Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chidindo cha Yukali

Chidindo cha Yukali

 Chidindo cha Yukali

M’ZAKA za m’ma 600 B.C.E., Nebukadinezara wolamulira wa Akasidi, anagonjetsa Yerusalemu, kutentha mzindawo, ndi kugumula makoma ake. Anagwira ndi kukolowola maso Zedekiya, mfumu ya Ayuda. Ndiponso, ‘Mfumu ya Babuloyi inapha aufulu onse a Yuda.’​—Yeremiya 39:1-8.

Mmodzi wa aufulu a Yuda, kapena kuti akulu, amene mwachidziwikire anaphedwa ndi Ababulo anali Yukali, mwana wa Selemiya. Panopa kwapezeka mfundo zina zonena za munthu wa m’Baibulo ameneyu. Koma, tisanakambirane za munthu ameneyu, tiyeni tione zimene Malemba amanena zokhudza Yukali ndi zochitika m’masiku ake.

“Sadzakuposa”

Yehova anatuma mneneri Yeremiya kuti akapereke uthenga wa chiweruzo cha Yuda ndi Yerusalemu. Mulungu anauza Yeremiya kuti mafumu a Yuda, akulu ake, ndi ansembe ake, ndi dziko lonse “adzamenyana” naye. “Koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe,” anatero Yehova.​—Yeremiya 1:17-19.

Pamene Ababulo ankalanda likulu la Yuda, Yerusalemu, Mfumu Zedekiya inatumiza kawiri mithenga kwa Yeremiya kuti idziwe ngati Nebukadinezara achoke mu mzindawo ndi kupempha mneneriyo kuti apemphere kuti mdaniyo achoke mumzindawo. Mmodzi mwa nthumwi za mfumuyi anali Yukali amene ankadziwikanso ndi dzina lakuti Yehukali. Uthenga umene Mulungu anapatsa Yeremiya unali wakuti Ababulo, kapena kuti Akasidi, adzawononga mzindawo. Munthu aliyense wa ku Yerusalemu amene adzatsale mumzindawo adzafa ndi njala, mliri, ndiponso lupanga. Koma amene adzatuluke kupita kwa Akasidi adzapulumuka. Mawu a Yeremiya anakwiyitsa kwambiri akulu a Yuda.​—Yeremiya 21:1-10; 37:3-10; 38:1-3.

Yukali anali mmodzi mwa akulu amene analimbikitsa Zedekiya kuti: “Munthu uyu [Yeremiya] aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo.” Yukali woipayu, analinso pagulu la anthu amene anaponya Yeremiya m’chitsime cha matope, mmene mneneriyu anatulutsidwamo pambuyo pake. (Yeremiya 37:15; 38:4-6) Chifukwa chakuti anamvera Yehova, Yeremiya anapulumuka pamene Yerusalemu ankawonongedwa, koma Yukali mwachionekere anafa pamene dongosolo la Ayuda limene ankalikhulupirira linawonongedwa.

Mbali Yochititsa Chidwi ya Nkhaniyi

Tinganene kuti mfundo zina zokhudza Yukali “zinalembedwa” posachedwapa ku Yerusalemu m’chaka cha 2005. Ofukula za m’mabwinja ankakumba malo ena pamene ankayembekezera kupezapo nyumba yachifumu ya Mfumu Davide. Anapeza chinthu china chachikulu chimene chinamangidwa ndi miyala chomwe akuchiganizira  kuti chinawonongedwa pamene Ababulo ankalanda Yerusalemu m’nthawi ya Yeremiya.

Kaya imeneyi inali nyumba yachifumu ya Davide kapena ayi sizikudziwika mpaka pano. Komabe, pa zinthu zimene ofukula za m’mabwinjawo anapeza, anazindikirapo kachidindo kadongo kakakulu sentimita imodzi, kamene kasonyezedwa patsamba 14. Kanagwiritsidwa ntchito kumatira mapepala ofunika amene anawola kalekale. Ndipo pakachidindoko pali mawu akuti: “Mwiniwake ndi Yehukali mwana wa Selemiyahu mwana wa Shovi.” Mwachionekere, mawu amenewa anasindikizidwa ndi chidindo cha mdani wa Yeremiya uja Yehukali, kapena kuti Yukali, mwana wa Selemiya.

Wofukula za m’mabwinja wina, Eilat Mazar, amene anatanthauzira mawuwo, analemba kuti kuchokera pa Gemariya, mwana wa Safani, Yehukali ndiye “nduna yachiwiri” yokha pa nduna zimene mayina awo aoneka pa mawu a pazidindo zopezeka m’Mudzi wa Davide. *

Kukhulupirira Mawu a Mulungu sikudalira kupeza chinthu chinachake chakale chokumbidwa pansi ayi; koma kukwaniritsidwa kwa ulosi wouziridwa ndiwo maziko enieni achikhulupiriro cha m’Baibulo. Mbiri imasonyeza kuti Yeremiya ananeneratu molondola za kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Mapeto ochititsa manyazi a adani a Yeremiya ayenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu kuti tikakhala okhulupirika monga Yeremiya, adani athu ‘sadzatiposa chifukwa Yehova ali ndi ife.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Kuti mudziwe zambiri za Gemariya ndi Safani, onani nkhani yakuti “Kodi Mumam’dziwa Safani ndi Banja Lake?” mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 2002, tsamba 19 mpaka 22.

[Chithunzi patsamba 15]

Yeremiya sanagonje pokakamizidwa kuti achepetse mphamvu ya uthenga wa Mulungu

[Mawu a Chithunzi patsamba 14]

Gabi Laron/​Institute of Archaeology/​ Hebrew University ©Eilat Mazar