Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Yesu analankhula mopanda ulemu kapena mosaganizira mayi ake pamene anali paphwando laukwati ku Kana?​—Yohane 2:4.

Atangobatizidwa kumene, Yesu ndi ophunzira ake anaitanidwa ku phwando laukwati ku Kana. Mayi ake analinso konko. Vinyo ataperewera, Mariya anauza Yesu kuti: “Alibe vinyo.” Poyankha mayi akewo, Yesu anati: “Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu?”​—Yohane 2:1-4, Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Masiku ano, anthu angaone kuti n’kusowa ulemu, kapenanso kuti ndi mwano, kutchula amayi ako kuti “mkazi” n’kuwauza kuti “ndili ndi chiyani ndi inu?” Koma kuimba Yesu mlandu woterewu n’kusadziwa za chikhalidwe ndiponso za chinenero chimene nkhaniyi inalembedwamo. Kumvetsetsa mmene anthu ankagwiritsira ntchito mawu amenewa m’nthawi za Baibulo kungatithandize.

Pankhani ya mawu akuti “mkazi,” buku la Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words limati: “Kugwiritsira ntchito mawuwa potchula mkazi si kulankhula modzudzula kapena mokhadzula, koma awa ndi mawu achikondi kapena olemekeza.” Mabuku ena amavomereza mfundo imeneyi. Mwachitsanzo, Baibulo la The Anchor Bible limati: “Awa si mawu odzudzula, kapena opanda ulemu, komanso si mawu osonyeza kusowa chikondi . . . Umu ndi mmene Yesu ankalankhulira ndi akazi posonyeza ulemu.” Buku la The New International Dictionary of New Testament Theology limalongosola kuti mawuwa “amagwiritsidwa ntchito monga mawu otchulira munthu ndipo alibe tanthauzo lina lililonse lonyoza.” Ndipo buku la Gerhard Kittel lotchedwa Theological Dictionary of the New Testament limati “kugwiritsa ntchito mawuwa m’njira imeneyi si kupanda ulemu kapena kunyoza ayi.” Choncho, potchula amayi ake kuti “mkazi,” tisaganize kuti Yesu analankhula mwamwano kapena mosaganizira mayi akewo.​—Mateyo 15:28; Luka 13:12; Yohane 4:21; 19:26; 20:13, 15.

Nanga bwanji za mawu akuti “ndili ndi chiyani ndi inu?” Zikuoneka kuti awa ndi mawu okuluwika amene Ayuda ambiri ankanena ndipo amapezeka kangapo konse m’Baibulo. Mwachitsanzo, lemba la 2 Samueli 16:10 limati Davide analetsa Abisai kuti asaphe Simeyi pomuuza kuti: “Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide?” Chimodzimodzinso pa 1 Mafumu 17:18 timawerenga kuti mkazi wamasiye wa ku Zarefati atapeza kuti mwana wake wamwalira, anauza Eliya kuti: “Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?”

Pa zitsanzo za m’Baibulo zimenezi, tingathe kuona kuti mawu akuti ‘ndili nanu chiyani?’ nthawi zambiri sagwiritsidwa ntchito posonyeza kunyoza kapena mwano. Koma amagwiritsidwa ntchito posonyeza kusafuna kulowerera ntchito inayake imene wina akuiganizira kapena akukupempha kuchita, kapenanso posonyeza kuti munthuwe uli ndi maganizo osiyana ndi amene atchulidwa. Nangano kodi tinganenepo chiyani pa mawu a Yesu kwa Mariya?

Mariya atauza Yesu kuti, “Alibe vinyo,” kwenikweni sikuti amangomuuza Yesu kuti adziwe zimenezo koma anali kutanthauza kuti Yesuyo achitepo kanthu. Yesu ananena mawuwa pokana kuchita zimene Mariyayo anali kutanthauza, ndipo mawu amene ananena pomaliza yankho lakelo, akuti, “nthawi yanga siinafike,” akutithandiza kuona chifukwa chimene anachitira zimenezi.

Kuchokera pa nthawi imene anabatizidwa ndi kudzozedwa mu 29 C.E., Yesu ankadziwa kuti chinali cholinga cha Yehova kuti iye, poti anali Mesiya wolonjezedwa, akhale wokhulupirika moyo wake wonse mpaka kudzafa, kuukitsidwa, ndi kupatsidwa ulemerero. Iye anati: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) Nthawi ya kufa kwake itayandikira, Yesu anamveketsa bwino zimenezi ponena kuti: “Nthawi yafika.” (Yohane 12:1, 23; 13:1) Motero, akupemphera usiku wa tsiku loti amwalira mawa, Yesu anati: “Atate, nthawi yafika; lemekezani mwana wanu,  kuti mwana wanu akulemekezeni.” (Yohane 17:1) Ndipo potsiriza, chigulu cha anthu chitabwera kudzam’manga ku Getsemane, Yesu anadzutsa atumwi ake kutulo n’kuwauza kuti: “Nthawi yakwana! Taonani! Mwana wa munthu akuperekedwa m’manja mwa ochimwa.”​—Maliko 14:41.

Komano paukwati wa ku Kana, Yesu anali atangoyamba utumiki wake monga Mesiya, ndipo “nthawi” yake inali isanafike. Cholinga chake chachikulu chinali choti achite cholinga cha Atate wake m’njira komanso panthawi imene Atate wake ananenera, ndipo palibe munthu amene akanasokoneza cholinga chakechi. Powauza mayi ake zimenezi, Yesu analankhula mosapita m’mbali, koma sanalankhule mwamwano ayi. Naye Mariya sanamve kuti mwana wakeyu wam’chititsa manyazi kapena kumunyoza. Ndipotu, pozindikira tanthauzo la mawu a Yesu, Mariya anauza anthu amene anali kutumikira paukwatiwo kuti: “Chilichonse chimene angakuuzeni, chitani chimenecho.” Yesu sananyalanyaze mayi ake, koma anachita chozizwitsa chake choyamba monga Mesiya posandutsa madzi kukhala vinyo wabwino kwambiri, ndipo potero anasonyeza kuti anali wosamala kuti achite chifuniro cha Atate wake koma panthawi yomweyo achiteponso kanthu pa vuto limene amayi ake anam’tchulira.​—Yohane 2:5-11.

[Chithunzi patsamba 31]

Yesu analankhula ndi mayi ake mokoma mtima koma mosapita m’mbali