Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani pa Deuteronomo 31:2, Baibulo la New World Translation limanena kuti Mose “sadzaloledwanso kutuluka ndi kulowa” monga mtsogoleri wa Israyeli, pamene Mabaibulo ena amasonyeza kuti sadzathanso kutero?

Ngakhale kuti liwu la Chihebri la palembali lingathe kumasuliridwa m’njira zonse ziwirizi, Mabaibulo ena a Chichewa amamasulira lembali mokhala ngati kuti cha kumapeto kwa moyo wake, Mose anali wofooka, moti sakanatha kukwaniritsa zinthu zofunika pa udindo wa utsogoleri. Mwachitsanzo, Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu limanena kuti Mose anati: “Ndine munthu wa zaka zana ndi makumi awiri lerolino; sindikhozanso kutuluka ndi kulowa.” Chimodzimodzinso Baibulo la Malembo Oyera limati: “Sindingathe kukutsogoleraninso.”

Koma lemba la Deuteronomo 34:7, limasonyeza kuti ngakhale kuti Mose anali ndi zaka zambiri, iye sanali wofooka. Limati: “Zaka zake za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lake silinachita mdima, ndi mphamvu yake siidaleka.” Motero Mose anali ndi mphamvu zokwanira kutsogolera mtunduwo, kungoti Yehova sanafune kuti iye apitirize kutero. Zimenezi zikuonekera pa mawu otsatira amene Mose ananena, akuti: “Yehova anati kwa ine, Sudzaoloka Yordano uyu.” Zikuoneka kuti pamenepa Yehova anali kubwereza zimene ananena kumadzi a Meriba.​—Numeri 20:9-12.

Mose anakhala moyo kwa nthawi yaitali ndipo anachita zinthu zambiri zodziwika bwino. Moyo wake ungathe kugawidwa m’mbali zitatu. Kwa zaka 40 iye anakhala ku Igupto, kumene “anaphunzira nzeru zonse za Aaigupto” ndipo anali “wamphamvu m’mawu ake ndi m’ntchito zake.” (Machitidwe 7:20-22) Kwa zaka zina 40 anakhala ku Midyani. Kukhala kumeneko kunam’thandiza kukhala ndi makhalidwe auzimu ofunika kutsogolera anthu a Yehova. Potsiriza, kwa zaka zinanso 40 Mose anatsogolera ndi kulamulira Aisrayeli. Koma tsopano, Yehova anaganiza kuti Yoswa, osati Mose, ndiye atsogolere mtunduwu kuti uwoloke mtsinje wa Yordano n’kulowa mu Dziko Lolonjezedwa.​—Deuteronomo 31:3.

Motero, Baibulo la New World Translation limamasulira mfundo yeniyeni ya Deuteronomo 31:2. Mfundo yake n’njakuti Mose sanapitirize kukhala mtsogoleri wa Israyeli, osati chifukwa chofooka m’thupi mwake, koma chifukwa choti Yehova sanamulole kutero.