Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Sitingaleke Kulankhula za Yesu’

‘Sitingaleke Kulankhula za Yesu’

 “Tiyenera Kumvera Mulungu Koposa Anthu”

‘Sitingaleke Kulankhula za Yesu’

MUNALI mu 33 C.E., ndipo malo ake anali chipinda chochititsa kaso kwambiri chimene khoti lalikulu la Ayuda linkazengeramo milandu, ku Yerusalemu. M’chochitika chimenechi, bwalo la akulu, lomwe limatchedwanso kuti Sanihedirini, linali litatsala pang’ono kuti liyambe kuzenga mlandu otsatira 12 a Yesu Kristu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anakhala akulalikira za Yesu. Aka kanali kachiwiri kuti mtumwi Petro ndi mtumwi Yohane azengedwe mlandu m’bwaloli. Koma kwa atumwi ena khumi amene anali nawo kanali koyamba.

Mkulu wa ansembe analankhula ndi atumwi khumi ndi awiriwo ponena za zimene khotilo linawalamula panthawi ina m’mbuyomo. Panthawi imeneyo, atawalamula kuti aleke kuphunzitsa za Yesu, mtumwi Petro ndi mtumwi Yohane anayankha kuti: “Weruzani, ngati n’kwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu; pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.” Ndipo atapemphera kuti awalimbitse mtima, ophunzira a Yesu anapitiriza kulalikira uthenga wabwino.​—Machitidwe 4:18-31.

Atadziwa kuti chiopsezo chake choyambacho sichinaphule kanthu, pozenga mlandu wachiwiriwu mkulu wa ansembe anati: “Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.”​—Machitidwe 5:28.

Anatsimikiza Mtima Kumvera Mulungu

Poyankha molimba mtima, Petro ndi atumwi ena anati, “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Zoonadi, m’malo momvera anthu, tiyenera kumvera Yehova ngati zofuna za anthu zikutsutsana ndi malamulo ake. *

Mawu a atumwi amenewa otsimikiza kuti akuimira Mulungu ayenera kuti anakhutiritsa a bwalo la akulu. Akanafunsidwa ponena za kumvera Mulungu, atsogoleri a Ayuda amenewa akanayenera kuyankha onse pamodzi kuti: “Mverani Mulungu.” Ndiiko komwe, kodi iwo sankakhulupirira kuti Mulungu ndi Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse?

Mwachionekere moimira atumwi onsewo, Petro ananena kuti pankhani zokhudza utumiki wawo, iwo amamvera Mulungu koposa anthu. Motero, iye anasonyeza kuti sanayenere kuimbidwa mlandu wophwanya malamulo womwe atumwiwo ankaimbidwa. Kuchokera m’mbiri ya mtundu wawo, mamembala a bwalo la akululo ankadziwa kuti pankakhala nthawi zina pamene kunali koonekeratu kuti m’poyenera kumvera Mulungu koposa anthu. Anamwino awiri ku Igupto amene anaopa Mulungu, osati Farao, sanaphe ana aamuna a Ahebri. (Eksodo 1:15-17) Mfumu Hezekiya inamvera Yehova, osati Mfumu Sanakeribu, pamene inakakamizidwa kuti ingopereka mzinda kwa mdani wakeyo. (2 Mafumu 19:14-37) Malemba Achihebri, amene a bwalo la akulu ankawadziwa bwino, amatsindika kuti Yehova amayembekezera kuti anthu ake azimumvera.​—1 Samueli 15:22, 23.

Anafupidwa Chifukwa Chomvera

Zikuoneka kuti mmodzi wa mamembala a khoti lalikululi anakhudzidwa ndi mawu akuti,  “tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” Gamaliyeli, woweruza wolemekezeka kwambiri m’khotili, analimbikitsa oweruza anzake kuti amvere malangizo ake anzeru omwe anawauza atatsala okha m’chipindamo. Popereka zitsanzo zakale, Gamaliyeli anasonyeza kuti n’kupanda nzeru kuletsa ntchito ya atumwi. Ndipo anatsiriza n’kunena kuti: “Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; . . . kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.”​—Machitidwe 5:34-39.

Mawu anzeru a Gamaliyeli anakhutiritsa akuluakulu a khotili kuti amasule atumwiwo. Ngakhale kuti anawakwapula, atumwiwo sanachite mantha chifukwa chokumana ndi zimenezi. M’malo mwake, Baibulo limati: “Masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.”​—Machitidwe 5:42.

Atumwiwo anadalitsidwa kwambiri chifukwa chonena molimba mtima kuti ulamuliro wa Mulungu ndiwo waukulu kuposa wina uliwonse. Akristu oona masiku ano ali ndi mtima wofanana ndi umenewo. Mboni za Yehova zimapitiriza kuyang’ana kwa Yehova monga Wolamulira Wamkulu. Zikalamulidwa kuchita zinthu zosiyana ndi malamulo a Mulungu, zimayankha mofanana ndi mmene anayankhira atumwi aja kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Onani Kalendala ya 2006 ya Mboni za Yehova, mwezi wa September/​October.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 9]

KODI MUNADZIFUNSAPO?

Kodi Luka, mmodzi wa anthu amene analemba nawo Baibulo, anadziwa bwanji zimene Gamaliyeli analankhula ndi anzake a m’bwalo la akulu atatsalamo okhaokha? Mwina Mulungu ndi amene anaulula mwachindunji mawu a Gamaliyeli kwa Luka. N’kutheka kuti Paulo (yemwe kale anali mmodzi wa ophunzira a Gamaliyeli) anadziwitsa Luka zimene Gamaliyeli analankhula. Kapena mwina Luka anafunsa mmodzi wa oweruza m’khotili yemwe anagwirizana ndi maganizo a atumwiwo.