Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Imene Ikukukhudzani

Nkhani Imene Ikukukhudzani

 Nkhani Imene Ikukukhudzani

KODI muli ndi mnzanu kapena mbale wanu amene mumakondana naye kwambiri? Bwanji munthu wina atakunenani kuti muli paubwenzi woterowo chifukwa choti ndinu wadyera? Kodi sizingakupwetekeni, kapena kukukwiyitsani kumene? Zimenezi n’zofanana ndi zimene Satana Mdyerekezi ananena zokhudza onse amene ali paubwenzi ndi Yehova Mulungu.

Taonani zimene zinachitika pamene Satana anapatutsa anthu awiri oyambirira, Adamu ndi Hava, kuti aswe lamulo la Mulungu ndiyeno n’kugwirizana naye popandukira Mulungu. Kodi zimene zinachitikazi zinatanthauza kuti anthu azimvera Yehova, pokhapokha ngati kumverako kukuwapindulitsa? (Genesis 3:1-6) Patadutsa zaka pafupifupi 2,500 Adamu atapanduka, Satana anabutsanso nkhaniyi, koma panthawi ino, ananena za mwamuna wina wotchedwa Yobu. Popeza zimene Mdyerekezi ananena zikusonyeza bwino nkhani imene iye anabutsa, tiyeni tifufuze mwachidwi nkhani imeneyi ya m’Baibulo.

“Sinditaya Ungwiro Wanga”

Yobu anali “munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.” Komabe, Satana anaderera kukhulupirika kwa Yobu. Iye anafunsa Yehova kuti: “Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe?” Kenaka, Mdyerekezi ananamizira Mulungu ndi Yobu yemwe ponena kuti Yehova wagula kukhulupirika kwa Yobu chifukwa chomuteteza ndi kum’dalitsa. Ndipo Satana anapitiriza kuti: “Koma mutambasule dzanja lanu ndi kum’khudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.”​—Yobu 1:8-11.

Kuti atsutse mabodzawa, Yehova analola kuti Satana ayese Yobu. Pofuna kum’patutsa Yobu kuti asiye kutumikira Mulungu, Mdyerekezi anabweretsa masoka otsatizanatsatizana kwa munthu wokhulupirikayu. Ziweto zonse za Yobu zinabedwa kapena kuwonongedwa, antchito ake anaphedwa, ndiponso ana ake anafa. (Yobu 1:12-19) Koma kodi Satana anapambana? Ayi, sanapambane. Ngakhale kuti Yobu sankadziwa kuti amene akuchititsa mavuto akewo ndi Mdyerekezi, iye anati: “Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.”​—Yobu 1:21.

Patapita nthawi, Satana anabweranso pamaso pa Yehova. Ndiye Yehova anauza Satanayo kuti: ‘[Yobu] anaumirirabe kukhala wangwiro, chinkana undisonkhezera ndimuwononge kopanda chifukwa.’ (Yobu 2:1-3) Mfundo yofunika kwambiri ndi yokhudza ungwiro wa Yobu, khalidwe lokhulupirika kwa Mulungu ndiponso kuchita chilungamo nthawi zonse. Apa Yobu anali atapambana pa nkhani ya kukhulupirika. Komabe, Mdyerekezi sanaisiyire pomwepa nkhaniyi.

Kenaka, Satana anabutsa chinenezo chachikulu chokhudza anthu onse. “Khungu kulipa khungu,” anatero kwa Yehova, “inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuwombola moyo wake. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.” (Yobu 2:4, 5) Mwa kugwiritsa ntchito mawu akuti “munthu” m’malo motchula dzina loti Yobu, Mdyerekezi anasonyeza  kuti palibe munthu aliyense amene angakhale wokhulupirika. Kwenikweni, iye anatanthauza kuti: ‘Munthu adzachita chilichonse kuti apulumutse moyo wake. Ndipatseni mpata, ndipo ndingachititse munthu aliyense kusiya kulambira Mulungu.’ Kodi n’zoona kuti palibe munthu amene angakhaledi wokhulupirika kwa Mulungu nthawi zonse ngati atakumana ndi mavuto a mtundu uliwonse?

Yehova analola kuti Mdyerekezi akanthe Yobu ndi nthenda yoopsa. Ndiyeno Yobu anadwala kwambiri mpaka anapemphera kuti angofa. (Yobu 2:7; 14:13) Komabe, Yobu anati: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.” (Yobu 27:5) Yobu ananena mawu amenewa chifukwa chokonda Mulungu, ndipo sanalole chilichonse kum’dodometsa. Zochita za Yobu zinatsimikiziradi kuti iye ndi munthu wokhulupirika. “Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake,” limatero Baibulo. (Yobu 42:10-17) Kodi pali enanso amene akhulupirika ngati Yobu? Kodi nthawi yaitali imene yadutsapo yasonyeza zotani?

Kutsutsa Bodzalo

M’chaputala 11 cha buku la m’Baibulo la Aheberi, mtumwi Paulo anatchula ena mwa amuna ndi akazi okhulupirika a m’nthawi yakale, Chikhristu chisanayambe. Ena mwa anthu amenewa ndi Nowa, Abulahamu, Sara, ndi Mose. Kenaka mtumwiyo anati: “Pakuti nthawi indichepera kuti ndipitirize kusimba za [ena].” (Aheberi 11:32) Atumiki okhulupirika a Mulungu anali ambiri zedi moti Paulo anawatchula kuti ndi ‘mtambo waukulu wa mboni,’ kuwayerekezera ndi mtambo waukulu womwe umakuta kumwamba. (Aheberi 12:1) N’zoona, kwa zaka mazanamazana, anthu ankhaninkhani asankha kukhala okhulupirika kwa Yehova Mulungu mwakufuna kwawo.​—Yoswa 24:15.

Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, anatsutsiratu bodza la Satana loti angachititse anthu kusiya kutumikira Yehova. Ngakhale imfa yopweteka ya pamtengo wozunzikirapo sinam’siyitse kukhulupirika kwake kwa Mulungu. Patangotsala mphindi zochepa kuti afe, Yesu anafuula kuti: “Atate, ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.”​—Luka 23:46.

Komanso, nthawi yaitali yomwe yadutsapo yasonyezeratu kuti Mdyerekezi sanathe kusintha munthu aliyense n’kumusiyitsa kutumikira Mulungu woona. Anthu osawerengeka aphunzira za Yehova ndipo ‘akumukonda ndi mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse, ndi maganizo awo onse.’ (Mateyo 22:37) Kukhulupirika kwawo kwa Yehova kwasonyeza bodza la Satana pa nkhani ya kukhulupirika kwa anthu. Inunso mungasonyeze kuti Mdyerekezi n’ngwabodza ngati mungapitirizebe kukhala munthu wokhulupirika.

Kodi Muyenera Kuchita Chiyani?

Cholinga cha Mulungu n’chakuti, “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:4) Kodi mungadziwe bwanji choonadi molondola? Konzani pulogalamu yophunzirira Baibulo ndipo ‘phunzirani ndi kudziwa za Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene anam’tuma.’​—Yohane 17:3.

Satana anatsutsa kukhulupirika kwa munthu mwa kukayikira zolinga zimene munthu amakhala nazo potumikira Mulungu. Choncho kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi mfundo zolondola zimene mwaphunzira, ndiye kuti mfundozo ziyenera kukufikani pamtima. Ndipo zimenezi kuti zichitike, pali chinanso chimene muyenera kuchita kuwonjezera pa kudziwa mfundo za m’Baibulo. Khalani ndi chizolowezi chosinkhasinkha mfundo zimene mwaphunzira. (Salmo 143:5) Mukamawerenga Baibulo kapena zofalitsa zofotokoza Baibulo, yesetsani kusinkhasinkha mafunso ngati awa: ‘Kodi ndikuphunzirapo chiyani za Yehova? Kodi ndi makhalidwe ati a Mulungu amene akulongosoledwa pano? Kodi ndingatsanzire makhalidwe amenewa pambali ziti za moyo wanga? Kodi ndi zinthu ziti zimene Mulungu amazivomereza kapena sazivomereza? Kodi zimenezi zimandichititsa kumuona motani Mulungu?’ Kusinkhasinkha mwanjira imeneyi kudzakuthandizani kukonda ndi kuyamikira Mlengi kuchokera pansi pa mtima.

Sikuti kukhala wokhulupirika kwa Mulungu kumangokhudza nkhani ya kupembedza yokha ayi. (1 Mafumu 9:4) Kukhala wokhulupirika kwa  Yehova Mulungu kumafunanso kukhala ndi makhalidwe abwino pamoyo wonse. Kuwonjezera apo, kukhalabe wokhulupirika sikungakutayitseni chinthu chilichonse. Yehova ndi “Mulungu wa chisangalalo,” ndipo amafuna kuti inuyo muzisangalala ndi moyo. (1 Timoteyo 1:11) Tsopano, onani za makhalidwe ena amene muyenera kuwapewa n’cholinga choti mukhalebe ndi khalidwe labwino, kuti mukhale ndi moyo wosangalala ndiponso woyanjidwa ndi Mulungu.

Pewani Khalidwe la Chiwerewere

Kudzera m’Mawu ake Baibulo, Yehova anakhazikitsa lamulo la ukwati lakuti: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:21-24) Popeza anthu okwatirana amakhala “thupi limodzi,” iwo amalemekeza makonzedwe a Mulungu a ukwati ngati amakondana ndiponso kugonana ndi mwamuna kapena mkazi wawo yekha basi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ukwati ukhale wolemekezeka pakati pa onse, ndi kama wa ukwati akhale wosaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweruza achiwerewere ndi achigololo.” (Aheberi 13:4) Mawu oti “kama wa ukwati” akutanthauza kugonana kwa mwamuna ndi mkazi okwatirana mwalamulo. Ndiyeno ngati munthu yemwe ali pabanja atagonana ndi munthu wina yemwe si mwamuna kapena mkazi wake, ndiye kuti wachita chigololo ndipo angadzalangidwe ndi Mulungu.​—Malaki 3:5.

Nanga bwanji za kugonana munthu asanakwatire? Kuchita zimenezinso n’kotsutsana ndi mfundo za makhalidwe abwino za Yehova. “Pakuti Mulungu akufuna kuti . . . [mupewe] dama,” limatero Baibulo. (1 Atesalonika 4:3) Kugonana akazi kapena amuna okhaokha, kugonana ndi wachibale, ndi kugona nyama, onsewa ndi machimo pamaso pa Mulungu. (Levitiko 18:6, 23; Aroma 1:26, 27) Aliyense amene akufuna kukondweretsa Mulungu ndiponso kusangalaladi ndi moyo, ayenera kupeweratu chiwerewere.

Nanga bwanji ngati munthu wosakwatira ali ndi chizolowezi chochita zinthu zodzutsa chilakolako cha kugonana? Khalidwe limenelinso silikondweretsa Yehova. (Agalatiya 5:19) Munthu ayeneranso kupewa kumaganizira zachiwerewere. Yesu ananena kuti: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.” (Mateyo 5:28) Mawu amenewa akukhudza kuona zithunzi zolaula m’mabuku, m’mafilimu, kapena pa Inteneti; kuwerenga nkhani zolaula; ndi kumvera nyimbo zopatsa maganizo a kugonana. Kupewa zinthu zimenezi kumakondweretsa Mulungu, ndiponso kumathandiza kuti munthu akhale ndi moyo wabwino.

Bwanji nanga za kukopana? Ngati munthu wokwatira kapena wokwatiwa akuchita zinthu zokopa munthu wina yemwe sanakwatirane naye, angasonyeze kuti sakumvera mfundo za m’Baibulo ndiponso sakulemekeza Yehova. (Aefeso 5:28-33) N’zosayenera m’pang’ono pomwe kwa anthu osakwatirana kukopana pongofuna kusangalala basi. Kodi zingakhale bwanji ngati munthu winayo atayamba kuganiza kuti mukum’funadi? Tangoganizani ululu umene angakhale nawo mumtima akazindikira kuti munkangochita zinthu mocheza chabe! Ndiponso mfundo yoopsa n’njoti kukopana kungatsogolere ku tchimo la chigololo kapena dama. Koma ngati tikhalabe ndi khalidwe labwino pochita zinthu ndi anthu omwe si amuna kapena akazi anzathu, ulemu wathu umakula.​—1 Timoteyo 5:1, 2.

Kukondweretsa Mulungu pa Nkhani Zina

M’mayiko ambiri, zakumwa zoledzeretsa zimapezeka mosavuta. Kodi kumwa zakumwa zimenezi n’kulakwa? Kumwa pang’ono vinyo, mowa, kapena zakumwa zina zoledzeretsa sikoletsedwa m’Malemba. (Salmo 104:15; 1 Timoteyo 5:23) Komabe, kumwetsa mowa ndiponso kuledzera n’zosavomerezeka pamaso pa Mulungu. (1 Akorinto 5:11-13) Ndithudi, inuyo simungafune kuti kumwetsa mowa kuwononge thanzi lanu komanso kusokoneze banja lanu.​—Miyambo 23:20, 21, 29-35.

Yehova ndi “Mulungu wa choonadi.” (Salmo 31:5) “N’kosatheka Mulungu kunama,” limatero Baibulo. (Aheberi 6:18) Choncho mudzapewa bodza ngati mukufuna kuti Mulungu azikuyanjani. (Miyambo 6:16-19; Akolose 3:9, 10) Baibulo limalangiza Akhristu kuti “aliyense wa inu  alankhule zoona kwa mnansi wake.”​—Aefeso 4:25.

Palinso chizolowezi chotchova njuga. Ngakhale kuti anthu ambiri amaikonda, njuga ndi dyera, chifukwa chakuti anthu amafuna kuti anzawo aluze kuti iwo apeze ndalama. Yehova sayanja anthu amene ‘amakonda kupeza phindu mwachinyengo.’ (1 Timoteyo 3:8) Ngati mukufuna kukondweretsa Yehova, muyenera kupewa mtundu uliwonse wa njuga, kuphatikizapo malotale. Mukatero, mudzaona kuti muzikhala ndi ndalama zambiri zosamalirira banja lanu.

Kuba, komwe ndi kutenga zinthu zomwe si zanu, ndi mtundu winanso wa dyera. “Usabe,” limatero Baibulo. (Eksodo 20:15) Si bwino kugula zinthu zomwe mukudziwa kuti n’zakuba, ndiponso kutenga zinthu za ena popanda chilolezo chawo. “Wakubayo asabenso,” limatero Baibulo, “koma agwire ntchito molimbika, kugwira ndi manja ake ntchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.” (Aefeso 4:28) M’malo mwa kuba nthawi kuntchito, anthu okonda Yehova amagwira ntchito tsiku lonse mokhulupirika. Iwo ‘amafuna kuchita zinthu zonse moona mtima.’ (Aheberi 13:18) Ndipo kukhala ndi chikumbumtima chabwino kumachititsa kuti munthu akhale ndi mtendere wa mumtima.

Kodi Mulungu amamuona bwanji munthu wa khalidwe laukali ndi lachiwawa? Baibulo limachenjeza kuti: “Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga; ngakhale kupita ndi mwamuna waukali.” (Miyambo 22:24) Mkwiyo wosalamulirika umachititsa munthu chiwawa. (Genesis 4:5-8) Ponena za kubwezera, Baibulo limati: “Musabwezere choipa pa choipa. Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino. Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Okondedwa, musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu; pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’” (Aroma 12:17-19) Tikamatsatira malangizo amenewa, tidzakhala ndi mtendere wochuluka pa moyo wathu, ndipo mtendere umenewo udzawonjezera chimwemwe chathu.

Mungathe Kukhala Wokhulupirika

Kodi n’zotheka kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale mutakumana ndi ziyeso? Inde, n’zotheka. Zindikirani kuti Mulungu akufuna kuti inuyo mupambane ndiponso musonyeze kuti Satana n’ngwabodza pa nkhani ya kukhulupirika, chifukwa Mawu Ake amati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”​—Miyambo 27:11.

Mungapemphere kwa Yehova kuti akuthandizeni kukhala wolimba n’cholinga choti muthe kuchita zinthu zabwino zimene iye amafuna. (Afilipi 4:6, 7, 13) Choncho, chitani khama kuti mudziwe zambiri za Mawu a Mulungu, Baibulo. Kusinkhasinkha mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zomwe mukuphunzira m’Baibulo, kungakuthandizeni kuti muzikonda Mulungu kwambiri ndiponso muzichita zinthu zom’kondweretsa. “Chifukwa kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake; ndipo malamulo akewo si olemetsa,” limatero lemba la 1 Yohane 5:3. Mboni za Yehova za kwanuko zidzasangalala kukuthandizani kuphunzira Baibulo. Mukhoza kuonana ndi wa Mboni aliyense, kapena kulembera kalata kwa ofalitsa magazini ino.

[Chithunzi patsamba 4]

Yobu anakhalabe wokhulupirika poyesedwa

[Chithunzi patsamba 7]

Mukamaphunzira zambiri za m’Mawu a Mulungu, mudzakhala olimba pochita zinthu zabwino