Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zidzatheka Kuti Anthu Azikhala Mwamtendere Chaka Chonse?

Kodi Zidzatheka Kuti Anthu Azikhala Mwamtendere Chaka Chonse?

 Kodi Zidzatheka Kuti Anthu Azikhala Mwamtendere Chaka Chonse?

“Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.”​—Luka 2:14.

ANTHU mamiliyoni ambiri amadziwa mawu amenewo olengeza kubadwa kwa Yesu omwe angelo a Mulungu anauza abusa amene anali kuyang’anira ziweto zawo usiku. Panthawi imene matchalitchi amanena kuti Yesu anabadwa, anthu ambiri amene amati ndi Akhristu amachita zambiri kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Inde, panthawi ya Khirisimasi m’pamene anthu amayesetsa kwambiri kukhala mwachimwemwe, mwamtendere, ndiponso kukondwera ndi anzawo, omwe ndi makhalidwe amene angelo anatchula m’zimene analengeza.

Maganizo abwinowa amakopa ngakhale anthu amene saona Khirisimasi ngati tchuti chachipembedzo. Iwonso amayamikira zabwino zimene tchuthichi chimaoneka kuti chimalimbikitsa anthu kuchita. Kumalo kumene anthu amapatsidwa tchuti kusukulu kapena kuntchito panyengo ya Khirisimasi, anthuwo amakhala ndi mpata wopumula, wocheza ndi mabanja awo, ndi anzawo, kapena amangokhala ndi mpata wosangalala. Koma n’zoona kuti anthu ambiri oona mtima amaona Khirisimasi makamaka monga nthawi yolemekeza Yesu Khristu.

Mulimonse mmene anthu amaonera Khirisimasi, ambiri a iwo angavomereze kuti maganizo abwino alionse omwe tchuthichi chimabweretsa sakhalitsa. Anthu sachedwa kukhalanso ndi maganizo amene anali nawo tchuthicho chisanafike. Nkhani ya mutu wakuti “Maganizo a Anthu Panyengo ya Khirisimasi,” yosindikizidwa ndi Royal Bank of Canada, inati: “Anthu ambiri amene amati ndi Akhristu amangoyesetsa kutsatira Khristu pa milungu yochepa chabe chaka chilichonse, akumakomera mtima kwambiri anzawo mpaka tchuti cha Chaka Chatsopano chitatha, kenako amayambiranso khalidwe lawo ladyera ndi losaganizira anthu ena.” Nkhaniyo inapitiriza n’kunena kuti, “vuto lenileni” la maganizo a anthu panyengo ya Khirisimasi n’lakuti sakhala nawo “chaka chonse.”

Kaya mukuvomereza zimene ananenazo kapena ayi, nkhaniyi ikudzutsa mafunso ofunika. Kodi anthu adzatha kukhala owolowa manja ndi omvetsetsana nthawi zonse? Kodi pali chiyembekezo chenicheni choti zimene angelo analengeza pa usiku womwe Yesu anabadwa zidzakwaniritsidwa? Kapena kodi chiyembekezo chokhala ndi mtendere weniweni n’kulota chabe?