Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupeza Chuma Chauzimu ku Guinea

Kupeza Chuma Chauzimu ku Guinea

 Kupeza Chuma Chauzimu ku Guinea

KWA zaka zambiri, anthu oyendera malo akhala akuika moyo wawo pangozi chifukwa chofunafuna chuma. Anthu olimba mtima amene anafika ku Guinea, ku West Africa, anapeza chuma chamitundu iwiri, chakuthupi ndi chauzimu. Dziko la Guinea, lomwe n’lodzadza ndi miyala ya diamondi, golide, ndi miyala yopangira zitsulo, ndiponso miyala ya aluminiyamu yapamwamba kwambiri, lili ndi anthu oposa naini miliyoni.

Ngakhale kuti m’dzikoli mulibe matchalitchi ambiri Achikristu, anthu amaona kuti kulambira n’kofunika ndipo ambiri amaona kuti chuma chauzimu ndicho chamtengo wapatali. Kodi chuma chimenechi n’chiyani kwenikweni? Ndicho atumiki okhulupirika a Yehova, amene anafotokozedwa pa Hagai 2:7 monga “zofunika za amitundu onse.”

Chuma Chauzimu

Kukumba pansi kwambiri pofunafuna chuma chobisika kumafuna khama lalikulu. N’chimodzimodzinso ndi utumiki wachikristu. Timafunika khama kuti tipeze chuma chauzimu. Ntchito yolalikira Ufumu inayambira pakatikati pa dziko la Guinea, kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1950, ndipo siinafike ku likulu la dzikoli, Conakry, mpaka kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1960. Tsopano m’dzikoli muli Mboni za Yehova pafupifupi 900, m’mipingo ndi m’magulu okwanira 21.

Amishonale anafika m’dzikoli m’chaka cha 1987 ndipo ankagwira ntchito limodzi ndi mpingo umodzi wokha womwe unali ku Conakry. Tsopano mu mzindawu ndiponso m’katikati mwa dzikoli muli amishonale oposa 20. Amishonalewa amachita khama polimbikitsa mipingo ndiponso popita mu utumiki limodzi ndi abale a m’dzikoli.

 Luc, yemwe amakhala ku Conakry, anasangalala atayamba kuphunzira Baibulo ndi Albert, mnyamata yemwe anali dokotala. Albert anali atafufuza choonadi m’matchalitchi osiyanasiyana, ndipo anayamba kukhulupirira zamizimu. Ankavala mphete imene wowombeza wina anam’patsa, ndi chikhulupiriro choti im’bweretsere mwayi. Atakhumudwa kwambiri chifukwa chakuti sankapeza chipembedzo choona, Albert anataya mphete yake ija ndi kupemphera kwa Mulungu kuti: “Mulungu, ngati muliko, ndithandizeni kuti ndikudziweni ndi kukutumikirani. Mukapanda kutero, ndileka kupemphera ndipo ndizingochita zimene ndikufuna.” Patangodutsa nthawi yochepa, Albert anapita ku nyumba kwa mchemwali wake ndipo n’kumeneko komwe anamva mmodzi wa Mboni za Yehova akuchititsa phunziro la Baibulo ndi mwana wamkazi wa mchemwali wakeyo. Posapita nthawi, panakonzedwa zoti Luc ayambe kuphunzira Baibulo ndi Albert.

Mlungu uliwonse, Luc ankasangalala kuyenda makilomita oposa asanu kukaphunzira ndi Albert. Ngakhale kuti Luc anali wosaphunzira kwambiri, Albert, yemwe anali atamaliza maphunziro ake ku yunivesite, anachita chidwi ndi mmene Luc ankakhulupirira Malemba ndiponso mmene ankawagwiritsira ntchito pamoyo wake. Albert anali wosangalala kudziwa kuti Mulungu sindiye amene amachititsa mavuto a anthu, koma kuti Yehova akufuna kuthetsa mavuto onse ndi kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso. (Salmo 37:9-11) Choonadi cha m’Baibulo kuphatikizapo khalidwe labwino limene anaona ku mpingo, zinam’khudza kwambiri Albert.

Komabe, mofanana ndi mwala wa diamondi umene umafunika kudulidwa bwino ndi akatswiri kuti unyezimire, Albert anafunika kuthana ndi makhalidwe oipa a anthu osapembedza Mulungu, kuti azikhala mogwirizana ndi miyezo yolungama ya Mulungu. Anasiya kupita kwa owombeza, anasiya kumwa mowa mwauchidakwa, ndiponso anasiya kutchova njuga. Albert anavutika kwambiri kusiya kusuta fodya. Atapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pamtima kuti am’thandize, anasiya kusuta. Patapita miyezi sikisi, analembetsa mtchatho wa ukwati wake. Mkazi wake anayamba kuphunzira Baibulo. Tsopano onse ndi atumiki obatizidwa a Yehova.

Martin ndi mwala wina wa diamondi wauzimu. Anayamba kuphunzira Baibulo ku Guéckédou ali  ndi zaka 15. Makolo ake omwe anali Akatolika sankafuna kuti iye azipita kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Anamuwonongera mabuku ake ofotokoza za m’Baibulo, anam’menya, ndi kumuthamangitsa kunyumba kwawo. Monga mmene diamondi amapangidwira mwala wa kaboni ukawotchedwa, Martin anayamba kukonda kwambiri choonadi cha m’Baibulo chifukwa chakuti anali kum’tsutsa. Patapita nthawi, maganizo a makolo ake aja anafewa, ndipo anabwerera kunyumba. Kodi chinachititsa kuti makolo ake asinthe n’chiyani? Anaona kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa makhalidwe a Martin ndi abale ake omwe anali ocheperapo kwa iyeyo. Abale akewo anali ndi mzimu wopanduka ndiponso anayamba kuchita zachisembwere. Atakhutira kuti chikhulupiriro chatsopano cha Martin chinali chabwino, bambo ake anayamba kuitana anthu akumpingo kwake kuti azibwera kunyumba kwawo. Mayi a Martin anathokoza kambirimbiri abale, chifukwa cha zonse zimene anachita pothandiza mwana wawoyo. Martin anabatizidwa ali ndi zaka 18, ndipo kenako anapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndipo tsopano ndi mpainiya wapadera.

Chuma Chauzimu Chochokera ku Mayiko Ena

Pamene dziko la Guinea likutumiza ku mayiko ena zinthu zachilengedwe zimene lili nazo, china mwa chuma chake chauzimu chakhala chikulowa m’dzikoli kuchokera ku mayiko ena. Anthu ambiri achoka ku mayiko ena a mu Africa, makamaka chifukwa cha mavuto a zachuma. Ena anathawa kwawo chifukwa cha nkhondo zosatha ndiponso zankhanza.

Ernestine, wochokera ku Cameroon, anakakhala ku Guinea zaka 12 zapitazo. Ankaphunzira ndi Mboni za Yehova ndipo anakhala akupezeka pa misonkhano kwa zaka zambiri koma osabatizidwa. M’chaka cha 2003, misozi inalengeza m’maso mwake pamene ankaonerera ubatizo pa msonkhano wadera wa Mboni za Yehova. Anayamba kudziimba mlandu ndipo anapemphera kwa Yehova kuti: “Ine tsopano ndili ndi zaka 51, ndipo palibe chilichonse chabwino chimene ndakuchitirani. Ndikufuna kukutumikirani.” Pambuyo pake, Ernestine anayamba kuchita zinthu mogwirizana ndi pemphero lake lodzichepetsalo.  Anafotokoza kwa mwamuna amene ankakhala naye kuti angapitirize kukhalira limodzi pokhapokha ngati atakwatirana mwalamulo. Mwamunayo anavomereza, ndipo kenako, Ernestine anatulutsa misozi yachimwemwe pa ubatizo wake mu November 2004.

Kuyambira kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1990, dziko la Guinea linalandira anthu zikwi zambiri othawa ku Liberia ndi Sierra Leone, kuphatikizapo mazana ambiri a atumiki a Yehova. Atangofika ku msasa wa othawa kwawo, abale anakonza kuti azichita misonkhano ya nthawi zonse, anakonzanso zolalikira, ndipo anamanga Nyumba ya Ufumu. Anthu ena anakhala atumiki a Yehova ku msasa komweko. Mmodzi mwa iwo ndi Isaac. Atabatizidwa, anamuuza kuti abwerere pa udindo wake womwe anali nawo pa kampani ina yaikulu ku Liberia, komwe ankagwira ntchito. Koma iye anasankha kukhalabe pa msasa wa Lainé ndipo anayamba upainiya wa nthawi zonse. Anafotokoza kuti: “Tsopano sindiyeneranso kupempha kwa abwana kuti ndipite ku misonkhano yampingo kapena ku msonkhano wadera. Tsopano ndikutumikira Yehova momasuka.” Mu December 2003, pamsasa wakutali ndi tawuni umenewu panachitikira msonkhano wachigawo wa Mboni 150 zomwe zinkakhalira limodzi ndi anthu othawa kwawo okwanira 30,000. Zinali zosangalatsa kuona anthu 591 atasonkhana, kuphatikizapo anthu 9 ogontha amene ankatsatira msonkhano wonse m’chinenero cha manja. Ndipo anthu 12 anabatizidwa. Abale anayamikira kwambiri khama limene linachitika kuti alandire phwando lauzimu limeneli.

Zinthu “Zofunika” Zikusintha Mofunikira

Palibe chopinga chilichonse chimene chingaoneke kuti n’chovuta kuthana nacho kwa anthu amene akufunafuna miyala ya golide ndi diamondi. Ndipo n’zolimbikitsa kuona khama limene anthu atsopano amachita kuti athane ndi zopinga zonse kuti atumikire Yehova. Taganizani zomwe Zainab anakumana nazo.

Ali ndi zaka 13, Zainab anakakamizidwa kupita kuukapolo. Anam’tenga kuchokera ku dziko lakwawo ku West Africa, n’kupita naye ku Guinea. Anamva za uthenga wa m’Baibulo ali ndi zaka 20, ndipo anali ndi chidwi kutsatira zimene ankaphunzira.

Kunali kovuta kuti Zainab azipita kukalambira nawo pa misonkhano yachikristu. Koma ankakonda kwambiri misonkhano ndipo ankaonetsetsa kuti asaphonye misonkhanoyo. (Ahebri 10:24, 25) Ankabisa mabuku ake panja kuti awatenge akamapita kumisonkhano. Maulendo angapo, mbuye wake anam’menya mwankhanza chifukwa chopita ku misonkhano yauzimu imeneyi.

Kenako zinthu zinasintha, ndipo Zainab anamasulidwa kuchoka mu ukapolo. Nthawi yomweyo anayamba kupita ku misonkhano yonse, ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti afulumire kupita patsogolo mwauzimu. Anakana kugwira ntchito yomwe inali ndi malipiro apamwamba, imene ikanamulepheretsa kupita ku misonkhano kuti akalandire malangizo achikristu. Analembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, anakhala wofalitsa Ufumu wosabatizidwa, ndipo kenako anasonyeza kudzipereka kwake kwa Yehova pobatizidwa m’madzi. Atangobatizidwa, anayamba upainiya wothandiza. Patangopita miyezi sikisi, anapempha kuti akhale mpainiya wokhazikika.

Atachita nawo misonkhano yowerengeka, munthu wina wokondwerera anati: “Ndimaiwala kuti ndine wosauka ndikakhala kumisonkhano kuno.” Pomwe anthu ambiri akukhala ndi chidwi pa chuma chakuthupi chokha cha ku Guinea, anthu amene amakonda Yehova akufufuza chuma chauzimu. Inde, “zofunika za amitundu onse” zikuyamba kulambira Yehova koyera komwe kukuchitika masiku ano!

[Bokosi patsamba 8]

GUINEA-2005

Mboni zonse: 883

Maphunziro a Baibulo: 1,710

Opezeka pa Chikumbutso: 3,255

[Mapu patsamba 8]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

GUINEA

Conakry

SIERRA LEONE

LIBERIA

[Chithunzi patsamba 9]

Albert ndi Luc

[Chithunzi patsamba 9]

Nyumba ya Ufumu ku Conakry

[Chithunzi patsamba 10]

Ernestine

[Chithunzi patsamba 10]

Martin

[Chithunzi patsamba 10]

Zainab

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

USAID