Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Anadalitsa Kwambiri Mtima Wanga Wofuna Kukhala Mmishonale

Yehova Anadalitsa Kwambiri Mtima Wanga Wofuna Kukhala Mmishonale

 Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Anadalitsa Kwambiri Mtima Wanga Wofuna Kukhala Mmishonale

Yosimbidwa ndi Sheila Winfield da Conceição

Mmishonale wina amene anabwera kudzacheza kuchokera ku Africa anatiuzapo kuti m’gawo lake aliyense amamuitana kuti alowe m’nyumba ndipo amamvetsera mwachidwi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndinaganiza kuti, ‘Ndingakonde kwabasi kugwira ntchito m’gawo ngati limenelo!’ Kukambirana kumeneko kunandipatsa ineyo, amene panthawiyo ndinali ndi zaka 13, mtima wofuna kudzakhala mmishonale.

KOMABE, banja lathu linayamba kale kwambiri kuphunzira za Yehova. Tsiku lina m’mawa mu 1939, anyamata awiri ovala bwino anafika pa nyumba yathu m’tawuni ya Hemel Hempstead, kunja pang’ono kwa dera la Greater London, m’dziko la England. Anali a Mboni za Yehova. Ine ndinali ndi chaka chimodzi chokha, choncho sindikumbukira ulendo wawowu. Mayi anawauza kuti bambo mwina angasangalale ndi uthenga wawowo, koma abwera kunyumba 9 koloko usiku, ndipo anatero pofuna kungowathamangitsa. Mayi anadabwa kwambiri kuwaona anthu aja atabweradi tsiku lomwelo madzulo. Bambo anga a Henry Winfield, anauza anthuwo kuti alowe m’nyumba ndipo anavomera kuti aziphunzira Baibulo, atayamba kaye atsimikizira mmene anthuwo amaonera nkhani za ndale ndi zokhudza fuko. Bambo anapita patsogolo mwamsanga mpaka kubatizidwa. Patapita zaka zingapo, mayi anga, a Kathleen, nawonso anayamba kuphunzira Baibulo. Anabatizidwa mu 1946.

Mu 1948 ndinayamba kumapita nthawi zonse kolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.  Ndinaganiza kuti ndikufunikira kukhala ndi wotchi kuti ndizipereka malipoti olondola a nthawi imene ndinkathera mu utumiki. Tikasonyeza khalidwe labwino, anafe tinkapatsidwa ndalama yachitsulo yokwana 6 pensi Loweruka lililonse. Ndinasunga ma 6 pensi anga kwa zaka pafupifupi ziwiri kuti ndigule wotchi yotsika mtengo kwambiri imene ndikanapeza pa nthawi imeneyo. Koma Ray, mchimwene wanga wamng’ono kwambiri pa azichimwene anga awiri aang’ono, nthawi zonse ankawauza bambo kuti azimupatsa ndalama makobidi awiri a 3 pensi, osati imodzi ya 6 pensi. Tsiku lina anakakamira kwambiri kuti amupatse makobidi awiri mpaka bambo anapsa mtima. Ray anayamba kulira n’kunena kuti amafuna ndalama ziwiri zachitsulo chifukwa cha chinsinsi chimene chinali pakati pa iyeyo ndi Yehova. Kenaka, Ray anafotokoza kuti: “Khobidi limodzi n’loti ndikaike m’bokosi la zopereka, ndipo linalo ndi langa.” Mayi atamva zimenezi, analira chifukwa cha chimwemwe, ndipo bambo nthawi yomweyo anafunafuna ndalama zachitsulo ziwiri. Ineyo ndinaphunzira kufunika kothandiza nawo pa ntchito ya Ufumu mwa kupereka ndalama zathu.

Chapanthawi imeneyi, bambo anakonza zoti tisamukire ku dera limene kumafunika olengeza Ufumu ambiri. Mu 1949 anagulitsa famu yawo ndi malo awo okumbapo mchenga ndi miyala, n’kuyamba kuchita upainiya, kumatumikira monga mtumiki wa nthawi zonse wa Mboni za Yehova. Ndinabatizidwa pa September 24, 1950, posonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova. Kuyambira nthawi imeneyi, pa nthawi ya tchuthi cha ku sukulu m’chilimwe, ndinkalembetsa upainiya wapatchuthi, (tsopano umatchedwa upainiya wothandiza), ndipo ndinkatha maola 100 pamwezi mu utumiki. Koma chimenechi chinali chiyambi chabe. Pasanapite nthawi yaitali, ndinayamba kufunitsitsa kwambiri mumtima mwanga kuchita zambiri popititsa patsogolo kulambira koona.

Ndinkafuna Kukhala Mmishonale

Mu 1951, bambo anatumizidwa ku tawuni ya Bideford, kumpoto kwa boma la Devon. Titangofika chakumene m’tawuniyi, mmishonale amene ankatumikira ku Africa anadzachezera mpingo wathu, monga ndinafotokozera koyambirira kuja. Pambuyo pa ulendo wakewo, mtima wanga wofuna kudzakhala mmishonale unakhudza zochita zanga zonse. Aphunzitsi anga ku sukulu ankadziwa za cholinga changachi ndipo anayesetsa kundinyengerera kuti ndisinthe, kuti ndidzagwire ntchito ina. Koma pa tsiku lomaliza sukulu, nditapita ku chipinda cha aphunzitsi kukawathokoza ndi kukatsanzikana nawo, mmodzi mwa iwo anati: “Wachita bwino kwambiri! Ndiwe mwana wa sukulu yekhayo amene akudziwadi chomwe akufuna kudzachita pamoyo wake. Tikufuna kuti udzakwaniritse cholinga chako.”

Pasanapite nthawi yaitali, ndinapeza ntchito yaganyu, ndipo pa December 1, 1955, ndinakhala mpainiya wokhazikika. Kenaka, mayi ndi azichimwene anga nawonso anakhala apainiya. Choncho kwa zaka zingapo, tonse m’banja mwathu tinali mu utumiki wa nthawi zonse.

Kupita ku Ireland

Chaka chotsatira, ndinalandira kalata yondipempha kuti ndikatumikire ku Ireland. Apa panali poyambira kukwaniritsa cholinga changa chodzakhala mmishonale. Mu February 1957, ndinafika m’boma la Cork, kum’mwera kwa dziko la Ireland, limodzi  ndi apainiya ena achitsikana, June Napier ndi Beryl Barker.

Utumiki wa kumunda ku Ireland unali wovuta. Anthu a tchalitchi cha Roma Katolika ankativutitsa kwambiri. Tinaphunzira kuti tizionetsetsa kuti pali njira yotulukira mu mdadada wa nyumba kapena m’nyumba zambirimbiri zofanana, kuchitira kuti tisavutike pothawa ngati titafunikira kutero. Tinkabisa njinga zathu chakutaliko, koma nthawi zambiri wina ankazipeza n’kucheka matayala ake kapena kuwaphwetsa.

Tsiku lina, ine ndi Beryl tinkachezera anthu okhala m’nyumba zambirimbiri zofanana, ndipo gulu la ana linayamba kutikuwiza n’kutiponya miyala. Choncho tinalowa m’sitolo, yomwe inali yogundizana ndi nyumba ya munthu wina, momwe ankagulitsamo mkaka. Gulu la anthu achipolowe linayamba kuunjikana panja. Popeza Berly ankakonda mkaka, anamwa matambula awiri kapena atatu a mkaka pang’onopang’ono, poganiza kuti mwina gulu la anthu lija limwazikana. Koma silinamwazikane. Kenaka wansembe wachinyamata analowa m’sitolomo. Poganiza kuti ndife alendo, anatiuza kuti angakonde kutionetsa malowo. Koma choyamba anatipititsa ku chipinda china m’nyumbayo, ndipo ife titakhala phe, anapereka sakramenti yomaliza kwa mwamuna wachikulire amene anali atatsala pang’ono kumwalira. Kenaka tinatuluka m’nyumbamo ndi wansembeyo. Gululo litationa tikucheza ndi wansembeyo, linamwazikana.

Kupita ku Gileadi

Mu 1958, msonkhano wa mayiko wa Divine Will unakonzedwa kuti uchitikire ku New York. Bambo anali kupita ku msonkhanoko, ndipo inenso ndinafuna kupita nawo, koma ndinalibe ndalama. Kenaka agogo anga anamwalira mwadzidzidzi n’kundisiyira ndalama zokwana mapaundi 100 (madola 280). Ndalama zokwerera ndege, kupita n’kubwera ku msonkhanoko zinali mapaundi 96, choncho nthawi yomweyo ndinapita kukagula tikiti ya ndege.

Patangotha masiku ochepa, m’bale woimira ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Britain anabwera kudzatiyendera ndipo anatipempha apainiya apadera tonse amene tinali kupita ku msonkhanowo kuti tilembe mafomu ofunsira maphunziro a umishonale ku Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Ndinangoona ngati kutulo! Anapereka zikalata zofunsira umishonale kwa aliyense kupatulapo ine, chifukwa anati ndachepa. Ndinamupempha kuti nanenso andipatseko, n’kumufotokozera kuti ndinali n’tachoka kale ku dziko lakwathu ndi kuti ndinali kale ngati mmishonale. Ataona kuumirira kwanga, anandipatsa fomu. Ndinapemphera kwambiri kuti andivomere. Yankho lake linabwera mwamsanga, ndipo ndinaitanidwa kupita ku Gileadi.

Ndinasangalala kwambiri kulowa nawo m’kalasi ya nambala 33 ya Gileadi, limodzi ndi apainiya ena 81 ochokera m’mayiko 14. Miyezi isanu imene tinali kumeneko inadutsa mwamsanga kwambiri. Chakumapeto, M’bale Nathan H. Knorr anatikambira nkhani yolimbikitsa kwambiri kwa maola anayi. Analimbikitsa amene angathe kukhala mbeta moyo wawo wonse kuti atero. (1 Akorinto 7:37, 38)  Koma kwa ife amene timafuna kuti tsiku lina tidzakhale pabanja, anatiuza kuti tilembe ndandanda ya zimene timafuna mwa mwamuna kapena mkazi amene tidzakwatirane naye. Kenaka, pakapezeka munthu amene tingathe kumanga naye banja, tiziyamba taona ngati akukwaniritsa zofunika zathu zija.

Ndandanda yanga ya zimene ndinkafuna kuti mwamuna wanga adzakwaniritse inali ndi zotsatirazi: Anayenera kukhala mmishonalenso ndipo azikonda Yehova, azidziwa choonadi cha m’Baibulo kuposa ineyo, akhale wokonzeka kusakhala ndi ana Armagedo isanafike kuti tipitirizebe kukhala mu utumiki wa nthawi zonse, akhale wodziwa bwino Chingelezi, ndipo akhale wamkulu kuposa ine. Ndandanda imeneyi inandithandiza kwambiri, popeza ndinali ndi zaka 20 zokha ndipo ndinali n’tatsala pang’ono kupita kukatumikira ku dziko lakutali.

Kupita ku Brazil

Lamlungu, pa August 2, 1959, tinamaliza maphunziro athu ndipo anatiuza komwe tinali kukatumikira. Ine ndi Vehanouch Yazedjian, Sarah Greco, Ray ndi Inger Hatfield, Sonia Springate, ndi Doreen Hines, tinatumizidwa ku Brazil. Tinasangalala kwambiri. Ndinkaganiza kuti kumeneko ndikaonako nkhalango, njoka, mitengo ya labala, ndiponso Amwenye a khungu lofiira. Koma n’tafika, ndinadabwa kwambiri! M’malo mofika ku nkhalango ya Amazon, ndinafika ku mzinda wamakono wa Rio de Janeiro, komwe kunali kotentha, ndipo panthawiyo unali likulu la dzikolo.

Ntchito yathu yoyamba inali kuphunzira Chipwitikizi. Mwezi woyamba, tinkaphunzira maola 11 tsiku lililonse. Nditalalikira ku Rio kwakanthawi n’kukhala pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova kumeneko, ndinatumizidwa ku nyumba ya amishonale mu mzinda wa Piracicaba, m’boma la São Paulo, ndipo kenaka ananditumiza ku nyumba ya amishonale mu mzinda wa Porto Alegre, m’boma la Rio Grande do Sul.

Kenaka, kumayambiriro kwa chaka cha 1963, ndinalandira kalata yondipempha kuti ndikagwire ntchito m’dipatimenti yomasulira mabuku ku nthambi. Floriano Ignez da Conceição, amene anatiphunzitsa Chipwitikizi titangofika kumene, ndi amene anali woyang’anira wa dipatimenti imeneyi. Anaphunzira choonadi mu 1944, pamene ku Brazil kunali Mboni 300 zokha, ndipo anaphunzira nawo kalasi ya nambala 22 ya Gileadi. Tsiku lina, patapita miyezi ingapo, M’bale Conceição anandipempha kuti nditsalire kuntchito nthawi yopita kodya chakudya chamasana ikakwana, chifukwa anali nane mawu. Poyamba ndinachita mantha. Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi chilipo chimene ndalakwa?’ Belu lopitira kokadya litalira, ndinawafunsa zomwe amafuna kundiuza. Poyankha, anandiuza kuti, “Ndikukufuna ukwati. Ndiye ukuti bwanji?” Ndinangoti kakasi. Ndinawauza kuti andipatse nthawi kuti ndiganizire kaye, kenaka ndinathamangira kokadya chakudya chamasana.

Floriano sanali m’bale woyamba kundifunsira. Koma mpaka kufika pa nthawi imeneyo, palibe amene anakwanitsa zofunika zomwe zinali pa ndandanda yanga ija. Ndikukhulupirira kuti ndandanda imeneyo inandithandiza kupewa kusankha molakwika. Komano Floriano anakwaniritsa zofunika zonse zija! Choncho tinakwatirana pa May 15, 1965.

Kupirira Matenda

Ine ndi Floriano tasangalala ndi ukwati wathu, ngakhale kuti takumana ndi mavuto osiyanasiyana. Vuto limodzi mwa amenewa ndi matenda a Floriano, amene anayamba titangotsala pang’ono kukwatirana. Zaka zingapo m’mbuyomo, phapo lake lakumanzere linaphwa, ndipo zotsatirapo za zimenezi tsopano zinayamba kumuvutitsa kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, tinachoka pa Beteli ndipo tinaikidwa kukhala apainiya apadera mu mzinda wa Teresópolis, m’dera lamapiri la m’boma la Rio de Janeiro. Tinkaganiza kuti nyengo ya kumeneko idzamuthandiza kuchira.

Kuwonjezera apo, mu December 1965, ndinalandira uthenga woti mayi anga akudwala kwambiri khansa. Tinkalemberana makalata pafupipafupi, koma panali patatha zaka 7 kuchokera pamene tinaonana komaliza. Choncho anatilipirira ndege kuti tipite ku England tikawaone. Anawachita opaleshoni, koma madokotala sanathe kuchotsa khansayo. Ngakhale kuti anali chigonere ndipo anali kudwala kwambiri, sanasiyebe kufuna kulalikira. Anali ndi makina a taipilaita m’chipinda mwawo kuti munthu aziwalembera makalata. Ankalalikiranso mwachidule kwa anthu obwera kudzawazonda. Anamwalira pa November 27, 1966. M’mwezi umenewo anapereka lipoti la maola khumi a utumiki wa kumunda! Bambo anapitirizabe kuchita upainiya mokhulupirika mpaka imfa yawo mu 1979.

 Mayi atamwalira, ine ndi Floriano tinabwerera ku Brazil, kumene takhala tikutumikira mpaka pano m’boma la Rio de Janeiro. Poyamba tinapatsidwa ntchito yoyendayenda ku likulu la bomali, koma mwayi umenewu sitinakhale nawo kwa nthawi yaitali, chifukwa Floriano anayambiranso kudwala kwambiri. Kenaka tinabwerera ku Teresópolis kukakhala apainiya apadera.

Mu 1974, pambuyo pa zaka zambiri zolandira chithandizo, chomwe chinali chopweteka, madokotala anachotsa phapo lakumanzere la Floriano. Panthawi imeneyo, sanathe kutumikira monga woyang’anira wotsogolera kapena mpainiya wapadera koma ankatha kuchititsa maphunziro a Baibulo panthawi yozonda odwala kuchipatala. Limodzi mwa maphunzirowa ankachititsa m’Chingelezi ndi Bob, munthu wachikulire wa ku United States amene anapuma pantchito. Bob anaphunzira choonadi ndipo kenaka anabatizidwa. Floriano anachira pang’onopang’ono ndipo wakhala akutumikira monga mpainiya wokhazikika kuyambira nthawi imeneyo.

Yehova Wadalitsa Utumiki Wanga

Pa zaka zonsezi, ndapitiriza kutumikira monga mpainiya wapadera, ndipo Yehova wadalitsa utumiki wanga. Ku Teresópolis, ndinakhala ndi mwayi wapadera wothandiza anthu oposa 60 kudzipereka kwa Yehova. Mmodzi mwa amenewa ndi mzimayi wina dzina lake Jupira, amenenso ndinamuphunzitsa kuwerenga. M’kupita kwa nthawi, ndinaphunzira ndi ana ake akuluakulu 8. Chifukwa cha zimenezi, Jupira ndi achibale ake oposa 20 akutumikira Yehova masiku ano. Mmodzi ndi mkulu, atatu ndi atumiki othandiza, ndipo awiri ndi apainiya.

Ndaphunzira kuti ndisamakayikire zoti anthu enaake akhoza kuphunzira choonadi. Panthawi inayake, ndinkachita phunziro la Baibulo ndi mtsikana winawake dzina lake Alzemira pamene mwamuna wake, Antônio, anandiopseza kuti andikuwizira agalu awiri akuluakulu ndikapanda kuchoka m’nyumba mwawo nthawi yomweyo. Kuyambira panthawi imeneyo, ndinkangoonana patalipatali ndi Alzemira mpaka patapita zaka 7, pamene Antônio anandilola kuti ndiyambirenso kuphunzira Baibulo ndi mkazi wakeyo. Komabe, Antônioyo payekha ankakana ndikati ndilankhule naye za Baibulo. Koma tsiku lina kukugwa mvula, ndinamupempha Antônio kuti akhale nawo pa phunziro lathu. Kenaka ndinazindikira kuti vuto lake linali loti sankatha kuwerenga. Kuyambira nthawi imeneyo, Floriano ndi anthu ena anaphunzira naye Baibulo ndipo anamuphunzitsa kuwerenga. Panopa, Alzemira ndi Antônio onse anabatizidwa. Antônio amathandiza kwambiri mu mpingo, ndipo nthawi zambiri amakonda kupitira limodzi mu utumiki ndi achinyamata osiyanasiyana.

Izi n’zochepa chabe mwa zinthu zimene zatichitikira pa zaka zoposa 20 zimene tinatumikira ku Teresópolis. Kumayambiriro kwa 1988, tinapatsidwa gawo latsopano, lomwe linali mzinda wa Niterói, kumene tinatumikira kwa zaka zisanu zotsatira tisanasamukire ku Santo Aleixo. Kenaka tinasamukira ku mpingo wa Japuíba pakatikati pa boma la Rio de Janeiro ndipo tinali ndi mwayi wapadera woyambitsa mpingo wa Ribeira.

Moyo Wabwino Koma Wosalira Zambiri

Pa zaka zapitazi, ine ndi Floriano takhala ndi mwayi wothandiza anthu oposa 300 kupereka miyoyo yawo kwa Yehova. Panopa, ena a iwo akutumikira ku nthambi, ena ndi apainiya, akulu, ndi atumiki othandiza. Ndine woyamikira kwambiri kuti Mulungu, kudzera mwa mzimu wake woyera, wandigwiritsa ntchito kuthandiza anthu ambiri chonchi!​—Maliko 10:29, 30.

N’zoona kuti Floriano wakhala akuvutika ndi matenda aakulu. Ngakhale ndi choncho, iye akadali wolimba mwauzimu, wachimwemwe, ndi wodalira Yehova. Nthawi zambiri amanena kuti: “Masiku ano chimwemwe sichibwera chifukwa chokhala ndi moyo wopanda mavuto. Chimabwera chifukwa chokhala ndi thandizo la Yehova polimbana ndi mavuto athu.”​—Salmo 34:19.

Mu 2003, anandipeza ndi khansa m’diso langa lakumanzere. Anandichita opaleshoni, ndipo anandichotsa disolo n’kundiika lina lochita kupanga, limene limafunika kulitsuka nthawi zambiri patsiku. Ngakhale ndi choncho, Yehova wandidalitsa pondipatsa mphamvu zimene ndimafunikira kuti ndipitirizebe kuchita upainiya wapadera.

Moyo wanga wakhala wosalira zambiri. Komabe, Yehova wandidalitsa mu utumiki wanga ndipo wandilemeretsa mwauzimu. Zimene ananena mlongo yemwe anali mmishonale uja za ntchito yolalikira ku Africa, zakhalanso chimodzimodzi kwa ife mu utumiki wathu ku Brazil. Zoonadi, Yehova wadalitsa kwambiri mtima wanga wofuna kukhala mmishonale!

[Chithunzi patsamba 9]

Ndili ndi anthu a m’banja mwathu, mu 1953

[Chithunzi patsamba 9]

Kulalikira ku Ireland, mu 1957

[Chithunzi patsamba 10]

Ndili ku Brazil mu 1959, limodzi ndi amishonale anzanga. Kuyambira kumanzere kupita kumanja: Ineyo, Inger Hatfield, Doreen Hines, ndi Sonia Springate

[Chithunzi patsamba 10]

Ndili ndi mwamuna wanga