Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaona Zinthu Zopatulika Monga Mmene Yehova Amazionera?

Kodi Mumaona Zinthu Zopatulika Monga Mmene Yehova Amazionera?

 Kodi Mumaona Zinthu Zopatulika Monga Mmene Yehova Amazionera?

“Muonetsetse kuti . . . pasakhale wachiwerewere kapena aliyense wosayamikira zinthu zopatulika.”​—AHEBERI 12:15, 16.

1. Kodi ndi mzimu uti wa masiku ano umene atumiki a Yehova alibe?

MASIKU ano, anthu ambiri m’dzikoli sachita chidwi kwambiri ndi zinthu zopatulika. Katswiri wina wa chikhalidwe cha anthu wachifalansa dzina lake Edgar Morin, anati: “Anthu asiya kutsatira zinthu zonse zimene kale zinkaonedwa ngati maziko a makhalidwe abwino, zinthu monga Mulungu, chilengedwe, dziko lako, mbiri yakale, ndi nzeru. . . . M’malo mwake akusankha okha makhalidwe amene akufuna kukhala nawo.” Zimenezi zikusonyeza “mzimu wa dziko” kapena “mzimu umene tsopano ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” (1 Akorinto 2:12; Aefeso 2:2) Koma anthu amene adzipereka kwa Yehova ndipo amavomereza kuti iye ndi woyenera kulamulira, alibe mzimu wosalemekeza zinthu zopatulika umenewu. (Aroma 12:1, 2) M’malo mwake, atumiki a Mulungu amazindikira kufunika kwa zinthu zopatulika, kapena zoyera, pa kulambira kwawo kwa Yehova. Kodi ndi zinthu ziti pamoyo wathu zimene ziyenera kukhala zopatulika? Nkhani ino ifotokoza zinthu zisanu zimene zili zoyera kwa atumiki onse a Mulungu. Nkhani yotsatira ifotokoza za kupatulika kwa misonkhano yathu yachikhristu. Koma kodi mawu akuti “kuyera” amatanthauza chiyani kwenikweni?

2, 3. (a) Kodi Malemba amagogomezera bwanji chiyero cha Yehova? (b) Kodi timasonyeza bwanji kuti timaona kuti dzina la Yehova n’loyera?

2 Mu Chiheberi cha m’Baibulo, mawu akuti “kuyera” ali ndi tanthauzo la kuikidwa padera. Pa kulambira, chinthu “choyera” n’chinthu chimene sichigwiritsidwa ntchito zawamba, kapena chimene chimaonedwa kuti n’chopatulika. Yehova ndi woyera kuposa chilichonse. Amatchedwa “Woyera Koposa Onse.” (Miyambo 9:10; 30:3, NW) Kale mu Isiraeli, mkulu wa ansembe ankavala nduwira yomatidwa chitsulo chagolide chozokotedwa mawu akuti “Chiyero n’cha Yehova.” (Eksodo 28:36, 37, NW) Malemba amasonyeza akerubi ndi aserafi akumwamba omwe azungulira mpando wachifumu wa Yehova akunena kuti: “Woyera, Woyera, Woyera, Yehova.” (Yesaya 6:2, 3; Chivumbulutso 4:6-8) Kubwereza kumeneku kukusonyeza kuti Yehova ndi woyera, wosadetsedwa, ndi waukhondo kuposa wina aliyense. Iye ndiye Gwero la chiyero chonse.

3 Dzina la Yehova n’lopatulika, kapena kuti, n’loyera. Wamasalmo anati: “Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa; ili ndilo loyera.” (Salmo 99:3) Yesu anatiphunzitsa kupemphera kuti: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyo 6:9) Mayi a Yesu a padziko lapansi, Mariya, analengeza kuti: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova. . . . Wamphamvuyo wandichitira zazikulu, ndipo dzina lake ndi loyera.” (Luka 1:46, 49) Monga atumiki a Yehova, timaona kuti dzina lake ndi loyera ndipo timapewa kuchita chilichonse chimene chingachititse kuti dzina loyera limenelo litonzedwe. Komanso, maganizo athu pa zinthu zopatulika ndi ofanana ndi a Yehova, kutanthauza kuti, zinthu zimene amaziona kuti n’zopatulika, nafenso timaziona kuti n’zopatulika.​—Amosi 5:14, 15.

Chifukwa Chimene Timalemekezera Kwambiri Yesu

4. N’chifukwa chiyani Baibulo limamutcha Yesu “Woyera”?

4 Yesu pokhala “mwana wobadwa yekha” wa  Mulungu woyera, Yehova, analengedwa woyera. (Yohane 1:14; Akolose 1:15; Aheberi 1:1-3) Choncho amatchedwa “Woyera wa Mulungu.” (Yohane 6:69) Anasunga chiyero chake pamene moyo wake unasamutsidwa kumwamba kubwera pa dziko lapansi, chifukwa Mariya anabereka Yesu mwa mphamvu ya mzimu woyera. Mngelo anauza Mariya kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe . . . wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35) Popemphera kwa Yehova, Akhristu ku Yerusalemu kawiri konse anatchula Mwana wa Mulungu kuti “Yesu, mtumiki wanu woyera.”​—Machitidwe 4:27, 30.

5. Kodi Yesu anakwanitsa ntchito yopatulika yotani ali padziko lapansi, ndipo n’chifukwa chiyani magazi ake ali a mtengo wapatali?

5 Yesu anali ndi ntchito yopatulika yoti akwanitse ali padziko lapansi. Pa ubatizo wake mu 29 C.E., Yesu anadzozedwa kukhala Mkulu wa Ansembe wa kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. (Luka 3:21, 22; Aheberi 7:26; 8:1, 2) Kuwonjezera apo, anafunika kudzafa imfa yansembe. Magazi ake okhetsedwa anadzapereka dipo lopulumutsa anthu ochimwa. (Mateyo 20:28; Aheberi 9:14) Choncho timaona kuti magazi a Yesu ndi opatulika, “a mtengo wapatali.”​—1 Petulo 1:19.

6. Kodi timamuona bwanji Khristu Yesu, ndipo n’chifukwa chiyani timatero?

6 Posonyeza kuti timalemekeza kwambiri Mfumu yathu ndi Mkulu wa Ansembe, Khristu Yesu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu anam’kwezera [Mwana wake] pamalo apamwamba. Ndipo anam’komera mtima kum’patsa dzina loposa lina lililonse. Anatero kuti m’dzina la Yesu, onse apinde maondo awo, aja akumwamba, a padziko lapansi, ndi a pansi pa nthaka. Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.” (Afilipi 2:9-11) Mwa kugonjera mwachimwemwe kwa Mtsogoleri wathu ndi Mfumu yathu yolamulira, Khristu Yesu, yemwe ndi Mutu wa mpingo wachikhristu, timasonyeza kuti timaona zinthu zopatulika monga mmene Yehova amazionera.​—Mateyo 23:10; Akolose 1:18.

7. Kodi timasonyeza bwanji kuti tikugonjera Khristu?

7 Kugonjera Khristu kumafunanso kusonyeza ulemu woyenerera kwa amuna amene akuwagwiritsa ntchito kutsogolera ntchito imene iyeyo akuyendetsa panopo. Ntchito ya anthu odzozedwa ndi mzimu amene amapanga Bungwe Lolamulira ndiponso ntchito ya oyang’anira oikidwa ndi bungwe limeneli mu nthambi, zigawo, madera, ndi mipingo tiyenera kuiona ngati udindo wopatulika. Choncho dongosolo limeneli limafunika kuti tizililemekeza kwambiri ndi kuligonjera.​—Aheberi 13:7, 17.

Anthu Oyera

8, 9. (a) Kodi Aisiraeli anali anthu oyera m’njira zotani? (b) Kodi Yehova anatsindika bwanji kwa Aisiraeli kufunika koona zinthu zinazake ngati zopatulika?

8 Yehova anachita chipangano ndi Isiraeli. Ubwenzi umenewu unapatsa mtundu watsopanowo udindo watsopano. Aisiraeli anayeretsedwa, kapena kuti kupatulidwa. Motero Yehova mwiniwakeyo anawauza kuti: “Muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga.”​—Levitiko 19:2; 20:26.

9 Mtundu wa Isiraeli utangobadwa kumene, Yehova anatsindika kwa Aisiraeli kufunika koona zinthu zinazake ngati zopatulika. Sanayenera  kukhudza ngakhale phiri lomwe anaperekerapo Malamulo Khumi, chifukwa akanatero akanaphedwa. Panthawi imeneyo, phiri la Sinai linakhala ngati lopatulika. (Eksodo 19:12, 23) Unsembe, chihema, ndi ziwiya zake zinayenera kuonedwanso ngati zopatulika. (Eksodo 30:26-30) Kodi zinthu zili bwanji masiku ano mu mpingo wachikhristu?

10, 11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mpingo wachikhristu wa odzozedwa ndi wopatulika, ndipo kodi zimenezi zimawakhudza bwanji a “nkhosa zina”?

10 Mpingo wachikhristu wa odzozedwa ndi wopatulika pamaso pa Yehova. (1 Akorinto 1:2) Ndipotu, gulu lonse la Akhristu odzozedwa omwe ali padziko lapansi panthawi ina iliyonse likuyerekezeredwa ndi kachisi wopatulika, ngakhale kuti si kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. Yehova amakhala m’kachisi ameneyo mwa mzimu wake woyera. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mogwirizana ndi [Khristu Yesu], nyumba yonse, pokhala yolumikizana bwino, ikukula kukhala kachisi woyera wa Yehova. Mogwirizana ndi iye, inunso mukumangidwa pamodzi kukhala malo oti Mulungu akhalemo mwa mzimu.”​—Aefeso 2:21, 22; 1 Petulo 2:5, 9.

11 Paulo analembanso kwa Akhristu odzozedwa kuti: “Kodi inu simukudziwa kuti ndinu kachisi wa Mulungu, ndi kuti mzimu wa Mulungu ukukhala mwa inu? . . . Kachisi wa Mulungu ndi woyera, ndipo kachisiyo ndinu amene.” (1 Akorinto 3:16, 17) Mwa mzimu wake, Yehova ‘amakhala’ pakati pa odzozedwa ndipo ‘amayenda pakati pawo.’ (2 Akorinto 6:16) Iye nthawi zonse amatsogolera “kapolo” wake wokhulupirika. (Mateyo 24:45-47) A “nkhosa zina” amayamikira mwayi wawo wochitira zinthu limodzi ndi odzozedwa.​—Yohane 10:16; Mateyo 25:37-40.

Zinthu Zopatulika Pamoyo Wathu Wachikhristu

12. Kodi ndi zinthu ziti zimene zili zopatulika pamoyo wathu, ndipo n’chifukwa chiyani zili zotero?

12 N’zosadabwitsa kuti zinthu zambiri zokhudzana ndi moyo wa anthu odzozedwa a mumpingo wachikhristu ndi anzawo n’zopatulika. Ubwenzi wathu ndi Yehova n’chinthu chopatulika. (1 Mbiri 28:9; Salmo 36:7) Ubwenziwu ndi wamtengo wapatali kwambiri kwa ife moti sitilola chinthu chilichonse kapena munthu aliyense kutisokonezera ubwenzi wathu ndi Mulungu wathu, Yehova. (2 Mbiri 15:2; Yakobe 4:7, 8) Pemphero limatithandiza kwambiri kuti tikhalebe ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova. Pemphero linali lopatulika kwambiri kwa mneneri Danieli moti anapitirizabe mokhulupirika chizolowezi chake chopemphera kwa Yehova ngakhale kuti  zimenezi zinaika moyo wake pangozi. (Danieli 6:7-11) “Mapemphero a oyera,” kapena kuti Akhristu odzozedwa, akuyerekezeredwa ndi zinthu zomwe ankafukiza polambira pakachisi. (Chivumbulutso 5:8; 8:3, 4; Levitiko 16:12, 13) Kuyerekezera kumeneku kukusonyeza bwino kupatulika kwa pemphero. Kulankhula ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse ndi mwayi wapadera kwambiri! Choncho n’zosadabwitsa kuti pemphero timaliona kuti ndi lopatulika pamoyo wathu.

13. Kodi ndi mphamvu iti imene ili yoyera, ndipo tizitani kuti tiilole kugwira ntchito pamoyo wathu?

13 Pamoyo wa Akhristu odzozedwa ndi anzawo, pali mphamvu imene amaionadi kuti ndi yopatulika. Mphamvu yake ndi mzimu woyera. Mzimu umenewo ndi mphamvu yogwira ntchito ya Yehova, ndipo popeza nthawi zonse umachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, amene ali woyera, moyenerera umatchedwa “mzimu woyera,” kapena “mzimu wa chiyero.” (Yohane 14:26; Aroma 1:4) Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Yehova amapatsa atumiki ake mphamvu yoti athe kulalikira uthenga wabwino. (Machitidwe 1:8; 4:31) Yehova amapereka mzimu wake “kwa anthu omvera iye monga wolamulira,” amene akupitiriza “kuyenda mwa mzimu,” osati motsatira zilakolako za thupi. (Machitidwe 5:32; Agalatiya 5:16, 25; Aroma 8:5-8) Mphamvu yaikulu imeneyi imathandiza Akhristu kubala “zipatso za mzimu,” zomwe ndi makhalidwe abwino, ndiponso kukhala ndi ‘khalidwe loyera ndi ntchito zosonyeza kudzipereka kwathu kwa Mulungu.’ (Agalatiya 5:22, 23; 2 Petulo 3:11) Ngati timaona kuti mzimu woyera ndi wopatulika, timapewa kuchita chilichonse chomwe chingamvetse chisoni mzimuwo, kapena kuulepheretsa kugwira ntchito pamoyo wathu.​—Aefeso 4:30.

14. Kodi ndi ntchito yapadera iti imene odzozedwa amaiona kuti ndi yopatulika, ndipo kodi a nkhosa zina amagwira nawo bwanji ntchito imeneyi?

14 Mwayi umene tili nawo wodziwika ndi dzina la Mulungu woyera, Yehova, ndi kukhala Mboni zake n’chinthu chinanso chimene timaona kuti n’chopatulika. (Yesaya 43:10-12, 15) Akhristu odzozedwa ayenerezedwa ndi Yehova “kukhala . . . atumiki a chipangano chatsopano.” (2 Akorinto 3:5, 6) Motero, apatsidwa ntchito yolalikira “uthenga wabwino uwu wa ufumu” ndi ‘kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Iwo akugwira ntchito imeneyi mokhulupirika, ndipo anthu mamiliyoni ambiri onga nkhosa akumvera, ndipo akunena mophiphiritsira kwa odzozedwa kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Mokondwera, iwowa amatumikira mwauzimu monga “olima” ndi ‘okonza minda ya mphesa’ a “atumiki a Mulungu wathu” odzozedwa. Mwanjira imeneyo, a nkhosa zina amathandiza kwambiri odzozedwa kukwaniritsa utumiki wawo padziko lonse lapansi.​—Yesaya 61:5, 6.

15. Kodi ndi ntchito iti imene mtumwi Paulo ankaona kuti ndi yopatulika, ndipo n’chifukwa chiyani tili ndi maganizo ofanana ndi ake?

15 Mtumwi Paulo ndi chitsanzo cha munthu amene ankaona kuti utumiki wake wolalikira ndi wopatulika, kapena kuti woyera. Iye anadzitcha “wantchito wa Khristu Yesu wotumikira mitundu ina, kuchita ntchito yoyera ya uthenga wabwino wa Mulungu.” (Aroma 15:16) Polembera kalata Akhristu a ku Korinto, Paulo  anatcha utumiki wake kuti “chuma.” (2 Akorinto 4:1, 7) Mwa utumiki wathu wolalikira, timauza anthu za “mawu opatulika a Mulungu.” (1 Petulo 4:11) Choncho kaya ndife odzozedwa kapena a nkhosa zina, timaona kuti ndi mwayi wopatulika kugwira nawo ntchito yochitira umboni.

‘Kukwaniritsa Chiyero Chathu Poopa Mulungu’

16. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipewe kukhala anthu ‘osayamikira zinthu zopatulika’?

16 Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu anzake kuti asakhale anthu ‘osayamikira zinthu zopatulika.’ M’malo mwake, anawalangiza kuti ‘asunge chiyero,’ ndi kuonetsetsa “kuti pasatumphuke muzu wa ululu woyambitsa mavuto, ndi kuti ochuluka asaipitsidwe nawo.” (Aheberi 12:14-16) Mawu akuti “muzu wa ululu” akuimira anthu ochepa mu mpingo wachikhristu amene angamanyinyirike ndi mmene zinthu zikuchitikira. Mwachitsanzo, akhoza kumatsutsa maganizo a Yehova okhudza kupatulika kwa ukwati kapena kufunika kokhala ndi makhalidwe oyera. (1 Atesalonika 4:3-7; Aheberi 13:4) Kapena mwina angamanene nawo zinthu zampatuko, “nkhani zopeka zimene zimaipitsa zoyera,” zokambidwa ndi anthu amene “apatuka pa choonadi.”​—2 Timoteyo 2:16-18.

17. N’chifukwa chiyani odzozedwa amafunika kuchita khama nthawi zonse kuti asonyeze kuti ali ndi maganizo ofanana ndi a Yehova pa nkhani ya zinthu zimene zili zoyera?

17 Paulo analembera abale ake odzozedwa kuti: “Okondedwanu, tiyeni tidziyeretse kuchotsa chilichonse choipitsa cha thupi ndi cha mzimu, tikumakwaniritsa chiyero chathu poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Mawu amenewa akusonyeza kuti Akhristu odzozedwa, “otenga mbali m’chiitano cha kumwamba,” ayenera kuchita khama nthawi zonse kuti asonyeze kuti amagwirizana ndi maganizo a Yehova pa zinthu zimene zili zoyera, ndipo azitero m’mbali zonse za moyo wawo. (Aheberi 3:1) Mofanana ndi zimenezo, mtumwi Petulo analimbikitsa abale ake obadwa mwa mzimu kuti: “Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa. Koma khalani motsanzira Woyerayo amene anakuitanani; inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse.”​—1 Petulo 1:14, 15.

18, 19. (a) Kodi a “khamu lalikulu” amasonyeza bwanji kuti amaona zinthu zopatulika ngati mmene Yehova amazionera? (b) Kodi nkhani yotsatirayi ikufotokoza mbali ina iti yopatulika ya moyo wathu wachikhristu?

18 Nanga bwanji a “khamu lalikulu,” amene adzapulumuke “chisautso chachikulu”? Nawonso ayenera kusonyeza kuti amaona zinthu zopatulika ngati mmene Yehova amazionera. Buku la Chivumbulutso limati iwowa akuchitira Yehova “utumiki wopatulika” m’bwalo lapadziko lapansi la kachisi wake wauzimu. Akhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu, ndipo mophiphiritsira “achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9, 14, 15) Zimenezi zimawachititsa kukhala ovomerezedwa ndi Yehova ndipo zimawapatsa udindo ‘wodziyeretsa kuchotsa chilichonse choipitsa cha thupi ndi cha mzimu, akumakwaniritsa chiyero chawo poopa Mulungu.’

19 Mbali yofunika pa moyo wa Akhristu odzozedwa ndi anzawo ndiyo kusonkhana nthawi zonse kuti alambire Yehova ndi kuphunzira Mawu ake. Yehova amaona kuti misonkhano ya anthu ake ndi yopatulika. Nkhani yotsatirayi ikufotokoza chifukwa chimene tiyenera kuonera zinthu zopatulika ngati mmene Yehova amazionera pa mbali yofunika kwambiri imeneyi, ndipo ikufotokozanso mmene tiyenera kuchitira zimenezi.

Kubwereza

• Kodi ndi maganizo ati a m’dzikoli amene atumiki a Yehova alibe?

• N’chifukwa chiyani Yehova ali Gwero la zinthu zonse zoyera?

• Kodi timasonyeza bwanji kuti timalemekeza chiyero cha Khristu?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuziona kuti n’zopatulika pamoyo wathu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Kale mu Isiraeli, unsembe, hema, ndi ziwiya zake zinayenera kuonedwa kuti ndi zopatulika

[Chithunzi patsamba 24]

Akhristu odzozedwa padziko lapansi amapanga kachisi woyera

[Zithunzi patsamba 25]

Pemphero ndiponso utumiki wathu wolalikira ndi mwayi wapadera wopatulika