tingasonyezere mokwanira chikondi chachikhristu.

Akorinto ‘Malo Anawachepera’

Paulo analemba kalata yake yoyamba kwa Akorinto mu 55 C.E. ndipo yachiwiri anailemba pasanathe chaka chimodzi chilembereni yoyambayo. Zimene ananena zikusonyeza kuti anthu ena mu mpingo wa Korinto sankalemekeza okhulupirira anzawo. Paulo anafotokoza zomwe zinkachitikazo m’mawu awa: “Takhala tikulankhula kwa inu mosabisa mawu Akorinto, tafutukula mtima wathu. Malo sakukucheperani mu mtima mwathu, koma m’chikondi chanu ndimo muli malo ochepa.” (2 Akorinto 6:11, 12) Kodi Paulo anatanthauza chiyani pamene ananena kuti ‘malo awachepera’?

Anatanthauza kuti anali ndi mtima wosafutukuka ndiponso wosapatsa. Katswiri wina wa Baibulo anati mwina chikondi cha Akorinto kwa Paulo “chinatchingidwa ndi zovuta zosiyanasiyana, chifukwa choti ankamukayikira popanda  chifukwa . . . ndiponso ankaona kuti Pauloyo wawalakwira m’njira inayake.”

Taonani malangizo amene Paulo anapereka: “Choncho, mutibwezere zomwezo zimene takuchitirani​—ndikulankhula nanu ngati ana anga​—inunso futukulani mtima wanu.” (2 Akorinto 6:13) Paulo analimbikitsa Akorinto kuti afutukule chikondi chawo kwa okhulupirira anzawo. Zimenezi zinatanthauza kuti azisonkhezeredwa ndi maganizo abwino ndi mtima wopatsa, osati ndi kukayikirana ndi kukwiya ndi zinthu zazing’ono.

Kufutukula Chikondi Masiku Ano

N’zosangalatsa kuona mmene olambira oona a Mulungu masiku ano amayesetsera kuti afutukule chikondi chawo pa wina ndi mnzake. Koma zoona zake n’zoti kufutukula chikondi kumafuna khama. Si chinthu chimene timangochiganizira basi. Kufutukula chikondi kumafuna kuti tizichita zinthu zosiyana ndi anthu amene satsatira mfundo za m’Baibulo. Anthu amenewa nthawi zambiri salemekeza anzawo. Akhoza kuchita zinthu mosaganizira ena, mopanda ulemu, ndiponso monyoza. Choncho ifeyo tiyesetse kuti tisatengere makhalidwe amenewa. Zingakhale zomvetsa chisoni ngati chikondi chathu chitazilala ngati cha Akorinto chifukwa cha kukayikirana. Zimenezi zingachitike ngati timafulumira kuona zophophonya za m’bale wathu wachikhristu koma osaona msanga makhalidwe ake abwino. Zingachitikenso ngati mtima wathu ukulephera kukonda munthu winawake chifukwa choti ndi wa chikhalidwe china.

Mosiyana ndi zimenezi, mtumiki wa Mulungu amene wafutukula chikondi chake amalemekezadi Akhristu anzake. Amawaona kuti ndi amtengo wapatali, amawachitira ulemu, ndipo amaganizira zosowa zawo. Ngakhale pakhale zifukwa zomveka zodandaulira, amakhululuka msanga ndipo sasunga chakukhosi. M’malo mwake amawaganizira zabwino Akhristu anzake.  Mtima wopatsa umamuthandiza kusonyeza chikondi chimene Yesu ankachiganizira pamene ananena mwaulosi kuti: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.”​—Yohane 13:35.

Chitani Khama Kuti Mupeze Anzanu Atsopano

Chikondi chochokera pansi pamtima chidzatilimbikitsa kuchita khama kuti tiyambe kucheza ndi anthu ena osati okhawo amene timati ndi anzathu komanso n’kuyesetsa kucheza ndi anthu a mu mpingo amene nthawi zambiri siticheza nawo kwenikweni. Kodi ena mwa anthu amenewa angakhale ati? Abale ndi alongo athu ena achikhristu ndi amanyazi, kapena, pa zifukwa zosiyanasiyana, ali ndi anzawo owerengeka. Poyamba tikhoza kuona ngati kuti m’zinthu zambiri ndife osiyana ndi anthu amenewa, kupatulapo kuti timalambirira nawo limodzi basi. Koma kodi si zoona kuti ena mwa anthu ogwirizana kwambiri m’Baibulo anali anthu amene, pongowaona chabe, angaoneke ngati kuti anali osiyana m’njira zambiri?

Mwachitsanzo, Rute ndi Naomi anali osiyana kwambiri zaka, anali ochokera ku mafuko ndi zikhalidwe zosiyana, ndiponso zinenero zawo zobadwira zinali zosiyana. Ngakhale anali osiyana choncho, ankakondana kwambiri. Jonatani analeredwa monga mwana wa mfumu, ndipo Davide anali wobusa ziweto. Anthuwa analinso osiyana kwambiri zaka, komatu ali m’gulu la anthu amene ankagwirizana kwambiri otchulidwa m’Malemba Oyera. Maubwenzi awiri onsewa anali osangalatsa ndiponso olimbikitsa mwauzimu kwa anthu amene anali paubwenziwo.​—Rute 1:16; 4:15; 1 Samueli 18:3; 2 Samueli 1:26.

Ngakhale masiku ano, Akhristu oona amene ali osiyana kwambiri zaka kapena amene moyo wawo uli wosafanana ngakhale pang’ono amatha kukhala pa ubwenzi wa ponda apa m’pondepo. Mwachitsanzo, Regina ndi mayi yemwe akulera yekha ana awiri achinyamata. * Amakhala wotanganidwa nthawi zonse ndipo sakhala ndi nthawi yambiri yocheza. Harald ndi mkazi wake Ute anapuma pantchito ndipo alibe ana. Kungoona mwamsangamsanga, mabanja awiri amenewa angaoneke ngati kuti n’ngosiyana m’njira zambiri. Koma Harald ndi Ute anamvera malangizo a m’Baibulo oti tifutukule mtima wathu. Motero anayamba kumaitana Regina ndi ana ake kuti achitire nawo limodzi zinthu zambiri, ndipo ankakhalira limodzi polalikira ndiponso pa zosangalatsa zina.

Kodi nafenso tingayambe kucheza ndi anthu ena kuwonjezera pa anzathu akale? Bwanji osayamba kucheza kwambiri ndi Akhristu anzanu ochokera ku mayiko ena, a chikhalidwe china, kapena osiyana nawo msinkhu?

Kuthandiza Ena Akafunika Thandizo

Mtima wopatsa umatilimbikitsa kuganizira kwambiri zosowa za ena. Zosowa ngati ziti? Taonani anthu a mu mpingo wachikhristu. Ana amafunika kuwatsogolera, okalamba amafunika kuwalimbikitsa, amene ali mu utumiki wa nthawi zonse amafunika kuwayamikira ndi kuwathandiza, ndipo Akhristu anzathu amene ali osasangalala amafunika wina woti amuuze za kukhosi. Aliyense amafunikira thandizo linalake. Timafunika kuyesetsa kuthandiza ena pa zimene akufunikirazo.

Kufutukula chikondi kumatanthauzanso kuti tiziwamvetsa anthu amene ali ndi zosowa zapadera. Kodi mukudziwa winawake amene akudwala matenda aakulu kapena amene akukumana ndi chiyeso chinachake pamoyo wake? Kufutukula chikondi chanu ndi kukulitsa mtima wopatsa, kudzakuthandizani kuwamvetsa ndi kuwathandiza anthu amene akufunikira thandizo.

Maulosi a m’Baibulo onena za m’tsogolomu akamakwaniritsidwa, mgwirizano wolimba mumpingo udzakhala wofunika kwambiri kuposa katundu, luso, kapena kuchita bwino zinthu zinazake. (1 Petulo 4:7, 8) Aliyense wa ife akhoza kuthandizira kulimbikitsa mgwirizano mu mpingo wathu mwa kufutukula chikondi chathu pa Akhristu anzathu. Tingakhale ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzatidalitsa kwambiri chifukwa chochita zinthu mogwirizana ndi mawu a Mwana wake, Yesu Khristu, akuti: “Lamulo langa ndi ili, mukondane wina ndi mnzake mmene inenso ndakondera inu.”​—Yohane 15:12.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Tasintha mayina ena.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Ngati timalemekeza abale ndi alongo athu, timaona kuti onse ndi a mtengo wapatali, timawachitira ulemu, ndipo timaganizira zosowa zawo