Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimba Mtima Kwambiri Chifukwa cha Chikondi

Kulimba Mtima Kwambiri Chifukwa cha Chikondi

 Kulimba Mtima Kwambiri Chifukwa cha Chikondi

“Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.”​—2 TIMOTEO 1:7.

1, 2. (a) Kodi chikondi chingalimbikitse munthu kuchita chiyani? (b) N’chifukwa chiyani kulimba mtima kwa Yesu kunali kwapadera kwambiri?

MWAMUNA ndi mkazi ongokwatirana kumene ankasambira pafupi ndi tauni ina kugombe la kum’mawa kwa Australia. Pamene anali pafupi kuyandama, nsomba yaikulu ya mtundu wa shaki inapita mofulumira kwa mkazi. Molimba mtima kwambiri, mwamunayu anakankhira mkazi wake kumbali n’cholinga choti shaki iphe iyeyo. Pa mwambo wa maliro a mwamunayu, mkazi wamasiyeyo anati: “Anapereka moyo wake chifukwa cha ine.”

2 Inde, chikondi chingalimbikitse anthu kukhala olimba mtima kwambiri. Yesu Kristu anati: “Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” (Yohane 15:13) Pasanadutse ndi tsiku limodzi kuchokera panthawi imene Yesu ananena mawuwa, iye anapereka moyo wake, osati kaamba ka munthu mmodzi, koma anthu onse. (Mateyu 20:28) Ndipo Yesu sanapereke moyo wake mwa kusonyeza kulimba mtima mwadzidzidzi. Iye ankadziwa pasadakhale kuti adzanyozedwa ndi kuchitidwa nkhanza, adzaweruzidwa mosalungama, ndipo adzaphedwa pamtengo wozunzirapo. Iye anakonzekeretsa ophunzira ake zimenezi, ndipo anati: “Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzam’weruza kuti ayenera imfa, nadzam’pereka Iye kwa anthu a mitundu; ndipo adzam’nyoza Iye, nadzam’thira malovu, nadzam’kwapula Iye, nadzamupha.”​—Marko 10:33, 34.

3. Kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kukhala wolimba mtima kwambiri?

3 Kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kusonyeza kulimba mtima kodabwitsa? Chikhulupiriro ndi kuopa Mulungu n’zomwe zinam’thandiza kwambiri. (Ahebri 5:7; 12:2) Koma chofunika kwambiri n’choti Yesu anali wolimba mtima chifukwa ankakonda Mulungu ndi anthu anzake. (1 Yohane 3:16) Ngati tikhala ndi chikondi chotero, kuphatikiza pa chikhulupiriro ndi kuopa Mulungu, ifenso tingasonyeze kulimba mtima konga kwa Kristu. (Aefeso 5:2) Kodi tingakhale bwanji ndi chikondi chotero? Tifunikira kuzindikira Gwero lake.

“Chikondi Chichokera kwa Mulungu”

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndiye Gwero la chikondi?

4 Yehova ndiye chikondicho komanso Gwero lake. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, nam’zindikira Mulungu. Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:7, 8) Motero, munthu angakhale ndi chikondi chonga cha Mulungu ngati ayandikira kwa Yehova mwa kum’dziwa molondola. Ayeneranso kusonyeza kumvera ndi mtima wonse mwa kuchita zimene akudziwazo.​—Afilipi 1:9; Yakobo 4:8; 1 Yohane 5:3.

5, 6. Kodi n’chiyani chinathandiza otsatira a Yesu oyambirira kukhala ndi chikondi chonga cha Kristu?

 5 M’pemphero lake lomaliza ali limodzi ndi atumwi ake 11 okhulupirika, Yesu anasonyeza kugwirizana kwa kudziwa Mulungu ndi kukhala ndi chikondi chochuluka. Iye anati: “Ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.” (Yohane 17:26) Yesu anathandiza ophunzira ake kukhala ndi chikondi chimene chinali pakati pa iye ndi Atate ake, ndipo anasonyeza mwa zonena zake ndi zochita zake kuti dzina la Mulungu limaimira makhalidwe a Mulungu apadera. Motero, Yesu anatha kunena kuti: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.”​—Yohane 14:9, 10; 17:8.

6 Chikondi chonga cha Kristu ndi chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Pa Pentekoste mu 33 C.E. pamene Akristu oyambirira analandira mzimu woyera umene analonjezedwa, iwo sanangokumbukira zinthu zimene Yesu anawaphunzitsa komanso anatha kumvetsa bwino kwambiri tanthauzo la Malemba. Mosakayikira, kudziwa zinthu mwakuya kumeneku kunawonjezera chikondi chawo pa Mulungu. (Yohane 14:26; 15:26) Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Ngakhale pamene moyo wawo unali pangozi, iwo analalikira uthenga wabwino molimba mtima ndi mwachangu.​—Machitidwe 5:28, 29.

Anasonyeza Kulimba Mtima ndi Chikondi

7. Kodi Paulo ndi Barnaba anapirira zotani ali limodzi paulendo wawo waumishonale?

7 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.” (2 Timoteo 1:7) Paulo ankanena zimene zinam’chitikira. Taonani zimene iye ndi Barnaba anakumana nazo ali limodzi paulendo wawo waumishonale. Iwo analalikira mu mizinda yambiri kuphatikizapo Antiokeya, Ikoniyo, ndi Lustra. Mu mzinda uliwonse, anthu ena anakhala okhulupirira, koma ena anakhala otsutsa kwambiri. (Machitidwe 13:2, 14, 45, 50; 14:1, 5) Pamene anali ku Lustra, gulu la anthu okwiya kwambiri linam’ponya miyala Paulo ndipo linam’siya litayesa kuti wafa. “Koma pamene anam’zinga akuphunzirawo, anauka iye, nalowa m’mudzi; m’mawa mwake anatuluka ndi Barnaba kumka ku Derbe.”​—Machitidwe 14:6, 19, 20.

8. Kodi kulimba mtima kumene Paulo ndi Barnaba anali nako kunasonyeza bwanji kuti ankakonda kwambiri anthu?

8 Kodi Paulo ndi Barnaba anachita mantha mpaka kugonja chifukwa choti iyeyo anatsala pang’ono kuphedwa? Ayi ndithu. Atapanga ophunzira angapo ku Derbe, amuna awiriwa “anabwera ku Lustra ndi Ikoniya ndi Antiokeya.” Chifukwa chiyani anatero? Kuti akalimbikitse ophunzira atsopano kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Paulo ndi Barnaba anati: “Tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.” N’zoonekeratu kuti anali olimba mtima chifukwa cha kukonda kwambiri “nkhosa” za Kristu. (Machitidwe 14:21-23; Yohane 21:15-17) Ataika akulu mu mpingo uliwonse watsopano, abale awiriwa anapemphera ndipo “anaikiza iwo kwa Ambuye amene anam’khulupirirayo.”

9. Kodi akulu a ku Efeso anachita chiyani chifukwa choti Paulo ankawakonda?

9 Paulo anali munthu wachikondi ndi wolimba mtima moti Akristu oyambirira ambiri ankamukonda kwambiri. Takumbukirani zimene zinachitika pamsonkhano umene Paulo anachita ndi akulu ochokera ku Efeso, kumene anakhala zaka zitatu ndiponso kumene anakumana ndi chitsutso chachikulu. (Machitidwe 20:17-31) Atawalimbikitsa kuweta nkhosa za Mulungu zimene anaikizidwa, Paulo anagwada pansi limodzi nawo ndipo anapemphera. Ndiyeno, “onsewa analira kwambiri, nam’kupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona, nalira makamaka chifukwa cha mawu adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yake.” Abalewa ankamukonda kwambiri Paulo. Ndithudi, nthawi yoti achoke itakwana, Paulo limodzi ndi omwe ankayenda nawo anadzikakamiza kulekana nawo, chifukwa akuluwo sanafune kuwalola kuti apite.​—Machitidwe 20:36–21:1.

10. Kodi Mboni za Yehova zamakono zasonyeza motani chikondi ndi kulimba mtima kaamba ka wina ndi mnzake?

10 Masiku ano, oyang’anira oyendayenda, akulu pampingo, ndi ena ambiri amakondedwa kwambiri chifukwa cha kulimba mtima komwe amasonyeza posamalira nkhosa za Yehova. Mwachitsanzo, m’mayiko mmene muli nkhondo yapachiweniweni  kapena mmene ntchito yolalikira ili yoletsedwa, oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo amaika moyo ndi ufuluwawo pangozi. Iwo amachita zimenezi kuti achezere mipingo. Mofananamo, Mboni zambiri zavutitsidwa ndi olamulira ankhanza ndi otsatira awo chifukwa chokana kuulula Mboni zinzawo kapena kukana kunena kumene ankachotsa chakudya chawo chauzimu. Mboni zina masauzande ambiri zazunzidwa, kuchitidwa nkhanza, ndipo ngakhale kuphedwa kumene chifukwa sizinasiye kulalikira uthenga wabwino kapena kusiya kupezeka pamisonkhano yachikristu ndi okhulupirira anzawo. (Machitidwe 5:28, 29; Ahebri 10:24, 25) Tiyeni titsanzire chikhulupiriro ndi chikondi cha abale ndi alongo olimba mtimawa.​—1 Atesalonika 1:6.

Chikondi Chanu Chisazirale

11. Kodi Satana amachita nkhondo yauzimu ndi atumiki a Yehova m’njira zotani, ndipo iwo afunikira kuchita chiyani?

11 Pamene Satana anaponyedwa padziko lapansi, analimbikira kulusira atumiki a Yehova chifukwa ‘amasunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.’ (Chivumbulutso 12:9, 17) Njira imodzi imene Mdyerekezi amagwiritsa ntchito ndi chizunzo. Koma nthawi zambiri, njira imeneyi siimuthandiza chifukwa choti imathandiza anthu a Mulungu kukhala Akristu ogwirizana ndi okondana kwambiri ndipo imalimbikitsa ambiri kukhala achangu kwambiri. Njira ina imene Satana amagwiritsa ntchito ndiyo kutikopa chifukwa cha mtima wathu wochimwa. Kuti tipewe machenjera amenewa tifunikira kulimba mtima mwapadera chifukwa nkhondo imeneyi ndi ya mu mtima, ndipo timalimbana ndi zikhumbo zoipa zomwe zili mu mtima wathu ‘wonyenga ndi wosachiritsika.’​—Yeremiya 17:9; Yakobo 1:14, 15.

12. Kodi Satana amagwiritsa ntchito motani “mzimu wa dziko” pofuna kuti tisiye kukonda Mulungu?

12 Chida china champhamvu chimene Satana ali nacho ndi “mzimu wa dziko,” umene umatanthauza makhalidwe kapena maganizo omwe ndi otsutsana kwambiri ndi mzimu woyera wa Mulungu. (1 Akorinto 2:12) Mzimu wa dziko umalimbikitsa umbombo ndi kukonda chuma zimene zili “chilakolako cha maso.” (1 Yohane 2:16; 1 Timoteo 6:9, 10) Ngakhale kuti katundu ndi ndalama si zoipa pazokha, koma ngati tikonda kwambiri zinthu zimenezi kuposa mmene timakondera Mulungu, ndiye kuti Satana watigonjetsa. Mphamvu, kapena kuti “ulamuliro” umene mzimu wa dziko uli nawo, yagona pakuti mzimuwo umakopa matupi athu ochimwa, ndi wonyenga, wankhanza, ndipo mofanana ndi mpweya, umapezeka kulikonse. Musalole mzimu wa dziko kuipitsa mtima wanu.​—Aefeso 2:2, 3; Miyambo 4:23.

13. Kodi kulimba mtima kwathu posunga khalidwe labwino kungayesedwa motani?

13 Koma kuti tikane ndi kupewa mzimu woipa wa dziko, tifunikira kulimba mtima kuti tisunge khaliwe lathu labwino. Mwachitsanzo, kulimba mtima n’kofunika kuti munthu anyamuke ndi kuchoka m’malo oonetsera mafilimu kapena kuti azimitse kompyuta kapena TV imene ikuonetsa  zinthu zoipa. Pamafunika kulimba mtima kuti munthu akane zinthu zoipa zimene anzake akuchita ndiponso kusiya mayanjano oipa. Pamafunikanso kulimba mtima kuti titsate malamulo a Mulungu ndi mfundo zake pamene tikunyozedwa, kaya ndi anzathu a kusukulu, kuntchito, anthu oyandikana nawo, kapena achibale athu.​—1 Akorinto 15:33; 1 Yohane 5:19.

14. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati mzimu wa dziko watilowerera?

14 Motero, n’kofunika kwambiri kuti tilimbitse chikondi chathu pa Mulungu ndi pa abale ndi alongo athu auzimu. Pezani nthawi yopenda zolinga zanu ndi moyo wanu kuti muone ngati penapake mzimu wa dziko wakulowererani. Ngati wakulowererani, ngakhale pang’ono chabe, pempherani kwa Yehova kuti mukhale olimba mtima kuuchotsa ndi kuupewa. Yehova sadzanyalanyaza mapemphero otero ochokera pansi pa mtima. (Salmo 51:17) Ndipo mzimu wake ndi wamphamvu kwambiri kuposa wa dziko.​—1 Yohane 4:4.

Analimba Mtima Pamavuto

15, 16. Kodi chikondi chonga cha Kristu chingatithandize motani kupirira mavuto athu? Perekani chitsanzo.

15 Mavuto ena amene atumiki a Yehova afunika kulimbana nawo amaphatikizapo kupanda ungwiro ndi ukalamba. Zinthu zimenezi nthawi zambiri zimayambitsa matenda, kulumala, kuvutika maganizo, ndi mavuto ena ambiri. (Aroma 8:22) Chikondi chonga cha Kristu chingatithandize kupirira mavuto otero. Taonani chitsanzo cha Namangolwa, amene analeredwa m’banja lachikristu ku Zambia. Ali ndi zaka ziwiri analumala. Iye anati: “Ndinali wamanyazi chifukwa choganiza kuti anthu azidabwa kwambiri akandiona. Koma abale anga auzimu anandithandiza kusiya kuganiza zimenezi. Chifukwa cha zimenezi, ndinasiya kuchita manyazi, ndipo m’kupita kwanthawi ndinabatizidwa.”

16 Ngakhale kuti Namangolwa ali ndi njinga ya opuwala, nthawi zambiri amayenda ndi manja ndi maondo ake pamene ali m’msewu wamchenga. Koma amachita nawo utumiki wa upainiya wothandiza kwa miyezi iwiri chaka chilichonse. Mwininyumba wina analira pamene Namangolwa anam’lalikira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chokhudzidwa kwambiri poona chikhulupiriro ndi kulimba mtima kwa mlongo wathu. Umboni woti Yehova wam’dalitsa kwambiri n’ngwakuti, anthu asanu omwe Namangolwa ankaphunzira nawo Baibulo anabatizidwa, ndipo mmodzi ndi mkulu pampingo. Iye anati: “Nthawi zambiri miyendo yanga imapweteka kwambiri, koma sindilola zimenezi kundilepheretsa kutumikira.” Mlongoyu wangokhala  chabe mmodzi mwa Mboni zambiri padziko lapansi zimene zili ndi matupi ofooka koma ndi zamphamvu mwauzimu chifukwa chokonda Mulungu ndi mnansi. Anthu onse otero ndi ofunika kwambiri pamaso pa Yehova.​—Hagai 2:7.

17, 18. Kodi n’chiyani chimene chimathandiza ambiri kupirira matenda ndi mayesero ena? Tchulani zitsanzo zakwanuko.

17 Matenda aakulu angakhale olefula, ngakhale kuvutitsa maganizo. Mkulu wina pampingo anati: “ Paphunziro la buku limene ndimapezekapo, mlongo wina amadwala matenda a shuga ndi kusagwira ntchito kwa impso, wina ali ndi khansa, alongo awiri ali ndi nyamakazi yoopsa ndipo mlongo wina ali ndi matenda a pakhungu ndi a m’minofu. Nthawi zina amataya mtima. Koma amalephera kufika pamisonkhano kokha ngati adwala kwambiri kapena ali kuchipatala. Onse ndi okhazikika mu utumiki wa kumunda. Iwo amandikumbutsa Paulo, amene ananena kuti: ‘Pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.’ Ndimasirira kwambiri chikondi ndi kulimba mtima kwawo. Mwina matenda awo amawathandiza kuika maganizo pa zolinga zabwino m’moyo ndiponso pa zinthu zimene zili zofunika.”​—2 Akorinto 12:10.

18 Ngati mukuvutika ndi kulumala, matenda, kapena mavuto ena, “pempherani kosaleka” kuti mulandire thandizo kotero kuti musataye mtima. (1 Atesalonika 5:14, 17) N’zoona kuti nthawi zina zinthu zidzakuyenderani bwino koma nthawi zina sizidzatero, koma yesetsani kuika maganizo anu pa zinthu zolimbikitsa zauzimu, makamaka chiyembekezo chathu cha Ufumu chamtengo wapatali. Mlongo wina anati: “Utumiki wa kumunda ndi mankhwala kwa ine.” Kulalikira uthenga wabwino kwa anthu ena kumam’thandiza kuika maganizo ake pa zinthu zolimbikitsa.

Chikondi Chimathandiza Olakwa Kubwerera kwa Yehova

19, 20. (a) Kodi n’chiyani chingathandize anthu omwe alakwa kuti alimbe mtima ndi kubwerera kwa Yehova? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 Anthu ambiri amene afooka mwauzimu kapena amene achita tchimo zimawavuta kwambiri kubwerera kwa Yehova. Koma kulimba mtima kumene akufunikira angakhale nako ngati alapadi ndi kuyambanso kukonda Mulungu. Taganizirani za Mario, * yemwe akukhala ku United States. Mario anasiya mpingo wachikristu, nakhala chidakwa ndiponso ankamwa mankhwala osokoneza bongo, ndipo patapita zaka 20 anamangidwa. Mario anati: “Ndinayamba kuganiza kwambiri za tsogolo langa ndipo ndinayambanso kuwerenga Baibulo. M’kupita kwanthawi, ndinazindikira makhalidwe a Yehova, makamaka chifundo chake, chimene nthawi zambiri ndinkapempha. Nditamasulidwa kundende, ndinasiya kucheza ndi mabwenzi anga akale, ndinkapita ku misonkhano yachikristu, ndipo m’kupita kwanthawi ndinabwezeretsedwa. M’thupi langa, ndikututa zimene ndinafesa, koma ndili ndi chiyembekezo chosangalatsa. Ndikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa cha kundisonyeza chifundo ndi kundikhululukira.”​—Salmo 103:9-13; 130:3, 4; Agalatiya 6:7, 8.

20 Mosakayikira, anthu omwe ali ndi moyo wofanana ndi wa Mario afunikira kuchita khama kuti abwerere kwa Yehova. Koma chikondi chimene angakhalenso nacho mwa kuwerenga Baibulo, kupemphera, ndi kusinkhasinkha, chidzawathandiza kukhala olimba mtima ndi akhama. Mario nayenso analimbikitsidwa ndi chiyembekezo cha Ufumu. Inde, kuwonjezera pa chikondi, chikhulupiriro, ndi kuopa Mulungu, chiyembekezo chingatithandize kwambiri pa moyo wathu. M’nkhani yotsatira, tidzakambirana mwatsatanetsatane mphatso yauzimu yofunika kwambiri imeneyi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Dzina lasinthidwa.

 Kodi Mungayankhe?

• Kodi chikondi chinathandiza motani Yesu kukhala wolimba mtima kwambiri?

• Kodi kukonda abale awo kunathandiza motani Paulo ndi Barnaba kukhala olimba mtima kwambiri?

• Kodi Satana akugwiritsa ntchito chiyani kuti athetse chikondi chachikristu?

• Kodi kukonda Yehova kungatithandize kukhala olimba mtima kuti tipirire mavuto otani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Kukonda anthu kunathandiza Paulo kukhala wolimba mtima kuti athe kupirira

[Chithunzi patsamba 24]

Kulimba mtima n’kofunika kuti titsatire miyezo ya Mulungu

[Chithunzi patsamba 24]

Namangolwa Sututu