Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

• Kodi n’chiyani chimene chingamuthandize Mkhristu woona ngati wachibale wake wasiya Yehova?

Muyenera kudzimanga mwauzimu inuyo limodzinso ndi okhulupirika ena a m’banja mwanu. Limbikirani kuchita zinthu zauzimu. Dziperekeni kuthandiza ena. Musataye mtima kuti wokondedwa ameneyo sangabwererenso kwa Mulungu. Musamadziimbe mlandu. Lemekezani njira ya Mulungu yoperekera chilango, ndipo uzani mabwenzi anu zakukhosi kwanu.​—9/1, tsamba 18 mpaka 21.

• Kodi ndi njira ziwiri ziti zimene Malemba amatithandizira kuzindikira ‘masiku otsiriza’?

Baibulo limaneneratu za zinthu zomwe zidzachitike pa nthawi ya “mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mateyo 24:3, 7, 8; Luka 21:11) Limafotokozanso za kusintha kwa makhalidwe ndi zochita za anthu a “m’masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1-5) N’zochititsa chidwi kuti uthenga wabwino wa ufumu unayenera kulalikidwa m’nthawi imeneyi.​—9/15, tsamba 4 mpaka 6.

• Kodi udindo wa mpingo n’ngotani, Mkhristu amene akuyendetsa galimoto akachita ngozi anthu ena n’kufapo?

Akulu omwe akufufuza nkhaniyo angaone kuti palibe mlandu wakupha, chifukwa chakuti zinali zovuta kwambiri kuti dalaivalayo apewe ngoziyo kapenanso zinali zosatheka n’komwe kuipewa. Koma ngati papezeka kuti munthu ali ndi mlandu wakupha, ndipo munthu yemwe ali ndi mlandu wakuphayo ndi wolapa, ayenera kudzudzulidwa mogwirizana ndi Malemba ndipo amaletsedwa kuchita nawo zinthu zina mu mpingo.​—9/15, tsamba 30.

• N’chifukwa chiyani moyo wosatha sudalira pa zimene asayansi amapeza?

Asayansi akuyesayesa kupeza njira zotalikitsira moyo wa munthu, monga kuyesa kupeza njira yoti munthu akamakalamba, thupi lake lizipangabe maselo atsopano, kapena kupanganso ziwalo zatsopano zogwirizana ndendende ndi thupi la odwala amene akufunika ziwalozo. Koma Baibulo limasonyeza kuti njira yokha imene anthu angapezere moyo wosatha ndi nsembe ya dipo ya Yesu.​—10/1, tsamba 3 mpaka 5.

• Kodi ubatizo wa Chikhristu unayambira pa mwambo wosamba wa Ayuda?

Ayi. Ayuda ankachita mwambo wodziyeretsa pa iwo okha, zimene ubatizo wa Yohane sunafune. Chilamulo cha Mose chinkafuna kudziyeretsa mobwerezabwereza, koma ubatizo wa Chikhristu umachitika kamodzi basi.​—10/15, masamba 12 mpaka 13.

• Kodi Sukulu Yophunzitsa Utumiki n’chiyani?

Imeneyi ndi sukulu imene akulu mumpingo komanso atumiki othandiza amene ali osakwatira ndiponso omwe angathe kukatumikira kumalo kumene kukufunika thandizo lalikulu, amapita kwa masabata asanu ndi atatu. Angatumizidwe kukatumikira ku mpingo umene iwo anachokera, ku mpingo wina uliwonse wa m’dzikolo, kapena ku dziko lina.​—11/15, masamba 10 mpaka 11.

• Kodi wokana Khristu amene anatchulidwa pa 1 Yohane 2:18; 4:3 ndani?

Nthawi zambiri, “wokana Khristu” amaimira anthu onse otsutsa kapena anthu amene monyenga amadzitcha kukhala Khristu kapena kukhala oimira ake a Khristu. Koma, mawu a Yesu ndi a Yohane amasonyeza kuti wokana Khristu ndi gulu limene limapangidwa ndi anthu ambirimbiri okana Khristu amene amafalitsa mabodza a chipembedzo ndipo amakana Ufumu wa Mulungu.​—12/1, masamba 4 mpaka 6.